Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 13

Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti

Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti

CHOLINGA CHA MUTUWU

Monga mmene Yesu ananenera, maboma komanso atsogoleri azipembedzo amakhazikitsa malamulo kuti alepheretse ntchito yathu yolalikira

1, 2. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo anachita chiyani pofuna kuletsa ntchito yolalikira, nanga atumwi anatani? (b) N’chifukwa chiyani atumwi sanamvere atawaletsa kulalikira?

 MPINGO wachikhristu wa ku Yerusalemu unakhazikitsidwa pa Pentekosite mu 33 C.E. Koma patangopita milungu yowerengeka mpingowu unayamba kukumana ndi mavuto. Satana anaona kuti imeneyi inali nthawi yabwino yoti awononge mpingowu chifukwa unali usanakhazikike. Iye anachititsa atsogoleri achipembedzo kuti aletse ntchito yolalikira za Ufumu. Komabe, atumwi anapitiriza kulalikira molimba mtima ndipo zimenezi zinachititsa kuti amuna ndi akazi ambiri akhale “okhulupirira Ambuye.”​—Mac. 4:18, 33; 5:14.

Atumwi anasangalala “chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu”

2 Chifukwa chokwiya ndi zimenezi, otsutsawo anayambanso kuzunza mpingo wachikhristu ndipo anachititsa kuti atumwi onse atsekeredwe m’ndende. Koma usiku mngelo wa Yehova anatsegula zitseko za ndende ndipo pamene kunkacha, atumwi anayambiranso kugwira ntchito yolalikira. Apanso atumwiwo anamangidwa n’kupita nawo kwa olamulira komwe anaimbidwa mlandu wophwanya lamulo lowaletsa kulalikira. Koma iwo anayankha molimba mtima kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” Olamulirawo atamva zimenezi anakwiya kwambiri moti ankafuna “kungowapha.” Zinthu zitafika povuta, mphunzitsi wina wa Chilamulo wolemekezeka, dzina lake Gamaliyeli, anachenjeza olamulirawo kuti: “Musamale . . . Alekeni amuna amenewa musalimbane nawo.” N’zodabwitsa kuti olamulirawo anamvera mawu ake ndipo anamasula atumwiwo. Kodi atumwi okhulupirikawa anachita chiyani? Mopanda mantha “anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.”​—Mac. 5:17-21, 27-42; Miy. 21:1, 30.

3, 4. (a) Kodi Satana wakhala akugwiritsa ntchito njira iti polimbana ndi anthu a Mulungu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu uno ndi m’mitu iwiri yotsatira?

3 Mlandu umenewu unapita kuti khoti mu 33 C. E., ndipo aka kanali koyamba kuti olamulira aletse ntchito ya mpingo wachikhristu. (Mac. 4:5-8; 16:20; 17:6, 7) Masiku anonso, Satana amachititsa anthu amene amatsutsa kulambira koona kuti azilimbikitsa anthu olamulira kukhazikitsa malamulo oletsa ntchito yathu yolalikira. Otsutsawa amaimba mlandu anthu a Mulungu kuti amaphwanya malamulo. Mwachitsanzo, amatiimba mlandu wakuti ndife osokoneza mtendere, oukira boma komanso wakuti kugawira mabuku kumene timachita ndi bizinezi. Abale akaona kuti n’zoyenera amapita kukhoti kuti akatsutse mabodza amenewa. Kodi zinthu zawayendera bwanji? Kodi zigamulo zimene makhoti anapereka zaka zambiri zapitazo zimakukhudzani bwanji inuyo panokha? Tiyeni tione mmene milandu ina inayendera kukhoti komanso mmene yathandizira “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.”​—Afil. 1:7.

4 M’mutu umenewu tikambirana zimene tachita poteteza ufulu wathu kuti tizitha kulalikira. M’mitu iwiri yotsatira tiona milandu ina imene tinapita nayo kukhoti chifukwa chosafuna kukhala mbali ya dziko komanso kuti tipitirize kutsatira mfundo za Ufumu.

Kodi Ndi Osokoneza Mtendere Kapena Ogwira Ntchito Yolalikira za Ufumu wa Mulungu Mokhulupirika?

5. N’chifukwa chiyani olalikira za Ufumu ankamangidwa m’zaka za m’ma 1930, nanga abale amene ankatsogolera gulu pa nthawiyo anachita chiyani?

