MUTU 18
“Pitiriza Kunditsatira”
1-3. (a) Kodi Yesu anatsanzikana nawo bwanji atumwi ake, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi sizinali zomvetsa chisoni? (b) N’chifukwa chiyani tifunika kudziwa zimene Yesu wakhala akuchita atabwerera kumwamba?
AMUNA okwana 11 anaimirira paphiri n’kumayang’anitsitsa mwachidwi munthu wina amene ankamukonda kwambiri. Munthu ameneyu ndi Yesu amene anali ataukitsidwa ndipo pa nthawiyi anali wamphamvu kwambiri kuposa ana onse auzimu a Yehova. Yesu anapangana ndi atumwi ake kuti akakumane nawo komaliza paphiri la Maolivi.
2 N’kutheka kuti Yesu ankakumbukira zinthu zambiri atafika paphiri limeneli, lomwe linali kutsidya lina la chigwa cha Kidironi kuchokera ku Yerusalemu. Mphepete mwa phiri limeneli munalinso mzinda wotchedwa Betaniya, kumene Yesu anaukitsa Lazaro. Milungu ingapo yapitayo, Yesu anayenda ulendo waufupi wochokera ku Betefage kulowa mumzinda wa Yerusalemu monga Mfumu. N’kuthekanso kuti munda wa Getsemane, kumene Yesu anazunzika kwambiri patatsala nthawi yochepa kuti amugwire, unalinso paphiri la Maolivi lomweli. Pa nthawiyi, Yesu anakonzanso zoti akatsanzikane ndi anzake apamtima ndiponso otsatira ake paphiri lomweli. Iye analankhula mwachifundo potsanzikana ndi anzakewo, ndipo kenako anayamba kukwera kumwamba. Atumwiwo anangoima n’kumayang’ana Mbuye wawo akukwera kumwamba. Kenako anabisika ndi mitambo ndipo sanamuonenso.—Machitidwe 1:6-12.
3 Kodi mukaganiza zimene zinachitika potsanzikanapo mukuona kuti zinali zosangalatsa kapena zomvetsa chisoni? Zimenezi sizinali zomvetsa chisoni, chifukwa zimene angelo awiri anauza atumwiwo zikusonyeza kuti Yesu sanawasiyiretu. (Machitidwe 1:10, 11) Ulendo wa Yesu wopita kumwamba unali chiyambi cha zinthu zosiyanasiyana. Mawu a Mulungu satibisira zimene zinachitika Yesu atabwerera kumwamba. Choncho, n’zofunika kwambiri kuphunzira zimene Yesu wakhala akuchita kumwambako. N’chifukwa chiyani? Kumbukirani kuti Yesu anauza Petulo kuti: “Pitiriza kunditsatira.” (Yohane 21:19, 22) Tonsefe tikufunika kumvera lamulo limeneli, osati kwa nthawi yochepa koma kwa moyo wathu wonse. Kuti tithe kuchita zimenezi, tikufunika kudziwa zimene Mbuye wathu akuchita panopa ndiponso udindo umene ali nawo kumwamba.
Zimene Yesu Wakhala Akuchita Atabwerera Kumwamba
4. Kodi Baibulo linaneneratu kuti chidzachitike n’chiyani Yesu akadzabwerera kumwamba?
4 Yesu atabwerera kumwamba, Malemba safotokoza chilichonse chokhudza mmene anamulandirira ndiponso chisangalalo chimene chinalipo atakumananso ndi Atate wake. Komabe, Baibulo linaneneratu zimene zidzachitike Yesu akadzabwerera kumwamba. Ndipotu Ayuda ankachita mwambo winawake wopatulika chaka chilichonse kwa zaka zoposa 1,500. Tsiku limodzi pa chaka, mkulu wa ansembe ankalowa m’Malo Oyera Koposa a kachisi kukawaza magazi a nsembe za Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo pafupi ndi likasa la pangano. Pa tsiku limenelo, mkulu wa ansembe ankaimira Mesiya. Ayuda ankachita mwambo umenewo kuti machimo awo akhululukidwe. Koma Yesu atabwerera kumwamba, anakwaniritsa cholinga cha mwambo umenewo kamodzi kokha, chifukwa anapereka nsembe imene imathandiza anthu onse kuti machimo awo akhululukidwe. Iye atapita kumwamba, kumalo oyera kuposa ena aliwonse, anakaonekera pamaso pa Yehova n’kupereka moyo wake wangwiro kwa Atate ake kuti ukhale nsembe ya dipo. (Aheberi 9:11, 12, 24) Kodi Yehova analandira nsembeyo?
