Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 13

“Ndimakonda Atate”

“Ndimakonda Atate”

1, 2. Kodi mtumwi Yohane ananena kuti n’chifukwa chiyani Yesu anali wofunitsitsa kufa?

 YOHANE ndi mtumwi yemwe anali womalizira kumwalira pa atumwi ena onse a Yesu Khristu ndipo anakalamba kwambiri mpaka kufika zaka pafupifupi 100. Pa nthawiyi, iye anayamba kulemba zinthu zimene zinachitika usiku wosaiwalika ndiponso womaliza umene iye limodzi ndi atumwi anzake anakhala ndi Yesu asanaphedwe, zaka pafupifupi 70 m’mbuyomo. Yohane anakwanitsa kukumbukira komanso kulemba mwatsatanetsatane nkhani zambiri chifukwa chakuti mzimu woyera wa Mulungu unkamutsogolera.

2 Usiku umenewo, Yesu anafotokoza momveka bwino kuti watsala pang’ono kuphedwa. Yohane yekha ndi amene anafotokoza chifukwa chimene chinapangitsa Yesu kulolera kufa imfa yopwetekayo. Yesu anati: “Koma kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Atatewo anandilamula. Nyamukani, tiyeni tichokeko kuno.”​—Yohane 14:31.

3. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda Atate wake?

3 Palibe chimene chinali chofunika kwambiri kwa Yesu kuposa kukonda Atate wake. Ngakhale kuti iye ananena kuti “ndimakonda Atate,” sankanena mawuwa kawirikawiri. Ndipotu m’Baibulo lonse, ndi pa Yohane 14:31 pokha pamene Yesu ananena mwachindunji kuti amakonda Atate wake. Ngakhale zinali choncho, zochita zake za tsiku ndi tsiku zinkasonyeza kuti amakondadi Yehova. Iye anali wolimba mtima, womvera komanso wopirira ndipo zimenezi zinali umboni woti amakondadi Mulungu. Chilichonse chimene ankachita pa utumiki wake, ankachichita chifukwa chokonda Mulungu.

4, 5. Kodi Baibulo limalimbikitsa anthu kuti akhale ndi chikondi chotani, nanga tinganene kuti Yesu anali ndi chikondi chotani kwa Yehova?

4 Masiku ano, anthu ambiri amaganiza kuti munthu wachikondi ndi wopusa. Mwina iwo amaganizira za ndakatulo ndi nyimbo zachikondi, kapena amaganizira za chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi chimene nthawi zina sichikhalitsa. Baibulo nalonso limafotokoza za chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi koma limafotokoza mwaulemu osati ngati mmene anthu ambiri amachitira masiku ano. (Miyambo 5:15-21) Komabe, Mawu a Mulungu amafotokoza kwambiri za chikondi cha mtundu wina. Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi samangotengeka maganizo kapena kutsatira nzeru za anthu amene amapereka malangizo pa nkhani zachikondi. Chikondi chimenechi chimakhudza mmene timamvera komanso mmene timaganizira ndipo chimachokera mumtima ndiponso chimagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Munthu amasonyeza chikondichi akamachita zinthu zabwino ndipo sachita zinthu mongotengeka maganizo. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amanena kuti, “chikondi sichitha.”​—1 Akorinto 13:8.

5 Palibe munthu wina aliyense amene amakonda kwambiri Yehova kuposa Yesu. Komanso palibe munthu aliyense amene anaposa Yesu potsatira mawu a m’Malemba amene iye ananena kuti ndi lamulo lalikulu limene Mulungu anapereka, lakuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.” (Maliko 12:30) N’chiyani chinathandiza Yesu kuti akhale ndi chikondi chimenechi? Nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti azikondabe kwambiri Mulungu pamene anali padziko lapansi? Ndipo kodi tingamutsanzire bwanji?

Yesu Amakondana Kwambiri ndi Mulungu Kuyambira Kalekale

6, 7. Tikudziwa bwanji kuti lemba la Miyambo 8:22-31 likunena za Mwana wa Mulungu osati nzeru zenizeni?

