Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

“Ndine . . . Wodzichepetsa”

“Ndine . . . Wodzichepetsa”

“Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe”

1-3. Kodi Yesu analowa bwanji mu Yerusalemu, nanga n’chifukwa chiyani anthu ena amene anaona zimenezi anadabwa?

 MUMZINDA wa Yerusalemu munali chisangalalo chokhachokha chifukwa anthu ankayembekezera munthu wofunika kwambiri amene anali atatsala pang’ono kulowa mumzindawo. Anthu ena anali atasonkhana m’mbali mwa msewu, kunja kwa mzindawo. Anthuwo ankayembekezera mwachidwi kulandira munthu ameneyu chifukwa anthu ena ankanena kuti iye ndi wolowa ufumu wa Davide ndipo ndi woyenera kukhala Mfumu ya Isiraeli. Ndipo ena mwa anthuwo ananyamula masamba a kanjedza n’kumawakupiza m’mwamba posonyeza kumulandira ndipo ena anayala zovala zawo ndiponso nthambi za mitengo mumsewu kuti iye adutsemo bwino. (Mateyu 21:7, 8; Yohane 12:12, 13) Komabe, anthu ambiri ayenera kuti ankadzifunsa kuti, kodi munthu ameneyu alowa bwanji mumzindawu?

2 Ena mwina ankaganiza kuti iye alowa mumzindawo modzionetsera chifukwa ayenera kuti ankadziwa anthu ena olemekezeka amene anachitapo zimenezi. Mwachitsanzo, Abisalomu mwana wa Davide, atadziika yekha kukhala mfumu, anasankha anthu 50 kuti azithamanga patsogolo pa galeta limene iye anakwera. (2 Samueli 15:1, 10) Komanso Juliasi Kaisara, yemwe anali wolamulira wa Chiroma, anachita zinthu mokokomeza kwambiri. Pa nthawi ina iye anayenda ulendo wachionetsero chosonyeza kuti wapambana pa nkhondo, mpaka kukafika kunyumba ya chifumu ya ku Roma. Ndipo pa ulendo wakewo anali ndi njovu zokwana 40 zimene anazimangirira nyale. Njovuzo zinkayenda kudzanja lake lamanja ndipo zina zinkayenda kudzanja lake lamanzere. Koma pa nthawiyi, anthu a ku Yerusalemu ankayembekezera munthu wofunika kwambiri kuposa anthu onsewa. Kaya gulu la anthulo limadziwa kapena ayi, munthu ameneyu anali Mesiya, munthu wofunika kwambiri kuposa onse amene anakhalapo. Komabe mwina anthu ena anadabwa ndi mmene munthu yemwe ankayembekezera kudzakhala Mfumu ameneyu analowera mumzindawo.

3 Panalibe magaleta, anthu othamanga pansi, mahatchi ndiponso panalibe njovu. Yesu anakwera pabulu, nyama yomwe ndi yonyozeka kwambiri. a Iye sanavale zovala zapadera zosonyeza ulemerero wake ndiponso pabulu amene anakwerapo sanaikepo chokhalira chamtengo wapatali. M’malomwake, otsatira ake amene ankamukonda kwambiri, anayala zovala zawo pamsana pa buluyo kuti iye akhalepo. N’chifukwa chiyani Yesu analowa mumzinda wa Yerusalemu modzichepetsa chonchi, pamene anthu amene anali ndi udindo wotsika kwambiri poyerekezera ndi iyeyo anasankha kuchita zinthu modzionetsera kwambiri?

4. Kodi Baibulo linalosera kuti Mfumu yemwenso ndi Mesiya adzalowa bwanji mumzinda wa Yerusalemu?

4 Yesu anakwaniritsa ulosi wakuti: “Sangalala kwambiri. Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe. Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso. Ndi yodzichepetsa ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.” (Zekariya 9:9) Ulosi umenewu ukusonyeza kuti Wodzozedwa wa Mulungu, kapena kuti Mesiya, tsiku lina adzadziulula kwa anthu a ku Yerusalemu kuti ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Ndipo mmene anadziululira komanso nyama imene anasankha kukwera, zinasonyeza kuti anali ndi khalidwe labwino kwambiri lodzichepetsa.

