MUTU 5
Mphamvu za Kulenga—“Amene Anapanga Kumwamba Komanso Dziko Lapansi”
1, 2. Kodi dzuwa limasonyeza bwanji kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kulenga zinthu mwadongosolo?
KODI chimachitika n’chiyani mukamawotha moto madzulo kukuzizira? Mwina mumakhala chapataliko kuti muzimva kutenthera bwino. Mukasendera pafupi kwambiri ndi motowo, mumamva kuwotcha. Mukasunthira kutali kwambiri, mumayamba kumva kuzizira.
2 Dzuwa tingaliyerekezere ndi “moto” umene umatithandiza kuti tizimva kutentha. Kuchokera padziko pano kukafika pamene pali dzuwa pali mtunda wa makilomita 150 miliyoni. a Ndiye kuti dzuwa ndi lamphamvu kwambiri chifukwa timamva kutentha kwake tili padziko pano ngakhale kuti lili kutali chonchi. Koma dziko lapansi limazungulira dzuwa ndipo lili pa mtunda wabwino kwambiri kuchokera pamene pali dzuwalo. Likanayandikira kwambiri, madzi onse padzikoli akanauma, ndipo likanatalikira kwambiri madzi onse akanaundana. Kuyandikira kwambiri kapena kutalikira kwambiri kukanachititsa kuti padzikoli pasakhale chamoyo chilichonse. Kuwala kwa dzuwa n’kofunika kwambiri kuti padziko lapansi pakhale zinthu zamoyo. Kumathandizanso kuti dzikoli likhale laukhondo komanso lokongola.—Mlaliki 11:7.
3. Kodi dzuwa limatiphunzitsa chiyani?
3 Komabe, anthu ambiri saganizira kwambiri kuti dzuwa ndi lofunika ngakhale kuti moyo wathu umadalira dzuwalo. Choncho sadziwa zimene dzuwa lingatiphunzitse. Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Munapanga kuwala komanso dzuwa.” (Salimo 74:16) Zoonadi, dzuwa limalemekeza Yehova “amene anapanga kumwamba komanso dziko lapansi.” (Salimo 19:1; 146:6) Dzuwa ndi chimodzi mwa zinthu zambirimbiri zakumwamba zimene zimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kulenga zinthu. Tiyeni tikambirane mozamirapo zinthu zina zakumwamba ndipo kenako tikambirana zokhudza dziko lapansi komanso zamoyo zimene zili padzikoli.
Yehova ‘anapanga kuwala komanso dzuwa’
“Kwezani Maso Anu Kumwamba Ndipo Muone”
4, 5. Kodi dzuwa lili ndi mphamvu zochuluka bwanji, nanga ndi lalikulu bwanji? Kodi dzuwa ndiye nyenyezi yaikulu kwambiri? Fotokozani.
4 Mwina mukudziwa kuti dzuwa lathuli ndi nyenyezi. Limaoneka lalikulu kuposa nyenyezi zomwe timaona usiku chifukwa lili pafupi kwambiri poyerekezera ndi nyenyezizo. Kodi dzuwa ndi lamphamvu bwanji? Pakatikati pake m’potentha pafupifupi madigiri seshasi 15 miliyoni. Mutatenga kachibenthu ka pakati pa dzuwa kangati njere ya therere lobala n’kukaika padziko lapansi pano, kuti musapse mungafunike kuima pa mtunda wa makilomita 140 kuchokera pamene mwakaikapo. Pa sekondi iliyonse, dzuwa limatulutsa mphamvu zofanana ndi zimene zimatuluka pakaphulika mabomba a nyukiliya mamiliyoni mahandiredi mahandiredi.