6 Kodi munayamba mwagwira ntchito limodzi ndi munthu wina ndiyeno n’kuyamba kugwirizana naye kwambiri? Zimenezi zingatithandize kumvetsa mmene chikondi cha pakati pa Yehova ndi Mwana wake wobadwa yekha chinakulira. M’buku lino tagwiritsa ntchito lemba la Miyambo 8:30 kangapo, koma panopa tiyeni tikambirane lembali poonanso mavesi ena oyandikana nalo. Kuyambira mu vesi 22 mpaka vesi 31, tikupezamo nzeru imene ikulankhula ngati munthu. Kodi tikudziwa bwanji kuti nzeru imeneyi ikuimira Mwana wa Mulungu?

7 Mu vesi 22, nzeru ikunena kuti: “Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova, ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.” Lembali silikungonena za nzeru zenizeni chifukwa nzeru sizinachite “kulengedwa.” Nzeru zilibe chiyambi chifukwa Yehova wakhala alipo kuyambira kalekale ndipo nthawi zonse ndi wanzeru. (Salimo 90:2) Koma Mwana wa Mulungu ali ndi chiyambi chifukwa ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” Iye anachita kupangidwa kapena kuti kulengedwa ndipo ndi woyamba pa zonse zimene Yehova analenga. (Akolose 1:15) Mwanayu analipo Mulungu asanalenge dziko lapansi komanso kumwamba ngati mmene buku la Miyambo likufotokozera. Monga Mawu, kapena kuti wolankhula m’malo mwa Mulungu, iye anasonyeza bwino kwambiri nzeru zimene Yehova ali nazo.​—Yohane 1:1.

8. Kodi Mwana wa Mulungu ankachita chiyani ali kumwamba, ndipo tikamachita chidwi ndi chilengedwe tiziganizira za ndani?

8 Kodi Mwanayu ankachita chiyani pa nthawi yonse imene anali kumwamba asanabwere padziko lapansi? Vesi 30 likusonyeza kuti Yesu anali pambali pa Mulungu monga “mmisiri waluso.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Lemba la Akolose 1:16 limanena kuti: “Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi . . . Analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye ndiponso chifukwa cha iye.” Choncho Yehova, yemwe ndi Mlengi, anagwiritsa ntchito Mwana wake, amene ndi Mmisiri Waluso, polenga zinthu zonse monga angelo kumwamba, zinthu zonse zakuthambo, dziko lapansi ndi zinthu zonse zodabwitsa monga zomera komanso nyama. Analenganso munthu, yemwe ndi wapamwamba kuposa chinthu chilichonse padziko lapansi. Mgwirizano wa Atate ndi Mwana wakeyu tingauyerekezere ndi wa katswiri wolemba mapulani a nyumba ndi mmisiri wake amene amatsatira mapulaniwo pomanga nyumba. Tikamachita chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, kwenikweni timakhala tikutamanda Yehova, Katswiri Wamkulu Wolemba Mapulani. (Salimo 19:1) Komanso tingakumbukire mgwirizano wabwino umene unalipo kwa nthawi yaitali pakati pa Mlengi ndi ‘mmisiri wake waluso’ ameneyo.

9, 10. (a) N’chiyani chinachititsa kuti chikondi cha pakati pa Yehova ndi Mwana wake chikule? (b) Kodi n’chiyani chingathandize kuti muzikondana kwambiri ndi Atate wanu wakumwamba?

9 Anthu awiri opanda ungwiro akamagwira ntchito limodzi nthawi zina amasemphana maganizo. Koma si mmene zinalili pakati pa Yehova ndi Mwana wake. Mwanayu anagwira ntchito limodzi ndi Atate wake kwa nthawi yaitali kwambiri ndipo iye ananena kuti: “Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miyambo 8:30) Iye ankasangalala kukhala ndi Atate wake ndipo ankakondana kwambiri. Mwanayu anayamba kuchita zinthu mofanana kwambiri ndi Atate wake ndipo anatengera makhalidwe ake. Mpake kuti Atate ndi Mwanayu anayamba kukondana kwambiri. Choncho tinganene motsimikiza kuti palibe amene amakondana kwambiri kuposa Atate ndi Mwana wakeyu. Iwo anayamba kukondana kalekale.

10 Koma kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife? Mwina mungaganize kuti n’zosatheka kuti muzikondana kwambiri ndi Yehova ngati mmene Yesu amachitira. N’zoona kuti palibe munthu amene ali ndi udindo waukulu ngati wa Mwanayo. Komabe kumbukirani kuti Yesu anayamba kukondana kwambiri ndi Atate wake pamene ankagwira nawo ntchito. Choncho tili ndi mwayi waukulu chifukwa Yehova watilola kuti tikhale “antchito anzake” chifukwa chakuti amatikonda. (1 Akorinto 3:9) Tikamatsanzira Yesu mu utumiki, nthawi zonse tizikumbukira kuti ndife antchito anzake a Mulungu. Tikamachita zimenezi, chikondi chimene chimatigwirizanitsa ndi Yehova chimakula kwambiri. Kukhala antchito anzake a Mulungu ndi mwayi waukulu kuposa wina uliwonse.

