MUTU 11
“Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyu N’kale Lonse”
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani alonda amene anatumidwa kukagwira Yesu anabwerako chimanjamanja? (b) N’chifukwa chiyani Yesu anali katswiri pophunzitsa?
AFARISI anakwiya kwambiri ndi Yesu yemwe ankaphunzitsa za Atate ake m’kachisi. Anthu amene ankamumvetsera anali ndi maganizo osiyana chifukwa ena anamukhulupirira koma ena ankafuna kumugwira. Atsogoleri achipembedzo atalephera kuugwira mtima, anatumiza alonda kuti akamugwire. Koma alondawo anabwerako chimanjamanja. Ndiyeno ansembe aakulu komanso Afarisi anafunsa alondawo kuti: “N’chifukwa chiyani simunabwere naye?” Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” Iwo anachita chidwi kwambiri ndi mmene Yesu ankaphunzitsira moti sakanatha kumugwira. a—Yohane 7:45, 46.
2 Si alonda okhawo amene anachita chidwi ndi mmene Yesu ankaphunzitsira, chifukwa anthu ambirimbiri ankasonkhana kudzamumvetsera akamaphunzitsa. (Maliko 3:7, 9; 4:1; Luka 5:1-3) N’chifukwa chiyani Yesu anali katswiri pophunzitsa? Monga mmene tinaonera m’Mutu 8, iye ankakonda choonadi chimene ankaphunzitsa komanso ankakonda anthu amene ankawaphunzitsawo. Analinso katswiri pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zophunzitsira. Tiyeni tikambirane njira zitatu zothandiza kwambiri zimene ankagwiritsa ntchito ndipo tione mmene ifeyo tingamutsanzirire.
Ankaphunzitsa M’njira Yosavuta Kumva
3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva pophunzitsa? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ulaliki wa paphiri ndi chitsanzo chosonyeza kuti Yesu ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva pophunzitsa?
3 Yesu ankadziwa mawu ambiri ozama amene akanatha kuwagwiritsa ntchito. Koma pophunzitsa, iye sankalankhula zinthu zimene anthu amene ankamumvetsera, omwe ambiri a iwo anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” sakanatha kuzimvetsa. (Machitidwe 4:13) Iye ankadziwa zimene anthuwo angathe kumvetsa ndipo sanafune kuwauza zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. (Yohane 16:12) Ndipotu ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva, koma choonadi chimene ankaphunzitsa chinali chamtengo wapatali.
4 Mwachitsanzo, tiyeni tione ulaliki wa paphiri pa Mateyu 5:3 mpaka 7:27. Pa ulaliki umenewu Yesu anapereka malangizo ogwira mtima komanso othandiza kwambiri. Iye anagwiritsa ntchito mfundo zotsatirika ndiponso mawu osavuta kumva moti ngakhale ana sangavutike kumva. N’chifukwa chake Yesu atamaliza kulankhula, gulu la anthuwo, omwe mwina anali alimi, abusa, ndi asodzi, “linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake.”—Mateyu 7:28.
5. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti nthawi zambiri Yesu ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva ndipo mfundo zake zinkakhala zogwira mtima.
5 Yesu pophunzitsa, nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito ziganizo zifupizifupi komanso zosavuta kumva ndipo ankanena mfundo zogwira mtima. Zimenezi zinathandiza kuti uthenga wake uwagwire mtima anthu amene ankamvetserawo, ngakhale kuti pa nthawi imeneyo kunalibe mabuku. Tiyeni tione zitsanzo zotsatirazi. “Siyani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe,” “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” “Mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” b (Mateyu 7:1; 9:12; 26:41; Maliko 12:17; Machitidwe 20:35) Mawu amenewa ndi osaiwalika ngakhale kuti anawalankhula zaka pafupifupi 2000 zapitazo.
6, 7. (a) N’chifukwa chiyani kugwiritsa ntchito mawu osavuta n’kothandiza pophunzitsa? (b) Kodi tingapewe bwanji kuuza munthu amene tikuphunzira naye Baibulo zinthu zambirimbiri nthawi imodzi?
