Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: Mlongo yemwe anali kopotala akulalikira ku Korea, mu 1931; Kumanja: Kulalikira m’chinenero chamanja ku Korea masiku ano

GAWO 2

Kulalikira za Ufumu​—Kufalitsa Uthenga Wabwino Padziko Lonse Lapansi

Kulalikira za Ufumu​—Kufalitsa Uthenga Wabwino Padziko Lonse Lapansi

TAYEREKEZERANI kuti mwakonzekera kuti mulowe muutumiki tsiku limene simupita kuntchito. Mukukayikira pang’ono chifukwa mukumva kutopa ndipo mukungofuna kupumula. Ndiyeno mukupemphera kuti Mulungu akupatseni mphamvu kenako mukunyamuka. Mukulowa muutumiki ndi mlongo wokhulupirika wachikulire yemwe ndi wokoma mtima komanso akupirira mavuto ambiri. Zimenezi zikukukhudzani mtima kwambiri. Pamene mukulalikira kunyumba ndi nyumba, mukukumbukira kuti abale ndi alongo anu padziko lonse lapansi akugwiranso ntchito yomweyi. Abale ndi alongowa akugawira mabuku ofanana ndi amene inuyo mukugawira komanso akugwiritsa ntchito malangizo amene inunso mumalandira. Pamene mukubwerera kunyumba mukuona kuti mwalimbikitsidwa kwambiri ndipo mukusangalala kuti munasankha kulowa muutumiki.

Panopa ntchito yaikulu ya Ufumu wa Mulungu ndi kulalikira. Yesu analosera kuti m’masiku otsiriza ntchito yolalikira izidzachitika padziko lonse. (Mat. 24:14) Kodi ulosi umenewu wakwaniritsidwa bwanji? M’gawo limeneli tikambirana zimene anthu akhala akuchita, njira zimene akhala akutsatira komanso zipangizo zimene zathandiza kuti anthu ambiri padziko lonse aone kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 6

Anthu Amene Akulalikira​—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa

N’chiyani chinachititsa Yesu kukhulupirira kuti m’masiku otsiriza adzakhala ndi gulu la anthu amene adzadzipereka kugwira ntchito yolalikira? Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mukufuna Ufumu choyamba?

MUTU 7

Njira Zolalikirira​—⁠Ankagwiritsa Ntchito Njira Zosiyanasiyana Kuti Anthu Amve Uthenga

Dziwani njira zina zimene atumiki a Yehova akhala akugwiritsa ntchito kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu ambiri mapeto asanafike.

MUTU 8

Zinthu Zogwiritsa Ntchito Polalikira​​—⁠Kukonza Mabuku Ogwiritsa Ntchito Polalikira Padziko Lonse

Kodi ntchito yomasulira magazini ndi mabuku athu imasonyeza bwanji kuti Mfumu ikutsogolera pogwira ntchitoyi? Fotokozani mfundo zonena za mabuku athu zimene zikukutsimikizirani kuti Ufumuwu ndi weniweni.

MUTU 9

Zotsatira za Ntchito Yolalikira​—“M’mindamo Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”

Yesu anathandiza ophunzira kudziwa mfundo ziwiri zofunika kwambiri pa ntchito yaikulu yokolola. Kodi mfundo ziwirizi zikutikhudza bwanji masiku ano?