Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 25

“Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”

“Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”

1, 2. (a) Kodi mayi amachita chiyani mwachibadwa mwana wake akayamba kulira? (b) Kodi ndi ndani amene amasonyeza chifundo kwambiri kuposa mayi?

 MWANA wakhanda akulira pakati pa usiku. Nthawi yomweyo mayi ake akudzuka. Kungoyambira pamene mwana wake anabadwa, mayiyu sagona kwambiri ngati mmene ankagonera poyamba. Anaphunzira kusiyanitsa kaliridwe kosiyanasiyana ka mwana wakeyo. Choncho nthawi zambiri amadziwa ngati mwanayo akufuna kuyamwa, kunyamulidwa kapena kumusamalira mwa njira ina. Kaya mwanayo akulira chiyani, mayi akewo amachitapo kanthu. Chifukwa choti amamukonda kwambiri, sanganyalanyaze zimene mwanayo akufuna.

2 Anthu ambiri amadziwa kuti mayi amakhala wachifundo kwambiri kwa mwana wake. Komabe, Mulungu wathu Yehova ndi amene amasonyeza kwambiri khalidwe la chifundo. Kuphunzira zokhudza khalidwe labwinoli kungatithandize kuti tiyandikire kwambiri Yehova. Choncho tiyeni tikambirane zimene chifundo chimatanthauza ndiponso mmene Mulungu wathu amachisonyezera.

Kodi Chifundo N’chiyani?

3. Kodi mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “kusonyeza chifundo” kapena “kumvera wina chisoni” amatanthauza chiyani?

3 M’Baibulo, mawu akuti chifundo amafanana ndi akuti chisoni. Mawu angapo a Chiheberi ndiponso Chigiriki amanena za kukhala ndi chifundo chachikulu. Mwachitsanzo, taganizirani za mawu a Chiheberi akuti ra·chamʹ, omwe nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “kusonyeza chifundo” kapena “kumvera wina chisoni.” Buku lina limafotokoza kuti mawu akuti ra·chamʹ “amanena za kumva chisoni kwambiri ngati chimene munthu amamva akaona munthu wina amene amamukonda akuvutika kapena akufunika kumuthandiza.” Mawu a Chiheberiwa, omwe Yehova amawagwiritsa ntchito ponena za iyeyo, amafanana ndi mawu otanthauza “chiberekero” ndipo angamasuliridwenso kuti “chifundo cha mayi.” a​—Ekisodo 33:19; Yeremiya 33:26.

“Kodi mayi angaiwale . . . mwana wochokera m’mimba mwake?”

4, 5. Kodi Baibulo limagwiritsa ntchito bwanji chifundo chimene mayi amasonyeza mwana wake potiphunzitsa za chifundo cha Yehova?

4 Baibulo limagwiritsa ntchito mfundo yoti mayi amasonyeza mwana wake chifundo, pofuna kutiphunzitsa tanthauzo la chifundo cha Yehova. Lemba la Yesaya 49:15 limati: “Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa kapena kulephera kuchitira chifundo [ra·chamʹ] mwana wochokera m’mimba mwake? Ngakhale amayi amenewa ataiwala, ine sindingakuiwale.” Lemba limeneli likusonyeza kuti Yehova amasonyeza anthu ake chifundo chachikulu. Kodi amachita bwanji zimenezi?

5 N’zovuta kuganiza kuti mayi angaiwale kuyamwitsa kapena kusamalira mwana wake wakhanda. Ndipotu mwana wakhanda sangathe kudzisamalira yekha, nthawi zonse amafunika kuti mayi ake azimusamalira komanso kumukonda. Koma n’zomvetsa chisoni kuti azimayi ambiri sasamalira ana awo, makamaka ‘m’nthawi yapadera komanso yovuta’ ino pomwe anthu ambiri ‘sakonda achibale awo.’ (2 Timoteyo 3:1, 3) Koma Yehova akutiuza kuti: “Ine sindingakuiwale.” Yehova sasiya kusonyeza atumiki ake chifundo. Chifundo chake n’chachikulu kwambiri kuposa chimene mayi mwachibadwa amasonyeza mwana wake. Choncho n’zosadabwitsa kuti munthu wina ponena za lemba la Yesaya 49:15 anati: “Amenewa ndi amodzi mwa mawu amphamvu kwambiri, mwinanso tingati ndiye amphamvu kwambiri pa mawu onse onena za chikondi cha Mulungu m’Chipangano Chakale.”