5, 6. (a) Kodi pali umboni uti wosonyeza kuti Yehova analandira nsembe ya dipo ya Khristu? (b) Ndi ndani amene akupindula ndi nsembe ya dipo, nanga akupindula nayo bwanji?
5 Yankho tikulipeza tikaganizira zimene zinachitika patangopita masiku ochepa Yesu atakwera kumwamba. Kagulu ka Akhristu pafupifupi 120 kanasonkhana ku Yerusalemu m’chipinda china cha m’mwamba, ndipo mwadzidzidzi kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu ndipo unadzaza m’chipindamo. Kenako pamutu pawo panaoneka malawi amoto ooneka ngati malilime, ndipo onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera n’kuyamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana. (Machitidwe 2:1-4) Zimene zinachitikazi zinali chizindikiro cha kubadwa kwa mtundu watsopano, womwe ndi Isiraeli wauzimu. Umenewu unali mtundu watsopano wa Mulungu, “fuko losankhidwa mwapadera” komanso “ansembe achifumu,” amene Mulungu anawasankha kuti achite zimene iye amafuna padziko lapansi. (1 Petulo 2:9) N’zoonekeratu kuti Yehova Mulungu analandira ndiponso kuvomereza nsembe ya dipo ya Khristu. Choncho mzimu woyera umene ophunzirawo analandira, unali m’gulu la madalitso oyambirira amene anabwera chifukwa cha dipo.
6 Kuchokera pa nthawi imeneyo, dipo la Khristu lathandiza otsatira ake m’njira zosiyanasiyana padziko lonse. Kaya tili ‘m’kagulu ka nkhosa’ ka Akhristu odzozedwa amene adzalamulire limodzi ndi Khristu kumwamba, kapena tili m’gulu la “nkhosa zina” zimene zidzakhale mu Ufumu wake padziko lapansi, tonsefe timapindula ndi nsembe ya Yesu. (Luka 12:32; Yohane 10:16) Machimo anthu amakhululukidwa chifukwa cha nsembe imeneyi ndiponso tikuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Tikapitiriza ‘kukhulupirira’ dipoli ndiponso kutsatira Yesu tsiku ndi tsiku, tidzakhala ndi chikumbumtima choyera komanso tidzayembekezera zinthu zabwino m’tsogolo.—Yohane 3:16.
7. Kodi Yesu anapatsidwa ulamuliro wotani atabwerera kumwamba, ndipo mungasonyeze bwanji kuti mumavomereza ulamuliro wake?
7 Kodi Yesu wakhala akuchita chiyani atabwerera kumwamba? Iye ali ndi ulamuliro waukulu. (Mateyu 28:18) N’zoonadi, Yehova anamuika kuti azitsogolera mpingo wa Chikhristu ndipo Yesu wakhala akugwira ntchito imeneyi mwachikondi komanso mwachilungamo. (Akolose 1:13) Mogwirizana ndi zimene Malemba ananena, Yesu waika amuna m’maudindo kuti azisamalira nkhosa zake. (Aefeso 4:8) Mwachitsanzo, iye anasankha Paulo kuti akhale “mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina,” kukalalikira uthenga wabwino m’mayiko akutali. (Aroma 11:13; 1 Timoteyo 2:7) Chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, Yesu anapereka uphungu, malangizo, komanso uthenga woyamikira kumipingo 7 ya ku Asia, m’madera olamulidwa ndi Aroma. (Chivumbulutso, chaputala 2 ndi 3) Kodi mumakhulupirira kuti Yesu ndi mutu wa mpingo wa Chikhristu? (Aefeso 5:23) Kuti mupitirizebe kumutsatira, mufunika kukhala omvera komanso kutsatira malangizo mumpingo wanu.
