Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 4

“Taona! Mkango wa Fuko la Yuda”

“Taona! Mkango wa Fuko la Yuda”

“Ndi ineyo”

1-3. Kodi Yesu anakumana ndi zinthu zoopsa ziti, nanga iye anatani?

 PA NTHAWI ina, gulu la anthu linapita kukafunafuna Yesu kuti limugwire. Pagululi panali amuna amene ananyamula malupanga ndi zibonga komanso panali asilikali. Popeza gulu la anthuwo linali ndi cholinga choipa, linayenda usiku m’misewu ya mu Yerusalemu kuwoloka chigwa cha Kidironi kupita kuphiri la Maolivi. Ngakhale kuti kunja kunali mwezi, anthuwo ananyamula zounikira. Kodi anthuwo ananyamula zounikirazo chifukwa chakuti mitambo inkaphimba mweziwo? Kapena kodi ankaganiza kuti munthu amene akufuna kumugwirayo angabisale? Sitikudziwa, koma chimene tikudziwa n’chakuti amene angaganize kuti Yesu ankachita mantha, ndiye kuti sakumudziwa bwino.

2 Yesu ankadziwa kuti anthu akubwera kudzamugwira, koma iye sanathawe. Anthuwo anafika ndipo Yudasi, yemwe poyamba anali mnzake weniweni wa Yesu, ndi amene ankawatsogolera. Mopanda manyazi Yudasi anapereka Yesu, amene kale anali mbuye wake, pomupatsa moni wachiphamaso ndiponso kumukisa. Komabe, Yesu sanachite mantha ndipo anapita kukakumana ndi anthuwo. Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndani?” Ndipo iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.”

3 Ambirife tingachite mantha gulu la anthu onyamula zida ngati amenewa litabwera kudzatigwira. Mwina anthuwa ankaganizanso kuti Yesu achita mantha kwambiri. Koma iye sanaope, sanathawe ndiponso sananame kuti adzipulumutse. M’malomwake iye anangonena kuti: “Ndi ineyo.” Iye ananena zimenezi mtima uli m’malo komanso mopanda mantha ndipo anthuwo anadabwa kwambiri, moti anabwerera m’mbuyo n’kugwa pansi.​—Yohane 18:1-6; Mateyu 26:45-50; Maliko 14:41-46.

4-6. (a) Kodi Mwana wa Mulungu amuyerekezera ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi Yesu anachita zinthu zitatu ziti zimene zimasonyeza kuti anali wolimba mtima?

4 N’chifukwa chiyani Yesu sanachite mantha kapena kunjenjemera gulu loopsali litabwera kudzamugwira? Kuyankha mwachidule tinganene kuti anali wolimba mtima. Kulimba mtima ndi limodzi mwa makhalidwe ofunika kwambiri ndiponso osiririka amene mtsogoleri aliyense ayenera kukhala nawo. Ndipo palibe munthu amene angafanane ndi Yesu kapena kum’posa pa nkhani ya kulimba mtima. M’mutu wapita uja, tinaphunzira kuti Yesu anali wodzichepetsa komanso wofatsa kwambiri. N’chifukwa chake ankatchedwa kuti “Mwanawankhosa.” (Yohane 1:29) Koma chifukwa choti Yesu anali wolimba mtima, Baibulo limatchula Mwana wa Mulungu ameneyu ndi dzina lapadera. Limati: “Taona! Mkango wa fuko la Yuda.”​—Chivumbulutso 5:5.

5 Mkango ndi nyama yolimba mtima kwambiri. Kodi munayamba mwaonapo maso ndi maso mkango waukulu waumuna? Ngati munauona, mwina mkangowo unali m’malo osungirako nyama zakutchire otetezedwa ndi mpanda. Komabe kuona mkango maso ndi maso, ngakhale uli mumpanda, n’kochititsa mantha. Mukamayang’anizana maso ndi maso ndi nyama yaikulu komanso yamphamvu imeneyi, simungaganize kuti mkangowo ungathawe chilichonse chifukwa cha mantha. Baibulo limanena kuti ‘mkango ndi wamphamvu kwambiri pa nyama zonse zakutchire ndiponso suopa chilichonse n’kubwerera m’mbuyo.’ (Miyambo 30:30) Khristu ndi wolimbanso mtima ngati mkango.

