Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 8

“Ndi Zimene Mulungu Anandituma Kudzachita”

“Ndi Zimene Mulungu Anandituma Kudzachita”

1-4. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji luso pophunzitsa mayi wa Chisamariya, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi atumwi ake anatani ataona zimenezi?

 YESU ndi atumwi ake anali atayenda maola ambiri pa ulendo wautali wochokera ku Yudeya kupita kudera la Galileya limene linali chakumpoto. Njira yachidule yomwe anadutsa inali yodzera ku Samariya ndipo ulendowo unali wa masiku atatu. Nthawi itatsala pang’ono kukwana 12 koloko masana, anaima mumzinda winawake waung’ono, wotchedwa Sukari, kuti apume ndiponso adye.

2 Atumwiwo atapita kukagula chakudya, Yesu anakhala pafupi ndi chitsime kunja kwa mzindawu n’kumapuma. Kenako mayi wina wa Chisamariya anafika kudzatunga madzi. Yesu akanatha kungomusiya osamulankhula chifukwa anali “atatopa ndi ulendowo.” (Yohane 4:6) Ndipotu zikanakhala zomveka ngati iye akanangoyang’ana kumbali mpaka mayiyo atatunga madzi n’kumapita. Monga mmene tinaonera m’Mutu 4 wa bukuli, mayiyu ankadziwa kuti sangalemekezedwe ndi Myuda aliyense. Komabe, Yesu anayamba kulankhula naye.

3 Iye anayamba ndi fanizo lonena za ntchito imene mayiyu ankagwira tsiku ndi tsiku ndipo pa nthawiyi, mayiyu anabwera kudzagwira ntchito imeneyo. Iye anabwera kudzatunga madzi ndipo Yesu anakambirana naye za madzi opatsa moyo amene akanathetsa ludzu lake lauzimu. Koma kangapo konse, mayiyu anayambitsa nkhani zimene zikanachititsa kuti asemphane maganizo. a Komabe Yesu anapewa nkhani zimenezo mwanzeru n’kupitiriza kukambirana naye nkhani yofunikirayo. Iye anafotokoza nkhani zokhudza zinthu zauzimu monga kulambira koona ndiponso Yehova Mulungu. Uthenga wa Yesu unamugwira mtima kwambiri mayiyu moti anapita kukafotokozera amuna a mumzindawo ndipo nawonso anabwera kwa Yesu kuti adzamve okha.​—Yohane 4:3-42.

4 Kodi atumwi aja atafika, anamva bwanji mumtima mwawo ataona Yesu akulalikira mayiyo mogwira mtima? Iwo sanasonyeze m’njira iliyonse kuti zawasangalatsa. Anadabwa kuona Yesu akulankhula ndi mayiyu ndipo zikuoneka kuti iwo sanamulankhule mayiyo. Mayiyo atachoka, iwo anapempha Yesu kuti adye chakudya chimene iwo anabweretsa. Koma Yesu anawauza kuti: “Ndili ndi chakudya chimene inu simukuchidziwa.” Poyamba, iwo anadabwa kwambiri chifukwa ankaganiza kuti ankanena chakudya chenicheni. Kenako iye anawafotokozera kuti: “Chakudya changa ndi kuchita zofuna za amene anandituma ndi kumaliza ntchito yake.” (Yohane 4:32, 34) Pamenepatu Yesu anawaphunzitsa kuti ntchito imene anabwerera inali yofunika kwambiri pa moyo wake kuposa chakudya. Iye ankafuna kuti atumwi akewo akhalenso ndi maganizo amenewa. Kodi ntchito imeneyo inali yotani?

5. Kodi ntchito yofunika kwambiri pa moyo wa Yesu inali yotani, nanga m’mutu uno tikambirana chiyani?

5 Pa nthawi ina, Yesu ananena kuti: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu . . . , chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Zoonadi, Yesu anatumidwa kudzalalikira ndi kuphunzitsa za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. b Masiku anonso otsatira a Yesu akuyenera kugwira ntchito imeneyi. Choncho ndi bwino kuti tione chifukwa chimene Yesu ankalalikirira, uthenga umene ankalalikira ndiponso mmene ankaonera ntchito yake yolalikirayi.