Kodi Yesu Ankatani Kuti Apitirize Kukonda Kwambiri Yehova?

11-13. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyerekezera chikondi ndi mbewu zakudimba, nanga Yesu ali mwana ankatani kuti azikondabe kwambiri Yehova? (b) Kodi Mwana wa Mulungu ali kumwamba komanso atabwera padziko lapansi, anasonyeza bwanji kuti ankafunitsitsa kuti Yehova azimuphunzitsa?

11 Zingakhale zothandiza kwambiri kuyerekezera chikondi chimene chili mumtima mwathu ndi mbewu zakudimba. Mbewu zimafunika kuthirira komanso kuzisamalira kuti zikule bwino. N’chimodzimodzinso ndi chikondi. Tikapanda kuchita zimenezi, chikondi chimachepa ndipo kenako chimatheratu. Yesu ankaona kuti kukonda Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri. Pamene anali padziko lapansi, iye anayesetsa kuchita zinthu zothandiza kuti chikondi chake chikhale champhamvu komanso chisafe. Tiyeni tione mmene anachitira zimenezi.

12 Taganizirani zimene zinachitika pakachisi ku Yerusalemu, Yesu ali mnyamata. Kumbukirani kuti anauza makolo ake amene anali ndi nkhawa kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?” (Luka 2:49) Zikuoneka kuti Yesu ali mwana sankakumbukira zimene ankachita kumwamba asanabwere padziko lapansi. Komabe, ankakonda kwambiri Atate wake Yehova. Iye ankadziwa kuti munthu amene amakonda Yehova amafunitsitsa kumulambira. Choncho padziko lapansi panalibe malo amene Yesu ankasangalala kwambiri kupitako kuposa kunyumba ya Atate wake kumene amakamulambira. Iye ankakonda kupita kukachisi ndipo sankafuna kuchokako. Komanso akapita kukachisi si kuti ankangoonerera zimene zinkachitika kumeneko. Iye ankafunitsitsa kuphunzira za Yehova komanso kufotokoza zimene akudziwa. Yesu anayamba kuchita zimenezi asanakwanitse zaka 12 ndipo atakula anapitirizabe.

13 Mwanayu asanabwere padziko lapansi, anaphunzira zambiri kuchokera kwa Atate wake. Ulosi wopezeka pa Yesaya 50:4-6 umasonyeza kuti Yehova anaphunzitsa Mwana wake mwapadera kwambiri kuti akwaniritse udindo wake monga Mesiya. Ngakhale kuti zina mwa zinthu zimene anaphunzirazo zinali zokhudza mavuto amene Wodzozedwa wa Yehova adzakumane nawo, Mwanayu anaphunzirabe modzipereka. Kenako Yesu anabwera padziko lapansi ndipo ngakhale atakula, sanasiye kupita kunyumba ya Atate wake kukalambira komanso kukaphunzira zinthu zimene Yehova ankafuna kuti anthu azidziwe. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti nthawi zonse Yesu ankapezeka pakachisi ndiponso kusunagoge. (Luka 4:16; 19:47) Kuti tipitirize kukonda Yehova, nthawi zonse tiyenera kumapezeka pamisonkhano ya Chikhristu, pamene timalambira Yehova ndi kuphunzira zambiri zokhudza iyeyo.

“Anakwera phiri yekhayekha kukapemphera”

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani nthawi zina Yesu ankakonda kukhala payekha? (b) Popemphera kwa Atate wake, kodi Yesu ankasonyeza bwanji kuti amawakonda komanso amawalemekeza?