5 M’zaka za m’ma 1930, akuluakulu a boma komanso oyang’anira mizinda m’dziko la America anayamba kukakamiza a Mboni za Yehova kuti azikhala ndi chikalata chochokera ku boma kapena kuti laisensi yowavomereza kugwira ntchito yolalikira. Koma abale athu sanapite ku boma kukapeza malaisensi chifukwa ankadziwa kuti akhoza kulandidwa laisensiyo nthawi ina iliyonse zomwe zingachititse kuti asiye kugwira ntchito yolalikira. Abalewa ankakhulupiriranso kuti palibe boma limene lili ndi mphamvu yoletsa anthu kumvera lamulo limene Yesu anapereka kwa Akhristu loti azilalikira za uthenga wa Ufumu. (Maliko 13:10) Chifukwa cha zimenezi abale ambiri anamangidwa. Pofuna kuthandiza abale ndi alongo, abale amene ankatsogolera gulu pa nthawiyo anaganiza zopititsa milanduyi kukhoti. Iwo ankafuna kusonyeza kuti boma laika malamulo omwe akuphwanya ufulu wopembedza wa Mboni za Yehova. Ndiyeno mu 1938, munachitika nkhani ina yomwe chigamulo chake chinathandiza poweruza nkhani zina. Kodi panachitika nkhani yotani?

6, 7. Kodi banja la a Cantwell linakumana ndi zotani?

6 Lachiwiri m’mawa pa April 26, 1938, M’bale Newton Cantwell, wazaka 60, ndi mkazi wake Esther komanso ana awo, omwe mayina awo ndi Henry, Russell ndi Jesse, anapita kukalalikira mumzinda wa New Haven, ku Connecticut. Onsewa anali apainiya apadera ndipo ngakhale kuti ankafuna kukalalikirako tsiku limodzi, ankadziwa kuti akhoza kukhalako kwa masiku angapo chifukwa anali atamangidwapo maulendo angapo ndipo ankadziwa kuti ulendowu akhoza kumangidwanso. Komabe zimenezi sizinachititse banjali kusiya kugwira ntchito yolalikira za Ufumu. Pa ulendowu anatenga magalimoto awiri. M’bale Newton ankayendetsa galimoto yodzaza mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo ndi magalamafoni. Mwana wawo Henry, yemwe anali ndi zaka 22, ankayendetsa galimoto yomwe inali ndi zokuzira mawu padenga lake. Koma atangolalikira kwa maola ochepa apolisi anawaimitsa.

7 Russell, yemwe anali ndi zaka 18, ndi amene anali woyamba kumangidwa, kenako bambo ake ndi mayi ake. Jesse, yemwe anali ndi zaka 16, ali chapatali anaona makolo ake ndi mchimwene wake akutengedwa ndi apolisi. Chifukwa chakuti Henry ankalalikira mbali ina ya tawuniyi, Jesse anatsala yekhayekha ndipo anapitiriza kulalikira pogwiritsa ntchito galamafoni. Azibambo awiri akatolika amene anakumana ndi Jesse anayamba kumvetsera nkhani ya M’bale Rutherford ya mutu wakuti “Adani.” Koma ali mkati momvetsera nkhaniyi azibambowo anakwiya kwambiri moti ankafuna kum’menya. Jesse anangochokapo mwakachetechete koma pasanapite nthawi yaitali nayenso anagwidwa ndi wapolisi wina. Apolisi sanaimbe mlandu Mlongo Cantwell. Anaimba mlandu M’bale Cantwell ndi ana ake koma onse anatuluka pa belo tsiku lomwelo.

8. N’chifukwa chiyani khoti linapeza Jesse Cantwell kuti ndi wolakwa pa mlandu woti anali wosokoneza mtendere?

8 Patapita miyezi ingapo, m’mwezi wa September 1938, banja la a Cantwell linakaonekera kubwalo la milandu mumzinda wa New Haven. Russell, Jesse ndi M’bale Newton anawapeza ndi mlandu wopemphetsa ndalama popanda laisensi. Ngakhale kuti Jesse anachita apilo mlanduwu kukhoti lalikulu la ku Connecticut, anapezekabe wolakwa chifukwa ankamuganizira kuti ankasokoneza mtendere. N’chifukwa chiyani anapereka chigamulo chimenechi? Chifukwa chakuti azibambo awiri akatolika aja anapereka umboni m’khoti woti nkhani imene anamvetsera inkanyoza chipembedzo chawo komanso inawakwiyitsa kwambiri. Pofuna kusonyeza kuti khotili linali litapereka chigamulo cholakwika, abale amene ankatsogolera gulu anachita apilo mlanduwu ku Khoti Lalikulu m’dziko la America.

9, 10. (a) Kodi Khoti Lalikulu la ku America linapereka chigamulo chotani pa mlandu wa banja la a Cantwell? (b) Kodi chigamulo chimenechi chikutithandiza bwanji masiku ano?

9 Kuyambira pa March 29, 1940, Woweruza Milandu Wamkulu, dzina lake Charles E. Hughes, pamodzi ndi oweruza ena 8 anamvetsera zimene loya woimira Mboni za Yehova, yemwenso anali m’bale, dzina lake Hayden Covington, ananena. a Loya woimira boma la Connecticut anapereka umboni wosonyeza kuti Mboni za Yehova ndi anthu ovutitsa. Atamaliza kupereka umboniwu, mmodzi mwa oweruza mlanduwu anamufunsa kuti: “Kodi si zoona kuti anthu ambiri sankasangalala ndi uthenga umene Khristu Yesu ankalalikira?” Poyankha loya wa bomayo anati: “Ndi zoona, ndipo ngati ndikukumbukira bwinobwino, Baibulo limanenanso zimene zinachitikira Yesu chifukwa cholalikira uthengawo.” Zimene ananenazi zinali zochititsa chidwi kwambiri. Ponena mawu amenewa, loya wa bomayo mosadziwa ankatanthauza kuti Mboni za Yehova zili kumbali ya Yesu ndipo boma lili kumbali ya anthu amene anaimba mlandu Yesu. Pa May 20, 1940, oweruza onse a ku Khoti Lalikululi anagamula mlanduwu mokomera Mboni za Yehova.

