Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 29

“Mudziwe Chikondi cha Khristu”

“Mudziwe Chikondi cha Khristu”

1-3. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa Yesu kuti azifuna kutsanzira Atate ake? (b) Kodi tikambirana njira zitatu ziti zimene Yesu anasonyezera chikondi?

 KODI munaonapo kamnyamata kakuyesera kukhala ngati bambo ake? Mwanayo angatsanzire mmene bambowo amayendera, amalankhulira komanso mmene amachitira zinthu. Akamakula, angatengerenso makhalidwe abwino a bambo akewo ndiponso zimene amakhulupirira. Chifukwa choti mnyamatayo amakonda bambo ake komanso amawalemekeza, amafuna atakhala ngati iwowo.

2 Nanga bwanji za Yesu ndi Atate ake akumwamba? Pa nthawi ina iye anati: “Ndimakonda Atate.” (Yohane 14:31) Palibe aliyense amene angakonde Yehova kwambiri kuposa Mwanayu, yemwe anakhala naye kwa zaka zambiri zinthu zina zonse zisanakhalepo. Chikondi chimenecho chinachititsa Mwana wokhulupirikayu kuti azifuna kukhala ngati Atate ake.​—Yohane 14:9.

3 Mitu yoyambirira ya bukuli yafotokoza mmene Yesu anatsanzirira mphamvu, chilungamo ndiponso nzeru za Yehova. Nanga anasonyeza bwanji kuti amatsanzira chikondi cha Yehova? Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Yesu anasonyezera chikondi, zomwe ndi mtima wodzipereka, chifundo chake chachikulu ndiponso mtima wokhululuka.

Anasonyeza “Chikondi Chachikulu”

4. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chikondi chachikulu kuposa chimene munthu aliyense anasonyezapo?

4 Yesu anapereka chitsanzo chapadera kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Kuti munthu asonyeze chikondi chimenechi amafunika kukhala wosadzikonda n’kuika patsogolo zofuna za ena osati zake. Ndiye kodi anachita bwanji zimenezi? Iye anafotokoza kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.” (Yohane 15:13) Mofunitsitsa Yesu anapereka moyo wake wangwiro chifukwa cha ife. Chimenechi chinali chikondi chachikulu kwambiri kuposa chimene munthu aliyense anasonyezapo. Komabe Yesu anasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena m’njira zinanso.

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mwana wa Mulungu anasonyeza chikondi pamene analolera kubwera padzikoli?

5 Mwana wobadwa yekha wa Mulungu asanakhale munthu padzikoli, anali ndi udindo wapadera komanso waukulu kumwamba. Ankagwirizana kwambiri ndi Yehova komanso angelo ambirimbiri. Ngakhale kuti anali ndi mwayi waukulu chonchi, Mwana wokondedwayu “anasiya zonse zimene anali nazo nʼkukhala ngati kapolo ndipo anakhala munthu.” (Afilipi 2:7) Mofunitsitsa, iye anabwera kudzakhala limodzi ndi anthu ochimwa m’dzikoli, lomwe “lili mʼmanja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Pamenepatu Mwana wa Mulungu anasonyeza chikondi chachikulu pololera kusiya zinthu zambiri.

6, 7. (a) Pamene ankachita utumiki wake padzikoli, kodi Yesu anasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena m’njira ziti? (b) Kodi ndi chitsanzo chabwino kwambiri chiti chokhudza chikondi chololera kuvutikira ena chomwe chili pa Yohane 19:25-27?

6 Pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padzikoli, Yesu ankasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Iye sankachita zinthu modzikonda. Maganizo ake onse anali pa utumiki wake moti sankalakalaka zinthu zapamwamba zimene anthu ambiri amafuna atakhala nazo. Iye anati: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zamumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti nʼkutsamiritsa mutu wake.” (Mateyu 8:20) Popeza Yesu anali kalipentala waluso, akanatha kusiya kaye ntchito yolalikira n’kumanga nyumba yabwino yoti azikhalamo kapena kupanga zinthu zokongola zamatabwa n’kugulitsa kuti apeze ndalama. Koma iye sanagwiritse ntchito luso lake kuti akhale ndi katundu wambiri.

