Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 2

‘Ankaphunzitsa Komanso Kulalikira Uthenga Wabwino’

‘Ankaphunzitsa Komanso Kulalikira Uthenga Wabwino’

Yesu anali kalipentala, ankachita zozizwitsa komanso ankachiritsa odwala. Si zokhazi, anachitanso zina zambiri, koma anthu sankagwiritsa ntchito mayina ogwirizana ndi ntchito zimenezi pomuitana. Iwo ankamuitana kuti Mphunzitsi. N’zoonadi, ntchito yake yaikulu inali ‘kuphunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino.’ (Mateyu 4:23) Monga otsatira a Yesu, ifenso tiyenera kugwira ntchito imeneyi. M’gawo lino, tiona chitsanzo chomwe iye anatipatsa chimene chimatithandiza kugwira bwino ntchitoyi.