8, 9. Kodi Yesu anapatsidwa udindo wotani mu 1914, nanga zimenezi ziyenera kukhudza bwanji zinthu zimene timasankha?
8 Yesu anapatsidwanso ulamuliro wina mu 1914. M’chaka chimenechi Yesu, amene ndi Mesiya, anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Yehova. Iye atayamba kulamulira, “kumwamba kunabuka nkhondo.” Ndiye kenako chinachitika n’chiyani? Satana ndi ziwanda zake anaponyedwa padziko lapansi ndipo zimenezi zinayambitsa mavuto osiyanasiyana. Timakumbukira kuti Yesu akulamulira kumwamba panopo, tikaona kuchuluka kwa nkhondo, chiwawa, uchigawenga, matenda, zivomerezi ndiponso njala zimene zikuchitika padzikoli. Satana ‘akulamulirabe dzikoli’ ndipo watsala ndi “kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:7-12; Yohane 12:31; Mateyu 24:3-7; Luka 21:11) Komabe, Yesu akupereka mwayi kwa anthu padziko lonse lapansi kuti avomereze kuti iye ndi wolamulira.
9 Choncho, tikufunika kukhala kumbali ya Mesiya yemwenso ndi Mfumu. Tikamasankha zochita tsiku lililonse, tiyenera kuyesetsa kusankha zinthu zimene zingamusangalatse osati zimene zingasangalatse dziko loipali. “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye” yemwe ndi wolungama, amasangalala kwambiri akamaona anthu akuchita zabwino komanso amakwiya akamaona anthu akuchita zoipa. (Chivumbulutso 19:16) N’chifukwa chiyani?
Zimene Zikukwiyitsa Komanso Kusangalatsa Mfumu Yomwe ndi Mesiya
10. Kodi Yesu ndi wotani mwachibadwa, koma n’chiyani chimene chimamukwiyitsa?
10 Mbuye wathu ndi wachimwemwe mwachibadwa monga mmenenso alili Atate wake. (1 Timoteyo 1:11) Yesu ali padziko lapansi sankatola anthu zifukwa ndiponso sanali wovuta kumusangalatsa. Koma padziko lapansi pakuchitika zinthu zambiri masiku ano zimene zikumukwiyitsa. Iye amakwiya ndi zipembedzo zimene zimanama kuti zimamutsatira. Iye ananeneratu kuti: “Sikuti aliyense amene amanditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa Ufumu wakumwamba, koma yekhayo amene akuchita zimene Atate wanga wakumwamba amafuna. Pa tsiku limenelo ambiri adzandiuza kuti: ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife . . . [sitinachite] ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanu?’ Koma ine ndidzawauza kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.’”—Mateyu 7:21-23.
11-13. N’chifukwa chiyani ena angadabwe ndi mawu amphamvu amene Yesu adzanene kwa anthu amene akuchita “ntchito zambiri zamphamvu” m’dzina lake, nanga n’chifukwa chiyani akuwakwiyira? Perekani chitsanzo.
11 Anthu ambiri amene amati ndi Akhristu angadabwe ndi mawu a mulemba limeneli. N’chifukwa chiyani Yesu adzalankhule mwamphamvu chonchi kwa anthu amene akhala akuchita “ntchito zambiri zamphamvu” m’dzina lake? Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu amapereka mphatso zachifundo, amathandiza osauka, amamanga zipatala ndi masukulu ndiponso amachita ntchito zina zambiri. Kuti tidziwe chifukwa chimene chachititsa kuti Yesu awakwiyire, tiyeni tione chitsanzo chotsatirachi.