5 Dzuwa ndi lalikulu kwambiri moti mukhoza kulowa mapulaneti aakulu ngati dziko lapansili okwanira 1,300,000. Kodi ndiye kuti nyenyezi yaikulu kwambiri ndi dzuwa? Ayi, asayansi amanena kuti dzuwa ndi nyenyezi yaing’ono kwambiri poyerekeza ndi nyenyezi zina. Mtumwi Paulo analemba kuti “ulemerero wa nyenyezi ina, umasiyananso ndi wa nyenyezi ina.” (1 Akorinto 15:41) Mzimu woyera ndi umene unathandiza Paulo kuti alembe mawu oonawa. Pali nyenyezi ina yaikulu imene ataiika pamalo pamene pali dzuwa, dziko lapansili likhoza kukhala m’kati mwa nyenyeziyo. Palinso nyenyezi ina yaikulu kwambiri yomwe ataiika pamalo omwewo ikhoza kudutsa dziko lapansi n’kukafika kupulaneti yotchedwa Saturn. Pulaneti imeneyi ili kutali kwambiri ndi dziko lapansili. Moti chombo cha mumlengalenga chinatenga zaka 4 kuti chikafike papulaneti imeneyo, komatu chinkathamanga pa liwiro loposa kuwirikiza maulendo 40 liwiro la chipolopolo cha mfuti yamphamvu kwambiri.
6. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti nyenyezi n’zochuluka kwambiri?
6 Chochititsa chidwi kwambiri kuposa kukula kwa nyenyezi ndi kuchuluka kwake. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti nyenyezi zilipo zambirimbiri ngati “mchenga” wakunyanja moti n’zosatheka kuziwerenga. (Yeremiya 33:22) Mawu amenewa akusonyeza kuti nyenyezi zilipo zambiri kuposa zimene maso athu angaone popanda kugwiritsa ntchito chipangizo chilichonse. Wolemba Baibulo ngati Yeremiya akanayang’ana kumwamba usiku kuti awerenge nyenyezi, akanangowerenga 3,000 zokha kapena kuposerapo, chifukwa ndi zimene munthu angathe kuona usiku kopanda mitambo. Tingayerekeze nambala imeneyi ndi mchenga wongodzaza dzanja. Koma zoona zake n’zakuti nyenyezi ndi zambiri ngati mchenga wakunyanja. b Ndiye ndani angathe kuziwerenga?
7. Kodi mlalang’amba wa Milky Way uli ndi nyenyezi zingati, nanga pali milalang’amba ingati?
7 Lemba la Yesaya 40:26 limati: “Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone. Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi? Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwerenga. Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake.” Lemba la Salimo 147:4 limati: “Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi zonse.” Kodi “chiwerengero cha nyenyezi zonse” n’chochuluka bwanji? Limeneli ndi funso lovuta kuyankha. Asayansi amati mumlalang’amba wathu wokhawu, womwe amautchula kuti Milky Way, muli nyenyezi zoposa 100 biliyoni. c Ena amati mumlalang’ambawu muli nyenyezi zoposa pamenepa. Komatu umenewu ndi umodzi mwa milalang’amba yambirimbiri yomwe ilipo ndipo yambiri ili ndi nyenyezi zoposa pamenepa. Ndiye kodi milalang’amba ilipo ingati? Asayansi ena amati ilipo mabiliyoni mahandiredi mahandiredi, mwinanso mathiriliyoni. Pofika pano zaoneka kuti anthu sangathe kudziwa kuchuluka kwa milalang’amba, ngakhalenso chiwerengero chenicheni cha nyenyezi mabiliyoni zomwe zili mumilalang’ambayi. Komatu Yehova amadziwa chiwerengero chake. Ndiponso nyenyezi iliyonse amaipatsa dzina.
8. (a) Kodi mlalang’amba wa Milky Way ndi waukulu bwanji? (b) Kodi Yehova amalamulira bwanji zinthu zakumwamba?
8 Timagoma kwambiri tikaganizira kukula kwa milalang’amba. Anthu amati kuchokera mbali ina kukafika mbali ina ya mlalang’amba wa Milky Way kutalika kwake n’kofanana ndi mtunda umene kuwala kumayenda pa zaka 100,000. Kuwala kumayenda mothamanga kwambiri pa liwiro la makilomita 300,000 pa sekondi imodzi. Ndiyeno taganizirani, kuwala kungatenge zaka 100,000 kuti kuyende kuchoka mbali ina ya mlalang’amba wathuwu kukafika mbali ina. Ndipo milalang’amba ina ndi yaikulu kwambiri kuposa mlalang’amba wathuwu. Baibulo limati Yehova amatambasula “kumwamba” ngati mmene munthu angatambasulire nsalu. (Salimo 104:2) Komanso iye anakonza mmene nyenyezi ndiponso milalang’amba iyenera kuyendera. Kuyambira pa tinthu ting’onoting’ono mpaka milalang’amba ikuluikulu, chilichonse chimayenda mogwirizana ndi malamulo a m’chilengedwe amene Mulungu anakhazikitsa. (Yobu 38:31-33) Choncho akatswiri asayansi amati mmene zinthu zakumwamba zimayendera mwadongosolo n’zofanana ndi kuvina gule amene masitepe ake ndi ovuta kwambiri. Ndiyeno taganizani za amene analenga zinthu zimenezi. Kunena zoona, timasowa chonena tikaganizira mphamvu zochuluka kwambiri zotha kulenga zinthu zimene Mulungu ali nazo.