6. Kodi nthawi zambiri anthu omwe si angwiro amaona kuti munthu wachifundo ndi wotani, koma kodi Yehova amatitsimikizira chiyani?

6 Kodi munthu akakhala wachifundo ndiye kuti ndi wofooka? Nthawi zambiri anthu omwe si angwiro amaganiza choncho. Mwachitsanzo, ku Roma kunali katswiri wina wa nzeru za anthu amenenso anali wotchuka dzina lake Seneca. Iyeyu anakhala ndi moyo pa nthawi imene Yesu anali padzikoli, ndipo ankaphunzitsa kuti “munthu akamamvera ena chisoni amasonyeza kuti ndi wofooka maganizo.” Seneca ankalimbikitsa chiphunzitso chakuti, kuti munthu akhale ndi moyo wabwino, azipewa kumva kuwawa, kumva chisoni ndiponso kukhala wosangalala. Iye ankati munthu wanzeru akhoza kuthandiza anthu amene akuvutika, koma iyeyo asamawamvere chisoni chifukwa kumva chisoni kungamuchititse kuti asakhale ndi mtendere wamumtima. Maganizo odzikondawa sankathandiza anthu kuti azisonyeza chifundo mochokera pansi pa mtima. Koma si mmene Yehova alili. M’Mawu ake, iye amatitsimikizira kuti “ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.” (Yakobo 5:11) Monga mmene tionere, kukhala wachifundo si kufooka, koma ndi khalidwe lofunika kwambiri. Tiyeni tione mmene Yehova, yemwe ndi kholo lachikondi, amasonyezera khalidweli.

Yehova Anachitira Chifundo Mtundu wa Aisiraeli

7, 8. Kodi Aisiraeli anavutika bwanji ku Iguputo, nanga Yehova anawathandiza bwanji?

7 Zimene Yehova ankachitira Aisiraeli zimatithandiza kumvetsa bwino chifundo chake. Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1500 B.C.E., Aisiraeli mamiliyoni anali akapolo ku Iguputo komwe ankazunzidwa kwambiri. Aiguputo “anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa, yomwe inali yoponda matope ndi kuumba njerwa. Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse.” (Ekisodo 1:11, 14) Chifukwa chovutika chonchi, Aisiraeli ankachonderera Yehova kuti awathandize. Kodi Mulungu yemwe ndi wachifundo anachita chiyani?

8 Yehova zinamukhudza mtima kwambiri. Iye anati: “Ndaona mmene anthu anga amene ali ku Iguputo akuvutikira, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Ndikudziwa bwino ululu umene akumva.” (Ekisodo 3:7) Sikuti Yehova ankangoona kapena kumva anthu ake akuvutika koma ankawamveranso chisoni. M’Mutu 24 wa bukuli, tinaona kuti Yehova ndi Mulungu amene amamvera ena chisoni. Ndipotu chisoni, chomwe chimatanthauza kumva ululu womwe munthu wina akumva, n’chogwirizana ndi chifundo. Yehova sanangomvera chisoni anthu ake koma anawathandizanso. Lemba la Yesaya 63:9 limati: “Iye anawawombola chifukwa cha chikondi komanso chifundo chake.” Yehova anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo ndi “dzanja lamphamvu.” (Deuteronomo 4:34) Kenako ankawapatsa chakudya modabwitsa ndiponso anawapatsa Dziko Lolonjezedwa.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ankapulumutsa Aisiraeli mobwerezabwereza m’Dziko Lolonjezedwa? (b) M’nthawi ya Yefita, kodi Yehova anapulumutsa Aisiraeli pamene ankaponderezedwa ndi ndani, ndipo n’chiyani chinamuchititsa zimenezi?

