Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

“Palibe Amene Ali ndi Chikondi Chachikulu Kuposa Ichi”

“Palibe Amene Ali ndi Chikondi Chachikulu Kuposa Ichi”

1-4. (a) N’chiyani chinachitika Pilato atabweretsa Yesu kwa gulu la anthu okwiya amene anasonkhana kunja kwa nyumba yake? (b) Kodi Yesu anatani pamene anthu ankamuzunza mochititsa manyazi, nanga ndi mafunso ati amene ndi ofunika kwambiri?

 M’MAWA wa tsiku la Pasika mu 33 C.E., kazembe wa Chiroma Pontiyo Pilato anapereka Yesu kwa gulu la anthu okwiya amene anasonkhana kunja kwa nyumba yake. Iye ananena kuti: “Taonani! Mwamuna uja ndi uyu!” (Yohane 19:5) Masiku angapo m’mbuyomu, gulu la anthu linatamanda Yesu mofuula pamene ankalowa mu Yerusalemu monga Mfumu yoikidwa ndi Mulungu. Koma pa nthawiyi, anthuwa anali atasintha ndipo sankaonanso Yesu ngati Mfumu.

2 Yesu anamuveka nsalu yapepo ngati imene ankavala mafumu ndiponso chisoti chachifumu chaminga. Nsaluyo inkaphimba mabala amene anabwera chifukwa chokwapulidwa kumsana omwe anali magazi okhaokha komanso chisoticho chinkamubaya n’kumamutulutsa magazi m’mutu. Anthuwo anachita zonsezi pomunyoza kuti ndi Mfumu. Gulu la anthuwo, omwe ankatsogoleredwa ndi ansembe aakulu, anakana Yesu, amene anaima patsogolo pawo atamenyedwa koopsa. Ansembewo ankafuula kuti: “Apachikidwe ameneyo! Apachikidwe ameneyo!” Ndipo gulu la anthuwo, lomwe linkafunitsitsa kuti Yesu aphedwe, linafuulanso kuti: “Iyeyu akuyenera kufa.”​—Yohane 19:1-7.

3 Ngakhale kuti Yesu anazunzidwa mochititsa manyazi chonchi, iye anapirira mavuto onsewa molimba mtima, modekha ndiponso mosanyinyirika. Iye anali wokonzeka kufa. Madzulo a tsiku la Pasika lomwelo, iye analolera kufa imfa yopweteka kwambiri pamtengo wozunzikirapo. a​—Yohane 19:17, 18, 30.

4 Pololera kuphedwa, Yesu anasonyeza kuti ankaona otsatira ake kuti ndi anzake enieni. Iye anati: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.” (Yohane 15:13) Mawu a mulembali akubweretsa mafunso ofunika kwambiri monga akuti: Kodi zinali zoyeneradi kuti Yesu azunzidwe mpaka kuphedwa? N’chifukwa chiyani analolera kuti akumane ndi zimenezi? Monga “anzake” ndiponso otsatira ake, kodi ifeyo tingamutsanzire bwanji?

N’chifukwa Chiyani Zinali Zoyenera Kuti Yesu Azunzidwe Ndiponso Aphedwe?

5. N’chiyani chinathandiza Yesu kudziwiratu mayesero osiyanasiyana amene anakumana nawo?

5 Yesu ankadziwa zimene adzakumane nazo, chifukwa anali Mesiya wolonjezedwa. Ankadziwa maulosi ambiri amene ali m’Malemba a Chiheberi, amene anafotokoza mwatsatanetsatane kuti Mesiya adzazunzidwa ndiponso adzaphedwa. (Yesaya 53:3-7, 12; Danieli 9:26) Ndipo kangapo konse, anauza ophunzira ake kuti iye adzakumana ndi mayesero osiyanasiyana. (Maliko 8:31; 9:31) Mwachitsanzo, ali pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu kukachita nawo mwambo wake womaliza wa Pasika, Yesu anauza ophunzira ake mosapita m’mbali kuti: “Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe ndipo akamupereka kwa anthu amitundu ina. Iwo akamuchitira chipongwe, kumulavulira, kumukwapula ndi kumupha.” (Maliko 10:33, 34) Mawu amenewa anali oona chifukwa monga mmene taonera kale, anthu anachitiradi Yesu chipongwe, anamulavulira, anamukwapula ndipo kenako anamupha.