5. N’chifukwa chiyani timakhudzidwa mtima kwambiri tikamaphunzira za kudzichepetsa kwa Yesu, nanga n’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizimutsanzira?

5 Kudzichepetsa ndi limodzi mwa makhalidwe abwino kwambiri amene Yesu ali nawo ndipo timakhudzidwa mtima kwambiri tikamaphunzira za khalidwe limeneli. Monga mmene tinaonera m’mutu wapita uja, Yesu yekha ndi amene ali “njira, choonadi ndi moyo.” (Yohane 14:6) N’zoonekeratu kuti pa anthu mabiliyoni ambirimbiri amene anakhalapo padzikoli, palibe munthu amene angafanane ndi Mwana wa Mulungu. Ngakhale zili choncho, Yesu sanasonyeze m’pang’ono pomwe kuti anali wonyada kapena wodzikuza. Koma anthu ambirimbiri omwenso si angwiro amakhala odzikuza. Kuti tikhale otsatira a Khristu, tiyenera kuyesetsa kupewa kudzikuza. (Yakobo 4:6) Kumbukirani kuti Yehova amadana ndi kudzikuza. Choncho n’zofunika kuti tiphunzire komanso kutsanzira kudzichepetsa kwa Yesu.

Yesu Ndi Wodzichepetsa Kuyambira Kalekale

6. Kodi kudzichepetsa n’kutani, nanga Yehova anadziwa bwanji kuti Mesiya adzakhala wodzichepetsa?

6 Kudzichepetsa kumatanthauza kusadzikuza, kusanyada komanso kudziona kuti ndiwe wotsika. Khalidwe limeneli limayambira mumtima ndipo munthu amadziwika kuti ndi wodzichepetsa chifukwa cha zolankhula zake, zochita zake ndiponso mmene amachitira zinthu ndi anthu ena. Kodi Yehova anadziwa bwanji kuti Mesiya adzakhala wodzichepetsa? Yehova ankadziwa kuti Mwana wake anatengera chitsanzo chake changwiro cha kudzichepetsa. (Yohane 10:15) Komanso ankaona mmene Mwana wakeyo ankachitira zinthu modzichepetsa. Kodi anachita zinthu ziti?

7-9. (a) Kodi Mikayeli anasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa atasemphana maganizo ndi Satana? (b) Kodi Akhristu angatsanzire bwanji Mikayeli posonyeza kudzichepetsa?

7 M’buku la Yuda muli chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti Yesu ndi wodzichepetsa. M’bukuli muli mawu akuti: “Koma pamene Mikayeli, mkulu wa angelo, anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose, sanayese n’komwe kumuweruza komanso kumunyoza, m’malomwake anati: ‘Yehova akudzudzule.’” (Yuda 9) Mikayeli ndi dzina limene Yesu ankadziwika nalo asanabwere padziko lapansi komanso limene amadziwika nalo atabwerera kumwamba. Iye anapatsidwa dzinali chifukwa cha udindo wake monga mkulu wa angelo, kapena kuti mkulu wa gulu lankhondo la angelo a Yehova kumwamba. b (1 Atesalonika 4:16) Ndiyeno tiyeni tione zimene Mikayeli anachita, atasemphana maganizo ndi Satana.

8 Nkhani imene ili m’buku la Yuda sifotokoza zimene Satana ankafuna kuchita ndi mtembo wa Mose, koma sitikukayikira kuti Mdyerekezi anali ndi zolinga zoipa mumtima mwake. Mwina ankafuna kulimbikitsa anthu kuti azilambira mafano pogwiritsira ntchito mtembo wa munthu wokhulupirikayo. Pamene Mikayeli ankaletsa Satana kuti asachite zolinga zake zoipazo, anasonyeza khalidwe labwino kwambiri lodziletsa. N’zoona kuti Satana ankafunika kudzudzulidwa, koma Mikayeli, amene pa nthawiyi ankakangana ndi Satana, anali asanapatsidwe “udindo wonse woweruza” umene ali nawo panopa. Choncho iye anazindikira kuti Yehova Mulungu yekha ndi amene anayenera kudzudzula Mdyerekeziyo. (Yohane 5:22) Pa angelo onse, Mikayeli ndi amene ali ndi udindo waukulu chifukwa ndi mkulu wa angelo. Komabe, m’malo mofuna kukhala ndi udindo winanso, iye modzichepetsa anasiyira Yehova udindo wodzudzula Mdyerekezi. Kuwonjezera pa khalidwe lodzichepetsa, Yesu anasonyezanso kuti ankadziwa kuti pali zinthu zina zimene ayenera kuchita ndiponso zimene sayenera kuchita.