Hayden Covington (kutsogolo, pakati), Glen How (kumanzere), ndiponso anthu ena akutuluka m’khoti atawina mlandu

10 Kodi zimene khotili linagamula zinathandiza bwanji? Zinateteza komanso kuthandiza kuti akuluakulu aboma kapenanso oyang’anira mizinda asamaike malamulo olepheretsa anthu kukhala ndi ufulu wa chipembedzo. Kuwonjezera pamenepo, khotili linapezanso kuti zimene Jesse ankachita “sizinkasokoneza mtendere.” Choncho, chigamulo chimenechi chinatsimikizira kuti anthu a Mboni za Yehova sasokoneza mtendere. Pamenepatu zinthu zinawayendera bwino kwambiri atumiki a Mulungu. Kodi chigamulo chimenechi chikutithandiza bwanji masiku ano? M’bale wina yemwe ndi loya ananena kuti: “Ufulu umene tili nawo wopembedza mopanda mantha kuti anthu ena akhoza kukhazikitsa malamulo otiletsa kulambira kapena kulalikira, ukuthandiza Mboni za Yehovafe masiku ano kuti tiziuza ena uthenga wopatsa chiyembekezo m’madera amene tikukhala.”

Kodi Ndi Oukira Boma Kapena Olengeza Uthenga wa Choonadi?

N’zomvetsa Chisoni Kuona Chidani Chachikulu Chimene Boma la Quebec Lili Nacho pa Mulungu ndi Khristu Komanso pa Ufulu wa Anthu

11. Kodi abale athu a ku Canada anagwira ntchito yapadera yotani, ndipo n’chifukwa chiyani anagwira ntchito imeneyi?

11 M’zaka za m’ma 1940, ntchito ya Mboni za Yehova inayamba kutsutsidwa kwambiri m’dziko la Canada. Pofuna kuthandiza anthu kudziwa kuti boma la Canada linkaphwanya ufulu wa chipembedzo, mu 1946 abale athu anagwira ntchito yapadera kwa masiku 16 yogawira kapepala ka mutu wakuti, N’zomvetsa Chisoni Kuona Chidani Chachikulu Chimene Boma la Quebec Lili Nacho pa Mulungu ndi Khristu Komanso pa Ufulu wa Anthu (Quebec’s Burning Hate for God and Christ and Freedom Is the Shame of All Canada). Kapepalaka kanafotokoza mwatsatanetsatane zinthu zachipolowe zimene atsogoleri achipembedzo anayambitsa, nkhanza za apolisi ndiponso zinthu zina zankhanza zimene anthu ankachitira abale athu m’dera la Quebec. Kapepalaka kananena kuti: “Anthu a Mboni za Yehova akungomangidwa popanda zifukwa zenizeni. Panopa milandu yokwana 800 yokhudza Mboni za Yehova siikuzengedwa m’khoti la Greater Montreal.”

12. (a) Kodi anthu otsutsa anatani ataona kapepala komwe abale athu ankagawira? (b) Kodi abale athu anaimbidwa mlandu wotani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

12 Nduna yaikulu ya m’dera la Quebec, dzina lake Maurice Duplessis, yomwe inkagwirizana kwambiri ndi Kadinala wa tchalitchi cha Katolika, dzina lake Villeneuve, itaona kapepalaka inalengeza kuti a Mboni za Yehova “akhaulitsidwe kwambiri.” Zimenezi zinachititsa kuti chiwerengero cha milandu imene inali kukhoti chiwonjezeke, kuchoka pa 800 kufika pa 1,600. Mlongo wina yemwe anali mpainiya ananena kuti: “Apolisi anatimanga maulendo ambirimbiri moti sindingakumbukire kuti anatimanga kangati.” Abale ndi alongo amene anamangidwa akugawira timapepalati ankaimbidwa mlandu wofalitsa “mapepala olimbikitsa anthu kuukira boma.” b

