Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”

Kodi mlimi angachite chiyani ngati mbewu zake ndi zambiri moti sangathe kukolola yekha?

1-3. (a) Kodi mlimi amatani ngati mbewu zake zachuluka kwambiri moti sangathe kukolola yekha? (b) Kodi Yesu anakumana ndi vuto lotani kumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., nanga anathana nalo bwanji?

 MLIMI wina analima munda wake ndi kudzala mbewu miyezi ingapo m’mbuyomo. Iye anasamalira kwambiri mbewuzo kuyambira nthawi imene zinangoyamba kumera ndipo anasangalala kwambiri ataona kuti mbewuzo zakhwima. Kenako nthawi yokolola itafika, iye anasangalala kwambiri chifukwa chakuti khama lake linapindula. Komabe mlimiyo anali ndi vuto limodzi ili: Mbewuzo zinali zochuluka kwambiri moti sakanatha kukolola yekha. Pofuna kuthana ndi vutoli iye anaganiza zolemba aganyu kuti amuthandize kukolola. Izi zinali zoyenera chifukwa anali ndi nthawi yochepa yoti akolole mbewuzo.

2 Kumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., Yesu ataukitsidwa anakumana ndi vuto ngati limeneli. Pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi, iye anafesa mbewu za choonadi. Choncho panali mbewu zambiri zofunika kukolola. Panali anthu ambiri achidwi amene ankafunika kuwasonkhanitsa kuti akhale ophunzira ake. (Yohane 4:35-38) Kodi Yesu anatani kuti ntchito imeneyi itheke? Atatsala pang’ono kupita kumwamba, anakumana ndi ophunzira ake paphiri ku Galileya ndipo anawalamula kuti akagwire ntchito yosonkhanitsa antchito ena. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza . . . , ndipo muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.”​—Mateyu 28:19, 20.

3 Otsatira enieni a Khristu amadziwika chifukwa chogwira ntchito imeneyi. Koma tsopano tiyeni tikambirane mafunso atatu awa: N’chifukwa chiyani Yesu analamula ophunzira ake kuti agwire ntchito yosonkhanitsa antchito ena? Kodi anaphunzitsa bwanji ophunzirawo kuti akwanitse kugwira ntchitoyi? Nanga ifeyo ntchito imeneyi ikutikhudza bwanji?

N’chifukwa Chiyani Pankafunika Antchito Ambiri?

4, 5. N’chifukwa chiyani Yesu sakanatha kumaliza ntchito imene anayamba, nanga ndi ndani amene ankafunika kupitiriza ntchitoyo iye atabwerera kumwamba?

4 Pamene Yesu ankayamba utumiki wake m’chaka cha 29 C.E., ankadziwa kuti akuyamba ntchito imene sangaimalize yekha. Pa nthawi yochepa imene anali nayo, sakanakwanitsa kulalikira uthenga wa Ufumu m’gawo lalikulu ndiponso kwa anthu ambiri. N’zoona kuti Yesu ankalalikira kwambiri Ayuda ndiponso anthu amene analowa chipembedzo cha Chiyuda omwe anali “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” (Mateyu 15:24) Komabe, “nkhosa zotayika” zimenezo zinali m’dziko lonse la Isiraeli limene linali lalikulu kwambiri. Kuwonjezera apo, uthenga wabwino unayenera kulalikidwa padziko lonse lapansi.​—Mateyu 13:38; 24:14.

5 Yesu ankadziwa kuti iye akadzamwalira ntchito yolalikira idzafunikabe kupitirira. Choncho iye anauza atumwi ake 11 okhulupirika aja kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi chifukwa ine ndikupita kwa Atate.” (Yohane 14:12) Popeza kuti Mwanayu ankapita kumwamba, otsatira ake, omwe ndi atumwi komanso ophunzira ake onse, ankafunika kupitiriza ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa. (Yohane 17:20) Yesu anavomereza modzichepetsa kuti otsatira akewo adzagwira ntchito “zazikulu kuposa” zake. Kodi otsatirawo akanachita bwanji zimenezi? Akanachita zimenezi m’njira zitatu.

6, 7. (a) Kodi otsatira a Yesu akanachita bwanji ntchito zazikulu kuposa zake? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti Yesu sanalakwitse pokhulupirira kuti otsatira akewo adzachita zimene anawatuma?