7 Chitsanzo chabwino kwambiri cha chikondi cha Yesu chololera kuvutikira ena chili pa Yohane 19:25-27. Taganizani zinthu zambirimbiri zimene zinkayenda m’mutu mwa Yesu masana a tsiku limene anaphedwa. Pamene ankavutika pamtengo wozunzikirapo, ankadera nkhawa ophunzira ake, ntchito yolalikira ndiponso makamaka mmene kukhulupirika kwake kukanathandizira kuti dzina la Atate ake lilemekezedwe. Tsogolo lonse la anthu linkadalira pa zimene iye akanachita. Komatu atatsala pang’ono kufa, Yesu anasonyeza kuti ankadera nkhawa amayi ake, Mariya, omwe pa nthawiyi ayenera kuti anali amasiye. Yesu anapempha mtumwi Yohane kuti azisamalira Mariya ngati mayi ake enieni ndipo kenako Yohaneyo anatenga Mariya n’kupita naye kunyumba kwake. Choncho Yesu anakonza zoti amayi ake azipeza zofunika pa moyo komanso zowathandiza pa ubwenzi wawo ndi Yehova. Apatu Yesu anasonyeza chikondi chachikulu.

“Anawamvera Chisoni”

8. Kodi mawu a Chigiriki amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofotokoza chifundo cha Yesu amatanthauza chiyani?

8 Mofanana ndi Atate ake, Yesu anali wachifundo. Malemba amanena kuti Yesu zinkamukhudza akaona anthu akuvutika ndipo ankayesetsa kuwathandiza. Pofotokoza chifundo cha Yesu, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “anawamvera chisoni.” Katswiri wina wa Baibulo anati ‘mawuwa amanena za munthu amene wakhudzidwa kwambiri ndi zinazake n’kuchita zinthu kuchokera pansi pa mtima. Amenewa ndi mawu a Chigiriki amphamvu kwambiri onena za chifundo.’ Tiyeni tione zochitika zina zomwe zinachititsa Yesu kugwidwa chifundo kwambiri n’kuchitapo kanthu.

9, 10. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Yesu ndi atumwi ake afune kukhala kwaokha? (b) Pamene anthu anawalepheretsa kukhala kwaokha, kodi Yesu anatani, ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Anathandiza anthu kuphunzira za Mulungu. Nkhani yopezeka pa Maliko 6:30-34 imasonyeza chifukwa chachikulu chimene chinachititsa Yesu kuti asonyeze chifundo. Taganizirani zimene zinachitika. Atumwi anali osangalala chifukwa anali atangomaliza kulalikira m’madera ambiri. Anabwerera kwa Yesu n’kumufotokozera zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo. Koma panabwera anthu ambiri moti Yesu ndi atumwi ake sanapeze nthawi yoti adye. Popeza nthawi zonse ankachita chidwi ndi atumwiwo, Yesu anazindikira kuti atopa. Choncho anawauza kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mukapume pangʼono.” Kenako anakwera ngalawa ndipo ankawoloka Nyanja ya Galileya n’kumalowera chakumpoto kuti akapeze malo opanda anthu. Koma gulu la anthu lija linaona kuti akuchoka. Enanso anamva za nkhaniyi. Anthu onsewa anathamangira kumene Yesu ndi atumwi ake ankapita ndipo iwowo ndi amene anayamba kukafika.

10 Kodi Yesu anakhumudwa chifukwa choti anthuwa anawalepheretsa kukhala kwaokha? Ayi ndithu. Zinamukhudza kwambiri ataona kuti anthuwa, omwe analipo masauzande ambiri, akumudikira. Maliko analemba kuti ‘ataona gulu lalikulu la anthu anawamvera chisoni, chifukwa anali ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa. Ndiye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.’ Yesu anaona kuti ankafunika kuwathandiza mwauzimu. Anali ngati nkhosa zosochera zopanda m’busa woziyang’anira. Yesu ankadziwa kuti atsogoleri achipembedzo ouma mtima, amene ankayenera kukhala abusa abwino, sankakonda komanso kusamalira anthuwo. (Yohane 7:47-49) Anawamvera chisoni moti anayamba kuwaphunzitsa “za Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:11) Kodi mwaona kuti Yesu anawamvera chisoni asanaone n’komwe zimene anthuwo achite akawaphunzitsa? M’mawu ena tinganene kuti, sikuti Yesu anagwidwa chifundo ataona kuti anthuwo akumvetsera zimene ankawaphunzitsa, koma chifundo n’chimene chinamuchititsa kuti awaphunzitse.

“Anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza”

11, 12. (a) Kodi kale anthu akhate ankawaona bwanji, koma Yesu anachita chiyani atakumana ndi munthu wina “wakhate thupi lonse”? (b) Kodi wakhate amene Yesu anamukhudza ayenera kuti anamva bwanji, nanga zimene zinachitikira dokotala wina zikutithandiza bwanji kumvetsa zimenezi?

