Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthawi Imene Zinthu Zosiyanasiyana Zinachitika

Nthawi Imene Zinthu Zosiyanasiyana Zinachitika
  1. “Pa chiyambi . . .”

  2. 4026 B.C.E. Adamu analengedwa

  3. 3096 B.C.E. Adamu anafa

  4. 2370 B.C.E. Chigumula chinayamba

  5. 2018 B.C.E. Abulahamu anabadwa

  6. 1943 B.C.E. Pangano la Abulahamu

  7. 1750 B.C.E. Yosefe anagulitsidwa ku ukapolo

  8. chaka cha 1613 B.C.E. chisanafike Mayesero a Yobu

  9. 1513 B.C.E. Ulendo wochoka ku Iguputo

  10. 1473 B.C.E. Aisiraeli analowa m’dziko la Kanani motsogoleredwa ndi Yoswa

  11. 1467 B.C.E. Anagonjetsa mbali yaikulu ya dziko la Kanani

  12. 1117 B.C.E. Sauli anadzozedwa kukhala mfumu

  13. 1070 B.C.E. Mulungu analonjeza Davide kuti adzam’patsa ufumu

  14. 1037 B.C.E. Solomo anakhala mfumu

  15. 1027 B.C.E. Anamaliza kumanga kachisi ku Yerusalemu

  16. cha m’ma 1020 B.C.E. Anamaliza kulemba Nyimbo ya Solomo

  17. 997 B.C.E. Ufumu wa Isiraeli unagawanika

  18. cha m’ma 717 B.C.E. Ntchito yolemba buku la Miyambo inatha

  19. mu 607 B.C.E. Yerusalemu anawonongedwa; Aisiraeli anapita ku ukapolo ku Babulo

  20. 539 B.C.E. Babulo anagonjetsedwa ndi Koresi

  21. 537 B.C.E. Ayuda amene anali ku ukapolo anabwerera ku Yerusalemu

  22. 455 B.C.E. Anamanganso mpanda wa Yerusalemu; kuyambika kwa masabata 69 a zaka

  23. 443 B.C.E. itadutsa Malaki anamaliza kulemba buku lake la ulosi

  24. Yesu anabadwa cha m’ma 2 B.C.E.

  25. 29 C.E. Yesu anabatizidwa ndipo anayamba kulalikira za Ufumu wa Mulungu

  26. 31 C.E. Yesu anasankha atumwi 12; analalikira paphiri

  27. 32 C.E. Yesu anaukitsa Lazaro

  28. Nisan 14, 33 C.E. Yesu anapachikidwa (Mwezi wa Nisani umayamba mkatikati mwa March ndipo umathera mkatikati mwa April)

  29. Nisan 16, 33 C.E. Yesu anaukitsidwa

  30. Sivani 6, 33 C.E. Pentekosite; kulandira mzimu woyera (Mwezi wa Sivani umayamba mkatikati mwa May ndipo umathera mkatikati mwa June)

  31. 36 C.E. Koneliyo akhala Mkhristu

  32. cha m’ma 47-48 C.E. Ulendo woyamba wa Paulo wopita kukalalikira

  33. cha m’ma 49-52 C.E. Ulendo wachiwiri wa Paulo wopita kukalalikira

  34. cha m’ma 52-56 C.E. Ulendo wachitatu wa Paulo wopita kukalalikira

  35. 60-61 C.E. Paulo analemba makalata ali m’ndende ku Roma

  36. chaka cha 62 C.E. chisanafike Yakobo, m’bale wake wa Yesu, analemba kalata

  37. 66 C.E. Ayuda anagalukira Aroma

  38. 70 C.E. Aroma anawononga Yerusalemu ndi kachisi

  39. cha m’ma 96 C.E. Yohane analemba buku la Chivumbulutso

  40. cha m’ma 100 C.E. Yohane, mtumwi womalizira anamwalira