“Amene Anapanga Dziko Lapansi Pogwiritsa Ntchito Mphamvu Zake”
9, 10. Kodi n’chifukwa chiyani tinanganene kuti Yehova anaika dzikoli pamalo abwino kwambiri, nanga zimenezi zimatiuza chiyani zokhudza iyeyo?
9 Mphamvu za Yehova zotha kulenga zinthu zimaonekeranso bwino tikaganizira mmene analengera dziko lapansili. Analiika pamalo abwino kwambiri m’chilengedwe chachikuluchi. Asayansi ena amakhulupirira kuti mwina m’milalang’amba yambiri mulibe pulaneti lokhala ndi zamoyo ngati pulaneti lathuli. Zikuonekanso kuti mbali yaikulu ya mlalang’amba wa Milky Way sinakonzedwe kuti kuzikhala zamoyo. Pakatikati pa mlalang’ambawu ndi podzaza ndi nyenyezi, pamatuluka mpweya wambiri wapoizoni ndipo nthawi zambiri nyenyezi zimatsala pang’ono kuwombana. M’mbali mwa mlalang’ambawu mulibe zinthu zambiri zothandiza kuti moyo ukhalepo. Koma dzuwa komanso zinthu zonse zimene zimayenda molizungulira zinaikidwa pamalo abwino a pakati pa mbali ziwirizi.
10 Dziko lapansi limatetezedwa ndi pulaneti lina lotchedwa Jupita lomwe lili kutali komanso n’lalikulu kwambiri. Chifukwa chakuti ndi lalikulu maulendo oposa 1,000 kuposa dziko lapansi, pulaneti la Jupita limakoka zinthu mwamphamvu kwambiri. Limakoka zinthu zimene zikuyenda mumlengalenga kuti zizipita kumene kuli pulanetili. Ndiye kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Asayansi anapeza kuti zikanakhala kuti pulanetili palibe, zinthu zochokera mumlengalenga zomwe zimagwera padzikoli, bwenzi zikugwa mwamphamvu kwambiri kuwirikiza nthawi 10,000 poyerekeza ndi mmene zimagwera panopa. Komanso dziko lathuli lili ndi setilaiti yapadera kwambiri yomwe ndi mwezi. Mwezi umathandiza kuti padzikoli pazikongola komanso umatiunikira usiku. Koma kuwonjezera pamenepo umachititsanso kuti nthawi zonse dziko liziima mopendekeka pamalo amodzi. Kupendekeka kumeneku n’kumene kumachititsa kuti padzikoli pazikhala nyengo zodziwika bwino, chinthu china chofunika kwambiri kuti padzikoli pakhale zamoyo.
11. Kodi mpweya wamumlengalenga unakonzedwa bwanji kuti uzititeteza?
11 Mphamvu za Yehova zotha kulenga zinthu zimaonekeranso pa chilichonse chimene anapanga chokhudza dziko lapansi. Chitsanzo cha zimenezi ndi mpweya wina wamumlengalenga umene umatiteteza. Dzuwa limatulutsa kuwala kwabwino ndiponso kwakupha. Kuwala kwakupha kukafika mlengalenga kumasintha mpweya wa okosijeni kuti ukhale mpweya wotchedwa ozoni. Kenako mpweya wa ozoni umayamwa gawo lalikulu la kuwala kwakupha kuja. Choncho tinganene kuti, dziko lapansili analipanga m’njira yoti lizidziteteza lokha.