6 Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene Yesu anachita zimene zimasonyeza kuti anali wolimba mtima ngati mkango. Tiona zimene anachita poteteza choonadi, potsatira chilungamo ndiponso pamene ankatsutsidwa. Tionanso kuti tonsefe, kaya ndife olimba mtima mwachibadwa kapena ayi, tingathe kutsanzira Yesu posonyeza kulimba mtima.

Yesu Anateteza Choonadi Molimba Mtima

7-9. (a) Kodi chinachitika n’chiyani Yesu ali ndi zaka 12, nanga n’chifukwa n’chiyani mukuona kuti zimene anachitazo zinali zochititsa mantha? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima pokambirana ndi aphunzitsi pakachisi?

7 M’dziko lolamuliridwa ndi Satanali, yemwe ndi “tate wake wa bodza,” pamafunika kulimba mtima kuti munthu ateteze choonadi. (Yohane 8:44; 14:30) Yesu ankateteza choonadi molimba mtima kuyambira ali wamng’ono. Mwachitsanzo, ali ndi zaka 12 anasiyana ndi makolo ake pambuyo pa chikondwerero cha Pasika ku Yerusalemu. Kwa masiku atatu, Mariya ndi Yosefe anamufufuza ali ndi nkhawa kwambiri. Kenako anamupeza m’kachisi. Kodi ankachita chiyani m’kachisimo? Anamupeza “atakhala pakati pa aphunzitsi ndipo ankawamvetsera n’kumawafunsa mafunso.” (Luka 2:41-50) Ndiye taganizirani mmene zinthu zinalili pamene ankakambirana ndi aphunzitsiwo.

8 Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti atsogoleri ena achipembedzo olemekezeka ankakonda kutsalira pakachisi pambuyo pa zikondwerero ndipo ankaphunzitsa anthu pakhonde lina lalikulu la kachisiyo. Anthu ankakhala pansi n’kumawamvetsera komanso kuwafunsa mafunso. Aphunzitsi amenewa anali ophunzira kwambiri moti ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose. Ankadziwanso bwino miyambo yawo yambirimbiri komanso malamulo ambirimbiri opanga okha amene anali ovuta kuwamvetsa. Kodi mukanamva bwanji ngati mukanakhala pakati pa anthu ngati amenewo? N’zosakayikitsa kuti mukanachita mantha ndipo zimenezo sizikanakhala zodabwitsa. Nanga bwanji mukanakhala kuti muli ndi zaka 12 zokha? N’zodziwikiratu kuti mukanaopa kwambiri chifukwa ana ambiri amachita mantha ndiponso manyazi. (Yeremiya 1:6) Ana ena akakhala m’kalasi amayesetsa kuchita zinthu zoti aphunzitsi awo asawatchule kuti ayankhe funso chifukwa amaopa kuti angachite manyazi kapena anzawo angawaseke.

9 Koma Yesu anali wolimba mtima chifukwa anakhala pakati pa anthu ophunzira kwambiri ndipo ankawafunsa mafunso okhwima molimba mtima. Ndipo si zokhazi zimene anachita. Nkhani ya m’Baibuloyi imati: “Onse amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:47) Baibulo silinena zimene iye ananena pa nthawiyo, komabe tikukhulupirira kuti sankanena zinthu zabodza zimene aphunzitsi achipembedzowo ankakonda kuphunzitsa. (1 Petulo 2:22) Iye anateteza choonadi cha m’Mawu a Mulungu, ndipo anthu amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri kuti mwana wa zaka 12 akulankhula zinthu zanzeru molimba mtima.

