Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 54

Yesu Ndiye “Chakudya Chopatsa Moyo”

Yesu Ndiye “Chakudya Chopatsa Moyo”

YOHANE 6:25-48

  • YESU NDIYE “CHAKUDYA CHOCHOKERA KUMWAMBA”

Ali chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya, Yesu anadyetsa anthu ambiri mozizwitsa koma kenako anachoka pamene anthuwo ankafuna kuti amuveke ufumu. Usiku wa tsiku limenelo Yesu anayenda panyanja pomwe panali mphepo yamphamvu. Anapulumutsanso Petulo yemwe anayamba kumira chifukwa cha mantha ataona mafunde amphamvu pamene ankayenda panyanja. Yesu analetsanso mphepo yamphamvu, zimene zinathandiza kuti boti limene ophunzira ake anakwera lisasweke ndi mafunde.

Atachoka kumeneko Yesu anapita m’dera la Kaperenao lomwe linali kumadzulo kwa nyanja ya Galileya. Ali m’derali anthu amene anawadyetsa mozizwitsa aja anamupeza ndipo anamufunsa kuti: “Mwafika nthawi yanji kuno?” Koma Yesu anawadzudzula ndipo anawauza kuti akumufunafuna n’cholinga choti awapatsenso chakudya. Anawalimbikitsa kuti ‘asamagwire ntchito kuti angopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti apeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha.’ Ndiyeno anthuwo anamufunsa kuti: “Tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”—Yohane 6:25-28.

N’kutheka kuti anthuwa ankaganiza kuti Yesu ankanena za zinthu zimene zinalembedwa m’Chilamulo koma Yesu ankanena za ntchito yofunika kwambiri. Iye ananena kuti: “Ntchito ya Mulungu ndi iyi, musonyeze chikhulupiriro mwa amene Iyeyo anamutuma.” Koma anthuwo sankakhulupirira Yesu ngakhale kuti anali atachita zinthu zambiri. Iwo anamuuza kuti awasonyeze chizindikiro kuti amukhulupirire. Anamufunsa kuti: “Muchita ntchito yotani? Makolo athu anadya mana m’chipululu, monga mmene Malemba amanenera kuti, ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”—Yohane 6:29-31; Salimo 78:24.

Anthuwo atapempha kuti Yesu awaonetse chizindikiro, Yesuyo anawathandiza kudziwa kumene ankatenga mphamvu yochitira zozizwitsa. Iye anati: “Ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. Iye wotsika kuchokera kumwamba, amene amapereka moyo kudziko ndiye chakudya chimene Mulungu amapereka.” Chifukwa chosamvetsa mfundo ya Yesu, anthuwo anamuchonderera kuti: “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenechi nthawi zonse.” (Yohane 6:32-34) Koma kodi Yesu ankanena za “chakudya” chiti?

Yesu anafotokoza kuti: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pang’ono, ndipo wokhulupirira mwa ine sadzamva ludzu. Koma ndakuuzani kuti, Ngakhale mwandiona, simukukhulupirirabe. . . . Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa. Chifuniro cha amene anandituma ine n’chakuti, ndisataye aliyense mwa onse amene iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse pa tsiku lomaliza. Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi chakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupirira mwa iye akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 6:35-40.

Atanena zimenezi Ayudawo anakhumudwa ndipo anayamba kung’ung’udza. Iwo ankanena kuti munthu ameneyu anganene bwanji kuti ndi “chakudya chotsika kumwamba”? (Yohane 6:41) Anthuwo ankangoona kuti Yesu ndi munthu wamba amene makolo ake anali ochokera mumzinda wa Nazareti ku Galileya, moti ankafunsana kuti: “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe, amene bambo ake ndi mayi ake tikuwadziwa?”—Yohane 6:42.

Koma Yesu anawayankha kuti: “Musang’ung’udze inu. Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine, ndipo ine ndidzamuukitsa tsiku lomaliza. Zinalembedwa m’Mabuku a Aneneri kuti, ‘Ndipo onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’ Aliyense amene wamva kwa Atate ndipo waphunzira amabwera kwa ine. Sikuti alipo munthu amene anaonapo Atate ayi, kupatulapo yekhayo amene anachokera kwa Mulungu, ameneyu anaona Atate. Ndithudi ndikukuuzani, Wokhulupirira ali nawo moyo wosatha.”—Yohane 6:43-47; Yesaya 54:13.

Kumbukirani kuti m’mbuyomu Yesu anafotokoza za kugwirizana kumene kulipo pakati pa moyo wosatha ndi kukhulupirira Mwana wa munthu. Pamene ankalankhula zimenezi anali ndi Nikodemo. Iye ananena kuti: “Aliyense wokhulupirira [Mwana wa Mulungu wobadwa yekha] asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:15, 16) Koma pa nthawiyi Yesu ankalankhula kwa anthu ambiri ndipo anawauza kuti iye anali ndi udindo wowathandiza kuti adzapeze moyo wosatha. Moyo umenewu sakanatha kuupeza chifukwa chodya mana kapena chakudya chilichonse chomwe chinkapezeka ku Galileya. Ndiye kodi anthuwa akanapeza bwanji moyo wosatha? Yesu anabwereza zimene ananena kuti: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo.”—Yohane 6:48.

Yesu anafotokozanso za nkhani ya chakudya chochokera kumwambayi pamene ankaphunzitsa ku sunagoge wa ku Kaperenao.