N’chifukwa Chiyani Yesu Ankalalikira?

6, 7. Kodi Yesu amafuna kuti “mphunzitsi aliyense” aziona bwanji ntchito youza ena uthenga wabwino? Perekani chitsanzo.

6 Choyamba tiyeni tikambirane mmene Yesu ankaonera choonadi chimene ankaphunzitsa, kenako tikambirana mmene ankaonera anthu amene ankawaphunzitsawo. Yesu anagwiritsa ntchito fanizo pofuna kusonyeza mmene ankaonera ntchito youza ena choonadi chimene Yehova anamuphunzitsa. Iye anati: “Mphunzitsi aliyense amene waphunzitsidwa za Ufumu wakumwamba ali ngati munthu yemwe ndi mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.” (Mateyu 13:52) N’chifukwa chiyani mwininyumba amene watchulidwa mufanizoli anatulutsa chumacho mosungiramo?

7 Si kuti mwininyumbayo akungotulutsa zinthu zake pofuna kunyaditsa anthu ena, ngati mmene anachitira Mfumu Hezekiya nthawi ina, zomwe zinamubweretsera mavuto aakulu. (2 Mafumu 20:13-20) Nanga n’chiyani chinapangitsa mwininyumbayo kuti atulutse zinthuzo? Kuti timvetse chifukwa chake, taganizirani fanizo ili: Tiyerekezere kuti muli pa sukulu ndipo mwapita kukacheza kunyumba kwa mphunzitsi amene mumagwirizana naye. Mphunzitsiyo akutsegula dilowa n’kutulutsa makalata awiri, ina yakale kwambiri ndipo inayo, yatsopano. Iye analandira makalatawa kuchokera kwa bambo ake. Kalata yoyamba anailandira kale kwambiri ali mnyamata, ndipo inayo wailandira posachedwapa. Iye akukuuzani mosangalala kwambiri kuti makalatawo amawaona kuti ndi ofunika kwambiri ndipo amawaganizira nthawi zonse chifukwa ali ndi malangizo amene anasintha moyo wake, moti akukuuzani kuti inunso malangizowo angakuthandizeni. (Luka 6:45) Iye akukuonetsani makalatawo, osati pofuna kukunyaditsani kapena kuti apeze phindu ayi, koma akufuna kuti inunso muone kufunika kwake komanso kuti mupindule ndi malangizo amene ali m’makalatawo.

8. N’chifukwa chiyani tili ndi chifukwa chabwino chokhulupirira kuti choonadi chimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu ndi chamtengo wapatali?

8 Yesu amene ndi Mphunzitsi Waluso, anali ndi mtima ngati umenewu, umene unamuchititsa kuti aziuza ena zimene Mulungu anamuphunzitsa. Iye ankadziwa kuti zimene anaphunzirazo ndi choonadi chamtengo wapatali kwambiri. Iye ankakonda kwambiri choonadichi ndipo ankafunitsitsa kuuza ena. Choncho ankafunanso kuti otsatira ake onse, kapena kuti “mphunzitsi aliyense,” azichita chimodzimodzi. Kodi ifeyo timachita zimenezi? Tili ndi chifukwa chabwino chotichititsa kukonda mfundo iliyonse imene taphunzira m’Mawu a Mulungu. Timaona kuti mfundo za choonadi ndi zofunika kwambiri, kaya ndi zakale kapena zimene tazimvetsa bwino posachedwapa. Tikamalankhula mochokera pansi pa mtima komanso tikapitiriza kukonda zimene Yehova watiphunzitsa, tingatsanzire Yesu amene anathandiza anthu kuti ayambe kukonda choonadi chamtengo wapatalichi.