12. Kodi kayendedwe ka madzi kamasonyeza bwanji kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kulenga?
12 Imeneyi ndi mbali imodzi yokha yokhudza mumlengalenga mmene muli mpweya wamitundumitundu wothandiza kuti padzikoli pakhale zinthu zamoyo. Chinthu chinanso chodabwitsa chimene chimachitika mumlengalenga ndi kayendedwe ka madzi. Chaka chilichonse dzuwa limachititsa madzi oposa makiyubiki kilomita 400,000 ochokera m’nyanja komanso nyanja zikuluzikulu kuti akhale nthunzi yomwe imapita mumlengalenga. Madziwo amapanga mitambo yomwe imamwazidwa ndi mphepo. Kenako madzi amenewa, amene tsopano amakhala osefedwa bwino komanso oyera, amagwa pansi ngati mvula, sinowo ndiponso madzi oundana n’kudzazanso m’mitsinje ndi m’nyanja. Zimachitika mogwirizana ndi zimene lemba la Mlaliki 1:7 limanena, kuti: “Mitsinje yonse imakathira m’nyanja koma nyanjayo sidzaza. Imabwerera kumalo kumene ikuchokera kuti ikayambirenso kuyenda.” Yehova yekha ndi amene anachititsa kuti madzi azizungulira chonchi.
13. Kodi zomera ndiponso dothi zimatiphunzitsa chiyani zokhudza mphamvu za Mlengi wathu?
13 Kulikonse kumene timaona zinthu zamoyo, timaona umboni wakuti Mlengi wathu ali ndi mphamvu zolenga zinthu. Kungoyambira mitengo yaikulu kwambiri yomwe imatalika kuposa nyumba 30 zosanjikizana mpaka tizomera ting’onoting’ono tooneka ndi maikosikopu tomwe timadzaza m’nyanja zikuluzikulu n’kumapereka mpweya wambiri wa okosijeni womwe timapuma, timaona umboni woti Yehova ali ndi mphamvu. Ngakhalenso mudothi muli zinthu zamoyo zambirimbiri monga nyongolotsi, tomera ting’onoting’ono tooneka ngati nkhungu ndiponso tizilombo ting’onoting’ono. Zonsezi zimathandizira kuti zomera zikule. M’pake kuti Baibulo limati nthaka ili ndi mphamvu yothandiza kuti anthu azikolola mokwanira.—Genesis 4:12.
14. Kodi atomu, yomwe ndi kanthu kakang’ono kwambiri, ili ndi mphamvu zambiri bwanji?
14 N’zosachita kufunsa kuti Yehova “anapanga dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake.” (Yeremiya 10:12) Umboni wakuti Mulungu ali ndi mphamvu timauonanso ngakhale m’tinthu ting’onoting’ono kwambiri timene analenga. Mwachitsanzo, mutaika pamodzi maatomu 1 miliyoni amaonekabe kanthu kakang’ono poyerekeza ndi tsitsi limodzi la munthu. Kuwonjezera pamenepa, kanthu komwe kali pakati pa atomu, komwe ndi kakang’ono kwambiri, kali ndi mphamvu zambiri moti anthu amakagwiritsa ntchito popangira mabomba amphamvu kwambiri a nyukiliya.
“Chamoyo Chilichonse”
15. Pofotokoza nyama zosiyanasiyana zakutchire, kodi Yehova ankafuna kumuphunzitsa chiyani Yobu?
15 Umboni wina wosatsutsika wakuti Yehova ali ndi mphamvu zolenga, timaupeza tikaona nyama zambirimbiri zomwe zili padzikoli. Salimo 148 limanena za zinthu zambiri zomwe zimatamanda Yehova, ndipo vesi 10 limatchula ‘nyama zakutchire ndi nyama zoweta.’ Posonyeza chifukwa chake munthu ayenera kupereka ulemu kwa Mlengi, Yehova analankhula ndi Yobu za nyama monga mkango, mbidzi, njati, mvuu ndi ng’ona. Kodi ankafuna kumuphunzitsa chiyani? Ngati anthu amachita mantha ndi nyama zimenezi zomwe ndi zamphamvu, zoopsa ndiponso zosazolowereka, kodi ayenera kumva bwanji akaganizira za Mlengi wa nyamazi?—Yobu, chaputala 38-41.
