Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi inuyo mumalakalaka mutaona malonjezo a Ufumu atakwaniritsidwa?

GAWO 7

Zimene Ufumu Walonjeza​—Udzapanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano

Zimene Ufumu Walonjeza​—Udzapanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano

TAYEREKEZERANI kuti mukuthyola apozi wopsa bwino. Mukununkhiza kafungo kake kabwino kenako mukumuika mubasiketi imene muli maapozi ena. Mwakhala mukugwira ntchitoyi kwa maola angapo koma mudakamvabe kuti muli ndi mphamvu zopitiriza kugwira ntchitoyo. Mayi anu akuthyola maapozi mumtengo wina wapafupi kwinaku akucheza ndi abale anu ena komanso anzawo omwe akukuthandizani ntchito yokololayo. Mayi anuwo akuoneka achitsikana ngati mmene ankaonekera muli mwana zaka zambirimbiri zapitazo. Panopo munaiwaliratu zoti nthawi ina anakalamba muli m’dziko lakale lomwe linatha kalekale. Munawaona akuwonda chifukwa cha matenda, munalipo pamene ankamwalira ndipo munalira pamene ankaikidwa m’manda. Koma panopa iwowo komanso anthu ena ambiri amene anamwalira muli nawonso limodzi ndipo ali ndi thanzi labwino.

Tikudziwa kuti zimenezi zidzachitika chifukwa nthawi zonse zimene Mulungu walonjeza zimachitika. M’chigawochi tikambirana mmene malonjezo ena a Ufumu akwaniritsidwire posachedwapa mpaka pa nkhondo ya Aramagedo. Tikambirananso malonjezo ena osangalatsa amene adzakwaniritsidwe pambuyo pa zimenezi. Tidzasangalala kwambiri kukhala ndi moyo pa nthawi imene Ufumu wa Mulungu uzidzalamulira padziko lonse lapansi komanso kuchititsa kuti zinthu zonse zikhale zatsopano.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 21

Ufumu wa Mulungu Udzachotsa Adani Ake

Mukhoza kukonzekera nkhondo ya Aramagedo.

MUTU 22

Ufumu Udzakwaniritsa Zimene Mulungu Amafuna Padziko Lapansi

N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu udzabweradi?