9. (a) Kodi Yesu ankawaona bwanji anthu amene ankawaphunzitsa? (b) Kodi tingatani kuti tiziona anthu ngati mmene Yesu ankawaonera?

9 Yesu ankakondanso anthu amene ankawaphunzitsa ndipo tiphunzira zimenezi mwatsatanetsatane m’gawo lachitatu la bukuli. Ulosi unaneneratu kuti Mesiya “adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka.” (Salimo 72:13) Zoonadi, Yesu ankakonda anthu. Iye ankaganizira kwambiri za mtima ndiponso maganizo amene ankachititsa anthuwo kuchita zinthu zina zake. Komanso ankada nkhawa ndi mavuto ndiponso zopinga zimene zinkalepheretsa anthuwo kumvetsa mfundo za choonadi. (Mateyu 11:28; 16:13; 23:13, 15) Mwachitsanzo, taganizirani mayi wa Chisamariya uja. N’zosakayikitsa kuti anasangalala kwambiri ataona kuti Yesu wachita naye chidwi. Popeza Yesu anasonyeza kuti akudziwa zinthu zokhudza moyo wa mayiyo, iye anavomereza zoti Yesuyo ndi mneneri ndipo anapita kukauza anthu ena za iye. (Yohane 4:16-19, 39) N’zoona kuti ife sitingadziwe zimene zili mumtima mwa anthu amene timawalalikira. Komabe, popeza ndife otsatira a Yesu, tingasonyeze kuti tili ndi chidwi ndi anthu monga mmene Yesu anachitira. Tingasonyeze kuti tikuwadera nkhawa ndipo tingasinthe ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi zimene anthuwo amakonda, mavuto awo ndiponso zimene amafunikira.

Kodi Yesu Ankalalikira Uthenga Wotani?

10, 11. (a) Kodi uthenga umene Yesu ankalalikira unali wotani? (b) N’chiyani chinachititsa kuti Ufumu wa Mulungu ufunikire?

10 Kodi uthenga umene Yesu ankalalikira unali wotani? Ngati mungafufuze zimene matchalitchi osiyanasiyana amaphunzitsa, mungaganize kuti Yesu ankangophunzitsa mfundo zimene zingathandize anthu kuthetsa mavuto awo panopa. Mwinanso mukhoza kuganiza kuti iye ankalimbikitsa kusintha zinthu pa nkhani za ndale kapenanso ankalimbikitsa kuti chinthu chofunika kwambiri n’chakuti munthu aliyense azichita zinthu zoti adzapulumuke basi. Komabe, monga mmene taonera koyambirira kwa nkhani ino, Yesu ananena momveka bwino kuti: ‘Ndiyenera kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.’ N’chiyani chinachititsa kuti ntchitoyi ikhale yofunika?

11 Kumbukirani kuti Yesu analipo kumwamba pamene Satana anatsutsa koyamba zoti Yehova ndi wolamulira wabwino. Yesu ayenera kuti zinamupweteka kwambiri mumtima kuona Satana akunamizira Atate ake kuti salamulira moyenera ndipo safuna kupereka zinthu zabwino kwa zolengedwa zake. Mwana wa Mulungu ayeneranso kuti zinamupweteka kwambiri pamene Adamu ndi Hava, omwe anadzakhala makolo a anthu onse, anakhulupirira bodza la Satana. Mwanayo anaona kuti anthu anakhala ochimwa n’kuyamba kufa chifukwa cha kusamvera kwa makolo awo. (Aroma 5:12) Komabe ayenera kuti anasangalala kwambiri kudziwa kuti tsiku lina Atate ake adzakonza zinthu mu Ufumu wake.

12, 13. Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa zinthu ziti zopanda chilungamo, nanga Yesu anasonyeza bwanji kuti nkhani yaikulu pa utumiki wake inali yonena za Ufumu?

