Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 7

“Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”

“Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”

1-3. (a) N’chiyani chimene chikusonyeza kuti Yesu anavutika kwambiri maganizo m’munda wa Getsemane, nanga n’chiyani chimene chinachititsa? (b) Kodi tinganene chiyani za chitsanzo cha Yesu cha kupirira, nanga zimenezi zikubweretsa mafunso otani?

 PANALI patangotsala nthawi yochepa chabe kuti Yesu aphedwe, ndipo iye anali asanavutikepo maganizo komanso kuda nkhawa ngati mmene anachitira pa nthawiyi. Iye limodzi ndi atumwi ake anafika m’munda wa Getsemane, malo amene ankakonda kupitako. Nthawi zambiri Yesu ankakumana ndi ophunzira ake malo amenewa. Komabe usikuwu, iye ankafuna kukhala payekha ndipo anasiya atumwi akewo n’kupita chapatali kenako anagwada pansi n’kuyamba kupemphera. Anapemphera mochokera pansi pa mtima ndipo anazunzika koopsa mumtima mwake moti thukuta lake linkaoneka “ngati madontho a magazi amene akugwera pansi.”​—Luka 22:39-44.

2 N’chifukwa chiyani Yesu anavutika maganizo chonchi? N’zoona kuti ankadziwa kuti posachedwa azunzidwa koopsa, koma chimenechi si chifukwa chimene chinachititsa kuti avutike maganizo. Panali nkhani ina yofunika kwambiri imene ankavutika nayo. Iye ankada nkhawa kwambiri ndi nkhani yokhudza kuyeretsedwa kwa dzina la Atate ake ndipo ankadziwa kuti akakhalabe wokhulupirika, anthu adzakhala ndi tsogolo labwino. Yesu ankadziwa kuti zimenezi zingatheke ngati atakhalabe wopirira. Ankadziwanso kuti dzina la Yehova likananyozedwa kwambiri akanalephera kupirira. Choncho tsiku lomwelo atatsala pang’ono kufa, Yesu amene anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kupirira, ananena mofuula kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”​—Yohane 19:30.

3 Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Ganizirani mozama za munthu amene anapirira.” (Aheberi 12:3) Choncho pali mafunso ofunika amene tiyenera kudziwa mayankho ake monga akuti: Kodi ena mwa mayesero amene Yesu anapirira ndi ati? Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Nanga tingamutsanzire bwanji? Koma tisanayankhe mafunsowa, tiyeni tione tanthauzo la kupirira.

Kodi Kupirira N’kutani?

4, 5. (a) Kodi “kupirira” n’kutani? (b) Kodi tingapereke chitsanzo chotani chosonyeza kuti kupirira sikumangotanthauza kukumana ndi mavuto amene munthu sangawapewe?

4 Nthawi zambiri, tonsefe timavutika chifukwa cha ‘mayesero osiyanasiyana amene tikukumana nawo.’ (1 Petulo 1:6) Kodi munthu akamakumana ndi mayesero ndiye kuti akupirira? Ayi. Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kupirira” amatanthauza “kukhalabe wolimba kapena kusagonja ukakumana ndi mavuto.” Ponena za kupirira kumene kwatchulidwa m’Baibulo, katswiri wina wa Baibulo anati: “Kupirira n’kukhala ndi mtima wosagonja ukakumana ndi mavuto, osati kungolimbana nawo mosanyinyirika, koma kulimbana nawo chifukwa cha chikhulupiriro cholimba . . . Khalidweli limathandiza munthu kuti akhalebe wolimba pamene akukumana ndi mavuto. Munthu wopirira saganizira kwambiri za mavuto amene akukumana nawo koma amaganizira za madalitso amene angapeze akapirira mavutowo.”