14 Chinthu china chimene chinathandiza Yesu kuti azikonda kwambiri Yehova chinali kupemphera nthawi zonse. Ngakhale kuti iye anali munthu wochezeka, n’zochititsa chidwi kuti nthawi zina ankakonda kukhala payekha. Mwachitsanzo, lemba la Luka 5:16 limati: “Nthawi zambiri iye ankapita kumalo kwayekha kukapemphera.” Komanso lemba la Mateyu 14:23 limanena kuti: “Atauza anthuwo kuti azipita, anakwera phiri yekhayekha kukapemphera. Iye anakhala kumeneko yekhayekha mpaka kunja kunada.” Pa nthawiyi komanso nthawi zina Yesu ankafuna kukhala payekha, osati chifukwa choti anali munthu wodzipatula kapena wodzikonda, koma chifukwa chakuti ankafuna kulankhula ndi Atate wake Yehova momasuka popemphera.

15 Nthawi zina popemphera Yesu ankagwiritsa ntchito mawu akuti “Abba, Atate.” (Maliko 14:36) Yesu ali padziko lapansi, anthu m’banja ankakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti “Abba” kutanthauza “ababa.” Mawu amenewa ndi ena mwa mawu oyamba amene kawirikawiri mwana ankaphunzira akangoyamba kulankhula. Komabe amenewa anali mawu aulemu. Pogwiritsa ntchito mawu amenewa, Mwanayu anasonyeza kuti amakonda Atate wake komanso kuti amalemekeza udindo umene Yehova ali nawo monga Atate. M’mapemphero onse a Yesu amene analembedwa, timaona kuti iye ankakonda ndiponso kulemekeza Atate wake. Mwachitsanzo, m’chaputala 17 cha buku la Yohane, muli pemphero lalitali komanso lochokera pansi pa mtima limene Yesu anapemphera usiku wake womaliza. Tiyenera kuphunzira zimene Yesu ananena m’pemphero limeneli ndi kumutsanzira popemphera. Apa sitikutanthauza kuti tizibwereza mawu a Yesu ayi, koma tiziyesetsa kawirikawiri kupeza njira zolankhulira ndi Atate wathu wakumwamba kuchokera pansi pa mtima. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti tizimukonda kwambiri komanso kuti chikondi chathucho chisathe.

16, 17. (a) Kodi zimene Yesu ankanena zinkasonyeza bwanji kuti amakonda Atate wake? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Atate wake ndi wowolowa manja?

16 Monga taonera kale, Yesu sankanena kawirikawiri mawu akuti “ndimakonda Atate.” Koma nthawi zambiri zimene Yesu ankanena zinkasonyeza kuti amakonda Atate wake. Mwachitsanzo, iye ananena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.” (Mateyu 11:25) Pamene tinkaphunzira gawo lachiwiri la buku lino, tinaona kuti Yesu ankakonda kutamanda Atate wake pothandiza anthu kuti awadziwe. Mwachitsanzo, anayerekezera Yehova ndi bambo amene ankafunitsitsa kukhululukira mwana wawo wolowerera, moti bambowo ankayembekezera kuti mwana wawo wolapayo abwerere kunyumba. Bambowo ataona mwanayo chapatali, anamuthamangira kukakumana naye ndipo anamukumbatira. (Luka 15:20) Aliyense akawerenga nkhaniyi imamukhudza kwambiri poona mmene Yesu anasonyezera kuti Yehova ndi wachikondi komanso wokhululuka.

17 Kawirikawiri Yesu ankatamanda Atate wake chifukwa choti ndi wowolowa manja. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito zimene makolo omwe si angwiro amachita pofuna kutitsimikizira kuti Atate wathu adzatipatsa mzimu woyera. (Luka 11:13) Yesu ananenanso kuti Atate wake akulonjeza kuti adzatipatsa zinthu zabwino mowolowa manja m’tsogolo. Mwachitsanzo, iye anafotokoza kuti ankayembekezera mwachidwi kubwerera kumwamba n’kukakhala pambali pa Atate wake, pamalo pamene ankakhala asanabwere padziko lapansi. (Yohane 14:28; 17:5) Yesu anauza otsatira ake za chiyembekezo chimene Yehova wapereka kwa “kagulu ka nkhosa” za Khristu. Iye anawauza kuti adzapita kumwamba n’kukalamulira nawo mu ufumu wa Mesiya. (Luka 12:32; Yohane 14:2) Komanso Yesu analimbikitsa munthu wochimwa amene anali atatsala pang’ono kufa, pomuuza kuti adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. (Luka 23:43) Kulankhula za Atate wake kuti ndi wowolowa manja, kunathandiza Yesu kuti apitirize kukonda kwambiri Yehova. Anthu ambiri amene akutsatira Khristu aona kuti palibe chimene chimawathandiza kuti azikonda komanso kukhulupirira kwambiri Yehova kuposa kulankhula za iye komanso chiyembekezo chimene wapereka kwa anthu amene amamukonda.