9 Pali chifukwa chimene chinachititsa kuti Yuda alembe nkhani imeneyi mouziridwa ndi Mulungu. N’zomvetsa chisoni kuti Akhristu ena munthawi ya Yuda sanali odzichepetsa. Iwo anali odzikweza ndipo ‘ankalankhula monyoza zinthu zonse zimene sankazimvetsa n’komwe.’ (Yuda 10) Zimakhala zosavuta kuti anthu omwe si angwirofe tiyambe kunyada. Ngati sitikumvetsa bwino zinthu zinazake zimene zikuchitika mumpingo wa Chikhristu, mwina ingakhale mfundo inayake imene akulu asankha kuti mpingo utsatire, kodi timachita chiyani? Ngati titayamba kudandaula n’kumalankhula zinthu zosonyeza kuti sitikugwirizana ndi zimene asankhazo, ngakhale kuti sitikudziwa zinthu zonse zimene zachititsa kuti asankhe zimenezo, kodi pamenepa sitingakhale kuti tikusonyeza kuti ndife odzikuza? Choncho, tiyeni tizitsanzira Mikayeli kapena kuti Yesu, popewa kuweruza pa zinthu zimene Mulungu sanatipatse udindo wochita zimenezo.

10, 11. (a) Kodi Mwana wa Mulungu anasonyeza bwanji khalidwe lodzichepetsa pamene anavomera kubwera padziko lapansi? (b) Kodi tingatsanzire bwanji khalidwe la Yesu la kudzichepetsa?

10 Mwana wa Mulungu anasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa chifukwa anavomera kubwera pano padziko lapansi. Taganizirani zinthu zimene anafunika kusiya. Iye anali mkulu wa angelo. Analinso “Mawu,” kapena kuti wolankhula m’malo mwa Yehova. (Yohane 1:1-3) Yesu ankakhala kumwamba, komwe ndi malo okhala a Yehova “apamwamba, oyera ndi aulemerero.” (Yesaya 63:15) Komabe, Mwanayo “anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo ndipo anakhala munthu.” (Afilipi 2:7) Taganizirani zimene zinachitika kuti abwere padziko lapansi. Moyo wake anausamutsira m’mimba mwa namwali wa Chiyuda ndipo anafunika akhale m’mimba mwa namwaliyo n’kumakula pang’onopang’ono kwa miyezi 9. Kenako anabadwa ngati khanda losadziwa kanthu m’nyumba ya kalipentala yemwenso anali wosauka. Anakula n’kukhala kamnyamata kenako n’kukhala mnyamata wamkulu. Ngakhale kuti anali wangwiro, pa nthawi yonse imene anali mnyamata, ankamvera makolo ake amene sanali angwiro. (Luka 2:40, 51, 52) Pamenepatu iye anasonyeza kudzichepetsa kwambiri.

11 Tiyeni tiziyesetsa kutsanzira kudzichepetsa kwa Yesu pochita utumiki umene nthawi zina ungaoneke ngati wonyozeka. Mwachitsanzo, ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ingaoneke ngati yonyozeka makamaka ngati anthu sakusonyeza chidwi, akutinyoza kapena kutilankhula mwachipongwe. (Mateyu 28:19, 20) Komabe, ngati titapirira n’kupitirizabe kugwira ntchitoyi, tingathandize kuti anthu ambiri adzapulumuke. Ndipotu tidzaphunzira kukhala odzichepetsa kwambiri komanso tidzatsatira bwino Mbuye wathu, Yesu Khristu.