6. N’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti Yesu azunzidwe ndiponso kufa?

6 Komabe, n’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti Yesu azunzidwe ndiponso aphedwe? Pali zifukwa zingapo zofunika kwambiri. Choyamba, pokhalabe wokhulupirika, Yesu anasonyeza kuti ankatumikira Mulungu mokhulupirika komanso anachititsa kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Kumbukirani kuti Satana ananena bodza lakuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. (Yobu 2:1-5) Pokhalabe wokhulupirika “mpaka imfa . . . yapamtengo wozunzikirapo,” Yesu anapereka yankho logwira mtima kwambiri pa bodza limene Satana ananenali. (Afilipi 2:8; Miyambo 27:11) Chachiwiri, kuvutika ndiponso imfa ya Mesiya zikanathandiza kuti machimo a anthu ambiri aphimbidwe. (Yesaya 53:5, 10; Danieli 9:24) Yesu anapereka “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri,” ndipo zimenezi zinatsegula njira yoti tizitha kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Mateyu 20:28) Chachitatu, popirira mayesero ndi mavuto osiyanasiyana, Yesu “anayesedwa pa zinthu zonse ngati ifeyo.” Choncho, zimenezi zachititsa kuti iye akhale Mkulu wa Ansembe, amene amatha ‘kutimvera chisoni pa zofooka zathu.’​—Aheberi 2:17, 18; 4:15.

N’chifukwa Chiyani Yesu Ankafunitsitsa Kupereka Moyo Wake?

7. Kodi Yesu anasiya chiyani kumwamba pamene ankabwera padziko lapansi?

7 Kuti timvetse bwino zimene Yesu anali wokonzeka kukumana nazo, tiyeni tiganizire mfundo iyi: Kodi ndi ndani amene angalolere kusiya banja lake kwawo n’kupita kudziko lina ngati akudziwa kuti anthu ambiri kumeneko akamukana, akamuzunza mochititsa manyazi ndiponso akamupha? Ndiyeno ganizirani zimene Yesu anachita. Asanabwere padziko lapansi, iye anali ndi udindo wapadera kwambiri kumwamba ndipo ankakhala pambali pa Atate wake. Komabe, Yesu anachoka kumwamba mofunitsitsa n’kubwera padziko lapansi kudzakhala munthu. Iye anachita zimenezi ngakhale ankadziwa kuti anthu ambiri adzamukana, adzamuzunza mwankhanza kwambiri ndiponso mochititsa manyazi, ndipo kenako adzamupha mwankhanza. (Afilipi 2:5-7) Kodi n’chiyani chinachititsa Yesu kuti alolere kukumana ndi zonsezi?

8, 9. N’chiyani chinachititsa kuti Yesu apereke moyo wake?

8 Chifukwa chachikulu n’chakuti Yesu amakonda kwambiri Atate wake. Yesu anapirira mavuto osiyanasiyana chifukwa chakuti amakonda Yehova. Chikondi chimenechi chinamuchititsa kuti aziganizira kwambiri za dzina ndiponso mbiri ya Atate wake. (Mateyu 6:9; Yohane 17:1-6, 26) Yesu ankaona kuti chofunika kwambiri n’chakuti dzina la Atate wake, limene linali litadetsedwa kwambiri, liyeretsedwe. Choncho, iye anaona kuti ndi mwayi waukulu kuvutika chifukwa cha chilungamo, ndipo ankadziwanso kuti akakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, adzathandiza kuyeretsa dzina lolemekezeka la Atate wake.​—1 Mbiri 29:13.

9 Chifukwa chinanso chimene chinachititsa Yesu kupereka moyo wake n’chakuti amakonda kwambiri anthu. Iye anayamba kukonda anthu kale kwambiri, anthu atangolengedwa kumene. Baibulo limafotokoza mmene Yesu ankaonera anthu asanabwere padziko lapansi, limati: “Ana a anthu ndi amene ankandisangalatsa kwambiri.” (Miyambo 8:30, 31) Yesu atabwera padziko lapansi, zinkaonekeratu kuti amakonda anthu. Monga taonera m’mitu itatu yapitayi, Yesu anasonyeza m’njira zambiri kuti amakonda anthu, makamaka otsatira ake. Koma pa Nisani 14, 33 C.E., iye anapereka moyo wake chifukwa cha ife. (Yohane 10:11) N’zoonadi, palibe njira ina imene akanasonyezera kuti amatikonda kwambiri kuposa zimene anachitazi. Kodi ifeyo tiyenera kumutsanzira? Inde, ndipotu Baibulo limatilamula kuti tizichita zimenezi.

