Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 5

Samueli Anapitiriza Kuchita Zinthu Zabwino

Samueli Anapitiriza Kuchita Zinthu Zabwino

Kuyambira ali mwana, Samueli ankakhala komanso kugwira ntchito kuchihema. Nthawi imeneyo anthu ankapita kuchihema kuti akalambire Yehova. Kodi ukudziwa zimene zinachitika kuti Samueli ayambe kukhala kuchihema? Poyamba, tiye tikambirane kaye za mayi ake a Samueli, omwe dzina lawo linali Hana.

Kwa nthawi yaitali Hana ankafuna atakhala ndi mwana koma anali wosabereka. Ndiye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Hana analonjeza kuti akakhala ndi mwana wamwamuna, adzamupereka kuti azikakhala komanso kugwira ntchito kuchihema. Yehova anayankha pemphero lake ndipo anakhaladi ndi mwana wamwamuna. Dzina lake linali Samueli. Mwanayo atakwanitsa zaka zitatu kapena zinayi, Hana anachita zimene analonjeza. Anatenga Samueli n’kukamupereka kuchihema kuti azikatumikira Mulungu.

Pa nthawi imeneyo mkulu wa ansembe kuchihemako anali Eli. Ana ake awiri ankagwiranso ntchito komweko. Usaiwale kuti chihema anali malo olambirirako Mulungu ndipo anthu okhala kumeneko ankafunika kuchita zinthu zabwino. Koma ana a Eli ankachita zinthu zoipa kwambiri ndipo Samueli ankaona zimene ana a Eli ankachita. Kodi nayenso Samueli anayamba kuchita zinthu zoipa ngati ana a Eli?— Ayi. Iye anapitiriza kuchita zinthu zabwino zimene makolo ake anamuphunzitsa.

Kodi ukuganiza kuti Eli anafunika kuchita chiyani ndi ana akewo?— Ankafunika kuwalanga komanso kuwaletsa kuti asapitirize kugwira ntchito panyumba ya Mulungu. Koma Eli sanachite zimenezo, choncho Yehova anakwiyira Eli ndi ana ake. Kenako Yehova anakonza zoti awalange.

Samueli anafotokozera Eli uthenga umene Yehova anamuuza

Tsiku lina usiku Samueli akugona, anamva munthu wina akumuitana kuti: ‘Samueli!’ Iye anathamanga kupita kwa Eli koma Eli anamuuza kuti: ‘Sindinakuitane.’ Zimenezi zinachitikanso maulendo ena awiri. Zitachitikanso ulendo wachitatu, Eli anauza Samueli kuti akamvanso kuitana anene kuti: ‘Lankhulani Yehova, ndikumva.’ Samueli anachitadi zimene Eli anamuuza. Kenako Yehova anauza Samueli kuti: ‘Umuuze Eli kuti ndilanga banja lake chifukwa cha zoipa zimene akhala akuchita.’ Kodi ukuganiza kuti zinali zophweka kwa Samueli kuuza Eli uthenga umenewu?— Ayi, zinali zovuta. Komabe Samueli anachita zimene Yehova anamuuza. Zimene Yehova ananena zinachitikadi. Ana a Eli anaphedwa ndipo Eli nayenso anafa.

Pamenepatu Samueli ndi chitsanzo chabwino kwa ifeyo. Iye anachita zinthu zabwino ngakhale kuti ankaona anthu ena akuchita zinthu zoipa. Kodi iweyo waphunzirapo chiyani? Kodi udzapitiriza kuchita zinthu zabwino ngati Samueli? Ukamachita zinthu zabwino udzasangalatsa Yehova ndiponso makolo ako.

WERENGANI MAVESI AWA