Kodi Yesu Anasonyeza Bwanji Kudzichepetsa Ali Padzikoli?

12-14. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa pamene anthu ankamutamanda? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa pamene ankachita zinthu ndi anthu? (c) N’chiyani chikusonyeza kuti kudzichepetsa kwa Yesu sikunali kongodzionetsera kapena kongotsatira miyambo?

12 Yesu anali wodzichepetsa pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padziko lapansi. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa poonetsetsa kuti ulemu ndi ulemerero wonse ukupita kwa Atate ake. Nthawi zina anthu ankatamanda Yesu chifukwa cholankhula mawu anzeru, kuchita zozizwitsa komanso chifukwa cha khalidwe lake labwino. Nthawi zonse Yesu ankakana kulandira ulemu umenewo ndipo ankanena kuti Yehova ndi amene ali woyenera kupatsidwa ulemuwo osati iyeyo.​—Maliko 10:17, 18; Yohane 7:15, 16.

13 Njira ina imene Yesu anasonyezera kuti anali wodzichepetsa ndi mmene ankachitira zinthu ndi anthu. Ndipo iye ananena momveka bwino kuti sanabwere padziko lapansili kudzatumikiridwa koma kudzatumikira ena. (Mateyu 20:28) Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa chifukwa anali wokoma mtima komanso wodekha akamachita zinthu ndi anthu. Mwachitsanzo, otsatira ake akamukhumudwitsa sankawadzudzula mwaukali, koma ankayesetsa kuwalangiza modekha. (Mateyu 26:39-41) Gulu la anthu litamutsatira pamene ankafunafuna malo opanda anthu komanso phokoso kuti apumule, sanawathamangitse koma anapitiriza kuwaphunzitsa “zinthu zambiri” modzipereka. (Maliko 6:30-34) Pamene mayi wina amene sanali Mwisiraeli ankamuchonderera kuti amuchiritsire mwana wake wamkazi, poyamba Yesu anakana. Komabe iye sanakane mwaukali komanso popeza mayiyo anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chachikulu, Yesu anamuchitira zimene anapemphazo. Tikambirana nkhani imeneyi m’Mutu 14.​—Mateyu 15:22-28.

14 Yesu anakwaniritsa mawu amene analankhula onena za iye m’njira zina zambiri. Iye anati: “Ndine wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mateyu 11:29) Sikuti iye ankasonyeza kudzichepetsa pongofuna kudzionetsera kapena kungotsatira miyambo yachikhalidwe. Koma kudzichepetsa kwake kunali kochokera pansi pa mtima. N’chifukwa chake Yesu ankaona kuti ntchito yophunzitsa otsatira ake kuti akhale odzichepetsa inali yofunika kwambiri.

Yesu Ankaphunzitsa Otsatira Ake Kuti Akhale Odzichepetsa

15, 16. Kodi Yesu ananena kuti pali kusiyana kotani pakati pa khalidwe la olamulira a dzikoli ndi khalidwe limene otsatira ake amafunika kukhala nalo?

15 Atumwi a Yesu zinawatengera nthawi kuti aphunzire kukhala odzichepetsa. Choncho Yesu anayesetsa kuwaphunzitsa mobwerezabwereza kuti akhale odzichepetsa. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yakobo ndi Yohane anatuma mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. Modzichepetsa, Yesu anayankha kuti: “Si ine woyenera kusankha amene adzakhale kudzanja langa lamanja kapena lamanzere. Atate wanga adzapereka mwayi umenewo kwa amene anawakonzera.” Atumwi ena 10 aja “anakwiya kwambiri” ndi zimene Yakobo ndi Yohane anachitazi. (Mateyu 20:20-24) Kodi Yesu anathetsa bwanji vuto limeneli?

16 Yesu anawadzudzula onse mwachifundo kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu. Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:25-27) N’zodziwikiratu kuti atumwiwo ankaona kuti “olamulira a anthu a mitundu ina” amakhala onyada, odzikuza ndiponso odzikonda. Koma Yesu anasonyeza kuti otsatira ake ayenera kukhala osiyana ndi atsogoleri ankhanza ndiponso okonda kulamulira ena amenewo. Otsatira akewo ankafunika kukhala odzichepetsa. Kodi atumwiwo anamvetsa mfundoyi?