13. Kodi anthu oyamba kuimbidwa mlandu woukira boma ku Canada anali ndani, ndipo khoti linaweruza bwanji mlanduwu?

13 Mu 1947, M’bale Aimé Boucher ndi ana ake aakazi, Gisèle wazaka 18 ndi Lucille wazaka 11, anali anthu oyamba kuweruzidwa kukhoti pa mlandu woukira boma. Anawagwira akugawira kapepala ka Chidani Chachikulu Chimene Boma la Quebec Lili Nacho pafupi ndi munda wawo womwe unali m’dera lamapiri chakum’mwera kwa mzinda wa Quebec. Aliyense ankaona kuti sizoona kuti M’bale Boucher angaukire boma kapena kusokoneza mtendere chifukwa anali munthu wofatsa komanso wosauka ndipo ankangolima m’munda mwake osayambana ndi anthu. Ankapita m’tawuni mwa apo ndi apo atakwera ngolo yokokedwa ndi mahatchi. Koma banja lake linakumana ndi mavuto ambiri amene anafotokozedwa pakapepala kameneka. Jaji amene ankaweruza milandu yawo ankadana kwambiri ndi Mboni za Yehova moti anakana umboni wonse wosonyeza kuti banja la a Boucher linali losalakwa. M’malomwake anagwirizana ndi maloya a boma amene ankanena kuti banjali ndi lolakwa chifukwa kapepalaka kankayambitsa chisokonezo. Choncho zimene jajiyo anachita zinasonyeza kuti n’kulakwa kunena zoona. Aimé ndi Gisèle anatsekeredwa m’ndende pa mlandu wolimbikitsa anthu kuukira boma ndipo ngakhale kuti Lucille anali wamng’ono anamutsekera m’ndende kwa masiku awiri. Koma abale anapanga apilo mlanduwu ku Khoti Lalikulu la ku Canada ndipo khotili linavomera kumva mlanduwo.

14. Kodi abale ndi alongo a ku Quebec ankachita chiyani pa zaka zonse zimene ankazunzidwa?

14 Pa nthawi yonseyi, abale ndi alongo a ku Quebec anapitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu ngakhale kuti anthu ankawachitira zankhanza. Patadutsa zaka 4 kuchokera m’chaka cha 1946, chomwe ndi chaka chimene anayamba kugawira kapepala kaja, chiwerengero cha Mboni ku Quebec chinawonjezeka kuchoka pa 300 kufika pa 1,000. c

15, 16. (a) Kodi Khoti Lalikulu la ku Canada linagamula bwanji mlandu wa a Boucher? (b) Kodi chigamulo chimenechi chinathandiza bwanji abale athu komanso anthu ena?

15 Mu June 1950, akuluakulu onse oweruza milandu ku Khoti Lalikulu la ku Canada, okwana 9, anamvetsera mlandu wa Aimé Boucher. Mlanduwu unatenga miyezi 6 chigamulo chisanaperekedwe ndipo pa December 18, 1950, khotili linagamula mlanduwu mokomera Mboni za Yehova. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? M’bale Glen How, yemwe anali loya woimira Mboni za Yehova pa mlanduwu, anafotokoza kuti khotili linavomereza mfundo imene iyeyo ananena yoti munthu angaimbidwe mlandu woukira boma ngati akulimbikitsa ena kuchita zachiwawa kapena ngati akulimbikitsa ena kuukira boma. Koma kapepalaka “sikankalimbikitsa anthu kuchita zinthu zimenezi ndipo kugawira kapepalaka kunali kogwirizana ndi ufulu wa kulankhula womwe anthu a m’dzikolo anali nawo.” M’bale How anawonjezera kuti: “Zimene khotili linagamula zinasonyeza kuti Yehova ndi amene anatithandiza kuti tiwine mlanduwu.” d

16 Zimene khotili linagamula unali umboni wakuti Ufumu wa Mulungu wapambana kwambiri. Chigamulochi chinachititsa kuti milandu yonse youkira boma yokwana 122 imene Mboni za Yehova za ku Quebec zinkaimbidwa ithere pomwepo. Kuwonjezera pamenepa, chigamulochi chinachititsanso kuti nzika za dziko la Canada ndiponso m’mayiko amene ali mu mgwirizano wa Commonwealth zikhale ndi ufulu wofotokoza maganizo awo ngati akuona kuti boma silikuyendetsa bwino zinthu. Chigamulochi chinachititsanso kuti atsogoleri a matchalitchi komanso boma asiye kuphwanya ufulu wa Mboni za Yehova. e

Kodi Amachita Malonda Kapena Kulengeza Ufumu wa Mulungu?

17. Kodi mayiko ena amachita chiyani pofuna kuletsa ntchito yathu yolalikira?

17 Mofanana ndi Akhristu oyambirira, atumiki a Yehova masiku ano ‘sachita nawo malonda’ Mawu a Mulungu. (Werengani 2 Akorinto 2:17.) Komabe mayiko ena amakhazikitsa malamulo pa nkhani zamalonda pofuna kulepheretsa ntchito yathu. Tiyeni tione nkhani ziwiri zimene zinakambidwa kukhoti zomwe zinathandiza anthu kudziwa kuti Mboni za Yehova zimalalikira uthenga wa Mulungu osati kuchita malonda.

18, 19. Kodi dziko la Denmark linachita chiyani pofuna kuletsa ntchito yolalikira?