12 Koposa zonsezi, kodi ndi nkhani iti imene inafunika kuthetsedwa? Dzina loyera la Yehova linafunika kuyeretsedwa. Zimenezi zikutanthauza kuti zinthu zonse zimene Satana ndi onse amene amamutsatira amachita ponyoza dzinali zinafunika kuchotsedwa. Popeza kuti dzina la Yehova likusonyezanso kuti iye ndi wolamulira wotani, panafunika umboni wosonyeza kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Ndipotu Yesu ankamvetsa bwino kwambiri nkhani zofunikazi kuposa munthu aliyense. N’chifukwa chake m’pemphero lake lachitsanzo, iye anaphunzitsa otsatira ake kuti choyamba, azipempha kuti dzina la Atate wake liyeretsedwe, chachiwiri, Ufumu wake ubwere, ndipo kenako chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu, womwe wolamulira wake ndi Khristu Yesu, uchotsa mavuto onse amene Satana wabweretsa padzikoli ndipo udzasonyeza mpaka kalekale kuti Yehova ndi wolamulira wabwino kwambiri.​—Danieli 2:44.

13 Nkhani yaikulu pa utumiki wa Yesu inali yonena za Ufumu umenewo. Zinthu zonse zimene ankalankhula komanso kuchita zinathandiza kuti anthu amvetse Ufumuwo komanso mmene udzakwaniritsire cholinga cha Yehova. Yesu sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Pa nthawi imeneyo, panali mavuto osiyanasiyana komanso pankachitika zinthu zambiri zopanda chilungamo. Komabe iye sanasiye ntchito yake yolalikira za Ufumu n’kuyamba kuthetsa mavuto amenewa. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yesu anali woumirira zinthu, wosasamala za ena komanso wokonda kuchita zinthu zimodzimodzi basi? Ayi ndithu.

14, 15. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali “woposa Solomo”? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikamalalikira?

14 Yesu ankaphunzitsa mogwira mtima mfundo zosiyanasiyana komanso zosangalatsa, ndipo tiona zimenezi m’chigawo chino. Zimenezi zikutikumbutsa mfumu yanzeru Solomo, amene ankafufuza mawu osangalatsa ndiponso mawu olondola a choonadi kuti afotokoze mfundo zimene Yehova anamuuza kuti alembe. (Mlaliki 12:10) Ngakhale kuti iye sanali wangwiro, Yehova anamupatsa “mtima womvetsa zinthu zambirimbiri” umene unkamuthandiza kuti alankhule zinthu zambiri zokhudza mbalame, nsomba, mitengo ndiponso nyama. Ndipo anthu ankabwera kuchokera kutali kuti adzamvetsere zimene Solomo ankalankhula. (1 Mafumu 4:29-34) Komatu Yesu anali “woposa Solomo.” (Mateyu 12:42) Iye anali wanzeru kwambiri ndiponso anali ndi “mtima womvetsa zinthu zambirimbiri.” Pophunzitsa anthu, Yesu anasonyeza kuti ankadziwa kwambiri Mawu a Mulungu ndiponso zinthu monga mbalame, nyama, nsomba, ulimi, nyengo, nkhani zimene zinali zitangochitika kumene, mbiri yakale komanso zochitika za tsiku ndi tsiku. Komatu, Yesu sankachita zinthu modzionetsera kuti agometse anthu. Uthenga wake unali wosavuta ndiponso womveka bwino. Ndipotu n’zosadabwitsa kuti anthu ankasangalala pomvetsera ulaliki wake.​—Maliko 12:37; Luka 19:48.

15 Masiku anonso, Akhristu amayesetsa kutsatira Yesu. N’zoona kuti nzeru zathu ndiponso zinthu zimene timadziwa n’zochepa poyerekezera ndi Yesu. Komabe, tingathe kuuza ena choonadi cha m’Mawu a Mulungu chifukwa tonsefe timadziwa zinthu ndithu, ndiponso taphunzira ndi kuona zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, pophunzitsa anthu mmene Yehova amakondera ana ake, makolo angagwiritse ntchito chitsanzo cha mmene iwowo amalerera ana awo mwachikondi. Ena angaphunzitse pogwiritsa ntchito zimene zimachitika kuntchito ndiponso kusukulu, kapena angagwiritse ntchito zinthu zosiyanasiyana zimene anthu amachita ndiponso nkhani zimene zangochitika kumene. Komabe, pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi, tiyenera kusamala kuti tisasokoneze uthenga wabwino umene tikulalikira wokhudza Ufumu wa Mulungu.​—1 Timoteyo 4:16.