17-19. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji atumwi ake phunziro losaiwalika la kudzichepetsa atatsala pang’ono kuphedwa? (b) Kodi ndi phunziro lalikulu komanso losaiwalika liti la kudzichepetsa limene Yesu anapereka pamene anali padziko lapansi?

17 Ophunzirawo ankavutika kwambiri kuti asonyeze khalidwe lodzichepetsa. Aka sikanali koyamba kapena komaliza kuti Yesu awaphunzitse kufunika koti akhale anthu odzichepetsa. M’mbuyomu, ophunzirawo atakangana pa nkhani yakuti wamkulu kwambiri ndi ndani pakati pawo, Yesu anabweretsa mwana wamng’ono pakati pawo n’kuwauza kuti azikhala ngati ana amene sanyada, sadzikuza komanso safuna udindo ngati mmene anthu akuluakulu amachitira. (Mateyu 18:1-4) Komabe, usiku womaliza Yesu asanaphedwe, anaona kuti atumwi akewo anali asanasiyebe kunyada. Choncho iye anawapatsa phunziro losaiwalika. Anamanga thaulo m’chiuno mwake n’kuyamba kugwira ntchito yonyozeka kwambiri imene pa nthawi imeneyo inkagwiridwa ndi antchito a pakhomo kukabwera alendo. Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake onse, kuphatikizapo Yudasi amene anali atatsala pang’ono kumupereka.​—Yohane 13:1-11.

18 Yesu anathandiza atumwiwo kumvetsa nkhani ya kudzichepetsa pamene anawauza kuti: “Ndakupatsani chitsanzo.” (Yohane 13:15) Kodi ophunzirawo anamvetsa bwino tanthauzo la zimene Yesu anachitazo? Taganizirani izi. Usiku wa tsiku lomwelo atumwiwo anakangananso pa nkhani yakuti wamkulu kwambiri ndi ndani pakati pawo. (Luka 22:24-27) Koma Yesu anapitiriza kuwalezera mtima ndipo ankawaphunzitsa modzichepetsa. Kenako anawaphunzitsa kudzichepetsa m’njira ina yapadera kwambiri. Iye “anadzichepetsa ndipo anakhala womvera mpaka imfa, inde imfa yapamtengo wozunzikirapo.” (Afilipi 2:8) Ngakhale kuti Yesu sananyozepo Mulungu, iye analolera kuphedwa mochititsa manyazi ngati chigawenga. Pamenepatu Mwana wa Mulungu anasonyeza kuti ndi wapadera, chifukwa anadzichepetsa kwambiri kuposa chilichonse chimene Yehova analenga.

19 N’kutheka kuti phunziro lomalizira la kudzichepetsali, limene Yesu anawapatsa ali padziko lapansi, ndi limene linathandiza atumwi okhulupirikawo kuti azikumbukirabe phunziro losaiwalika limene Yesu anapereka. Baibulo limatiuza kuti amuna amenewa anagwira ntchito limodzi modzichepetsa kwa zaka zambirimbiri. Nanga bwanji ifeyo?

Kodi Inuyo Mutsanzira Chitsanzo Chimene Yesu Anatipatsachi?

20. Kodi tingadziwe bwanji ngati ndife odzichepetsa?

20 Paulo akulimbikitsa aliyense wa ife kuti: “Khalani ndi maganizo amenenso Khristu Yesu anali nawo.” (Afilipi 2:5) Tiyenera kukhala odzichepetsa ngati mmene Yesu analili. Kodi tingadziwe bwanji ngati tili odzichepetsa? Paulo akutikumbutsa kuti, “Musamachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena chifukwa chodzikuza, koma modzichepetsa, muziona kuti ena amakuposani.” (Afilipi 2:3) Choncho tingadziwe kuti ndife odzichepetsa kapena ayi tikaganizira mmene timaonera anthu ena poyerekezera ndi mmene timadzionera tokha. Tiyenera kumaona kuti anthu ena amatiposa komanso kuti ndi ofunika kwambiri kuposa ifeyo. Kodi inuyo mumvera malangizo a Paulowa?