5 Choncho, kupirira sikutanthauza kungokumana ndi mavuto amene munthu sangawapewe. Mogwirizana ndi Baibulo, munthu wopirira amakhalanso wokhulupirika, amaona moyenerera mayesero amene akukumana nawo ndiponso amakhala ndi chiyembekezo. Taganizirani chitsanzo ichi: Anthu awiri atsekeredwa m’ndende pa zifukwa zosiyana koma awapatsa chilango chofanana. Wina ndi chigawenga ndipo akugwira ukaidi wake monyinyirika, koma winayo ndi Mkhristu woona amene wamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Mkhristuyo akugwira ukaidi wake mokhulupirika ndiponso mosanyinyirika chifukwa akudziwa kuti umenewo ndi mwayi woti asonyeze chikhulupiriro chake. Sitinganene kuti chigawengacho ndi chitsanzo chabwino cha kupirira, koma tinganene kuti Mkhristu wokhulupirikayo ndi amene wasonyeza chitsanzo chabwino cha kupirira, ndipo limeneli ndi khalidwe labwino kwambiri.​—Yakobo 1:2-4.

6. Kodi tingaphunzire bwanji kukhala anthu opirira?

6 Kupirira n’kofunika kwambiri kuti tidzapulumuke. (Mateyu 24:13) Komabe anthufe sitibadwa ndi khalidwe lofunika kwambiri limeneli, koma timafunika kuliphunzira. Kodi tingaliphunzire bwanji? Lemba la Aroma 5:3 limati: “Mavuto athu amachititsa kuti tipirire.” N’zoonadi, ngati tikufuna kukhala opirira, sitingachite mantha n’kumazemba mayesero onse amene tingakumane nawo chifukwa cha chikhulupiriro chathu. M’malomwake tidzalolera kukumana ndi mayeserowo. Timakhala opirira ngati tikuthana ndi mayesero akuluakulu komanso ang’onoang’ono amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Mayesero aliwonse amene tawapirira amatilimbitsa kuti tipirirenso mayesero ena otsatira. Komabe n’zodziwikiratu kuti patokha sitingathe kukhala opirira. Timakhala opirira “modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.” (1 Petulo 4:11) Pofuna kutithandiza kuti tikhalebe opirira, Yehova anatipatsa Mwana wake, yemwe anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kupirira. Tiyeni tione bwinobwino chitsanzo chimene Yesu anatipatsachi.

Mayesero Amene Yesu Anapirira

7, 8. Kodi Yesu anapirira zinthu zotani atatsala pang’ono kufa?

7 Yesu atatsala pang’ono kufa, anapirira nkhanza zambiri zosiyanasiyana. Usiku wake womaliza iye anavutika kwambiri maganizo komanso kuda nkhawa. Kuwonjezera pa zimenezi, taganiziraninso ululu umene anamva chifukwa cha kukhumudwitsidwa ndi zinthu zosiyanasiyana ndiponso kuchititsidwa manyazi. Mwachitsanzo, iye anaperekedwa ndi mnzake weniweni, anzake apamtima anamuthawa ndiponso anaimbidwa mlandu womunamizira. Pomuimba mlanduwu akuluakulu a bwalo lachipembedzo m’dzikolo anamunyoza, kumulavulira ndiponso kum’menya. Koma iye anapirira zonsezo modekha komanso molimba mtima.​—Mateyu 26:46-49, 56, 59-68.

8 Pa nthawi imene ankaphedwa, Yesu anapiriranso zinthu zina zopweteka kwambiri. Iye anakwapulidwa kwambiri moti buku lina limati, “zikwapuzo zinachititsa kuti akhale ndi mabala akuluakulu pathupi lake amene ankatuluka magazi ambiri ndithu.” Anamukhomera pamtengo m’njira yoti “amve ululu kwambiri ndiponso afe mwapang’onopang’ono.” Taganizirani ululu umene anamva pamene ankamukhomerera pamtengo ndi misomali ikuluikulu m’manja ndiponso m’mapazi. (Yohane 19:1, 16-18) Taganiziraninso ululu wosaneneka umene anamva pamene ankadzutsa mtengowo thupi lake n’kumalendewera ndipo mtengowo n’kumakhula msana wake womwe unali mabala okhaokha. Yesu anapirira zonsezi ngakhale kuti ankavutika maganizo kwambiri monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa mutuwu.

