Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 46

Anachira Atagwira Malaya a Yesu

Anachira Atagwira Malaya a Yesu

MATEYU 9:18-22 MALIKO 5:21-34 LUKA 8:40-48

  • MZIMAYI WINA ANACHIRA ATAGWIRA MALAYA A YESU

Ayuda ambiri omwe ankakhala kumpoto chakumadzulo kwa nyanja ya Galileya anamva zoti Yesu akubwera kuchokera ku Dekapole. N’kutheka kuti anthuwa anamva zoti Yesu analamula mphepo komanso mafunde amphamvu kuti zikhale bata komanso mwina anamva zoti Yesu anachiritsa anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda. Choncho, “khamu lalikulu la anthu” linasonkhana m’mbali mwa nyanja, mwina m’dera la Kaperenao, kuti limuchingamire. (Maliko 5:21) Pamene Yesu ankafika anthuwo ankayembekezera kuti aone zimene achite.

Munthu wina amene ankafunitsitsa kuona Yesu anali Yairo. Yairo anali mtsogoleri wa sunagoge, mwina sunagoge wa ku Kaperenao. Iye anagwada pamapazi a Yesu n’kumupempha mobwerezabwereza kuti: “Mwana wanga wamkazi akudwala mwakayakaya. Chonde tiyeni mukamuike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.” (Maliko 5:23) Yairo anali ndi mwana mmodzi yekha yemwe ankamukonda kwambiri ndipo anali ndi zaka 12. Kodi Yesu anamuyankha bwanji Yairo atamupempha kuti akamuchiritsire mwana wakeyu?—Luka 8:42.

Ali pa ulendo wopita kunyumba kwa Yairo panachitika zinthu zina. Anthu ambiri amene anatsagana ndi Yesu pa ulendowu ankayembekezera kuona Yesu akuchita chozizwitsa china. Koma m’chigulumo munali mzimayi wina amene ankaganizira kwambiri za matenda omwe ankavutika nawo.

Mzimayiyu anali Myuda ndipo anali atavutika ndi matenda otaya magazi kwa zaka 12. Anali ataonana ndi madokotala osiyanasiyana ndipo anali atawononga ndalama zake zonse polipirira mankhwala komanso zinthu zina zimene madokotalawo ankamuuza. Koma matendawo sanathe, m’malomwake “ankangokulirakulira.”—Maliko 5:26.

Mukaganizira za matenda a mzimayiyu mungaone kuti ankamufooketsa komanso anali matenda ochititsa manyazi moti zinali zovuta kuwafotokoza pagulu. Komanso Chilamulo cha Mose chinkati ngati mzimayi akukha magazi azikhala wodetsedwa pa nthawi yonse yomwe akukha magaziyo. Munthu aliyense akakhudza mzimayi kapena zovala zake zomwe zili ndi magazi, ankafunika kusamba ndipo ankakhala wodetsedwa mpaka madzulo.—Levitiko 15:25-27.

Mzimayiyu anali “atamva zambiri zokhudza Yesu” moti anayamba kumufunafuna ndipo anamupeza. Koma chifukwa chakuti anali wodetsedwa analowa m’chigulu cha anthucho mobisa kuti anthu asamuzindikire ndipo mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” Ndipo zinachitikadi kuti atangogwira malaya a Yesu anazindikira kuti magazi aja asiya kutuluka. Nthawi yomweyo ‘anachira nthenda yake yaikuluyo.’—Maliko 5:27-29.

Kenako Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwira?” Kodi mukuganiza kuti mzimayiyo anamva bwanji Yesu atafunsa funso limeneli? Petulo anayankha mosonyeza kuti akudzudzula Yesu chifukwa ananena kuti: “Mlangizi, anthu onsewa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.” Ndiye n’chifukwa chiyani Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwira?” Koma Yesu ananena kuti: “Wina wandigwira, chifukwa ndamva kuti mphamvu yatuluka mwa ine.” (Luka 8:45, 46) Zimene zinachitikazi zinasonyeza kuti Yesu anali ndi mphamvu zotha kuchiritsa.

Mzimayiyu atazindikira kuti Yesu wadziwa zimene zachitikazo anagwada ali ndi mantha komanso akunjenjemera. Kenako anayamba kufotokoza za matenda akewo pamaso pa anthu onse komanso zimene zachitika kuti achire. Yesu anamulimbikitsa pomuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”—Maliko 5:34.

Zimenezi zikusonyeza kuti munthu Amene Mulungu anamusankha kuti adzalamulire dzikoli ndi wokoma mtima, wachifundo, amachita zinthu moganizira ena komanso ali ndi mphamvu zothandizira anthu ovutika.