Akhristu ambiri achinyamata amauza anzawo molimba mtima zimene amakhulupirira

10. Kodi Akhristu achinyamata masiku ano amatsanzira bwanji kulimba mtima kwa Yesu?

10 Masiku ano, achinyamata ambiri a Chikhristu akutsanzira Yesu. N’zoona kuti iwo ndi osiyana ndi Yesu chifukwa si angwiro. Komabe mofanana ndi Yesu, iwo sayembekeza kuti akule kaye kuti adzateteze choonadi. Mwachitsanzo, kusukulu kapena m’madera amene akukhala, iwo amafunsa anthu mafunso mwanzeru, amawamvetsera ndipo amawauza choonadi mwaulemu. (1 Petulo 3:15) Achinyamata amenewa athandiza ana asukulu anzawo, aphunzitsi awo komanso anthu amene amakhala moyandikana nawo kukhala otsatira a Khristu. Iwo amasangalatsa kwambiri Yehova chifukwa cha kulimba mtima kwawo. Mawu a Mulungu anayerekezera achinyamata amenewa ndi mame chifukwa amakhala otsitsimula, osangalatsa ndiponso ochuluka.​—Salimo 110:3.

11, 12. Kodi Yesu atakula anasonyeza bwanji kulimba mtima poteteza choonadi?

11 Yesu atakula anasonyezanso kulimba mtima mobwerezabwereza poteteza choonadi. Ndipotu anthu ambiri angavomereze kuti zimene zinachitika pamene ankayamba utumiki wake zinali zoopsa. Yesu anafunika kulimbana ndi Satana, amene ndi mdani wa Yehova wamphamvu komanso woopsa kwambiri pa adani ake onse. Komatu pa nthawiyi Yesu anali munthu wamba, sanali mkulu wa angelo wamphamvu ayi. Komabe iye anatsutsa Satana ndipo anakana kuchita zimene anamupempha, Satanayo atagwiritsa ntchito Malemba molakwika. Pamapeto pake, Yesu anathetsa zokambiranazo pokalipira Satana kuti: “Choka Satana!”​—Mateyu 4:2-11.

12 Choncho Yesu anasonyeza kuti pa utumiki wake, adziteteza Mawu a Atate ake molimba mtima kuti asapotozedwe kapena kugwiritsidwa ntchito molakwika. Mofanana ndi masiku ano, pa nthawiyo atsogoleri ambiri achipembedzo anali osaona mtima. N’chifukwa chake Yesu anauza atsogoleri achipembedzo a nthawi imeneyo kuti: “Mumapangitsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu imene munaipereka kwa anthu.” (Maliko 7:13) Anthu ankalemekeza kwambiri atsogoleri amenewo, koma Yesu anawadzudzula mopanda mantha ndipo anawanena kuti ndi atsogoleri akhungu komanso anthu achinyengo. a (Mateyu 23:13, 16) Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yesu kumeneku?

13. Tikamatsanzira Yesu, kodi tizikumbukira chiyani, nanga tili ndi mwayi wapadera uti?

13 N’zoona kuti tilibe mphamvu yodziwa za mumtima mwa munthu kapena yoweruza anthu ngati mmene Yesu ankachitira. Komabe tingateteze choonadi molimba mtima ngati mmene iye ankachitira. Mwachitsanzo, tikamatsutsa mabodza amene zipembedzo zimaphunzitsa, monga onena za Mulungu, cholinga chake komanso Mawu ake, timathandiza anthu kuti aone kuwala kwa choonadi m’dziko limene Satana walichititsa mdima ndi ziphunzitso zake zabodza. (Mateyu 5:14; Chivumbulutso 12:9, 10) Timathandiza anthu kuti amasuke ku ziphunzitso zabodza zimene zimawachititsa kuti aziopa zinthu zomwe sizingachitike ndiponso zimene zimawononga ubwenzi wawo ndi Mulungu. Tilitu ndi mwayi wapadera kwambiri kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

Molimba Mtima, Yesu Ankaonetsetsa Kuti Zinthu Zikuchitika Mwachilungamo

14, 15. (a) Kodi ndi njira imodzi iti imene Yesu anasonyezera bwinobwino “chilungamo chenicheni”? (b) Kodi Yesu anapewa maganizo a tsankho ati kuti athe kulankhula ndi mkazi wa Chisamariya?