6 Njira yoyamba, otsatira a Yesu ankayenera kulalikira ndi kuphunzitsa m’dera lalikulu. Masiku ano iwo akulalikira mpaka kumalekezero a dziko lapansi, kupitirira malire a dziko limene Yesu ankalalikira. Njira yachiwiri, iwo ankayenera kulalikira ndi kuphunzitsa anthu ambiri. Kagulu kakang’ono ka ophunzira amene Yesu anawasiya kanakula mofulumira kwambiri n’kukhala gulu lalikulu. (Machitidwe 2:41; 4:4) Panopa alipo mamiliyoni ambiri ndipo anthu enanso masauzande ambiri amabatizidwa chaka chilichonse. Njira yachitatu, ankayenera kulalikira ndi kuphunzitsa kwa nthawi yaitali. Iwo akhala akugwira ntchito imeneyi mpaka lero ndipo papita zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene Yesu anamaliza utumiki wake umene anauchita zaka zitatu ndi hafu.

7 Pamene Yesu ananena kuti otsatira ake adzachita “ntchito zazikulu kuposa zimenezi” anasonyeza kuti ankawadalira. Iye anawapatsa ntchito imene ankaona kuti ndi yofunika kwambiri, yolalikira ndi kuphunzitsa “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Iye ankakhulupirira kuti otsatira akewo adzagwira ntchitoyi mokhulupirika. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Tikamachita utumiki wathu mwachangu komanso ndi mtima wonse, timasonyeza kuti Yesu sanalakwitse pokhulupirira kuti otsatira akewo adzachita zimene anawatuma. Tili ndi mwayi waukulu kwambiri kugwira nawo ntchito imeneyi.​—Luka 13:24.

Anawaphunzitsa Ntchito Yolalikira

Chikondi n’chimene chimatilimbikitsa kulalikira kulikonse kumene tingapeze anthu

8, 9. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani mu utumiki, nanga tingatsanzire bwanji chitsanzo chakecho?

8 Yesu anaphunzitsa bwino kwambiri ophunzira akewo kuti akwanitse utumiki wawo. Koma koposa zonsezi, iye anawapatsa chitsanzo chabwino kwambiri. (Luka 6:40) M’mutu wapitawu tinakambirana mmene Yesu ankaonera utumiki wake. Taganizirani za ophunzira amene ankayenda ndi Yesu pokalalikira. Iwo ankamuona akulalikira kulikonse kumene anthu akupezeka, monga m’mbali mwa nyanja, mphepete mwa phiri, m’mizinda, m’misika ndi m’nyumba za anthu. (Mateyu 5:1, 2; Luka 5:1-3; 8:1; 19:5, 6) Iwo ankaonanso kuti Yesu ndi wakhama pa utumiki, chifukwa ankadzuka m’mamawa n’kumagwira ntchito mpaka usiku. Iye sankachita utumiki chifukwa choti wasowa chochita. (Luka 21:37, 38; Yohane 5:17) Mosakayikira iwo ankaona kuti akuchita zonsezi chifukwa chokonda kwambiri anthu. Mwina iwo ankaona kuti nkhope yake ikusonyeza kuti iye ndi wachifundo. (Maliko 6:34) Kodi mukuganiza kuti chitsanzo cha Yesu chinakhudza bwanji ophunzira akewo? Nanga inuyo chikanakukhudzani bwanji?

9 Popeza kuti ndife otsatira a Yesu, timatengera chitsanzo chake mu utumiki wathu. Choncho timayesetsa kuchita zonse zimene tingathe kuti ‘tipereke umboni wokwanira.’ (Machitidwe 10:42) Mofanana ndi Yesu, timalalikira anthu m’makomo mwawo. (Machitidwe 5:42) Timasintha zochita zathu ngati pakufunika kutero, kuti tizilalikira pa nthawi imene tingapeze anthu pakhomo. Komanso timafufuza ndi kulalikira anthu m’malo aliwonse amene tingapeze anthu ambiri monga m’misewu, m’malo ochitira malonda ndi m’malo ogwirira ntchito, ndipo timachita zimenezi mosamala kwambiri. Timayesetsa ‘kugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu’ mu utumiki chifukwa timaona kuti ntchitoyi ndi yofunika kwambiri. (1 Timoteyo 4:10) Timayesetsanso kufufuza mpata uliwonse woti tilalikire anthu kulikonse kumene tingawapeze chifukwa chakuti timawakonda kuchokera pansi pa mtima.​—1 Atesalonika 2:8.

“Anthu okwana 70 aja anabwerera akusangalala”

10-12. Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa ophunzira ake asanawatumize kokalalikira?

