Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

Wokondedwa Wowerenga:

Yesu Khristu ananena kuti “ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Maliko 10:21) Ndi mawu amenewa, iye akutiitana kuti tizimutsatira. Kodi inuyo mukufuna kukhala wotsatira wake? Mukakhala wotsatira wa Yesu, moyo wanu udzasintha kwambiri. Chifukwa chiyani?

Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake monga dipo. (Yohane 3:16) Kuwonjezera pa kutifera, Mwana ameneyu anatisonyeza mmene tiyenera kukhalira. Pa chilichonse chimene ankachita, anasonyeza kuti anali wokhulupirika ndipo anasangalatsa mtima wa Atate wake. Yesu anatisonyezanso zimene tingachite kuti tizitsanzira Atate wake. Zonse zimene Mwanayu ankachita komanso kulankhula, zinasonyeza bwino kwambiri mmene Atate wake amaganizira ndiponso mmene amachitira zinthu.​—Yohane 14:9.

Baibulo limanena kuti Yesu ndi “chitsanzo” chathu ndipo tiyenera ‘kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri.’ (1 Petulo 2:21) Ngati tikufuna kuyandikira kwambiri Yehova, ngati tikufuna kuti panopa tizisangalala komanso ngati tikufuna kupitiriza kuyenda m’njira ya kumoyo wosatha, tiyenera kutsatira mapazi a Khristu mosamala kwambiri.

Kuti tiyambe kumutsatira, tiyenera kudziwa bwino zimene Yesu anachita ali padziko lapansi. Choncho tiyenera kuphunzira mozama nkhani za moyo wa Yesu zimene zili m’Baibulo. Chinanso chimene chingatithandize kuti tizitsatira Yesu mosamala kwambiri ndi kuganizira zimene iye ankalankhula ndiponso kuchita. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizimutsanzira.

Tikukhulupirira kuti bukuli likuthandizani kuti muyambe kukonda kwambiri Yesu ndiponso Yehova. Ndipo chikondi chimenecho chikuthandizani kuti muzitsatira Yesu mosamala kwambiri n’cholinga choti muzisangalatsa mtima wa Yehova panopa mpaka m’tsogolo.

Ofalitsa