12 Bambo ndi mayi akufuna kuchokapo, koma sangathe kutenga ana awo pa ulendowo. Choncho akulemba wantchito kuti aziwasamalira ndipo akumuuza kuti: “Uzisamalira anawa, uzionetsetsa kuti adya, asamba ndi kuvala zovala zoyera ndiponso uziwateteza.” Koma makolowo atabwera kuchokera kumene anapitako, akudabwa kuona anawo akulira ndi njala, akuoneka osasamba, odwala ndiponso osasangalala. Ngakhale kuti anawo akulira, wantchitoyo sakuwasamala. Kodi n’chifukwa chiyani sakuwasamala? Iye watanganidwa ndi kutsuka mawindo a nyumba. Makolowo akupsa mtima ndipo akumufunsa chifukwa chake sakusamalira anawo. Wantchitoyo akuyankha kuti: “Onani ntchito imene ndagwira, ndatsuka mawindo onse ndipo ndakukonzerani nyumbayi m’malo ena ndi ena amene anali owonongeka.” Kodi makolowo angasangalale kumva zimenezi? Ayi ndithu. Iwo sanauze wantchitoyo kuti achite zimenezo, koma anamuuza kuti asamalire ana basi. Makolowo angakwiye kwambiri chifukwa wantchitoyo sanamvere zimene anamuuza kuti achite.
13 Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu achita zinthu zofanana ndi zimene wantchitoyu anachita. Yesu anapereka malangizo kwa otsatira ake kuti azidyetsa anthu mwauzimu powaphunzitsa choonadi cha m’Mawu a Mulungu ndi kuwathandiza kuti akhale oyera mwauzimu. (Yohane 21:15-17) Koma Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu alephereratu kutsatira malangizo amenewa. Iwo achititsa kuti anthu akhale ndi njala yauzimu, awaphunzitsa zinthu zabodza ndipo zimenezi zachititsa kuti anthu asadziwe mfundo zofunika za choonadi cha m’Baibulo. (Yesaya 65:13; Amosi 8:11) Ngakhale kuti matchalitchiwa akuchita zinthu zothandiza kuti dzikoli litukuke, palibe chifukwa chomveka cholepherera kutsatira malangizo a Yesu. Ndipotu, dzikoli lili ngati nyumba imene ikufunika kugwetsedwa. Komanso Mawu a Mulungu amanena momveka bwino kuti dziko la Satanali liwonongedwa posachedwapa.—1 Yohane 2:15-17.
14. Kodi Yesu amasangalala ndi ntchito iti masiku ano, ndipo n’chifukwa chiyani?
14 Mosiyana ndi zimenezi, Yesu ayenera kuti amasangalala kwambiri akayang’ana padziko lapansi n’kuona anthu mamiliyoni ambiri akugwira ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake. Yesu anasiyira ntchito imeneyi otsatira ake asanabwerere kumwamba. (Mateyu 28:19, 20) Kugwira ntchito yosangalatsa Mesiya yemwenso ndi Mfumu, ndi mwayi waukulu kwambiri. Choncho, tiyeni tipitirize kuthandiza “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” pogwira ntchito imeneyi mwakhama. (Mateyu 24:45) Mosiyana ndi atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu, Akhristu odzozedwa akusonyeza kuti ndi omvera ndipo akutsogolera ntchito yolalikira komanso akudyetsa mokhulupirika nkhosa za Khristu.
15, 16. (a) Kodi Yesu amamva bwanji akamaona kuti anthu ambiri alibe chikondi masiku ano, ndipo tikudziwa bwanji kuti amamva choncho? (b) N’chifukwa chiyani Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu amakwiyitsa Yesu?
15 Sitikukayikira kuti Mfumuyi imakwiya ikaona kuti anthu ambiri alibe chikondi masiku ano. Mwina tingakumbukire kuti Afarisi ankadzudzula Yesu akachiritsa munthu pa Sabata. Iwo anali ouma mtima kwambiri ndipo ankangotsatira Chilamulo cha Mose chimene ankachitanthauzira molakwika ndiponso malamulo amene anapanga okha. Zozizwitsa zimene Yesu ankachita zinkathandiza anthu kwambiri, koma Afarisi analibe nazo ntchito ngakhale kuti zinkasangalatsa anthu, kuwathandiza ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Kodi Yesu ankamva bwanji ndi zimene Afarisiwo ankachita? Nthawi ina, iye “anawayang’ana mokwiya ndipo anamva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.”—Maliko 3:5.