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani oyang’anira a Chikhristu ayenera kukhala odzichepetsa? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzichepetsa?

21 Patapita zaka zambiri Yesu atamwalira, mtumwi Petulo ankaganizabe za kufunika kokhala munthu wodzichepetsa. Petulo anaphunzitsa oyang’anira a Chikhristu kuti azigwira ntchito yawo modzichepetsa, osati kumachita zinthu ngati mafumu pakati pa nkhosa za Yehova. (1 Petulo 5:2, 3) Udindo si chifukwa choti munthu akhalire wonyada. M’malomwake, munthu amene ali ndi udindo ayenera kuyesetsa kuti akhale wodzichepetsa kwambiri. (Luka 12:48) Sikuti khalidweli ndi lofunika kwa oyang’anira okha koma kwa Mkhristu aliyense.

22 N’zoonekeratu kuti Petulo sanaiwale usiku umene Yesu anasambitsa mapazi ake, ngakhale kuti iyeyo ankakana. (Yohane 13:6-10) Petulo analembera Akhristu kuti: “Nonsenu muzichita zinthu modzichepetsa.” (1 Petulo 5:5) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “muzichita zinthu” amatanthauzanso “kuvala,” ndipo amanena zimene wantchito ankachita. Iye ankavala epuloni kuti agwire ntchito yonyozeka. Mawu amenewa akutikumbutsa zimene Yesu anachita pomanga thaulo m’chiuno mwake n’kugwada kuti agwire ntchito yosambitsa mapazi a ophunzira ake. Ngati ndife odzichepetsa mofanana ndi Yesu, sitidzakana ntchito iliyonse imene Mulungu angatipatse ngakhale itaoneka ngati yonyozeka. Choncho tikhale odzichepetsa ndipo anthu onse aziona kudzichepetsa kwathu ngati mmene amaonera zovala zimene tavala.

23, 24. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuchita chilichonse chosonyeza kudzikuza? (b) Kodi mutu wotsatira utithandiza kupewa maganizo abodza ati okhudza kudzichepetsa?

23 Kudzikuza kuli ngati poizoni ndipo kumawononga zinthu kwambiri. Munthu amene ali ndi luso lochita bwino zinthu zosiyanasiyana angakhale wachabechabe pamaso pa Mulungu ngati wayamba kudzikuza. Koma munthu wodzichepetsa, ngakhale atakhala wooneka ngati wonyozeka, amakhala wamtengo wapatali kwa Yehova. Tikamasonyeza khalidwe lofunika kwambiri limeneli tsiku ndi tsiku, poyesetsa kutsatira Khristu modzichepetsa, tidzalandira mphoto yamtengo wapatali kwambiri. Petulo analemba kuti: “Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.” (1 Petulo 5:6) Yehova anakwezadi Yesu chifukwa anali wodzichepetsa kwambiri. Inunso Mulungu wathu adzasangalala kukupatsani mphoto chifukwa cha kudzichepetsa kwanu.

24 Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amaganiza kuti munthu akakhala wodzichepetsa ndiye kuti ndi wopusa. Chitsanzo cha Yesu chatithandiza kuona kuti maganizo amenewo ndi abodza, chifukwa iye anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa aliyense komanso anali wolimba mtima kwambiri kuposa wina aliyense. M’mutu wotsatira tidzakambirana nkhani imeneyi.

a Pofotokoza za nyama zimenezi, buku lina limanena kuti, nyama zimenezi “zimayenda pang’onopang’ono, n’zosamvera, n’zosaoneka bwino ndipo kawirikawiri amene amakhala nazo ndiponso kuzigwiritsa ntchito ndi anthu osauka.”

b Kuti mupeze umboni wina wosonyeza kuti Yesu ndi Mikayeli, onani nkhani yakuti “Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?” yomwe ikupezeka pambali yakuti, “Kuyankha Mafunso a M’baibulo” pa webusaiti ya Mboni za Yehova ya jw.org.