‘Muzikondana Ngati Mmene Ine Ndakukonderani’

10, 11. Kodi ndi lamulo latsopano liti limene Yesu anapatsa otsatira ake, ndipo lamulo limeneli limafuna kuti tizichita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizimvera lamulo latsopanoli?

10 Usiku womaliza Yesu asanaphedwe, anauza ophunzira ake amene ankayenda nawo nthawi zonse kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana choncho. Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) N’chifukwa chiyani lamulo lakuti “muzikondana” lili “latsopano”? N’zoona kuti m’Chilamulo cha Mose munali kale lamulo lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Levitiko 19:18) Koma lamulo latsopanoli limafuna kuti anthu azikondana kwambiri, mpaka azilolera kuferana. Yesu anatchula mfundo imeneyi momveka bwino pamene ananena kuti: “Ndikukulamulani kuti muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani. Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.” (Yohane 15:12, 13) Choncho tingati lamulo latsopanoli silikunena kuti: “Muzikonda ena ngati mmene mumadzikondera,” koma likuti: “Muzikonda ena kuposa mmene mumadzikondera.” N’zoonekeratu kuti Yesu anasonyeza chikondi chimenechi pa moyo wake wonse ngakhalenso mmene anafera.

11 N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti timvere lamulo latsopanoli? Kumbukirani kuti Yesu anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana. [ngati mukusonyeza chikondi chololera kuvutikira ena.]” N’zoonadi, timadziwika kuti ndife Akhristu enieni ngati timasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Chikondi chimenechi tingachiyerekezere ndi baji. Tikamapita kumsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova, umene umachitika chaka ndi chaka, timavala baji imene imasonyeza dzina lathu ndi mpingo umene tachokera. Chikondi chololera kuvutikira ena chili ngati “baji” imene imathandiza anthu kuti adziwe Akhristu enieni. Zimenezi zikutanthauza kuti, mofanana ndi baji imene imaonekera mosavuta, anthu azionanso mosavuta kuti timakondana ndipo azidziwa kuti ndifedi otsatira enieni a Khristu. Choncho aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amaona kuti zochita zanga zimasonyeza kuti ndili ndi chikondi chololera kuvutikira ena, chimene chili ngati “baji”’?

Kodi Tingasonyeze Bwanji Chikondi Chololera Kuvutikira Ena?

12, 13. (a) Kodi tiyenera kukhala ndi mtima wofunitsitsa kudzimana zinthu ziti kuti tisonyeze kuti timakondana? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalolera kuvutikira ena?

12 Popeza ndife otsatira a Yesu, tiyenera kumakondana ngati mmene iye anatikondera. Izi zikutanthauza kuti tizikhala ndi mtima wofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti tithandize Akhristu anzathu. Kodi tiyenera kufunitsitsa kudzimana zinthu ziti? Baibulo likutiuza kuti: “Tadziwa chikondi chifukwa chakuti Yesu Khristu anapereka moyo wake chifukwa cha ife, ndipo ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.” (1 Yohane 3:16) Mofanana ndi Yesu, tiyenera kukhala ndi mtima wofunitsitsa kufera ena ngati pakufunika kutero. Mwachitsanzo, anthu akamatizunza chifukwa cha chikhulupiriro chathu, timalolera kuti atiphe m’malo mopereka abale athu kwa adaniwo. M’mayiko amene anthu amaphana chifukwa chosiyana fuko kapena mtundu, ife timalolera kuika moyo wathu pangozi kuti titeteze abale athu, ngakhale kuti si a fuko kapena mtundu wathu. Mayiko akamamenyana, ife timalolera kutsekeredwa m’ndende kapena kufa kumene m’malo mopita kunkhondo n’kukapha Akhristu anzathu kapena munthu wina aliyense.​—Yohane 17:14, 16; 1 Yohane 3:10-12.