Muzikonda Yehova Ngati Mmene Yesu Amachitira

18. Kodi tifunika kutsanzira Yesu m’njira yofunika kwambiri iti, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Pa njira zonse zimene tingatsanzirire Yesu, palibe yofunika kwambiri kuposa kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse ndi mphamvu zathu zonse. (Luka 10:27) Zochita zathu ndi zimene zimasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova osati kungonena kuti timamukonda. Yesu sankangokhutira chabe ndi kumva mumtima mwake kapena kungonena kuti “ndimakonda Atate.” Iye ananena kuti: “Koma kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Atatewo anandilamula.” (Yohane 14:31) Satana ananena kuti anthu onse amene amatumikira Yehova amam’tumikira chifukwa cha dyera. (Yobu 2:4, 5) Choncho pofuna kuyankha momveka bwino bodza la Satanali, Yesu molimba mtima anasonyeza anthu padziko lonse kuti amakonda kwambiri Atate wake. Iye anachita zimenezi pomvera Mulungu mpaka analolera kuphedwa. Kodi inuyo mungatsatire chitsanzo cha Yesu chimenechi? Kodi mudzasonyeza dziko kuti mumakondadi Yehova Mulungu?

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani timaona kuti kupezeka pamisonkhano ya Chikhristu nthawi zonse n’kofunika? (b) Kodi tiyenera kuona bwanji kuphunzira Mawu a Mulungu patokha, kusinkhasinkha ndiponso kupemphera?

19 Mwachibadwa timafuna kusonyeza kuti timakonda Mulungu. Choncho Atate wathu Yehova anakonza zoti tikamamulambira, chikondi chathu pa iye chizikula. Mukapita kumisonkhano ya Chikhristu, muzikumbukira kuti mwapita kumeneko kukalambira Mulungu. Polambira timachita zinthu zosiyanasiyana monga kumvetsera mapemphero mwatcheru, kuimba nawo nyimbo zotamanda Mulungu, kumvetsera mwatcheru nkhani zikamakambidwa ndiponso kuyankha ngati n’zotheka. Misonkhano imeneyi imakupatsaninso mwayi wolimbikitsa Akhristu anzanu. (Aheberi 10:24, 25) Kulambira Yehova nthawi zonse pamisonkhano ya Chikhristu kudzakuthandizani kuti muzikonda kwambiri Mulungu.

20 Komanso tingapitirize kukonda Mulungu ngati timaphunzira Mawu ake patokha, kuwaganizira mozama ndiponso ngati timapemphera. Muziona zinthu zimenezi ngati mwayi wanu wolankhula ndi Yehova. Mukamaphunzira Mawu a Mulungu n’kumawaganizira mozama, Yehova amakhala akulankhula nanu. Mukamapemphera, mumakhala mukumuuza zamumtima mwanu. Kumbukirani kuti popemphera, simuyenera kumangopempha zinthu kwa Mulungu basi. Mukamapemphera, mumakhalanso ndi mwayi wothokoza Yehova chifukwa cha madalitso amene amatipatsa komanso womutamanda chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa. (Salimo 146:1) Kuwonjezera pamenepo, kutamanda Yehova pagulu mosangalala ndiponso mochokera pansi pa mtima ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti timamukonda.

21. Kodi kukonda Yehova n’kofunika bwanji, nanga m’mitu yakutsogoloku tiphunzira chiyani?

21 Palibe chimene chingakuthandizeni kuti mukhale osangalala kuposa kukonda Mulungu. Adamu ndi Hava analephera kumvera Mulungu chifukwa chakuti analibe chikondi chimenechi. Kukonda Mulungu n’kofunika kwambiri kuti munthu akhalebe wokhulupirika pamene akukumana ndi mavuto, apirire mayesero aliwonse komanso kuti asagonje akamayesedwa. Kuchita zimenezi n’kofunika kuti munthu akhale wotsatira wa Yesu. Komatu munthu amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso anzake. (1 Yohane 4:20) M’mitu yakutsogoloku tiphunzira mmene Yesu anasonyezera kuti amakonda anthu, koma m’mutu wotsatirawu tikambirana chifukwa chake anthu ambiri ankaona kuti Yesu anali munthu wosavuta kumufikira.