9. Kodi kunyamula ‘mtengo wathu wozunzikirapo’ n’kumatsatira Yesu kumatanthauza chiyani?

9 Monga otsatira a Khristu, kodi tingafunike kupirira chiyani? Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, . . . anyamule mtengo wake wozunzikirapo n’kupitiriza kunditsatira.” (Mateyu 16:24) Palembali, mawu akuti ‘mtengo wozunzikirapo’ awagwiritsira ntchito mophiphiritsa ndipo akutanthauza kuvutika, kuchititsidwa manyazi ngakhale kuphedwa kumene. Choncho, kutsatira Khristu si kophweka. Timakhala osiyana ndi anthu ena chifukwa timatsatira mfundo za Chikhristu ndipo dzikoli limadana nafe chifukwa sitili kumbali yake. (Yohane 15:18-20; 1 Petulo 4:4) Komabe ndife ofunitsitsa kunyamula mtengo wathu wozunzikirapo, kapena kuti ndife okonzeka kuvutika, ngakhale kufa kumene, m’malo mosiya kutsatira Yesu, amene anatisiyira chitsanzo.​—2 Timoteyo 3:12.

10-12. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anakumana ndi mayesero ena chifukwa cha anthu omwe si angwiro amene ankakhala nawo? (b) Nanga ndi mayesero enanso ati amene Yesu anapirira?

10 Pa utumiki wake, Yesu anakumana ndi mayesero ena obwera chifukwa cha anthu omwe si angwiro amene ankakhala nawo. Kumbukirani kuti iye anali “mmisiri waluso” amene Yehova anamugwiritsira ntchito polenga dziko lapansi komanso zinthu zonse zamoyo zimene zili m’dzikoli. (Miyambo 8:22-31) Choncho, Yesu ankadziwa cholinga cha Yehova polenga anthu. Mulungu ankafuna kuti anthuwo akhale ndi makhalidwe ofanana ndi ake komanso azisangalala ndi moyo wangwiro. (Genesis 1:26-28) Koma Yesu atabwera padziko lapansi, anali munthu amene ankatha kumva ndiponso kuona zinthu mofanana ndi munthu wina aliyense ndipo anaona yekha mavuto amene anabwera chifukwa cha uchimo. Yesu ayenera kuti zinamupweteka kwambiri mumtima chifukwa anaona kuti kupanda ungwiro kwa anthu kwafika poipa kwambiri poyerekezera ndi mmene Adamu ndi Hava analili asanachimwe. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu azikumana ndi mayesero ambiri ofunika kuwapirira. Kodi iye anakhumudwa n’kuyamba kuona anthu ochimwawo kuti sangasinthe? Tiyeni tione.

11 Mwachitsanzo, Ayuda anali osamvera ndipo Yesu anamva chisoni mpaka analira. Kodi kuuma khosi kwa anthu amenewo kunamufooketsa kapena kumuchititsa kuti asiye kulalikira? Ayi, chifukwa “tsiku ndi tsiku iye anapitiriza kuphunzitsa” m’kachisi. (Luka 19:41-44, 47) Iye “anamva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima” kwa Afarisi amene ankamuyang’anitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthu winawake pa Sabata. Kodi Yesu anachita mantha ndi anthu odzilungamitsawo, omwe ankamutsutsa? Ayi ndithu. Iye analimba mtima n’kuchiritsa munthuyo m’sunagoge momwemo.​—Maliko 3:1-5.