9 Yehova anapitirizabe kuwasonyeza chifundo. Atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa, Aisiraeli ankachita zinthu zosakhulupirika mobwerezabwereza, zomwe zinkachititsa kuti azikumana ndi mavuto. Koma akazindikira kulakwa kwawo, ankalapa n’kupempha Yehova kuti awathandize. Iye ankawapulumutsa mobwerezabwereza. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? “Chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo.”​—2 Mbiri 36:15; Oweruza 2:11-16.

10 Taganizirani zomwe zinachitika m’nthawi ya Yefita. Aisiraeli atayamba kulambira mafano, Yehova analola kuti Aamoni awapondereze kwa zaka 18. Koma kenako Aisiraeli analapa. Baibulo limatiuza kuti: “Iwo anachotsa milungu yonse yachilendo imene anali nayo ndipo anayamba kutumikira Yehova, moti iye sanalole kuti Aisiraeli apitirize kuvutika.” (Oweruza 10:6-16) Anthu ake atalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova sanalole kuti azingowaona akuvutika. Choncho Mulungu wachifundo chachikuluyu, anagwiritsa ntchito Yefita kuti apulumutse Aisiraeli kwa adani awo.​—Oweruza 11:30-33.

11. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza chifundo tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli?

11 Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza chifundo tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli? Mfundo imodzi yofunika kwambiri imene tikuphunzira ndi yakuti chifundo sichitanthauza kungodziwa mavuto amene ena akukumana nawo n’kumawamvera chisoni. Taganiziraninso chitsanzo cha mayi amene chifundo chake chimamuchititsa kuti athandize mwana wake yemwe akulira. Mofanana ndi zimenezi, Yehova akamva anthu ake akumupempha kuti awathandize pamavuto awo, chifundo chimamuchititsa kuti amve pemphero lawo n’kuwathandiza. Timaphunziranso kuti munthu amene amasonyeza chifundo si wofooka, chifukwa chifundo chinachititsa Yehova kumenya nkhondo kuti apulumutse Aisiraeli. Koma kodi Yehova amangochitira chifundo atumiki ake monga gulu?

Yehova Amachitira Chifundo Munthu Aliyense Payekha

12. Kodi Chilamulo chinkasonyeza bwanji kuti Yehova amachitira chifundo munthu aliyense payekha?

12 Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli chinasonyeza kuti iye amachitira chifundo munthu aliyense payekha. Mwachitsanzo, taganizirani mmene anasonyezera kuti ankaganizira anthu osauka. Yehova ankadziwa kuti pakhoza kuchitika zinthu zosayembekezereka zomwe zikanachititsa kuti munthu wina wa Chiisiraeli akhale pa umphawi. Ndiye kodi Aisiraeli ankayenera kumachita bwanji zinthu ndi munthu wosauka? Yehova anawalamula mwamphamvu kuti: “Muzimupatsa mowolowa manja zimene akufunazo, ndipo musamamupatse zinthuzo monyinyirika. Mukamachita zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita ndi ntchito zanu zonse.” (Deuteronomo 15:7, 10) Yehova analamulanso Aisiraeli kuti asamakolole m’mbali mwa minda yawo kapenanso kukatenga mbewu zomwe zatsala kumunda. Anthu ovutika ndi amene ankayenera kutenga zimenezo. (Levitiko 23:22; Rute 2:2-7) Aisiraeli akamatsatira lamulo limeneli, lomwe linkathandiza osauka, anthu osaukawo sankapemphetsa chakudya. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yehova ndi wachifundo chachikulu?

13, 14. (a) Kodi mawu a Davide amatitsimikizira bwanji kuti Yehova amadera nkhawa kwambiri munthu aliyense pa yekha? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amakhala pafupi ndi “anthu a mtima wosweka” kapena “amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo”?