14 Ulosi wa m’Baibulo unaneneratu kuti Mesiya adzasonyeza bwinobwino anthu a mitundu ina “chilungamo chenicheni.” (Mateyu 12:18; Yesaya 42:1) Yesu anayamba kuchita zimenezi ali padziko lapansi pano. Yesu anali wolimba mtima ndipo nthawi zonse ankachita zinthu mwachilungamo komanso mopanda tsankho. Mwachitsanzo, ngakhale kuti anthu ambiri ankachita zinthu mwatsankho ndiponso mokondera, Yesu anakana kuchita nawo zimenezi chifukwa zinali zosagwirizana ndi malemba.

15 Pamene Yesu ankalankhula ndi mayi wa Chisamariya pachitsime cha ku Sukari, ophunzira ake anadabwa kwambiri. N’chifukwa chiyani anadabwa? Pa nthawi imeneyo, Ayuda ankadana kwambiri ndi Asamariya ndipo chidani chimenechi chinayamba kale kwambiri Yesu asanabwere padziko lapansi. (Ezara 4:4) Komanso arabi ena ankakhulupirira kuti akazi ndi otsika poyerekezera ndi amuna. Iwo anafika polemba malamulo oletsa amuna kuti asamalankhule ndi akazi. Ankaonanso kuti akazi si oyenera kuwaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu ndipo akazi a Chisamariya ankawaona kuti ndi odetsedwa. Koma Yesu sanatengere maganizo a tsankho amenewo. Mosabisa, Yesu anaphunzitsa mkazi wa Chisamariya (amene anali wachiwerewere) ndipo anauza mkaziyo kuti iye ndi Mesiya.​—Yohane 4:5-27.

16. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala olimba mtima kuti apewe tsankho?

16 Kodi munayamba mwakhalapo ndi anthu atsankho? Mwina iwo amanena nthabwala zonyoza anthu a mtundu kapena fuko lina, amalankhula zinthu zonyoza anthu amene si amuna kapena akazi anzawo, kapenanso amanyoza anthu ooneka ngati onyozeka kapena osauka. Otsatira a Khristu amapewa khalidwe limeneli ndipo amachita khama kuti achotse maganizo alionse atsankho mumtima mwawo. (Machitidwe 10:34) Aliyense wa ife ayenera kukhala wolimba mtima kuti apewe tsankho.

17. Kodi Yesu anachita chiyani m’kachisi, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezo?

17 Popeza anali wolimba mtima, Yesu analimbikitsa anthu a Mulungu kuti akhale oyera ndiponso kuti kulambira kwawo kukhale kosadetsedwa. Kumayambiriro kwa utumiki wake, iye analowa m’kachisi wa ku Yerusalemu ndipo ananyansidwa kwambiri ataona anthu akugulitsa malonda ndi kusintha ndalama m’kachisimo. M’pomveka kuti Yesu anakwiya ndipo anathamangitsa anthu adyerawo n’kutulutsa malonda awo m’kachisimo. (Yohane 2:13-17) Kenako, atatsala pang’ono kutsiriza utumiki wake padzikoli, Yesu anachitanso chimodzimodzi. (Maliko 11:15-18) Anthu ena anayamba kudana naye kwambiri chifukwa cha zimenezi, komabe iye anapitiriza kutsatira chilungamo. Chifukwa chiyani? Kuyambira ali wamng’ono, ankanena kuti kachisiyo ndi nyumba ya Atate ake ndipo zinali zoona. (Luka 2:49) Kuchita zinthu zodetsa kulambira koyera kumene kunkachitika pakachisiyo kunali kupanda chilungamo ndipo iye sakanalekerera zimenezo. Chifukwa chakuti anali wodzipereka kwambiri, iye analimba mtima n’kuchita zimene zinali zoyenera.