16 Masiku anonso, Yesu amaona zinthu zambiri zimene ‘zimamumvetsa chisoni kwambiri.’ Atsogoleri a zipembedzo achita khungu chifukwa chodzipereka kwambiri potsatira miyambo ndi ziphunzitso zawo zimene sizigwirizana ndi Malemba. Komanso amakwiya akaona kuti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa. M’mayiko ambiri, atsogoleri a zipembedzo achititsa kuti Akhristu amene amayesetsa kulalikira moona mtima uthenga umene Yesu ankalalikira, azizunzidwa kwambiri. (Yohane 16:2; Chivumbulutso 18:4, 24) Ndiponso nthawi zambiri atsogoleri a zipembedzo amenewa amalimbikitsa otsatira awo kuti azipita kunkhondo n’kukapha anthu. Ndipo amachita zimenezi mwakhama ngakhale kuti Yesu Khristu sasangalala nazo.
17. Kodi otsatira enieni a Yesu amasangalatsa bwanji mtima wake?
17 Mosiyana ndi atsogoleri a zipembedzo, otsatira enieni a Yesu amayesetsa kukonda anthu ena. Ngakhale akamatsutsidwa, iwo amatsanzira Yesu popitiriza kulalikira uthenga wabwino kwa “anthu osiyanasiyana.” (1 Timoteyo 2:4) Iwo amakondana kwambiri ndipo chimenechi ndi chizindikiro chachikulu chimene anthu amawadziwira. (Yohane 13:34, 35) Akhristu akamakondana ndi kulemekezana amasonyeza kuti akutsatiradi Yesu ndipo amasangalatsa mtima wa Mesiya yemwenso ndi Mfumu.
18. Kodi n’chiyani chimene chimakhumudwitsa kwambiri Mbuye wathu, nanga ifeyo tingatani kuti tizimusangalatsa?
18 Tiyeneranso kudziwa kuti Mbuye wathu amakhumudwa akaona otsatira ake akulephera kupirira, akusiya kukonda Yehova ndiponso akusiya kumutumikira. (Chivumbulutso 2:4, 5) Koma Yesu amasangalala ndi anthu amene amapirira mpaka mapeto. (Mateyu 24:13) Choncho, tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti tipitirize kumvera lamulo la Khristu lakuti: “Pitiriza kunditsatira.” (Yohane 21:19) Tiyeni tikambirane ena mwa madalitso amene Mesiya yemwenso ndi Mfumu adzapereke kwa anthu amene adzapirire mpaka mapeto.
Atumiki Okhulupirika a Mfumuyi Akupitiriza Kulandira Madalitso
19, 20. (a) Kodi kutsatira Yesu kumabweretsa madalitso otani panopa? (b) Kodi kutsatira Khristu kungatithandize bwanji kuti iye akhale ‘Atate wathu Wamuyaya’?
19 Kutsatira Yesu ndi njira imene ingatithandize kupeza madalitso panopa. Tikamavomereza Khristu kuti ndi Mbuye wathu ndiponso tikamatsatira malangizo ake ndi chitsanzo chake, tidzapeza chuma chimene anthu padziko lonse amachifunafuna koma osachipeza. Tidzakhala ndi ntchito yabwino ndiponso yosangalatsa, tidzakhala m’gulu la Akhristu omwe amagwirizana komanso kukondana kuchokera pansi pa mtima, tidzakhala ndi chikumbumtima choyera komanso mtendere wa mumtima. Mwachidule tinganene kuti tidzakhala ndi moyo wosangalatsa ndiponso tidzapeza madalitso ena ambiri.