13 Pali njira zambiri zimene tingasonyezere chikondi chololera kuvutikira ena, osati kungokhala ofunitsitsa kufera abale athu basi. Ndipotu si aliyense amene angafunikiredi kufera ena posonyeza chikondi chimenechi. Komabe, ngati timakonda abale athu mpaka kukhala ofunitsitsa kuwafera, kodi sitiyeneranso kukhala ofunitsitsa kudzimana m’njira zina n’kuyesetsa kuwathandiza panopa? Kuti tisonyeze chikondi chimenechi, timafunikira kudzimana zinthu zimene ifeyo timakonda kapena zimene zimatisangalatsa kuti tithandize ena. Tisanaganizire mavuto athu, choyamba timaganizira zimene ena akusowa kapena mavuto amene akukumana nawo, ngakhale pamene zinthu sizili bwino kwa ifeyo. (1 Akorinto 10:24) Kodi tingasonyeze m’njira ziti chikondi chololera kuvutikira ena?

Mumpingo Ndiponso M’banja

14. (a) Kodi akulu amafunika kudzipereka m’njira ziti? (b) Kodi mumamva bwanji mumtima mwanu mukaganizira ntchito imene akulu akugwira mumpingo wanu?

14 Akulu mumpingo amadzimana m’njira zambiri kuti ‘awete gulu la nkhosa.’ (1 Petulo 5:2, 3) Kuwonjezera pa udindo wosamalira mabanja awo, akulu angafunikenso kupatula nthawi madzulo kapena kumapeto kwa mlungu kuti agwire ntchito zina za kumpingo, monga kukonzekera nkhani, kupanga maulendo aubusa ndiponso kuweruza milandu. Akulu enanso ambiri amadzipereka m’njira zina chifukwa amagwira ntchito kwambiri pamisonkhano ikuluikulu. Enanso amatumikira m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala, m’Magulu Oyendera Odwala komanso m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga. Inu akulu, musaiwale kuti mukamatumikira ndi mtima wonse, mukamagwiritsa ntchito nthawi yanu, mphamvu zanu ndiponso chuma chanu poweta gulu la nkhosa, ndiye kuti mukusonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. (2 Akorinto 12:15) Dziwani kuti Yehova ndiponso abale anu amene mukuwatumikira mwakhamawo amayamikira kwambiri utumiki wanu.​—Afilipi 2:29; Aheberi 6:10.

15. (a) Kodi akazi a akulu amasonyeza mtima wodzimana m’njira ziti? (b) Kodi mumamva bwanji mukaona akazi a akulu amene amalolera kuti amuna awo agwire ntchito za mpingo pa nthawi imene amafunika kucheza ndi banja lawo?

15 Nanga bwanji akazi a akulu? Kodi nawonso sasonyeza mtima wodzimana polola kuti amuna awo azisamalira nkhosa za Mulungu? Zoonadi, akazi amenewa amasonyeza mtima wodzimana akalolera kuti amuna awo akasamalire zinthu zina zokhudza mpingo pa nthawi imene akanafunika kukhala panyumba n’kumacheza ndi banja lawo. Ndiyeno ganiziranso mtima wodzimana umene akazi a oyang’anira dera amasonyeza akamayenda limodzi ndi amuna awo pamene akuyendera mipingo komanso madera osiyanasiyana. Iwo amalolera kukhala opanda nyumba yawoyawo ndipo nthawi zina amafunika kugona m’nyumba zosiyanasiyana mlungu uliwonse. Tiyenera kuyamikira akazi amene amadzimana mofunitsitsa kuti athandize mpingo mwanjira imeneyi, chifukwa amasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena.​—Afilipi 2:3, 4.

16. Kodi makolo a Chikhristu amadzimana zinthu ziti kuti athandize ana awo?

16 Kodi tingasonyeze bwanji chikondi chololera kuvutikira ena m’banja? Makolo, mumadzimana zinthu zambiri kuti musamalire ana anu ndipo mumawapatsa “malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.” (Aefeso 6:4) Mwina mumagwira ntchito yotopetsa kwa maola ambiri kuti muthe kupeza chakudya cha banja lanu komanso kuti ana anu azigona malo abwino ndiponso kuti akhale ndi zovala zokwanira. Inuyo mumalolera kudzimana zinthu zambiri kuti ana anu apeze zinthu zofunika pa moyo wawo. Mumachitanso khama kuphunzira ndi ana anu, kupita nawo kumisonkhano ya Chikhristu ndiponso kolalikira. (Deuteronomo 6:6, 7) Mukamachita zimenezi, mumasangalatsa Mulungu amene anayambitsa banja ndiponso mumathandiza ana anuwo kuti adzapeze moyo wosatha.​—Miyambo 22:6; Aefeso 3:14, 15.