Kodi Yesu Ankaona Bwanji Utumiki Wake?

16, 17. (a) Kodi Yesu ankaona bwanji utumiki wake? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti utumiki wake unali wofunika kwambiri pa moyo wake?

16 Yesu ankaona kuti utumiki wake unali chuma chamtengo wapatali. Iye ankasangalala kuthandiza anthu kuti adziwe zoona zenizeni za Atate ake akumwamba, mosiyana ndi miyambo ndiponso zikhulupiriro zovuta kumva zimene anthu ankaphunzitsa ponena za Mulungu. Yesu ankakonda kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova ndiponso kuti akhale ndi chiyembekezo chodzalandira moyo wosatha. Iye ankasangalalanso kuuza anthu uthenga wabwino umene unali wolimbikitsa ndiponso wosangalatsa. Kodi iye anasonyeza bwanji zimenezi? Taonani njira zitatu zotsatirazi.

17 Njira yoyamba, Yesu ankaona kuti utumiki wake unali wofunika kwambiri pa moyo wake. Ntchito yaikulu komanso yofunika kwambiri pa moyo wake inali yolengeza za Ufumu. N’chifukwa chake, monga mmene tinaonera m’Mutu 5, Yesu ankakhala moyo wosafuna zambiri. Maganizo ake onse anali pa ntchito imene inali yofunika kwambiri ndipo zimenezi zinali zogwirizana ndi zimene ankaphunzitsa. Iye sanalole kukhala ndi zinthu zimene zikanasokoneza utumiki wake. Mwachitsanzo, sanagule kapena kukhala ndi zinthu zimene zikanafunika kuti azizisamalira ndiponso azizikonzetsa zikaonongeka. Iye ankakhala moyo wosafuna zambiri n’cholinga choti pasapezeke chilichonse chosokoneza utumiki wake.​—Mateyu 6:22; 8:20.

18. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wakhama pa utumiki wake?

18 Njira yachiwiri, Yesu ankachita utumiki wake mwakhama kwambiri. Iye ankachita utumikiwu ndi mphamvu zake zonse ndipo ankayenda pansi maulendo ataliatali m’dziko lonse la Palesitina, pofunafuna anthu oti awauze uthenga wabwino. Iye ankaphunzitsa anthu m’nyumba zawo, m’misika ndiponso m’malo osiyanasiyana. Ankaphunzitsanso anthu ngakhale pa nthawi imene ankafuna kupuma, kudya, kumwa madzi ndiponso pa nthawi imene ankafuna kukhala payekha ndi anzake a pamtima. Yesu anapitiriza kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ngakhale pamene iye anali atatsala pang’ono kufa.​—Luka 23:39-43.

19, 20. Kodi Yesu ananena fanizo lotani losonyeza kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuigwira mwachangu?

19 Njira yachitatu, Yesu ankaona kuti utumiki wake ndi wofunika kuuchita mwachangu. Kumbukirani zimene anakambirana ndi mayi wa Chisamariya uja pachitsime, kunja kwa mzinda wa Sukari. Zikuoneka kuti pa nthawiyo, atumwi a Yesu sankaona kufunika kouza ena uthenga wabwino mwachangu. Choncho Yesu anawauza kuti: “Kodi inu simunena kuti kwatsala miyezi 4 kuti tiyambe kukolola? Koma ndikukuuzani kuti: Kwezani maso anu muone m’mindamo. Muona kuti mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”​—Yohane 4:35.

