GAWO 17
Yesu Ankaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu
Yesu ankaphunzitsa ophunzira ake zinthu zambiri, komabe mfundo yaikulu inali yonena za Ufumu wa Mulungu
KODI Yesu anali ndi ntchito yotani pano padziko lapansi? Iye anati: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Tiyeni tione zinthu zinayi zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza Ufumu, womwe unali mfundo yaikulu ya ulaliki wake.
1. Yesu anaikidwa kukhala Mfumu. Yesu ananena mosapita m’mbali kuti iye ndi Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 4:25, 26) Iye anasonyezanso kuti ndi Mfumu imene mneneri Danieli anaona m’masomphenya. Yesu anauza atumwi ake kuti tsiku lina iye adzakhala “pampando wachifumu waulemerero” ndipo ophunzira akewo adzakhalanso m’mipando yachifumu. (Mateyu 19:28) Iye ananena kuti olamulira amenewa ndi “kagulu ka nkhosa” ndipo ananenanso kuti ali ndi “nkhosa zina,” zimene si zili m’gulu la olamulirawo.—Luka 12:32; Yohane 10:16.
2. Ufumu wa Mulungu udzabweretsa chilungamo chenicheni. Yesu anasonyeza kuti Ufumu umenewu udzachotsa kupanda chilungamo kumene Satana anachitira dzina la Yehova. Ufumuwo udzachita zimenezi mwa kuyeretsa dzina la Yehova Mulungu ndiponso kuchotsa zinthu zonse zimene Satana wadetsa nazo dzinali kuyambira pa nthawi imene iye anachititsa Adamu ndi Hava kuti agalukire Mulungu m’munda wa Edeni. (Mateyu 6:9, 10) Tsiku ndi tsiku Yesu ankasonyeza kuti analibe tsankho pophunzitsa amuna, akazi, anthu olemera ngakhalenso osauka. Ngakhale kuti ntchito yake yaikulu inali yophunzitsa Aisiraeli, iye anayesetsanso kuthandiza Asamariya ndiponso anthu amitundu ina. Mosiyana ndi atsogoleri azipembedzo a m’nthawi imeneyo, iye analibe tsankho ngakhale pang’ono.
3. Ufumu wa Mulungu sudzakhala mbali ya maufumu a dziko lapansili. Pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi, dziko la kwawo linali ndi mavuto ambiri a zandale, chifukwa linkalamulidwa ndi dziko lina. Komabe, iye anathawa pamene anthu ankafuna kumuveka ufumu kuti azichita nawo zandale. (Yohane 6:14, 15) Iye anauza munthu wina wandale kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Ndipo anauzanso otsatira ake kuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Iye sanawalole kugwiritsa ntchito zida za nkhondo ngakhale pofuna kumuteteza.—Mateyu 26:51, 52.
“Yesu anayamba ulendo woyenda . . . mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.”—Luka 8:1
4. Khristu adzakhala wolamulira wachikondi. Yesu analonjeza kuti adzatsitsimula anthu ndi kuwachepetsera mavuto. (Mateyu 11:28-30) Yesu anachitadi zimene analonjezazo chifukwa mwachikondi, anapereka malangizo othandiza pa nkhani ya kuthana ndi nkhawa, kukhala bwino ndi anthu, kuthetsa mtima wokonda kwambiri chuma ndiponso mmene tingapezere chimwemwe. (Mateyu, chaputala 5 mpaka 7) Anthu onse ankafika kwa iye momasuka chifukwa chakuti anali wachikondi. Ngakhale anthu amene anali oponderezedwa kwambiri ankakhamukira kwa iye, ali ndi chikhulupiriro kuti Yesu akawathandiza mwachifundo ndiponso mwaulemu. N’zoonekeratu kuti Yesu adzakhala Wolamulira wabwino kwambiri.
Yesu ankaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu m’njira inanso yamphamvu kwambiri. Iye ankachita zozizwitsa zambiri. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezo? Tiyeni tione.
—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Mateyu, Maliko, Luka, ndi Yohane.