6 Kodi ifeyo tingatani kuti tiziphunzitsa m’njira yosavuta kumva? M’pofunika kwambiri kuti tizilankhula mawu omwe anthu ambiri angathe kumva mosavuta. Ndipotu choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu n’chosavuta kumva. Yehova anaulula zolinga zake kwa anthu oona mtima ndiponso odzichepetsa. (1 Akorinto 1:26-28) Mawu osavuta ndiponso osankhidwa bwino angathandize anthu kumvetsa choonadi cha m’Mawu a Mulungu.
7 Kuti tiziphunzitsa m’njira yosavuta kumva, tiyenera kupewa kuuza anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Choncho tikamaphunzira Baibulo ndi anthu, tizipewa kufotokoza mfundo iliyonse, kapena kuphunzira nawo ndime zambiri mofulumira n’cholinga choti timalize msanga bukulo. Koma ndi bwino kuphunzira mogwirizana ndi mmene wophunzira wathuyo alili komanso mmene amamvetsera zinthu. Cholinga chathu n’kuthandiza wophunzira wathu kuti akhale wotsatira wa Khristu ndiponso kuti azilambira Yehova. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumupatsa nthawi yokwanira wophunzira wathuyo kuti amvetse zimene akuphunzirazo ngakhale phunzirolo litatenga nthawi yaitali. Tikatero, choonadi cha m’Baibulo chidzakhazikika mumtima mwake ndipo adzayamba kugwiritsa ntchito zimene waphunzirazo.—Aroma 12:2.
Ankafunsa Mafunso Oyenera
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ankafunsa mafunso? (b) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mafunso pothandiza Petulo kudziwa yankho lolondola pa nkhani yokhoma msonkho wa pakachisi?
8 Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso mwaluso ngakhale kuti sizikanamutengera nthawi yaitali kungonena mfundo yofunikayo. Nanga n’chifukwa chiyani ankafunsa mafunso? Nthawi zina ankagwiritsa ntchito mafunso ozama kuti zolinga zoipa za anthu omutsutsa zionekere poyera n’kuwasowetsa chonena. (Mateyu 21:23-27; 22:41-46) Koma nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mafunso kuti ophunzira ake anene maganizo awo komanso kuti aziganiza mozama. Choncho ankafunsa mafunso monga akuti “Mukuganiza bwanji?” komanso “Kodi ukukhulupirira zimenezi?” (Mateyu 18:12; Yohane 11:26) Pogwiritsa ntchito mafunso, Yesu ankawafika pamtima ophunzira akewo. Tiyeni tione chitsanzo chotsatirachi.
9 Pa nthawi ina, okhometsa msonkho anafunsa Petulo ngati Yesu amapereka ndalama za msonkho wa pakachisi. c Nthawi yomweyo Petulo anayankha kuti, “Inde amapereka.” Kenako Yesu anamufunsa kuti: “Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?” Petulo anayankha kuti: “Kuchokera kwa anthu achilendo.” Kenako Yesu anamuuza kuti: “Ndiye kuti ana sakuyenera kukhoma msonkho.” (Mateyu 17:24-27) N’zosakayikitsa kuti Petulo anamvetsa cholinga cha mafunso amenewa, chifukwa chakuti zinali zodziwikiratu kuti anthu a m’banja lachifumu sankayenera kukhoma msonkho. Choncho, Yesu sankafunika kukhoma msonkho chifukwa ndi Mwana wobadwa yekha wa Mfumu yakumwamba, imene anthu ankalambira pakachisipo. Onani kuti m’malo mongouza Petulo yankho lolondola, Yesu anagwiritsa ntchito mafunso mwaluso kuti amuthandize kudziwa yankho lolondola komanso kuti mwina aone kufunika koyamba waganiza kaye mofatsa asanayankhe.
10. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso mwaluso tikamalalikira nyumba ndi nyumba?