10 Njira ina imene Yesu anaphunzitsira ophunzira ake inali kuwapatsa malangizo atsatanetsatane a mmene angachitire utumiki wawo. Mwachitsanzo, Yesu asanatumize atumwi 12 aja ndipo kenako ophunzira 70 kuti akalalikire, anachititsa msonkhano kuti awapatse malangizo owathandiza polalikira. (Mateyu 10:1-15; Luka 10:1-12) Malangizowo anawathandiza kwambiri chifukwa lemba la Luka 10:17 limati: “Anthu okwana 70 aja anabwerera akusangalala.” Tiyeni tione mfundo ziwiri zofunika zimene Yesu anaphunzitsa ndipo tikumbukire kuti mfundozi zikugwirizana ndi miyambo ya Chiyuda ya pa nthawiyo.

11 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azidalira Yehova. Iye anawauza kuti: “Musatenge golide, siliva kapena kopa m’zikwama zanu za ndalama. Musatenge thumba la chakudya cha pa ulendo kapena malaya awiri kapena nsapato kapenanso ndodo chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake.” (Mateyu 10:9, 10) Pa nthawiyo anthu apaulendo ankakonda kutenga zikwama za ndalama ndi matumba a zakudya komanso nsapato zapadera. Polangiza ophunzira akewo kuti asamade nkhawa ndi zinthu zimenezi, iye kwenikweni ankatanthauza kuti: “Muzidalira Yehova ndi mtima wonse chifukwa iye adzakupatsani zosowa zanu.” Yehova akanawasamalira pochititsa kuti anthu amene angamvetsere uthenga wabwino achereze ophunzirawo, ndipotu anthu a ku Isiraeli ankakonda kuchereza alendo.​—Luka 22:35.

12 Yesu anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azipewa zinthu zosafunika zimene zingawasokoneze pa utumiki wawo. Iye anati: “Musamapereke moni kwa wina aliyense panjira.” (Luka 10:4) Kodi pamenepa Yesu ankawauza kuti asamacheze ndi anthu kapena kuti akhale onyada? Ayi ndithu. Popatsana moni pa nthawi imeneyo, anthu ankachita zinthu zambirimbiri zokhudzana ndi chikhalidwe chawo komanso ankalankhulana kwa nthawi yaitali. Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Moni wa anthu a ku Isiraeli ndi mayiko ozungulira, sunali wongogwirana chanza n’kuwerama pang’ono ngati mmene anthu ena amachitira, koma ankakumbatirana ndi kuwerama mobwerezabwereza, ndipo nthawi zina ankagona pansi chafufumimba. Zonsezi zinkafuna nthawi yambiri.” Pouza ophunzira akewo kuti asamachite miyambo yonseyi popereka moni, Yesu kwenikweni ankatanthauza kuti: “Muzigwiritsa ntchito nthawi mwanzeru chifukwa uthenga wanu ndi wofunika kuulalikira mwachangu.” a

13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timatsatira malangizo amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake oyambirira?

13 Ifenso timatsatira malangizo amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake oyambirirawo. Tikamachita utumiki wathu, timadalira Yehova ndi mtima wonse. (Miyambo 3:5, 6) Timadziwa kuti sitidzasowa zinthu zofunikira pa moyo ngati ‘nthawi zonse tikuika Ufumu pamalo oyamba pa moyo wathu.’ (Mateyu 6:33) Padziko lonse, anthu amene amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse angachitire umboni kuti ngakhale m’nthawi zovuta, Yehova amapereka zinthu zofunika kwa anthu ake. (Salimo 37:25) Komanso timaona kuti n’kofunika kupewa zinthu zimene zingatisokoneze. Ngati sitingasamale, zochitika m’dzikoli zingatisokoneze mosavuta. (Luka 21:34-36) Choncho ino si nthawi yolola kuti zinthu zina zizitisokoneza. Uthenga wathu ndi wofunika kuulengeza mwamsanga chifukwa ngati sititero anthu angadzawonongedwe. (Aroma 10:13-15) Tikamaganizira nthawi zonse kuti tili ndi ntchito yofunika kuigwira mwamsanga, tidzapewa zinthu za m’dzikoli zimene zingatiwonongere mphamvu ndi nthawi yathu imene tikanaigwiritsa ntchito mu utumiki. Kumbukirani kuti nthawi imene yatsala ndi yochepa koma ntchito yokolola ndi yaikulu.​—Mateyu 9:37, 38.

Ntchito Imene Tikuyenera Kugwira Nawo

14. N’chiyani chikusonyeza kuti lamulo lopezeka pa Mateyu 28:18-20 likukhudza otsatira onse a Khristu? (Onaninso mawu a m’munsi.)