16. N’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi mbalame zina zimene Yehova analenga?
16 Salimo 148:10 likutchulanso “mbalame zamapiko.” Ndipotu mbalame zimenezi zilipo zamitundu yambirimbiri. Yehova anauza Yobu za nthiwatiwa, imene “imaseka hatchi ndi wokwerapo wake.” Mbalameyi ndi yaitali mamita awiri ndi hafu ndipo siuluka. Komatu imathamanga makilomita 65 pa ola limodzi ndipo ikamathamanga, imaponya phazi lake mamita 4 ndi hafu kuchokera paphazi lina. (Yobu 39:13, 18) Ndiye palinso mbalame ina yotchedwa albatross imene nthawi yambiri ya moyo wake imakhala ikuuluka pamwamba pa nyanja. Imatha kuuluka kwa maola ambirimbiri popanda kukupiza mapiko ake omwe ikawatambasula ndi aatali mamita atatu. Ndiyeno tasiyanitsani ndi mbalame inanso yofanana ndi choso yotchedwa bee hummingbird. Mbalameyi ndi yaitali masentimita 5 okha ndipo ndi mbalame yaing’ono kwambiri pa mbalame zonse. Imatha kukupiza mapiko ake ka 80 pa sekondi imodzi. Mbalamezi zimanyezimira ngati miyala ing’onoing’ono yamtengo wapatali, ndipo zimatha kuuluka chobwerera m’mbuyo komanso zimatha kuima m’malere ngati ndege za helikoputa.
17. Kodi nsomba yotchedwa blue whale ndi yaikulu bwanji, nanga tinganene chiyani pambuyo poganizira nyama zimene Yehova analenga?
17 Lemba la Salimo 148:7 limanena kuti ngakhalenso ‘zamoyo zam’nyanja’ zimalemekeza Yehova. Taganizirani za nangumi wotchedwa blue whale, nyama imene ambiri amati ndi yaikulu kwambiri pa nyama zonse. Chinsomba chimenechi, chomwe chimasambira “m’madzi akuya,” chimatha kutalika mpaka kufika mamita 30 kapena kuposa. Kulemera kwake kungafanane ndi kulemera kwa njovu zikuluzikulu 30. Kulemera kwa lilime lake lokha kumafanana ndi njovu imodzi. Mtima wake ndi waukulu ngati galimoto yaing’ono. Chiwalo chachikulu chimenechi chimagunda maulendo 9 okha pa 1 miniti, mosiyana ndi mtima wa mbalame yotchedwa hummingbird ija womwe umagunda pafupifupi maulendo 1,200 pa 1 miniti. Chinsomba chimenechi chili ndi mtsempha wina waukulu kwambiri moti mwana akhoza kukwawamo. Kunena zoona, timagwirizana ndi mawu omaliza a m’buku la Masalimo akuti: “Chamoyo chilichonse chitamande Ya.”—Salimo 150:6.
Zimene Tingaphunzire Tikaganizira Mphamvu za Yehova
18, 19. Kodi zinthu zamoyo zimene Yehova analenga padzikoli ndi zochuluka bwanji, nanga kodi chilengedwe chimatiphunzitsa chiyani zokhudza ulamuliro wake?
18 Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu? Timasowa chonena tikaona kuchuluka kwa zinthu zosiyanasiyana zimene analenga. Wolemba masalimo wina anati: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! . . . Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.” (Salimo 104:24) Zimenezitu ndi zoona. Asayansi apeza kuti padzikoli pali mitundu ya zamoyo yopitirira 1 miliyoni. Koma ena amati n’kutheka kuti pali zamoyo zambiri kuposa pamenepa. Nthawi zina munthu waluso angaone kuti akusowa zinthu zatsopano zoti achite. Koma luso la Yehova komanso mphamvu zake zotha kulenga zinthu zatsopano ndiponso zosiyanasiyana, sizidzatha.