11 Anathandiza wodwala. Anthu odwala matenda osiyanasiyana ankadziwa kuti Yesu ndi wachifundo, choncho ankapita kwa iye kuti akawathandize. Umboni wa zimenezi ndi zomwe zinachitika pamene munthu wina “wakhate thupi lonse” anafika kwa Yesu, Yesuyo ali ndi gulu la anthu lomwe linkamutsatira. (Luka 5:12) Kale, anthu akhate ankawaika kwaokha kuti asapatsire ena. (Numeri 5:1-4) Koma patapita nthawi, atsogoleri ena omwenso anali Arabi, ankachititsa kuti anthu asamachitire chifundo akhate ndipo anapanga malamulo awoawo opondereza. a Koma taonani zimene Yesu anachitira wakhate uja. Baibulo limati: “Munthu wina wakhate anafika kwa iye ndipo anagwada pansi nʼkumuchonderera kuti: ‘Ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.’ Yesu atamva zimenezo, anagwidwa chifundo moti anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo anamuuza kuti: ‘Inde ndikufuna. Khala woyera.’ Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.” (Maliko 1:40-42) Yesu ankadziwa kuti zinali zosaloledwa kuti wakhateyo apezeke pagulupo. Komatu m’malo momuuza kuti achoke, anamva chisoni kwambiri moti anachita zinthu zimene anthu sankayembekezera. Iye anakhudza wakhateyo.

12 Kodi mukuganiza kuti wakhateyo anamva bwanji Yesu atamukhudza? Taganizirani chitsanzo ichi. Dokotala wina wa anthu akhate, dzina lake Paul Brand, anafotokoza za mnyamata wina wakhate amene anamuchiritsa ku India. Pamene ankamuyeza, dokotalayo anagwira phewa la wodwalayo. Kenako kudzera mwa munthu wina womasulira, anamufotokozera mankhwala amene ankafunika kulandira. Mwadzidzidzi, wodwalayo anayamba kulira. Dokotalayo anafunsa kuti: “Kodi ndalankhula zinazake zolakwika?” Womasulirayo anafunsa mnyamatayo m’chilankhulo chake, ndiyeno anayankha dokotalayo kuti: “Ayi adokotala. Akuti akulira chifukwa choti mwamugwira paphewa. Akuti patha zaka zambiri munthu aliyense asanamugwireko.” Choncho kwa wakhate amene anakumana ndi Yesu uja, kumukhudza kunatanthauza zambiri. Atangokhudzidwa kamodzi kokhako, matenda amene ankachititsa kuti anthu azimusala, anatheratu.

13, 14. (a) Kodi Yesu atatsala pang’ono kulowa mumzinda wa Nayini anakumana ndi anthu akupita kuti, nanga n’chiyani chinachititsa kuti zimenezi zikhale zomvetsa chisoni kwambiri? (b) Popeza Yesu anali wachifundo, kodi anathandiza bwanji mayi wamasiye wa ku Nayini?

13 Anathandiza anthu omwe anali ndi chisoni. Yesu zinkamukhudza kwambiri akaona anthu ali ndi chisoni chifukwa choti aferedwa. Mwachitsanzo, taganizirani nkhani yopezeka pa Luka 7:11-15. Inachitika Yesu atatsala pang’ono kufika mumzinda wina wa ku Galileya wotchedwa Nayini, chapakatikati pa utumiki wake. Atafika pafupi ndi geti la mzindawo, anakumana ndi anthu akukaika maliro. Koma maliro ake anali omvetsa chisoni kwambiri. Womwalirayo anali mnyamata yemwe anali mwana yekhayo wa mayi wina wamasiye. N’kutheka kuti pa nthawi ina, mayiyu analinso ndi anthu atanyamula maliro a mwamuna wake kupita kumanda. Koma pa nthawi imene anakumana ndi Yesuyi n’kuti akukaika maliro a mwana wake, yemwe n’kutheka kuti anali munthu yekhayo amene ankamuthandiza. Mwina pagululo panalinso anthu ena amene ankaimba nyimbo zapamaliro. (Yeremiya 9:17, 18; Mateyu 9:23) Komabe, Yesu ankayang’anitsitsa mayi woferedwayo yemwe mosakayikira anali ndi chisoni chachikulu ndipo ankayenda pafupi ndi chithatha chimene ananyamulirapo malirowo.