17. Kodi amuna a Chikhristu okwatira angatsanzire bwanji Yesu amene anali wosadzikonda?

17 Kodi amuna okwatira angatsanzire bwanji Yesu posonyeza chikondi chololera kuvutikira ena? Baibulo limayankha kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aefeso 5:25) Monga mmene taonera, Yesu ankakonda kwambiri otsatira ake mpaka anawafera. Mwamuna wa Chikhristu amatsanzira Yesu, amene anali wosadzikonda ndipo “sankachita zinthu zodzikondweretsa yekha.” (Aroma 15:3) Mwamuna wotero amayesetsa kuganizira zosowa za mkazi wake choyamba. Iye saumirira maganizo ake, koma amavomereza maganizo a mkazi wake ngati sakusemphana ndi Malemba. Yehova amasangalala ndi mwamuna amene amasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena ndiponso mkazi ndi ana ake amamukonda ndi kumulemekeza kwambiri.

Kodi Inuyo Muchita Chiyani?

18. N’chiyani chimene chimatilimbikitsa kutsatira lamulo latsopano lakuti tizikondana?

18 N’zoona kuti kutsatira lamulo latsopano lakuti tizikondana sikophweka, komabe tili ndi chifukwa chomveka chimene chimatichititsa kuti tizilitsatira. Paulo analemba kuti: “Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse  . . . Iye anafera onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.” (2 Akorinto 5:14, 15) Popeza Yesu anatifera, ndi bwino kuti zochita zathu zizigwirizana ndi zimene iye ankachita. Tingachite zimenezi posonyeza chikondi chololera kuvutikira ena ngati mmene iye anachitira.

19, 20. Kodi Yehova watipatsa mphatso ya mtengo wapatali iti, nanga tingasonyeze bwanji kuti tailandira?

19 Sikuti Yesu ankakokomeza zinthu pamene ananena kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.” (Yohane 15:13) Yesu anapereka moyo wake mofunitsitsa chifukwa cha ife, ndipo imeneyi ndi njira yaikulu imene anasonyezera kuti amatikonda. Koma pali winanso amene anasonyeza kuti amatikonda kwambiri. Yesu anafotokoza kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mulungu amatikonda kwambiri moti anatipatsa Mwana wake monga dipo, limene linatiwombola ku uchimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Ngakhale kuti dipo ndi mphatso ya mtengo wapatali kwambiri imene Yehova watipatsa, iye satikakamiza kuti tiilandire.

20 Tiyenera kusankha tokha kulandira mphatso yochokera kwa Yehova imeneyi. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tailandira? Tingachite zimenezi ‘pokhulupirira’ Mwanayo. Komabe, tiyenera kusonyeza kuti timamukhulupirira mwa zochita zathu zatsiku ndi tsiku, osati kungonena ndi pakamwa chabe. (Yakobo 2:26) Timasonyeza kuti timakhulupirira Yesu Khristu tikamamutsatira tsiku ndi tsiku ndipo tikamachita zimenezi, tidzapeza madalitso panopa ndiponso m’tsogolo. Tidzakambirana zimenezi m’mutu womaliza wa buku lino.

a Pa tsiku limeneli, anthu analavulira Yesu kawiri konse. Koyamba, atsogoleri a chipembedzo ndi amene anamulavulira ndipo kachiwiri, asilikali achiroma. (Mateyu 26:59-68; 27:27-30) Ngakhale kuti Yesu ananyozedwa mwanjira imeneyi, anapirira mosanyinyirika ngakhale pang’ono. Anachita zonsezi pokwaniritsa ulosi wakuti: “Sindinabise nkhope yanga kuti asaichitire zinthu zochititsa manyazi komanso kuti asailavulire.”​—Yesaya 50:6.