20 Yehova wapereka Yesu kuti akhale “Atate Wamuyaya” wa anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Yesu analowa m’malo mwa kholo lathu loyamba, Adamu, amene anabweretsera ana ake onse mavuto oopsa. (Yesaya 9:6, 7) Tikamavomereza kuti Yesu ndi ‘Atate wathu Wamuyaya,’ komanso tikamamukhulupirira, tingakhale otsimikiza kuti tidzapeza moyo wosatha. Ndiponso tikamachita zimenezi, tidzayandikira kwambiri Yehova Mulungu. Monga mmene taonera, kuyesetsa kutsanzira Yesu tsiku ndi tsiku ndi njira yabwino koposa yomvera lamulo la Mulungu lakuti: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.”—Aefeso 5:1.
21. Kodi otsatira a Khristu amasonyeza bwanji kuwala m’dziko la mdimali?
21 Tikamatsanzira Yesu ndiponso Atate wake Yehova, timakhala ndi mwayi wapadera wosonyeza kuwala kwambiri. M’dziko la mdimali, limene anthu ambiri asocheretsedwa ndi Satana ndipo amasonyeza makhalidwe ake, ife amene tikutsatira Khristu timasonyeza kuwala kwambiri. Kuwala kumeneku ndi kwa choonadi cha m’Malemba, kuwala kwa makhalidwe abwino a Chikhristu, kuwala kwa chimwemwe chenicheni, mtendere weniweni ndiponso chikondi chenicheni. Tikamachita zimenezi, timayandikira kwambiri Yehova ndipo chimenechi ndi cholinga chachikulu chimene munthu komanso mngelo aliyense ayenera kukhala nacho.
22, 23. (a) Kodi anthu amene akutsatira Yesu mokhulupirika adzalandira madalitso otani m’tsogolo? (b) Kodi tiyenera kutsimikiza kuchita chiyani?
22 Taganizirani zimene Yehova akufuna kukuchitirani m’tsogolo pogwiritsira ntchito Mesiya yemwenso ndi Mfumu. Posachedwapa Mfumu imeneyi imenya nkhondo yolungama n’kuwononga Satana ndi dziko lake loipali. Sitikukayikira m’pang’ono pomwe kuti Yesu adzapambana. (Chivumbulutso 19:11-15) Kenako, Khristu adzalamulira dziko lapansi kwa zaka 1,000. Boma lake limene lili kumwamba lidzabweretsa madalitso kwa anthu onse okhulupirika. Madalitso amenewa adzatheka chifukwa cha nsembe ya dipo ndipo kenako anthuwo adzakhala angwiro. Yerekezerani kuti inuyo muli m’dziko limeneli ndipo simukudwala, simukukalamba, muli ndi mphamvu komanso mogwirizana ndi anthu ena onse, mukusangalala kugwira ntchito yokonza dziko kuti likhale paradaiso. Pamapeto pa zaka 1,000 zimenezo, Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24) Mukapitiriza kutsatira Khristu mokhulupirika mudzalandira madalitso osangalatsa kwambiri komanso amene sitingawayerekezere ndi chilichonse, chifukwa mudzakhala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Inde, tidzakhala ndi madalitso onse amene Adamu ndi Hava anali nawo asanachimwe. Monga ana a Yehova aamuna ndi aakazi, tidzamasuka ku uchimo wa Adamu. N’zoonadi, “imfa sidzakhalaponso.”—Chivumbulutso 21:4.
23 Takumbukirani wolamulira wachinyamata uja yemwenso anali wolemera, amene tinamutchula m’mutu woyamba. Yesu atamuitana kuti: “Ubwere udzakhale wotsatira wanga,” iye anakana. (Maliko 10:17-22) Musayerekeze kuchita zimene wolamulira ameneyu anachita. Vomerani kuitana kwa Yesu mosangalala ndiponso mofunitsitsa. Khalani otsimikiza kupirira, kupitiriza kutsatira M’busa Wabwino tsiku ndi tsiku ndiponso chaka ndi chaka kuti mudzaone akukwaniritsa mochititsa chidwi zolinga zonse za Yehova.