10 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso mwaluso mu utumiki? Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, tingagwiritse ntchito mafunso kuti tithandize munthu kukhala ndi chidwi ndipo zimenezi zingatipatse mpata womuuza uthenga wabwino. Mwachitsanzo, tikafika pakhomo la munthu wachikulire mu utumiki tingamufunse mwaulemu kuti, “Kodi pa moyo wanu mwaona kuti dzikoli lasintha bwanji”? Tingayembekezere kuti ayankhe, kenako n’kumufunsa kuti, “Kodi mukuganiza kuti chofunika n’chiyani kuti dzikoli likhale malo abwino oti tizikhalamo?” (Mateyu 6:9, 10) Ngati titafika pakhomo la mayi amene ali ndi ana ang’onoang’ono, tingamufunse kuti, “Kodi munayamba mwadzifunsa kuti dzikoli lidzakhala lotani ana anuwa akadzakula?” (Salimo 37:10, 11) Tikakhala ndi chidwi choona mmene zinthu zilili pakhomo limene tafika, tingathe kufunsa funso logwirizana ndi zimene mwininyumba angakonde kudziwa.
11. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino mafunso pophunzira Baibulo ndi munthu?
11 Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino mafunso pophunzira Baibulo ndi munthu? Mafunso osankhidwa bwino angatithandize kudziwa zimene zili mumtima mwa munthu amene tikuphunzira naye. (Miyambo 20:5) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tikuphunzira mutu 43 m’buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale d umene umanena kuti “Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Mowa?” Mutu umenewu umafotokoza mmene Mulungu amaonera kumwa mowa mopitirira malire komanso uchidakwa. Mayankho a wophunzira wathu angasonyeze kuti akumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa. Koma kodi iye akugwirizana ndi zimene akuphunzirazo? Mwina tingamufunse kuti, “Kodi mukuona kuti m’pomveka kuti Mulungu aziona nkhani zimenezi mwanjira imeneyi?” Tingamufunsenso kuti, “Kodi inuyo mungagwiritse ntchito bwanji mfundo zimenezi pa moyo wanu?” Koma tisaiwale kuti tifunika kufunsa mafunsowa mosamala ndiponso mwaulemu. Tisafunse mafunso amene angachititse manyazi wophunzirayo.—Miyambo 12:18.
Ankagwiritsa Ntchito Mfundo Zomveka Komanso Zamphamvu
12-14. (a) Kodi Yesu anasonyeza m’njira ziti luso logwiritsa ntchito mfundo zosatsutsika? (b) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito mfundo ziti zomveka komanso zamphamvu Afarisi atamunena kuti mphamvu zake zimachokera kwa Satana?
12 Yesu anali katswiri pokambirana ndi anthu chifukwa chakuti anali wangwiro. Nthawi zina ankagwiritsa ntchito mfundo zomveka komanso zamphamvu pofuna kutsutsa mabodza a anthu amene ankamutsutsa. Nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mfundo zokopa pophunzitsa otsatira ake zinthu zofunika kwambiri. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
13 Yesu atachiritsa munthu wogwidwa ndi chiwanda amenenso anali ndi vuto losaona komanso losalankhula, Afarisi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi koma ndi mphamvu za Belezebule [Satana], wolamulira ziwanda.” Iwo anavomereza ndithu kuti pankafunika mphamvu zapadera kuti munthu athe kutulutsa ziwanda. Koma ananena kuti mphamvu zimene Yesu anali nazo zinachokera kwa Satana. Mfundo imeneyi inali yosamveka komanso yabodza. Posonyeza kuti maganizo awo anali olakwika, Yesu anawayankha kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo mzinda kapena nyumba iliyonse yogawanika sikhalitsa. Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji?” (Mateyu 12:22-26) Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti: “Ngati ine ndikutumikira Satana powononga ntchito za Satana, ndiye kuti Satanayo akuwononga ntchito zake zomwe, ndipo ufumu wake sungachedwe kugwa.” Afarisi sakanatha kutsutsa mfundo yomveka bwino imeneyi.