13 Masiku anonso, Mulungu wathu wachikondi amadera nkhawa kwambiri munthu aliyense payekha. Sitikayikira kuti amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo. Wolemba masalimo Davide analemba kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo. Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.” (Salimo 34:15, 18) Ponena za anthu amene afotokozedwa palembali, katswiri wina wa Baibulo ananena kuti “ndi anthu amene afooka chifukwa chodziona kuti ndi ochimwa komanso achabechabe.” Anthu oterewa akhoza kumaona kuti Yehova ali nawo kutali kwambiri komanso ndi anthu osafunika moti sawawerengera. Koma zimenezi si zoona. Mawu a Davidewa amatitsimikizira kuti Yehova sasiya anthu amene ‘amadziona kuti ndi achabechabe.’ Mulungu wathu wachifundo amadziwa kuti pa nthawi ngati imeneyi m’pamene timafunikira kwambiri kuti atithandize ndipo amakhala nafe pafupi.

14 Taganizirani zomwe zinachitika ku United States. Mayi wina anathamangira kuchipatala ndi mwana wake wazaka ziwiri yemwe ankabanika. Atamuyeza, madokotala anauza mayi akewo kuti ayenera kumugoneka m’chipatalamo. Ndiye kodi mayiyo anagona kuti usiku umenewo? Anagona m’chipinda chomwe anagoneka mwanayo pampando womwe unali pafupi ndi bedi lake. Mwana wakeyo ankadwala choncho ankafunika kukhala naye pafupi. Zimene anachitazi zinangosonyeza chifundo chimene Yehova ali nacho. Pajatu tinapangidwa m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Choncho n’zosakayikitsa kuti Atate wathu wakumwamba angatichitire zambiri kuposa pamenepa. Mawu olimbikitsa a pa Salimo 34:18 amatiuza kuti pamene ‘tasweka mtima’ kapena ‘kudzimvera chisoni,’ Yehova yemwe ndi kholo lachikondi amakhala nafe “pafupi.” Izi zikutanthauza kuti nthawi zonse amatisonyeza chifundo ndipo amakhala wokonzeka kutithandiza.

15. Kodi Yehova amathandiza bwanji aliyense payekhapayekha?

15 Kodi Yehova amatithandiza bwanji aliyense payekhapayekha? Si nthawi zonse pamene amachotsa zomwe zikuyambitsa mavuto athu. Koma pali zinthu zambiri zimene wapereka kuti zizithandiza amene akumupempha kuti awathandize. Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, lili ndi malangizo amene angatithandize kupirira mavuto alionse. Yehova watipatsanso akulu mumpingo omwe amayesetsa kutsanzira chifundo chake akamatithandiza. (Yakobo 5:14, 15) Monga “Wakumva pemphero,” iye amapereka “mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Salimo 65:2; Luka 11:13) Mzimu umenewo ungatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tizipirira mpaka pamene Ufumu wa Mulungu udzachotse mavuto onse. (2 Akorinto 4:7) Timathokoza kwambiri Yehova chifukwa watipatsa zonsezi kuti zitithandize. Ndipo tisamaiwale kuti zinthu zimenezi zimasonyeza kuti iye ndi wachifundo chachikulu.

16. Kodi ndi njira yaikulu kwambiri iti imene Yehova anatisonyezera chifundo chake, ndipo aliyense ayenera kukumbukira chiyani?

16 Komabe, njira yaikulu kwambiri imene Yehova anatisonyezera chifundo chake ndi kupereka Mwana wake kuti akhale dipo lotiwombola. Chifukwa chotikonda, Yehova anapereka nsembe imeneyi kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa. Muzikumbukira kuti dipo limeneli linaperekedwa kwa aliyense payekha. M’pake kuti Zekariya, yemwe anali bambo a Yohane M’batizi, ananeneratu kuti mphatso imeneyi idzasonyeza bwino “chifundo chachikulu cha Mulungu wathu.”​—Luka 1:78.