18 Denmark. Pa October 1, 1932, dziko la Denmark linakhazikitsa lamulo loletsa kugulitsa mapepala, magazini kapena mabuku popanda laisensi. Koma abale athu sanapite ku boma kuti akatenge malaisensi. Tsiku lotsatira, ofalitsa 5 analalikira tsiku lonse m’tawuni ya Roskilde, yomwe ili pamtunda wa makilomita oposa 30, chakumadzulo kwa mzinda wa Copenhagen, womwe ndi likulu la dziko la Denmark. Pamene ankamaliza ntchito yolalikirayo madzulo, abale anazindikira kuti M’bale August Lehmann sakuoneka. Anali atamangidwa pa mlandu wogulitsa zinthu popanda laisensi.

19 Pa December 19, 1932, M’bale August Lehmann anakaonekera kukhoti. M’baleyo anavomereza kuti ankagawiradi anthu mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo koma anakana zoti ankagulitsa mabukuwo. Khotili linagwirizana ndi zimene m’baleyo ananena chifukwa linanena kuti: “Tapeza kuti munthu akuimbidwa mlanduyu . . . amakwanitsa kupeza ndalama zoti azitha kupeza zinthu zofunikira pa moyo wake komanso tapeza kuti sanapeze phindu lililonse pa ntchitoyi ndipo analibe cholinga chimenecho, m’malo mwake ntchito imene wakhala akugwira yamuchititsa kuti akumane ndi mavuto azachuma.” Khotilo linachita zinthu mokomera Mboni za Yehova chifukwa linagamula kuti zimene M’bale Lehmann ankachita “sitinganene kuti ndi kuchita malonda.” Komabe, anthu amene ankadana ndi anthu a Mulungu anali atatsimikiza mtima kuletsa ntchito yolalikira m’dzikoli. (Sal. 94:20) Loya woimira boma pa mlanduwu anachita apilo ku Khoti Lalikulu la m’dzikoli. Kodi abale athu anachita chiyani?

20. Kodi Khoti Lalikulu la ku Denmark linagamula bwanji mlanduwu, nanga abale athu anatani atamva za chigamulochi?

20 Kutatsala mlungu umodzi kuti Khoti Lalikulu limve mlanduwu, Mboni za Yehova zonse za ku Denmark zinagwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri. Lachiwiri pa October 3, 1933, Khoti Lalikululi linalengeza chigamulo chake. Linagwirizana ndi zimene khoti loyamba lija linanena kuti August Lehmann sanaphwanye lamulo lililonse. Chigamulo chimenechi chinachititsa kuti Mboni za Yehova zikhale ndi ufulu wolalikira. Pofuna kuthokoza Yehova kuti wawathandiza kuwina mlanduwu, abale ndi alongo anachita khama kwambiri polalikira kuposa mmene ankachitira poyamba. Kungoyambira nthawi imeneyi, abale athu ku Denmark akhala akulalikira popanda kusokonezedwa ndi boma.

Mboni zolimba mtima za ku Denmark m’zaka za m’ma 1930

21, 22. Kodi Khoti Lalikulu la ku America linapereka chigamulo chotani pa mlandu wa M’bale Murdock?

21 United States. Lamlungu pa February 25, 1940, mpainiya wina dzina lake Robert Murdock, Jr., pamodzi ndi abale ndi alongo ena 7, anamangidwa pamene ankalalikira m’tawuni ya Jeannette, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Pittsburgh, ku Pennsylvania. Abale ndi alongowa anaweruzidwa kuti ndi olakwa pa mlandu wogawira mabuku opanda laisensi. Atachita apilo, Khoti Lalikulu la ku America linavomera kumva mlanduwu.

22 Pa May 3, 1943, Khoti Lalikululi linalengeza chigamulo chake ndipo mlanduwu unakomera Mboni za Yehova. Linanena kuti munthu sayenera kukhala ndi laisensi chifukwa kuchita zimenezi “n’kulipiritsa ufulu umene munthu aliyense ali nawo womwe umapezeka m’malamulo a dziko lino.” Khotili linathetsanso lamulo limene akuluakulu a mzindawo anakhazikitsa loti anthu azikhala ndi laisensi yoti azigawira mabuku kwa anthu ena. Linanenanso kuti “lamulolo linkaphwanya ufulu wofalitsa nkhani komanso ufulu wa chipembedzo.” Polengeza chigamulo chimene oweruza ambiri anagwirizana nacho, Woweruza dzina lake William O. Douglas ananena kuti ntchito ya Mboni za Yehova “ndi kulalikira komanso kugawa mabuku a chipembedzo.” Anawonjezeranso kuti: “Ntchito yachipembedzo imeneyi iyenera kutetezedwa ngati mmene timatetezera ufulu wopembedza m’matchalitchi komanso kulalikira kugome.”

