Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 23

Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao

Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao

MATEYU 8:14-17 MALIKO 1:21-34 LUKA 4:31-41

  • YESU ANATULUTSA CHIWANDA

  • YESU ANACHIRITSA APONGOZI AKE A PETULO

Yesu anali atangosankha kumene ophunzira 4, omwe mayina awo anali Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane kuti akhale asodzi a anthu. Tsiku la Sabata litafika, iwo anapita ku sunagoge wa ku Kaperenao ndipo Yesu anayamba kuphunzitsa m’sunagogemo. Anthu anadabwa ndi mmene ankaphunzitsira chifukwa ankaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro ndipo izi zinali zosiyana kwambiri ndi mmene alembi ankaphunzitsira.

Pa tsiku limeneli, m’sunagogemo munalinso munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa ndiyeno munthu uja anafuula mwamphamvu kuti: “Kodi tili nanu chiyani, Yesu Mnazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu.” Yesu anadzudzula mzimu umene unagwira munthuyo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!”—Maliko 1:24, 25.

Pamenepo mzimuwo unagwetsera munthu uja pansi moti anayamba kugubuduka komanso kukuwa kwambiri. Koma mzimuwo unatuluka mwa munthuyo “osamuvulaza.” (Luka 4:35) Anthu amene anali m’sunagogemo anadabwa kwambiri ndipo anafunsa kuti: “Kodi chimenechi n’chiyani? Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu, ndipo ikumumvera.” (Maliko 1:27) N’zosadabwitsa kuti nkhani yochititsa chidwiyi inafalikira ku Galileya konse.

Atachoka ku sunagogeko, Yesu ndi ophunzira ake anapita kwawo kwa Simoni amene ankadziwikanso kuti Petulo. Kumeneko apongozi ake a Petulo ankadwala malungo aakulu ndipo anapempha Yesu kuti akawachiritse. Atafika kumeneko, anagwira dzanja la mayiwo n’kuwadzutsa. Atangotero malungowo anatheratu ndipo sanalole kuti Yesu ndi ophunzirawo anyamuke nthawi yomweyo. Mwina anachita zimenezo kuti awaphikire kaye chakudya.

Dzuwa litatsala pang’ono kulowa, anthu ochokera m’madera osiyanasiyana anabwera ndi anthu odwala kunyumba kwa Petulo moti pakhomopo panadzaza anthu ambiri. Kodi anthuwo ankabwera kudzatani? Ankabwera kuti Yesu adzawathandize, chifukwa “onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa mwa kuika manja ake pa aliyense.” (Luka 4:40) Yesu anachiritsa matenda a mtundu uliwonse mogwirizana ndi zimene Malemba ananena. (Yesaya 53:4) Iye anathandizanso anthu amene anagwidwa ndi mizimu yoipa. Pamene mizimuyo inkatuluka, inkafuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” (Luka 4:41) Koma Yesu anaidzudzula ndipo sanailolenso kuti ilankhule chilichonse. Mizimuyo inkadziwa kuti Yesu anali Khristu ndipo iye sankafuna kuti izidzionetsa ngati kuti nayonso inkatumikira Mulungu woona.