12 Mayesero enanso amene Yesu ankakumana nawo anali ochokera pa zinthu zimene ophunzira ake, amene ankawakonda kwambiri, ankalakwitsa. Monga mmene tinaonera m’Mutu 3, iwo ankakangana mobwerezabwereza pa nkhani yakuti wamkulu ndi ndani. (Mateyu 20:20-24; Luka 9:46) Ndipo Yesu anawadzudzula kangapo konse kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa. (Mateyu 18:1-6; 20:25-28) Koma zinawatengera nthawi kuti amvetse malangizowo. Ndipotu, pamene anali nawo limodzi usiku wake womaliza, “anayamba kukangana kwambiri” pa nkhani yoti wamkulu kwambiri ndi ndani. (Luka 22:24) Kodi Yesu anawanyanyala poganiza kuti ndi anthu amene sangasinthe? Ayi ndithu. Iye anali woleza mtima ndipo anatsimikiza komanso kukhulupirira kuti ophunzirawo adzasintha, choncho anapitiriza kuona makhalidwe awo abwino. Iye ankadziwa kuti ophunzira akewo ankakonda Yehova kuchokera pansi pa mtima ndipo ankafunitsitsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu.​—Luka 22:25-27.

Anthu akamatitsutsa, sitiyenera kufooka, koma tiyenera kupitiriza kulalikira mwakhama

13. Kodi tingakumane ndi mayesero ati ofanana ndi amene Yesu anakumana nawo?

13 Ifenso tingakumane ndi mayesero ofanana ndi amene Yesu anawapirira. Mwachitsanzo, tingakumane ndi anthu opanda chidwi kapena amene amatsutsa uthenga wa Ufumu umene timalalikira. Kodi tidzalola kuti zimenezo zitifooketse, kapena tidzapitiriza kulalikira modzipereka? (Tito 2:14) Mwinanso tingakumane ndi mayesero ena chifukwa cha zimene Akhristu anzathu amalakwitsa. Mwachitsanzo iwo angalankhule kapena kuchita zinthu mosaganiza bwino ndipo zimenezo zingatikhumudwitse. (Miyambo 12:18) Kodi tidzalola kuti tiyambe kudana ndi okhulupirira anzathu chifukwa cha zolakwa zawo, kapena tidzapitiriza kupirira zolakwazo n’kumaona zabwino mwa iwo?​—Akolose 3:13.

N’chiyani Chimene Chinathandiza Yesu kuti Apirire?

14. Kodi ndi zinthu ziwiri ziti zimene zinathandiza Yesu kukhalabe wokhulupirika?

14 N’chiyani chinathandiza Yesu kuti akhalebe wolimba ndiponso kuti azitumikirabe Mulungu mokhulupirika ngakhale kuti ankanyozedwa, ankakhumudwitsidwa ndiponso ankazunzidwa? Pali zinthu ziwiri zikuluzikulu zimene zinamuthandiza. Choyamba, iye ankadalira Yehova ndipo ankapemphera kuti “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira,” amuthandize. (Aroma 15:5) Chachiwiri, Yesu ankayang’ana kutsogolo ndipo ankaganizira madalitso amene adzabwere akakhalabe wokhulupirika. Tsopano tiyeni tione zifukwa zimenezi, chilichonse pachokha.

15, 16. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu sankadalira mphamvu zake kuti apirire mayesero? (b) Pa nkhani ya pemphero, kodi Yesu ankakhulupirira kuti Atate ake achita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

15 Ngakhale kuti Yesu ndi wangwiro ndiponso ndi Mwana wa Mulungu, sankadalira mphamvu zake kuti apirire mayesero. M’malomwake ankadalira Atate ake akumwamba ndipo ankapemphera kuti amuthandize. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Khristu anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi.’ (Aheberi 5:7) Onani kuti lembali silikunena kuti Yesu “anapereka” mapemphero ochonderera okha, koma anaperekanso mapemphero opempha. Mawu akuti “mapemphero ochonderera” akutanthauza makamaka kupempha thandizo mwakhama ndiponso mochokera pansi pa mtima. Ndipotu mawuwa akusonyeza kuti Yesu ankapemphera mobwerezabwereza, osati kamodzi kokha. N’zoonadi, m’munda wa Getsemane, Yesu anapemphera mobwerezabwereza ndiponso kuchokera pansi pa mtima.​—Mateyu 26:36-44.