23. Kodi milandu imene tinawina mu 1943 imatithandiza bwanji masiku ano?

23 Zimene Khoti Lalikululi linagamula pa mlanduwu zinathandiza anthu kudziwa kuti anthu a Mulungu amalalikira za Ufumu wa Mulungu osati kuchita malonda. Pa tsiku losaiwalikali, a Mboni za Yehova anawinanso milandu ina 12 pa milandu 13 imene ankaimbidwa kukhotili, kuphatikiza mlandu wa M’bale Murdock. Zimene khoti linagamula pa milandu imeneyi zathandiza pa milandu ina yaposachedwapa imene anthu otitsutsa amafuna kusokoneza ufulu wathu wolalikira uthenga wa Ufumu poyera komanso kunyumba ndi nyumba.

“Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira, Osati Anthu”

24. Kodi timatani maboma akaletsa ntchito yathu yolalikira?

24 Ifeyo monga atumiki a Yehova timayamikira kwambiri mayiko akamatipatsa ufulu wolalikira uthenga wa Ufumu. Koma maboma akatiletsa ntchito yathu yolalikira timapeza njira zina zolalikirira uthengawu chifukwa mofanana ndi atumwi, “tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:29; Mat. 28:19, 20) Koma nthawi zina timachita apilo nkhaniyo kukhoti kuti atipatse ufulu. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri.

25, 26. Ndi nkhani iti imene inachitika ku Nicaragua yomwe inafika ku Khoti Lalikulu, ndipo zinthu zinayenda bwanji?

25 Nicaragua. Pa November 19, 1952, M’bale Donovan Munsterman amene anali mmishonale komanso ankayang’anira nthambi m’dziko la Nicaragua, anapita kuti ofesi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dzikoli. Ofesiyi ili mumzinda wa Managua, womwe ndi likulu la dzikoli. M’baleyu anali ataitanidwa kuti akaonekere pamaso pa bwana wamkulu wa ofesiyi, yemwe dzina lake anali Arnoldo García. Bwanayu anauza M’bale Munsterman kuti Mboni za Yehova zonse ku Nicaragua “zaletsedwa kulalikira zimene amakhulupirira komanso kusonkhana monga chipembedzo.” Pofotokoza chifukwa chake, Bwana García ananena kuti Mboni za Yehova zinalibe chilolezo chochokera kwa nduna ya boma chowaloleza kuti azilalikira komanso kuti anthu ena ankanena kuti a Mboni amalimbikitsa chikomyunizimu. Kodi ndani ankanena zimenezi? Anali atsogoleri achipembedzo cha Katolika.

Abale a ku Nicaragua pa nthawi imene ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’dzikoli

26 Nthawi yomweyo M’bale Munsterman anachita apilo nkhaniyi ku Unduna Woona za Boma ndi Zipembedzo komanso kwa Pulezidenti Anastasio Somoza García, koma palibe chimene chinachitika. Choncho abale athu anasintha mmene ankachitira zinthu. Mwachitsanzo, anatseka Nyumba za Ufumu n’kuyamba kukumana m’magulu ang’onoang’ono. Ngakhale kuti anasiya kulalikira m’misewu, anapitirizabe kulalikira uthenga wa Ufumu. Pa nthawi imeneyinso, abale analemba chikalata chopempha Khoti Lalikulu la ku Nicaragua kuti lichotse lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Manyuzipepala analemba nkhani ya kuletsedwa kwa Mboni za Yehova komanso zimene a Mboni analemba m’chikalatacho ndipo Khoti Lalikulu linavomera kumva mlanduwu. Kodi zinthu zinayenda bwanji? Pa June 19, 1953, Khoti Lalikululi linalengeza zimene oweruza onse anagwirizana ndipo mlanduwu unakomera Mboni za Yehova. Khotili linapeza kuti malinga ndi zimene malamulo a dzikoli amanena, kuletsedwa kwa Mboni za Yehova kunali kuphwanya ufulu wa kulankhula, kusankha zinthu malinga ndi chikumbumtima cha munthu komanso kuphwanya ufulu wouza ena zimene munthu amakhulupirira. Khotili linalamulanso kuti boma liyambe kuchita zinthu ndi Mboni za Yehova ngati mmene linkachitira poyamba.

27. (a) N’chifukwa chiyani anthu a ku Nicaragua anadabwa kwambiri ndi chigamulo chimene Khoti Lalikulu linapereka? (b) Kodi abale anaona kuti n’chiyani chinawathandiza kuwina mlanduwu?

27 Anthu a ku Nicaragua anadabwa kwambiri kuona kuti Khoti Lalikulu lagamula mlanduwu mokomera Mboni za Yehova. M’mbuyo monsemo atsogoleri azipembedzo anali ndi mphamvu kwambiri moti oweruza milandu m’khotili ankapewa kusemphana maganizo ndi atsogoleriwa. Nawonso akuluakulu a boma anali ndi mphamvu kwambiri zimene zinkachititsa kuti oweruza m’khotili azipewa kugamula milandu mosiyana ndi zimene akuluakulu a bomawo ankafuna. Abale athu amakhulupirira kuti anawina mlanduwu chifukwa chakuti Mfumu yawo inawateteza komanso chifukwa chakuti anapitiriza kulalikira.​—Mac. 1:8.