14 Ponena mawu akuti “pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga,” Yesu anapereka udindo waukulu kwambiri kwa otsatira ake. Sikuti iye ankangoganizira ophunzira ake amene anali nawo paphiri ku Galileya pa tsiku limenelo. b Kuti agwire ntchito imene anawalamula, iwo anafunika kufikira “anthu a mitundu yonse,” ndipo ntchito imeneyi ikupitirira “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Apa n’zookeratu kuti ntchitoyi ikukhudza otsatira onse a Khristu, kuphatikizapo ifeyo masiku ano. Tsopano tiyeni tione bwinobwino mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 28:18-20.

15. N’chifukwa chiyani n’chinthu chanzeru kumvera lamulo la Yesu loti tiphunzitse anthu kuti akhale ophunzira ake?

15 Yesu asanapereke lamuloli, ananena kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Vesi 18) Kodi Yesu alidi ndi ulamuliro wonsewo? Inde ali nawo, chifukwa iye ndi mkulu wa angelo, ndipo amalamulira angelo masauzande ambirimbiri. (1 Atesalonika 4:16; Chivumbulutso 12:7) Popeza kuti iye ndi “mutu wa mpingo,” ali ndi ulamuliro pa otsatira ake padziko lapansi. (Aefeso 5:23) Iye wakhala akulamulira kumwamba monga Mfumu komanso Mesiya kuyambira m’chaka cha 1914. (Chivumbulutso 11:15) Yesu alinso ndi ulamuliro pa anthu amene anamwalira chifukwa ali ndi mphamvu zoukitsa akufa. (Yohane 5:26-28) Popeza Yesu anayamba ndi kunena za ulamuliro umene ali nawo, iye anasonyeza kuti akufuna kupereka lamulo osati pempho. Kumvera lamulo limene Yesu anaperekali n’chinthu chanzeru chifukwa ulamuliro wake sanadzipatse yekha koma anapatsidwa ndi Mulungu.​—1 Akorinto 15:27.

16. Ponena kuti “pitani,” kodi Yesu akutilamula kuti tichite chiyani, nanga timasonyeza bwanji kuti tikumvera lamulo limeneli?

16 Tsopano popereka lamulolo Yesu anayamba ndi mawu akuti: “Choncho pitani.” (Vesi 19) Pamenepa iye akutilamula kuti tizipita kwa anthu kukawauza uthenga wa Ufumu. Tingagwiritse ntchito njira zosiyanasiyana kuti tikwanitse kugwira ntchito imeneyi. Kulalikira kunyumba ndi nyumba, ndi njira yabwino kwambiri yolankhulira ndi anthu pamasom’pamaso. (Machitidwe 20:20) Timafufuzanso mpata wolalikira mwamwayi. Mwachitsanzo, tsiku ndi tsiku timayesetsa kuyamba kukambirana ndi anthu za uthenga wabwino pa mpata uliwonse umene tingapeze. Tingagwiritse ntchito njira zosiyanasiyana polalikira mogwirizana ndi dera limene tili komanso mmene zinthu zilili. Komabe mfundo imene simasintha ndi yakuti: ‘Timapita’ kukafunafuna anthu oyenerera.​—Mateyu 10:11.

17. Kodi tingathandize bwanji anthu kuti ‘akhale ophunzira a Yesu’?

17 Kenako Yesu anafotokoza chifukwa chimene anaperekera lamuloli. Iye anawauza kuti ‘akaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake.’ (Vesi 19) Kodi tingathandize bwanji anthu kuti ‘akhale ophunzira a Yesu’? Kuphunzitsa munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu n’kosiyana ndi kuphunzitsa munthu kuti angodziwa zinthu. Tikamaphunzira Baibulo ndi anthu achidwi, cholinga chathu chimakhala kuwathandiza kuti akhale otsatira a Khristu. Timayesetsa kufotokoza chitsanzo cha Yesu kuti munthu amene tikuphunzira nayeyo aziona kuti Yesu ndi Mphunzitsi wake ndiponso Chitsanzo chake. Zimenezi zingamuthandize kuti atengere chitsanzo cha Yesu pa moyo wake komanso kuti azigwira ntchito imene iye ankagwira.​—Yohane 13:15.