20 Yesu ananena fanizoli mogwirizana ndi mmene nyengo inalili pa nthawiyo. Zikuoneka kuti unali mwezi wa Kisilevi (November/December). Kunali kutatsala miyezi 4 kuti nthawi yokolola balere ndi tirigu ifike, ndipo Pasika akamachitika pa Nisani 14, anthu ankakhala atayamba kale kukolola. Choncho, pamene Yesu ankanena fanizoli, alimi sankakonzekera ntchito yokolola chifukwa nthawi yake inali isanakwane. Koma kodi nthawi yokolola mwauzimu inali isanafike? Inali itafika, chifukwa anthu ambiri anali okonzeka kumvetsera, kuphunzira, kukhala ophunzira a Khristu ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chodzalandira moyo wosatha umene Yehova adzapereke. Zinali ngati kuti Yesu akayang’ana munda wophiphiritsa, ankangoona munda wonse utayera, tirigu yense atauma ndiponso akugwedezeka ndi mphepo, kusonyeza kuti nthawi yokolola yakwana. c Nthawi yokolola inali itakwana ndipo ntchitoyo inafunika kuchitika mwamsanga. N’chifukwa chake anthu a mumzinda winawake atapempha Yesu kuti asachoke mumzindawo, iye anawauza kuti: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.”​—Luka 4:43.

21. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

21 Tingatsanzire Yesu m’njira zonse zitatu zimene takambiranazi. Tiyenera kuona utumiki umene timachita monga Akhristu kuti ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu. Ngakhale kuti mwina tili ndi udindo wosamalira banja komanso zinthu zina, tiyenerabe kulalikira nthawi zonse mwachangu, ngati mmene Yesu anachitira, posonyeza kuti timaona utumiki wathu kuti ndi wofunika kwambiri. (Mateyu 6:33; 1 Timoteyo 5:8) Tiyenera kuchita utumiki wathu mwakhama, pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso chuma chathu mowolowa manja pothandizira ntchito yolalikirayi. (Luka 13:24) Ndipo tisamaiwale kuti tikuyenera kugwira ntchitoyi mwachangu. (2 Timoteyo 4:2) Tiyenera kugwiritsira ntchito mpata uliwonse umene tingapeze, kulalikira uthenga wabwino.

22. Kodi m’mutu wotsatira tikambirana chiyani?

22 Yesu anasonyezanso kuti ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri chifukwa anaonetsetsa kuti ntchitoyi idzapitirizebe iye akadzamwalira. Iye anauza otsatira ake kuti apitirize kugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. M’mutu wotsatira, tikambirana za ntchito imeneyi.

a Mwachitsanzo, pofunsa chifukwa chimene Myudayo ankalankhulira ndi Msamariya, mayiyo anayambitsa nkhani yokhudza chidani cha kalekale pakati pa anthu a mitundu iwiriyi. (Yohane 4:9) Iye ananenanso zoti Asamariya ndi mbadwa za Yakobo, mfundo imene Ayuda ankakanitsitsa kwa mtu wagalu. (Yohane 4:12) Ayuda ankawanena Asamariya kuti ndi Akuta, pofuna kutsindika mfundo yakuti iwo si mbadwa za Yakobo, koma ndi anthu amene anachokera kwa anthu a mitundu ina.

b Kulalikira kumatanthauza kufalitsa kapena kulengeza uthenga. Tanthauzo la kuphunzitsa ndi lofananako ndi kulalikira, koma kuphunzitsa kumafuna zambiri monga kufotokoza zinthu mozamirapo ndiponso mwatsatanetsatane. Mphunzitsi wabwino amaphunzitsa mogwira mtima n’cholinga choti wophunzirayo achite zimene waphunzirazo.

c Pofotokoza za vesili, buku lina linati: “Tirigu akakhwima, sakhalanso wobiriwira koma amakhala wachikasu, kapena woyererako. Zimenezi zimasonyeza kuti nthawi yokolola yakwana.”