28, 29. Kodi zinthu zinasintha bwanji ku Zaire pakatikati pa zaka za m’ma 1980?

28 Zaire. M’zaka za m’ma 1980, ku Zaire, komwe panopa kumadziwika ndi dzina lakuti Democratic Republic of Congo, kunali Mboni pafupifupi 35,000. Chifukwa cha kuwonjezeka kwa ntchito ya Ufumu m’dzikoli, ofesi ya nthambi inayamba kumanga maofesi ena atsopano. M’mwezi wa December 1985, mumzinda wa Kinshasa, womwe ndi likulu la dzikoli munachitika msonkhano wa mayiko ndipo anthu 32,000 ochokera ku mayiko osiyanasiyana anadzaza m’sitediyamu ya mumzindawu. Koma pasanapite nthawi yaitali zinthu zinasintha kwambiri. Kodi chinachitika n’chiyani?

29 M’bale Marcel Filteau, yemwe anali mmishonale wochokera mumzinda wa Quebec, ku Canada, anali ku Zaire pa nthawi imeneyi. M’baleyu anali atazunzidwapo pa nthawi imene Duplessis ankalamulira ku Quebec. Iye anafotokoza zimene zinachitika kuti: “Pa March 12, 1986, abale analandira kalata yomwe inanena kuti ntchito ya Mboni za Yehova ku Zaire yaletsedwa.” Pulezidenti wa dzikolo, Mobutu Sese Seko, ndi amene anasainira kalatayo.

30. Kodi abale a mu Komiti ya Nthambi anafunika kusankha mwanzeru pa nkhani yaikulu iti, ndipo anasankha kuchita chiyani?

30 Tsiku lotsatira wailesi ya boma inalengeza kuti: “Sitidzamvanso za Mboni za Yehova m’dziko la Zaire.” Kenako abale athu anayamba kuzunzidwa. Nyumba za Ufumu zinaphwanyidwa, abale athu analandidwa katundu, anamangidwa, anatsekeredwa m’ndende komanso kumenyedwa. Ngakhalenso ana a Mboni ankawatsekera m’ndende. Pa October 12, 1988, boma linalanda katundu wa gulu lathu ndipo gulu lina la asilikali lotchedwa Civil Guard, linayamba kugwiritsa ntchito ofesi ya nthambi. Abale amene anali ndi maudindo analemba kalata yopita kwa Pulezidenti Mobutu Sese Seko koma sanawayankhe. Pa nthawi imeneyi, abale a m’Komiti ya Nthambi anayenera kusankha zinthu mwanzeru chifukwa imeneyi inali nkhani yaikulu kwambiri. Anafunika kusankha kuti achite apilo mlanduwu ku Khoti Lalikulu la m’dzikoli kapena kuti adikire kaye. M’bale Timothy Holmes, yemwe anali mmishonale komanso wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi, ananena kuti: “Tinapemphera kwa Yehova kuti atipatse nzeru komanso kuti atitsogolere.” Atakambirana komanso kupempherera nkhaniyi, abalewa anaona kuti imeneyi siinali nthawi yabwino yochita apilo nkhaniyi. M’malomwake anapitiriza kuthandiza abale komanso kupeza njira zina zolalikirira.

“Pa nthawi yonse ya mlanduwu, tinaona kuti Yehova amasintha zinthu”

31, 32. Kodi Khoti Lalikulu la ku Zaire linapereka chigamulo chotani, nanga chigamulo chimenechi chinathandiza bwanji abale athu?

31 Patapita zaka zingapo, anthu a m’dzikoli anasiya kuchitira nkhanza Mboni za Yehova ngati kale komanso anayamba kulemekeza kwambiri ufulu wa anthu. Pa nthawi imeneyi, Komiti ya Nthambi inaona kuti tsopano inali nthawi yabwino yochita apilo nkhaniyi ku Khoti Lalikulu Loona za Chilungamo ku Zaire. Zinali zosangalatsa kumva kuti Khoti Lalikulu lavomera kumva mlanduwu. Kenako, pa January 8, 1993, Khoti Lalikululi linagamula kuti zimene boma linachita poletsa ntchito ya Mboni za Yehova, kunali kuphwanya malamulo ndipo Mboni za Yehova zinaloledwanso kuyamba kugwira ntchito yawo. Zimenezi zinachitika patapita zaka pafupifupi 7 kuchokera pamene Pulezidenti wa dzikoli analetsa ntchito ya Mboni za Yehova. Chigamulo chimenechi chinali choopsa ndipo chinachititsa kuti moyo wa oweruzawo ukhale pangozi chifukwa anathetsa lamulo limene pulezidenti anakhazikitsa. M’bale Holmes anati: “Pa nthawi yonse ya mlanduwu, tinaona kuti Yehova amasintha zinthu.” (Dan. 2:21) Chikhulupiriro cha abale athu chinalimba kwambiri atawina mlanduwu. Anaona kuti Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu, anatsogolera anthu ake kudziwa zoyenera kuchita komanso nthawi yoyenera kuchita zinthuzo.