14 Yesu “anamvera chisoni” mayiyo. Kenako anamulimbikitsa ndi mawu akuti: “Tontholani mayi.” Ngakhale kuti palibe amene anamupempha, Yesu anapita pafupi ndi chithathacho n’kuchigwira. Anthu amene ananyamula chithathacho anaima, ndipo mwina gulu lonselo linaimanso. Kenako Yesu analankhula mwamphamvu kwa mnyamata womwalirayo kuti: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, dzuka!” Zitatero, mnyamatayo “anadzuka nʼkuyamba kulankhula.” Ndipo zinangokhala ngati anagona tulo tofa nato ndiye amudzutsa. Kenako Baibulo limanena mawu olimbikitsa akuti: “Yesu anamupereka kwa mayi ake.”

15. (a) Kodi nkhani za m’Baibulo zofotokoza za Yesu kuti ankamvera ena chisoni zimasonyeza kuti pali kugwirizana kotani pakati pa chifundo ndi kuchitapo kanthu? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhaniyi?

15 Kodi nkhani zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Kodi mwaona kuti munkhani iliyonse chifundo chikuyendera limodzi ndi kuchitapo kanthu? Nthawi zonse Yesu akaona ena akuvutika ankawamvera chisoni, ndipo akatero ankawathandiza. Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji? Akhristufe, tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino ndiponso kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Chifukwa chachikulu chimene timachitira zimenezi ndi choti timakonda Mulungu. Komabe tizikumbukira kuti chifukwa china n’chakuti timamvera chisoni anthu. Tikamamvera chisoni anthu ngati mmene Yesu ankachitira, timayesetsa kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwauze uthenga wabwino. (Mateyu 22:37-39) Nanga bwanji za Akhristu anzathu amene akuvutika kapena amene ali ndi chisoni? Sitingachiritse anthu modabwitsa kapena kuukitsa akufa. Komabe, tingasonyeze chifundo poyesetsa kupeza njira zowathandizira komanso kuwatsimikizira kuti timawakonda.​—Aefeso 4:32.

“Atate, Akhululukireni”

16. Pamene Yesu anali pamtengo wozunzikirapo, kodi anasonyeza bwanji kuti anali wofunitsitsa kukhululuka?

16 Yesu anasonyezanso chikondi cha Atate ake m’njira ina yofunika kwambiri. Iye anali “wokonzeka kukhululuka.” (Salimo 86:5) Umboni wa zimenezi ndi zimene anachita pamene anali pamtengo wozunzikirapo. Kodi Yesu analankhula zotani ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kufa imfa yochititsa manyazi komanso ankamva ululu chifukwa choti anali atamukhoma ndi misomali? Kodi anapempha Yehova kuti alange amene ankamuphawo? Ayi. Ena mwa mawu omalizira amene Yesu analankhula, anali akuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.”​—Luka 23:34. b

17-19. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anakhululukira mtumwi Petulo ngakhale kuti anamukana katatu?

17 Mwina chitsanzo chogwira mtima chosonyeza kuti Yesu anali wokhululuka tingachione tikaganizira zimene anachitira mtumwi Petulo. N’zosakayikitsa kuti Petulo ankakonda kwambiri Yesu. Pa Nisani 14, usiku womaliza wa Yesu, Petulo anamuuza kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu limodzi kundende kapena kufa nanu limodzi.” Koma patangotha maola ochepa, Petulo anakana katatu kuti sankamudziwa Yesu. Baibulo limatiuza zimene zinachitika pamene Petulo ankamukana kachitatu. Limati: “Ambuye anacheuka nʼkuyangʼana Petulo.” Atazindikira kuti walakwitsa kwambiri, “Petulo anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.” Yesu atamwalira madzulo a tsikulo, mwina mtumwiyu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Ambuye anandikhululukira?’​—Luka 22:33, 61, 62.

18 Koma pasanapite nthawi yaitali anapeza yankho. Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16 m’mawa, ndipo zikuoneka kuti tsiku lomwelo anakumana ndi Petulo. (Luka 24:34; 1 Akorinto 15:4-8) N’chifukwa chiyani Yesu anaonetsetsa kuti akumane ndi mtumwiyu, yemwe anamukanitsitsa? N’kutheka kuti ankafuna kutsimikizira Petulo, yemwe anali atalapa, kuti ankamukondabe komanso ankamuonabe kuti ndi wofunika. Koma Yesu anachitanso zinthu zina kuti amutsimikizire kuti wamukhululukira.