18. Kodi Akhristu masiku ano angasonyeze bwanji kulimba mtima kuti mpingo ukhalebe woyera?

18 Mofanana ndi Yesu, otsatira a Khristu masiku ano amafunitsitsa kuti aliyense m’gulu la atumiki a Mulungu akhale woyera komanso kuti apitirize kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Iwo salekerera akadziwa kuti Mkhristu mnzawo wachita tchimo lalikulu, koma molimba mtima amalankhula naye. (1 Akorinto 1:11) Amaonetsetsa kuti akulu mumpingo adziwa za nkhaniyo. Akulu amathandiza anthu amene akudwala mwauzimu ndipo amayesetsa kuteteza nkhosa za Yehova kuti zisadetsedwe.​—Yakobo 5:14, 15.

19, 20. (a) Kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamo zimene zinkachitika m’masiku a Yesu, nanga ndi mavuto otani amene Yesu anakumana nawo? (b) N’chifukwa chiyani otsatira Khristu amakana kulowerera ndale komanso kuchita zachiwawa, nanga amapeza madalitso otani chifukwa cha zimenezi?

19 Kodi tinganene kuti Yesu ankafuna kuthetsa zinthu zonse zopanda chilungamo? Ayi. Zinthu zambiri zopanda chilungamo zinkachitika paliponse. Mwachitsanzo, dziko limene iye anabadwira linkalamuliridwa ndi Aroma. Iwo ankagwiritsira ntchito asilikali awo pozunza Ayudawo ndipo ankawalamula kuti azipereka ndalama zambiri za msonkho komanso ankasokoneza miyambo ya chipembedzo chawo. N’chifukwa chake Ayuda ambiri ankafuna kuti Yesu azichita nawo ndale kuti akhale mtsogoleri wawo. (Yohane 6:14, 15) Apanso, Yesu ankafunika kusonyeza kulimba mtima.

20 Yesu anafotokoza kuti Ufumu wake sunali wa padziko lapansi. Iye anaphunzitsa otsatira ake kuti asamalowerere m’mikangano ya ndale za nthawi imeneyo ndipo anachita zimenezi powasonyeza chitsanzo chabwino. Komanso anawalimbikitsa kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Yohane 17:16; 18:36) Iye anawapatsa phunziro labwino pankhani yopewa chiwawa, pamene gulu la anthu linabwera kuti lidzamugwire. Mwamsanga Petulo anasolola lupanga lake n’kuvulaza munthu wina pagululo. Anthu angaganize kuti Petulo sanalakwitse kugwiritsa ntchito lupanga pamene anthu anabwera kudzagwira Mwana wa Mulungu yemwe anali wosalakwa. Koma pa nthawiyo Yesu anapereka phunziro limene likugwirabe ntchito kwa otsatira ake mpaka lero. Iye anati: “Bwezera lupanga lako m’chimake, chifukwa onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:51-54) Otsatira a Khristu ankafunika kukhala olimba mtima kuti athe kuchita zinthu mwamtendere pa nthawi imeneyo ndipo masiku anonso timafunika kulimba mtima. Anthu a Mulungu masiku ano ali ndi mbiri yabwino yoti samenya nawo nkhondo, sachita ziwawa ndi zina zotero chifukwa chakuti salowerera ndale. Amenewatu ndi madalitso amene amapeza chifukwa cha kulimba mtima kwawo.

Yesu Analimba Mtima Pamene Ankatsutsidwa

21, 22. (a) Kodi Yesu analimbikitsidwa bwanji asanayambe kukumana ndi mayesero aakulu? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima mpaka imfa?