14 Yesu anali ndi mfundo inanso yoti awauze. Podziwa kuti ophunzira ena a Afarisiwo ankatulutsanso ziwanda, iye anawafunsa funso losavuta koma lamphamvu lakuti: “Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule, nanga otsatira anu [kapena kuti, ophunzira anu] amazitulutsa ndi mphamvu za ndani?” (Mateyu 12:27) Pamenepa mfundo ya Yesu inali yakuti: “Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Satana, ndiye kuti ophunzira anunso amagwiritsa ntchito mphamvu yomweyo.” Kodi Afarisiwo akanavomereza kuti ophunzira awo amagwiritsa ntchito mphamvu ya Satana? Ayi ndithu. Choncho Yesu anagwiritsa ntchito maganizo awo olakwikawo powathandiza kudziwa zoona zenizeni. N’zochititsa chidwi ngakhale kungowerenga mmene Yesu anafotokozera mfundo zake pokambirana ndi Afarisiwo. Gulu la anthu amene ankamumvetsera ayenera kuti ankachita chidwi kwambiri akamamuona n’kumamvetsera mawu ake ogwira mtimawo.
15-17. Fotokozani chitsanzo chosonyeza mmene Yesu ankagwiritsira ntchito mawu akuti “kuli bwanji” pophunzitsa choonadi chosangalatsa chonena za Atate ake.
15 Yesu ankagwiritsanso ntchito mfundo zomveka bwino komanso zokopa pophunzitsa choonadi chosangalatsa chonena za Atate ake. Kawirikawiri iye ankachita zimenezi pogwiritsa ntchito mawu akuti “kuli bwanji.” Pogwiritsa ntchito mawu amenewa, ankathandiza omvera ake kuti amvetsetse bwino mfundo za choonadi zimene ankazidziwa kale. Njira yoyerekezera zinthu ziwiri imeneyi ndi yothandiza kwambiri kuti munthu asaiwale zimene wamva. Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri zokha.
16 Poyankha ophunzira ake amene anamupempha kuti awaphunzitse kupemphera, Yesu anafotokoza kuti makolo omwe si angwiro amafunitsitsa “kupereka mphatso zabwino kwa ana” awo. Kenako iye anamaliza ndi mawu akuti: “Ngati inuyo mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, ngakhale kuti ndinu oipa, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Luka 11:1-13) Yesu ananena mfundo yakeyi poyerekezera zinthu ziwiri. Ngati makolo ochimwa amapatsa ana awo zinthu zofunika, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba, amene ndi wangwiro komanso wolungama. Iye angapereke mzimu woyera kwa olambira ake okhulupirika amene akumupempha modzichepetsa.
17 Yesu anagwiritsanso ntchito njira yomweyi popereka malangizo a zimene tingachite tikakhala ndi nkhawa. Iye anati: “Ganizirani za akhwangwala: Iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nkhokwe kapena nyumba yosungiramo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame? Ganizirani za mmene maluwa amakulira: Iwo sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. . . . Ndiye ngati Mulungu amaveka chonchi zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha mawa n’kuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo.” (Luka 12:24, 27, 28) Ngati Yehova amasamalira mbalame ndiponso maluwa, kuli bwanji anthu amene amamukonda komanso kumulambira. N’zosakayikitsa kuti Yesu anawafika pamtima omvera akewo pokambirana nawo mwa njira imeneyi.
18, 19. Kodi tingathandize bwanji munthu amene akunena kuti sangakhulupirire Mulungu amene samuona?
18 Tikamalalikira tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo zomveka bwino pothandiza anthu kumvetsa kuti zinthu zina zimene amakhulupirira ndi zabodza. Tiyeneranso kugwiritsa ntchito mfundo zokopa pophunzitsa anthu choonadi chonena za Yehova. (Machitidwe 19:8; 28:23, 24) Kodi ndiye kuti tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mfundo zokhwima komanso zovuta kumva? Ayi ndithu. Chitsanzo cha Yesu chatisonyeza kuti tikafotokoza mfundo zomveka bwino m’njira yosavuta kumva, mfundozo zimakhala zogwira mtima.