Nthawi Imene Yehova Angasiye Kusonyeza Chifundo

17-19. (a) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amafika posiya kuchitira anthu chifundo? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anasiya kuchitira chifundo anthu ake?

17 Kodi tiyenera kumaganiza kuti chifundo cha Yehova n’chopanda malire? Ayi, chifukwa Baibulo limasonyeza bwino kuti anthu amene amapitiriza kuchita zoipa, iye amasiya kuwachitira chifundo. (Aheberi 10:28) Kuti timvetse chifukwa chake, tiyeni tiganizirenso zimene Aisiraeli ankachita.

18 Ngakhale kuti Yehova ankapulumutsa Aisiraeli mobwerezabwereza, m’kupita kwanthawi anasiya kuwachitira chifundo. Anthu amenewa anapitiriza kulambira mafano moti mpaka anafika potenga mafano awo onyansawo n’kuwaika m’kachisi wa Yehova. (Ezekieli 5:11; 8:17, 18) Baibulo limatiuzanso kuti: “Iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona, kunyoza mawu ake ndiponso kuseka aneneri ake. Anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri n’kuwalanga.” (2 Mbiri 36:16) Aisiraeli anafika poipa kwambiri moti sizinali zoyenera kuti Yehova awachitire chifundo. Zochita zawo zinamukwiyitsa kwambiri. Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani?

19 Yehova anasiya kuchitira chifundo anthu ake. Iye ananena kuti: “Sindidzawakomera mtima, kuwamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo. Palibe chimene chidzandilepheretse kuti ndiwawononge.” (Yeremiya 13:14) Choncho mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi zinawonongedwa, ndipo Aisiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Zimakhala zomvetsa chisoni kwambiri anthu akasiya kumvera Yehova mpaka kufika poti sizingathekenso kuwachitira chifundo.​—Maliro 2:21.

20, 21. (a) Kodi chidzachitike n’chiyani Mulungu akadzaona kuti wasonyeza chifundo mokwanira? (b) Nanga ndi njira ina iti imene Yehova amasonyezera chifundo yomwe tidzakambirane m’mutu wotsatira?

20 Nanga bwanji masiku ano? Yehova sanasinthe. Chifukwa cha chifundo, iye wauza Mboni zake kuti zilalikire ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Anthu a mtima wabwino akamvetsera, Yehova amawathandiza kumvetsa uthengawo. (Machitidwe 16:14) Koma sikuti ntchito yolalikira idzagwiridwa mpaka kalekale. Yehova sangakhale kuti akusonyeza chifundo ngati atalola kuti dziko loipali limodzi ndi mavuto ake onse zipitirire mpaka kalekale. Akadzafika poona kuti wasonyeza chifundo mokwanira, adzapereka chiweruzo. Ndipo akamadzachita zimenezi, adzakhalanso kuti akuchitira chifundo atumiki ake okhulupirika komanso adzaonetsetsa kuti ‘dzina lake loyera’ lalemekezedwa. (Ezekieli 36:20-23) Yehova adzachotsa zoipa zonse ndipo adzabweretsa dziko latsopano lolungama. Koma ponena za anthu oipa, iye anati: “Diso langa silimva chisoni ndipo sindiwasonyeza chifundo. Ndiwabwezera mogwirizana ndi zochita zawo.”​—Ezekieli 9:10.

21 Komabe, panopa Yehova akupitiriza kusonyeza chifundo ngakhale kwa anthu amene akhoza kudzawonongedwa. Anthu ochimwa amene alapa mochokera pansi pa mtima, Yehova akhoza kuwasonyeza chifundo m’njira ina yaikulu. Iye akhoza kuwakhululukira machimo. M’mutu wotsatira, tidzakambirana mawu ena ochititsa chidwi amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofuna kutithandiza kumvetsa kuti Yehova amakhululuka ndi mtima wonse.

a Komabe n’zochititsa chidwi kuti pa Salimo 103:13, mawu a Chiheberi akuti ra·chamʹ amanena za chifundo chimene bambo amasonyeza ana ake.