16 Yesu ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova ayankha mapemphero ake ochonderera, chifukwa ankadziwa kuti Atate ake ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Asanabwere padziko lapansi, Mwana woyamba kubadwayu ankaona Atate ake akuyankha mapemphero a atumiki ake okhulupirika. Mwachitsanzo, Mwanayu anaona pamene Yehova anatumiza mngelo kuchokera kumwamba kuti akayankhe pemphero la mneneri Danieli, mneneriyo asanamalize n’komwe kupemphera. (Danieli 9:20, 21) Ndiyeno kodi Atatewo akanalephera bwanji kuyankha pemphero lochokera pansi pa mtima la Mwana wake wobadwa yekha limene anapemphera “mofuula komanso akugwetsa misozi”? Yehova anayankhadi mapemphero a Mwana wakeyo ndipo anatumiza mngelo kukamulimbikitsa kuti athe kupirira mayeserowo.​—Luka 22:43.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Mulungu kuti tipirire mayesero, nanga tingachite bwanji zimenezi?

17 Kuti tipirire, tiyenera kudalira Mulungu, amene ‘amatipatsa mphamvu.’ (Afilipi 4:13) Ngati Mwana wa Mulungu, yemwe anali wangwiro, anaona kufunika kopempha thandizo kwa Yehova, kuli bwanji ifeyo? Mofanana ndi Yesu, tiyenera kupemphera kwa Yehova mobwerezabwereza. (Mateyu 7:7) N’zoona kuti Mulungu sangatitumizire mngelo, koma timakhulupirira kuti Mulungu wathu wachikondi adzayankha mapemphero a Akhristu okhulupirika amene “amapitiriza kupemphera ndi kupembedzera masana ndi usiku.” (1 Timoteyo 5:5) Ngakhale kuti tingakumane ndi mayesero osiyanasiyana, monga matenda, imfa ya wachibale wathu kapena kuzunzidwa ndi anthu amene amatitsutsa, Yehova adzayankha mapemphero athu ochokera pansi pa mtima opempha nzeru, kulimba mtima ndiponso mphamvu zoti tithe kupirira.​—2 Akorinto 4:7-11; Yakobo 1:5.

Yehova adzayankha mapemphero athu ochokera pansi pa mtima opempha kuti atithandize kupirira

18. Kodi ndi chinthu chinanso chiti chimene chinathandiza Yesu kuti athe kupirira?

18 Chinthu chachiwiri chimene chinathandiza Yesu kupirira n’chakuti iye ankaganizira madalitso amene angabwere ngati angakhalebe wokhulupirika. Baibulo limanena za Yesu kuti: “Chifukwa chodziwa kuti adzasangalala m’tsogolo, anapirira mtengo wozunzikirapo.” (Aheberi 12:2) Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti timafunika kukhala ndi chikhulupiriro komanso chimwemwe kuti tikwanitse kupirira. Kuti tione kugwirizana kwake tinganene kuti: Chikhulupiriro chimachititsa kuti munthu akhale wachimwemwe ndipo chimwemwe chimathandiza munthu kupirira. (Aroma 15:13; Akolose 1:11) Yesu ankadziwa kuti akapirira padzachitika zinthu zambiri zabwino. Iye ankadziwa kuti akakhalabe wokhulupirika, zidzathandiza kuyeretsa dzina la Atate ake komanso zidzathandiza kuti akwanitse kuwombola mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa. Yesu ankadziwanso kuti adzalamulira monga Mfumu komanso adzatumikira monga Mkulu wa Ansembe ndipo adzabweretsa madalitso ambiri kwa anthu okhulupirika. (Mateyu 20:28; Aheberi 7:23-26) Popeza Yesu anali ndi chiyembekezo ndiponso ankaganizira kwambiri madalitso amene anali m’tsogolo, iye anali ndi chimwemwe chosaneneka ndipo chimwemwecho chinamuthandiza kuti apirire mayesero.