18. N’chifukwa chiyani nthawi ya ubatizo imakhala yosaiwalika pa moyo wa wophunzira?

18 Mbali yofunika kwambiri ya lamulo limeneli yatchulidwa m’mawu akuti: “Muziwabatiza m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera.” (Vesi 19) Nthawi ya ubatizo ndi nthawi yosaiwalika pa moyo wa wophunzira, chifukwa akamabatizidwa amasonyeza kuti wadzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu. Choncho ubatizo ndi wofunika kuti munthu adzapulumuke. (1 Petulo 3:21) Ndipotu wophunzira wobatizidwa akapitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse, amayembekezera kudzapeza madalitso osatha m’dziko lapansi latsopano. Kodi munayamba mwathandizapo munthu kuti akhale wophunzira wa Khristu wobatizidwa? Palibe chinthu chosangalatsa kwambiri mu utumiki kuposa kuchita zimenezi.​—3 Yohane 4.

19. Kodi anthu amene akuphunzira kumene choonadi timawaphunzitsa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuwaphunzitsa ngakhale atabatizidwa?

19 Kenako Yesu anafotokoza mbali ina ya lamuloli kuti: “Muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.” (Vesi 20) Timaphunzitsa anthu kuti azimvera malamulo a Yesu, kuphatikizapo malamulo akuti tizikonda Mulungu, tizikonda anzathu ndiponso tiziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake. (Mateyu 22:37-39) Timawaphunzitsa nthawi zonse kuti azitha kufotokoza choonadi cha m’Baibulo ndiponso kuti azitha kuteteza chikhulupiriro chawo chimene chikukula kumenecho. Akayenerera kugwira nawo ntchito yolalikira, timayenda nawo limodzi mu utumiki. Timachita zimenezi kuti aziona zimene tikuchita mu utumiki kuti nawonso azigwira ntchito imeneyi mwaluso. Ndipotu munthu akabatizidwa sitiyenera kusiya kumuphunzitsa. Anthu amene angobatizidwa kumene amafunika kuwaphunzitsabe zinthu zina zimene zingawathandize kuthana ndi mayesero amene angakumane nawo akamatsatira Khristu.​—Luka 9:23, 24.

“Ine Ndili Limodzi Ndi Inu Masiku Onse”

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchita mantha pamene tikugwira ntchito imene Yesu anatilamula? (b) N’chifukwa chiyani ino si nthawi yobwerera m’mbuyo, ndipo tiyenera kutsimikiza ndi mtima wonse kuchita chiyani?

20 Mawu omalizira palamulo limene Yesu anapereka ndi olimbikitsa kwambiri. Iye anati: “Dziwani kuti ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mateyu 28:20) Yesu ankadziwa kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri. Iye ankadziwanso kuti otsatira ake adzatsutsidwa pogwira ntchito imeneyi. (Luka 21:12) Komabe palibe chifukwa chilichonse chochitira mantha. Mtsogoleri wathu sayembekezera kuti tizigwira ntchitoyi tokhatokha popanda wotithandiza. Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti amene ali ndi “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi” ali limodzi ndi ife ndipo akutithandiza kukwaniritsa ntchitoyi?

21 Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti adzakhala nawo mu utumiki wawo kwa zaka zonse “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Choncho tiyeni tipitirize kugwira ntchito imene Yesu anatisiyira mpaka mapeto afike. Ino si nthawi yobwerera m’mbuyo. Tili ndi ntchito yambiri yokolola mwauzimu ndipo anthu ambiri achidwi akusonkhanitsidwa. Monga otsatira a Khristu, tiyeni tiyesetse kugwira ntchito yofunika kwambiri imene tapatsidwa. Tiyeni titsimikize ndi mtima wonse kugwiritsira ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndiponso chuma chathu pomvera lamulo la Khristu lakuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga.”

a Pa nthawi ina mneneri Elisa anapereka malangizo ofanana ndi amenewa kwa Gehazi. Pamene ankatumiza mtumiki wakeyu kunyumba ya mayi wina amene mwana wake anamwalira, Elisa anamuuza kuti: “Ukakumana ndi munthu aliyense panjira usam’patse moni.” (2 Mafumu 4:29) Zimene anam’tumazo zinali zofunika kwambiri, choncho sanafunike kutaya nthawi.

b Yesu ataukitsidwa, anaonekera kwa “abale oposa 500.” (1 Akorinto 15:6) Popeza kuti pa nthawiyi otsatira ake ambiri anali ku Galileya, n’kutheka kuti imeneyi ndi nthawi yomwe yatchulidwa pa Mateyu 28:16-20. Choncho payenera kuti panali anthu ambiri pamene Yesu ankapereka lamulo loti otsatira akewo aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.