19 Mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu zimatiphunzitsa kuti iye ndi woyenera kulamulira. Ndipotu mawu akuti “Mlengi” amasiyanitsa Yehova ndi aliyense m’chilengedwechi chifukwa zinthu zina zonse zinachita kulengedwa ndi iyeyo. Ngakhalenso Mwana wobadwa yekha wa Yehova, amene anali “mmisiri waluso” pa nthawi yolenga zinthu, m’Baibulo samutchula kuti Mlengi kapena Mlengi mnzake. (Miyambo 8:30; Mateyu 19:4) M’malomwake, iye ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Popeza Yehova ndi amene analenga chilichonse, iye yekha ndi amene ali ndi ufulu wolamulira aliyense komanso chilichonse.—Aroma 1:20; Chivumbulutso 4:11.
20. Kodi tikamati Yehova atamaliza kulenga zinthu padziko lapansi anapuma zikutanthauza chiyani?
20 Kodi Yehova anasiya kugwiritsa ntchito mphamvu zake zolengera zinthu? Baibulo limanena kuti Yehova atamaliza ntchito yake yolenga pa tsiku la 6, ‘pa tsiku la 7 anayamba kupuma pa ntchito yonse imene ankagwira.’ (Genesis 2:2) Mtumwi Paulo anasonyeza kuti “tsiku” la 7 limeneli ndi lalitali zaka masauzande ambiri, poti linali lidakalipo m’nthawi yake. (Aheberi 4:3-6) Koma kodi ‘kupuma’ kukutanthauza kuti Yehova anasiyiratu kugwira ntchito? Ayi, Yehova sasiya kugwira ntchito. (Salimo 92:4; Yohane 5:17) Choncho mfundo yoti anapuma iyenera kuti ikungotanthauza kuti anasiya kugwira ntchito yolenga zinthu padzikoli. Komabe, akupitiriza kugwira ntchito yokwaniritsa zolinga zake ndipo ntchito imeneyi sinaimitsidwe. Zina mwa zimene anachita ndi kuuzira anthu kuti alembe Malemba Opatulika komanso anapanga “cholengedwa chatsopano.” Tidzakambirana za zimenezi m’Mutu 19.—2 Akorinto 5:17.
21. Kodi kuganizira mphamvu za Yehova zolenga zinthu kudzathandiza bwanji anthu okhulupirika omwe adzakhalepo mpaka kalekale?
21 Tsiku lopuma la Yehova likadzatha, iye adzanena kuti ntchito zake zonse zapadziko lapansi ndi “zabwino kwambiri,” ngati mmene ananenera tsiku la 6 lolenga zinthu litatha. (Genesis 1:31) Tidzaona nthawi yomweyo mmene pa nthawiyo azidzagwiritsira ntchito mphamvu zake zolenga zinthu. Koma tingakhale otsimikiza kuti nthawi zonse tizidzachita chidwi ndi mmene Yehova azidzagwiritsira ntchito mphamvu zotha kulenga. Tizidzaphunzira zokhudza Yehova mpaka kalekale kudzera m’zinthu zimene analenga. (Mlaliki 3:11) Pamene tizidzaphunzira zambiri zokhudza Mlengi wathu wamkuluyu, m’pamenenso tizidzamulemekeza kwambiri, kuchita naye chidwi ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.
a Kuti mumvetse bwino kutalika kwa mtunda umenewu, ganizirani izi: Kuti muyende mtunda umenewu pa galimoto, ngakhale mutamayendetsa pa liwiro la makilomita 160 pa ola limodzi kwa maola 24 pa tsiku, zingakutengereni zaka zoposa 100 kuti mukafike.
b Ena amaganiza kuti kale anthu ankagwiritsa ntchito chipangizo chachikale choonera zinthu zomwe zili kutali. Iwo amati, kodi anthu a nthawi imeneyo paokha akanadziwa bwanji kuti nyenyezi zilipo zambiri ndipo n’zosawerengeka? Koma amanyalanyaza mfundo yoti Yehova, yemwe ndi Mlembi wamkulu wa Baibulo, ndi amene ankathandiza anthuwo kudziwa zimenezi.—2 Timoteyo 3:16.
c Taganizirani kuti mungatenge nthawi yaitali bwanji kuti muwerenge nyenyezi 100 biliyoni zokha. Ngati mungakwanitse kumawerenga nyenyezi imodzi pa sekondi iliyonse, kwa maola 24 pa tsiku, mungatenge zaka 3,171 kuti mumalize kuwerenga zonsezo.