19 Mwachitsanzo, kodi tingathandize bwanji munthu yemwe akunena kuti sangakhulupirire Mulungu amene samuona? Tingakambirane naye mfundo yakuti chinachake chikachitika timadziwa kuti pali chimene chachititsa. Mwachitsanzo, tinganene kuti: “Ngati inuyo mutapita kumudzi winawake, n’kupeza nyumba yokongola kwambiri mutadzaza chakudya (zochitika), kodi mungakayikire kuti pali winawake (wochititsa) amene anamanga nyumbayo n’kuikamo chakudyacho? N’chimodzimodzinso tikaona zinthu zolengedwa ndiponso chakudya chochuluka chimene chili padziko lapansi (zochitika), kodi tingakayikire kuti pali winawake (Wochititsa) amene anazipanga? Baibulo limafotokozanso zinthu mwa njira imeneyi kuti: ‘Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.’” (Aheberi 3:4) N’zoona kuti si aliyense amene angavomereze mfundo zathu ngakhale titazifotokoza bwino kwambiri.—2 Atesalonika 3:2.
20, 21. (a) Kodi tingagwiritse bwanji ntchito mawu akuti “kuli bwanji” pothandiza anthu kumvetsa makhalidwe a Yehova ndiponso mmene amachitira zinthu? (b) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani?
20 Tikamaphunzitsa mu utumiki kapena pampingo, tingagwiritsenso ntchito mawu akuti “kuli bwanji” pothandiza anthu kumvetsa makhalidwe a Yehova ndiponso mmene amachitira zinthu. Mwachitsanzo, kuti tisonyeze kuti chiphunzitso chakuti anthu oipa adzapsa kumoto wosazima chimanyozetsa Yehova, tinganene kuti: “Kodi alipo bambo wachikondi amene angalange mwana wake poika dzanja la mwanayo pamoto? Ngati bamboyo sangachite zimenezi, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi. Mulungu amanyansidwa anthu akamanena kuti iye adzawotcha anthu pamoto wosazima.” (Yeremiya 7:31) Mkhristu mnzathu yemwe akuvutika maganizo tingamutsimikizire kuti Yehova amamukonda ponena kuti: “Ngati Yehova amaona kuti mpheta, yomwe ndi mbalame yaing’ono, ndi yofunika, kuli bwanji anthu amene amamulambira padziko lapansi, kuphatikizapo inuyo. Iye amakonda komanso kusamalira munthu aliyense payekha.” (Mateyu 10:29-31) Kukambirana ndi anthu mwa njira imeneyi kungathandize kuti tiwafike pamtima.
21 Tangophunzira njira zitatu zokha zimene Yesu anagwiritsa ntchito pophunzitsa, ndipo taona bwino kuti alonda amene analephera kugwira Yesu aja, sankakokomeza zinthu pamene ananena kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” M’mutu wotsatira, tidzakambirana njira yophunzitsira imene Yesu ankadziwika nayo kwambiri, yogwiritsa ntchito mafanizo.
a Alondawo ayenera kuti ankatumikira pa Khoti Lalikulu la Ayuda ndipo ansembe aakulu ndi amene ankawayang’anira.
b Mtumwi Paulo yekha ndi amene ananena mawu amenewa omwe amapezeka pa Machitidwe 20:35. Zikuoneka kuti anachita kuuzidwa (ndi munthu wina amene anamva Yesu akulankhula kapena anawamva kwa Yesu ataukitsidwa) kapenanso anachita kuuziridwa ndi Mulungu.
c Chaka chilichonse, Ayuda ankafunika kukhoma msonkho wa pakachisi wa ndalama zokwana madalakima awiri, ndipo ndalamazi zinkakwana pafupifupi malipiro a ntchito ya masiku awiri. Buku lina limati: “Ndalama za msonkhozi kwenikweni ankazigwiritsa ntchito polipirira zinthu zofunika popereka nsembe yopsereza imene inkaperekedwa tsiku ndi tsiku komanso nsembe zonse zimene ankaperekera anthu onse.”
d Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.