19. Tikamakumana ndi mayesero kodi chiyembekezo ndiponso chimwemwe zingatithandize bwanji kupirira?

19 Mofanana ndi Yesu tikufunika kukhala ndi chiyembekezo komanso chimwemwe kuti tikhale opirira. Mtumwi Paulo anati: “Kondwerani chifukwa cha chiyembekezo. Muzipirira mavuto.” (Aroma 12:12) Kodi panopa chikhulupiriro chanu chikuyesedwa kwambiri? Ngati zili choncho ganizirani kwambiri za zinthu zabwino zimene zidzachitike ngati mutapirira. Musaiwale kuti mukapirira, dzina la Yehova lidzalemekezedwa kwambiri. Pitirizani kuyembekezera mwachidwi Ufumu wa Mulungu. Yerekezerani kuti muli m’dziko latsopano la Mulungu limene likubwerali, ndipo mukusangalala ndi madalitso amene ali m’Paradaiso. Tikamaganizira za kukwaniritsidwa kwa madalitso osangalatsa amene Yehova walonjeza, monga kuyeretsedwa kwa dzina lake, kuthetsedwa kwa matenda, imfa komanso zoipa zonse padziko lapansi, zingatithandize kukhala ndi chimwemwe, ndipo chimwemwecho chingatithandize kupirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo. Tikayerekezera madalitso amene tidzakhale nawo mu Ufumu wa Mulungu ndi mavuto aliwonse m’dzikoli, timaona kuti mavutowo ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.”​—2 Akorinto 4:17.

“Mutsatire Mapazi Ake Mosamala Kwambiri”

20, 21. Pa nkhani ya kupirira, kodi Yehova amayembekezera kuti tizitani, nanga tiyenera kutsimikiza kuchita chiyani?

20 Yesu ankadziwa kuti si zophweka kuti munthu akhale wotsatira wake chifukwa munthuyo amafunika kupirira. (Yohane 15:20) Pa nkhani yopirira, iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri ndipo ankadziwa kuti chitsanzo chakecho chingalimbikitse anthu ena. (Yohane 16:33) N’zoona kuti iye anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa anali wangwiro, koma ifeyo si ife angwiro. Ndiyeno kodi Yehova amayembekezera kuti ifeyo tizichita chiyani? Petulo anafotokoza kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Petulo 2:21) Tikaganizira zimene anachita popirira mayesero, timaona kuti Yesu anatisiyira “chitsanzo” chabwino choti tizitsanzira. a Zinthu zonse zimene Yesu anachita posonyeza kuti ndi wopirira kwambiri tingaziyerekezere ndi “mapazi,” kapena kuti zidindo za mapazi. N’zosatheka kuti titsatire ndendende mapazi a wina, n’kumaponda mosalakwitsa malo amene mapazi ake adinda. Koma n’zotheka kutsatira mapaziwo “mosamala kwambiri.”

21 Choncho, tiyeni titsimikize kuchita zonse zimene tingathe kuti titsanzire Yesu. Tisamaiwale kuti tikamayesetsa kwambiri kutsatira mapazi a Yesu, timakhala olimba ndiponso okonzeka kupirira “mpaka pamapeto,” kaya a dzikoli kapena mapeto a moyo wathu. Pa zinthu ziwirizi, sitikudziwa kuti chimene chingayambe kuchitika ndi chiti, koma zimene tikudziwa n’zakuti: Tikapitiriza kupirira mpaka pamapeto, Yehova adzatipatsa madalitso ambirimbiri omwe sadzatha.​—Mateyu 24:13.

a Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chitsanzo,” kwenikweni amatanthauza “pepala lokhala ndi zilembo limene linkaikidwa pansi pa pepala lina limene ankafuna kulembapo.” Pa anthu onse amene anauziridwa kulemba Malemba a Chigiriki, mtumwi Petulo yekha ndi amene anagwiritsa ntchito mawu amenewa ndipo anthu ena amanena kuti mawuwa amatanthauza “‘pepala lokhala ndi zilembo’ limene mwana amene akuphunzira kulemba ankaika pansi pa pepala lina kuti azilemba motsatira zilembozo ndipo amayesetsa kuti zifanane ndendende.”