19 Patapita nthawi, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake ku Nyanja ya Galileya. Pa nthawiyi, anafunsa Petulo katatu ngati ankamukonda (paja Petulo anakana Ambuye katatu). Atamufunsa kachitatu, Petulo anati: “Ambuye, inu mumadziwa zinthu zonse. Mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu, yemwe ankatha kudziwa za mumtima mwa munthu, ankadziwadi kuti Petulo amamukonda. Komabe iye anamupatsa mwayi wotsimikizira zimenezo. Kuwonjezera pamenepo, Yesu anamupatsanso ntchito yoti ‘azidyetsa’ komanso ‘kuweta’ “ana a nkhosa” ake. (Yohane 21:15-17) M’mbuyomo, Petulo anapatsidwa ntchito yolalikira. (Luka 5:10) Koma tsopano, posonyeza kuti ankamudalira kwambiri, Yesu anamupatsa udindo wina waukulu woti azidzasamalira otsatira a Khristu. Patapita nthawi yochepa, anamugwiritsanso ntchito m’njira yapadera pa ntchito imene ophunzira ankagwira. (Machitidwe 2:1-41) Petulo ayenera kuti anasangalala kwambiri atadziwa zoti Yesu anamukhululukira ndipo ankamudalirabe.

Kodi ‘Mumadziwa Chikondi cha Khristu’?

20, 21. Kodi tingatani kuti ‘tidziwe bwino chikondi cha Khristu’?

20 Kunena zoona, Mawu a Mulungu amafotokoza bwino chikondi cha Khristu. Koma kodi tiyenera kuchita chiyani podziwa kuti Yesu amatikonda? Baibulo limatiuza kuti ‘tidziwe chikondi cha Khristu chimene chimaposa kudziwa zinthu.’ (Aefeso 3:19) Monga taonera, nkhani za m’Mauthenga Abwino zonena za moyo wa Yesu ndiponso utumiki wake zimatiphunzitsa zambiri zokhudza chikondi cha Khristu. Komabe, ‘kudziwa bwino chikondi cha Khristu’ kumafuna zambiri osati kungophunzira nkhani zokhudza iyeyo zimene Baibulo limanena.

21 Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kudziwa” amatanthauza kuchidziwa chinthu “kuchokera pa zimene ukudziwa kale komanso zomwe wakumana nazo pa moyo.” Tikamasonyeza chikondi ngati mmene Yesu ankachitira, mwachitsanzo tikamadzipereka kuthandiza ena, kuwachitira chifundo komanso kukhululuka ndi mtima wonse, tidzadziwa maganizo a Khristu. Tikamachita zimenezi ‘timadziwa chikondi cha Khristu chimene chimaposa kudziwa zinthu.’ Ndipo tisaiwale kuti tikamayesetsa kutsanzira Khristu, timayandikira kwambiri Yehova Mulungu wathu wachikondi amenenso Yesuyo amamutsanzira.

a Malamulo a Arabi ankanena kuti munthu azitalikirana ndi wakhate pafupifupi mamita awiri. Ndipo ngati kukuwomba mphepo, wakhate ankafunika kutalikirana ndi anthu pafupifupi mamita 45. Buku lina limanena za Rabi wina yemwe ankabisala akaona akhate ndiponso wina amene ankawathamangitsa powagenda ndi miyala. (Midrash Rabbah) Choncho anthu akhate ankadziwa mmene zimapwetekera ukamakanidwa, kunyozedwa komanso kuona kuti anthu sakukufuna.

b M’mipukutu ina yakale, mulibe mawu oyambirirawa apalemba la Luka 23:34. Koma chifukwa chakuti mawuwa amapezeka m’mipukutu ina yambiri yodalirika, anaikidwa mu Baibulo la Dziko Latsopano komanso m’Mabaibulo ena ambiri. Yesu ayenera kuti ankanena za asilikali a Chiroma amene anamupachika. Iwo sankadziwa zimene ankachita chifukwa sankadziwa kuti Yesu anali ndani. Mwinanso Yesu ankaganizira za Ayuda omwe anapempha kuti iye aphedwe koma patapita nthawi anayamba kumukhulupirira. (Machitidwe 2:36-38) Koma atsogoleri achipembedzo amene anachititsa kuti Yesu aphedwe, anali ndi mlandu waukulu chifukwa ankadziwa zimene akuchita ndipo anachita zimenezo chifukwa chongodana naye. Ambiri mwa anthu amenewa sanakhululukidwe.​—Yohane 11:45-53.