21 Mwana wa Yehova ankadziwa bwino kuti akadzabwera padziko lapansi adzatsutsidwa kwambiri. (Yesaya 50:4-7) Anthu osiyanasiyana ankafuna kumupha ndipo zolinga zawozo zinakwaniritsidwadi monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino. Kodi Yesu anatani kuti akhalebe wolimba mtima pa nthawi yovutayo? Kumbukirani zimene Yesu ankachita gulu la anthu lija lisanafike kudzamugwira. Iye ankapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Ndipo Yehova anamuyankha chifukwa Baibulo limanena kuti “anamumvera.” (Aheberi 5:7) Yehova anatumiza mngelo kuchokera kumwamba kuti adzalimbikitse Mwana wake wolimba mtimayo.​—Luka 22:42, 43.

22 Patangopita nthawi yochepa mngeloyo atamulimbikitsa, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita.” (Mateyu 26:46) Mawu amenewatu akusonyeza kuti Yesu anali wolimba mtima kwambiri. Ngakhale ananena kuti “nyamukani, tiyeni tizipita,” Yesu ankadziwa kuti auza gulu la anthu odzamugwirawo kuti asavulaze anzakewo. Ankadziwanso kuti anzakewo amusiya n’kuthawa komanso kuti akhala yekhayekha akamazunzidwa mwankhanza kwambiri. Iye analidi yekhayekha pamene ankamuimba mlandu womunamizira ndi kumuweruza mopanda chilungamo, kumunyoza, kumuzunza komanso kumupha mwankhanza. Pa nthawi yonse imene ankazunzikayo, Yesu anakhalabe wolimba mtima.

23. Fotokozani chifukwa chake tikunena kuti zimene Yesu anachita pamene anthu ankafuna kumupha sizikusonyeza kuti sankasamala za moyo wake.

23 Kodi Yesu anasonyeza kuti sankasamala za moyo wake? Ayi si choncho, chifukwa kulimba mtima n’kosiyana ndi kuchita zinthu mosasamala. Ndipotu polimbikitsa otsatira ake kuti apitirize kutumikira Mulungu, Yesu anawauza kuti azikhala osamala komanso kuti azichoka pamalo akaona kuti china chake choopsa chichitika. (Mateyu 4:12; 10:16) Koma pa nthawiyi, Yesu ankadziwa kuti palibe chilichonse chimene akanachita kuti apewe mayeserowo. Ankadziwa zimene Mulungu akufuna kuti iyeyo achite. Yesu anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupirika, choncho sakanachitira mwina koma kulola kuti akumane ndi mayeserowo basi.

A Mboni za Yehova amasonyeza kulimba mtima akamazunzidwa

24. N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti tingakhalebe olimba mtima pamene takumana ndi mayesero alionse?

24 N’zosangalatsa kuti otsatira a Yesu mobwerezabwereza atengera chitsanzo cha Mbuye wawo molimba mtima. Ambiri asonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba akamanyozedwa, kuzunzidwa, kumangidwa, kumenyedwa mwankhanza ngakhale kulolera kuphedwa kumene. Kodi zimatheka bwanji kuti anthu omwe si angwiro akhale olimba mtima choncho? Sikuti zimangochitika mwamwayi. Mulungu ndi amene anathandiza Yesu ndipo amathandizanso otsatira ake. (Afilipi 4:13) Choncho musamaope zimene zingadzakuchitikireni m’tsogolo. Koma tsimikizani mtima kuti mukhalabe okhulupirika ndipo Yehova adzakuthandizani kuti mukhale olimba mtima. Chitsanzo cha Mtsogoleri wathu Yesu chizikulimbitsani mtima, chifukwa iye anati: “Limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”​—Yohane 16:33.

a Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti anthu ankalemekeza kwambiri manda a atsogoleri a chipembedzo ngati mmene ankalemekezera manda a aneneri ndi makolo akale.