Mboni za Yehova za ku Democratic Republic of Congo zikusangalala chifukwa cha ufulu wolambira Yehova

32 Chifukwa cha zimene Khotilo linagamula, ofesi ya nthambi inaloledwa kuitana amishonale, kumanga maofesi atsopano ndiponso kuitanitsa mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo. f Kunena zoona, n’zosangalatsa kwambiri kwa atumiki a Mulungu padziko lonse lapansi kuona mmene Yehova amatetezera mwauzimu anthu ake.​—Yes. 52:10.

“Yehova Ndiye Mthandizi Wanga”

33. Kodi taphunzira chiyani pa milandu yochepa imene takambiranayi?

33 Zimene taona pa milandu yochepa imene takambiranayi zikutitsimikizira kuti Yesu wakhala akukwaniritsa zimene analonjeza. Iye anati: “Ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.” (Werengani Luka 21:12-15.) Nthawi zina Yehova amachititsa anthu ena kuteteza anthu ake ngati mmene Gamaliyeli anachitira, kapena amachititsa oweruza komanso maloya kulimba mtima kuti achite zinthu mwachilungamo. Yehova wachititsa kuti zida za adani athu zisapambane. (Werengani Yesaya 54:17.) Izi zikutsimikizira kuti anthu otsutsa sangalepheretse ntchito ya Mulungu.

34. N’chifukwa chiyani milandu imene tinawinayi ndi yochititsa chidwi kwambiri, nanga umenewu ndi umboni wa chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “ Milandu Ikuluikulu Imene Yathandiza Kuti Ntchito Yolalikira za Ufumu Iziyenda Bwino.”)

34 Milandu imene tinawinayi ndi yochititsa chidwi kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani izi: Mboni za Yehova si anthu otchuka, savota, saimira chipani chilichonse komanso salimbikitsa atsogoleri andale kuti achite zimene iwowo akufuna. Kuwonjezera pamenepa, abale ndi alongo athu amene nkhani zawo zimafika kukhoti nthawi zambiri amaoneka kuti ndi “anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Choncho malinga n’kuona kwa anthu, n’zosatheka kuti makhoti akhale kumbali yathu n’kugamula motsutsana ndi zimene atsogoleri andale komanso achipembedzo akufuna. Tikutero chifukwa atsogoleri azipembedzo ndi andale amakhala amphamvu kwambiri moti akhoza kuchititsa makhotiwa kusintha chigamulo chawo. Koma nthawi zambiri makhotiwa amagamula milandu mokomera atumiki a Mulungufe. Milandu imene takhala tikuwina ndi umboni wakuti tikuyenda “monga otsatira Khristu, okhala pamaso pa Mulungu.” (2 Akor. 2:17) Choncho, mogwirizana ndi mtumwi Paulo tikunena kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”​—Aheb. 13:6.

a Mlandu wa M’bale Cantwell unali mlandu woyamba pa milandu 43 imene M’bale Hayden Covington anaimira monga loya wa abale ku Khoti Lalikulu la ku America. M’bale Covington anamwalira mu 1978. Mkazi wake, dzina lake Dorothy, anatumikirabe mokhulupirika mpaka pamene anamwalira mu 2015 ali ndi zaka 92.

b Abale ndi alongowa ankaimbidwa milanduyi chifukwa cha lamulo limene linakhazikitsidwa mu 1606. Lamulolo linkapereka mphamvu zoti oweruza akhoza kugamula kuti munthu ndi wolakwa ngati iwowo akuona kuti zimene munthuyo wanena zikulimbikitsa anthu kuchita zachiwawa, ngakhale zitakhala kuti zimene wanenazo ndi zoona.

c Mu 1950, abale ndi alongo okwana 164 ankachita utumiki wa nthawi zonse ku Quebec komanso panali abale ndi alongo 63 amene analowa Sukulu ya Giliyadi omwe anali atavomera kukatumikira ku Quebec ngakhale kuti ankadziwa zoti akatsutsidwa kwambiri.

d M’bale W. Glen How anali loya wolimba mtima komanso waluso ndipo anamenyera ufulu wa Mboni za Yehova m’dziko la Canada komanso m’mayiko ena pa milandu yambirimbiri. Anagwira ntchitoyi kuyambira mu 1943 mpaka mu 2003.

e Kuti mudziwe zambiri za mlanduwu, werengani nkhani yachingelezi yamutu wakuti, “The Battle Is Not Yours, but God’s” yomwe inatuluka mu Galamukani! ya April 22, 2000, tsamba 18-24.

f Patapita nthawi gulu la asilikali lotchedwa Civil Guard linasiya kugwiritsa ntchito ofesi ya nthambi komabe gulu linamanga ofesi ya nthambi yatsopano pamalo ena.