Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 33

Ulosi wa Yesaya Unakwaniritsidwa

Ulosi wa Yesaya Unakwaniritsidwa

MATEYU 12:15-21 MALIKO 3:7-12

  • KHAMU LA ANTHU LINAPANIKIZA YESU

  • YESU ANAKWANIRITSA ULOSI WA YESAYA

Yesu atazindikira kuti a chipani cha Herode komanso Afarisi akonza zoti amuphe, iye ndi ophunzira ake analowera ku nyanja ya Galileya. Anthu ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana anabwera kwa Yesu. Ena anali ochokera ku Galileya, ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Turo ndi Sidoni yomwe inali m’mbali mwa nyanja. Ena anali ochokera m’madera a kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano komanso m’dera la Idumeya, lomwe linali chakum’mwera kwa Yudeya. Yesu anachiritsa odwala ambiri omwe anachokera m’madera amenewa. Pofuna kuti achiritsidwe, anthuwa ankapanikizana n’cholinga choti afike pamene panali Yesu. Anthuwa sanadikire Yesu kuti awagwire, m’malomwake iwowo ndi amene ankapita kwa iye kuti angomukhudza.—Maliko 3:9, 10.

Anthuwo anali ambiri moti Yesu anauza ophunzira ake kuti amubweretsere boti laling’ono kuti asunthireko m’madzi komanso kuti anthu asamupanikize. Yesu ankafuna kuti aziphunzitsa atakwera m’boti komanso mwina akanatha kupita kudera lina la m’mphepete mwa nyanjayo kuti akathandizenso anthu ena.

Mateyu, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anaona kuti zimene Yesu anachitazi zinkakwaniritsa “zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya.” (Mateyu 12:17) Kodi ulosiwo unali woti chiyani?

Ulosi wake unali wakuti: “Taonani mtumiki wanga amene ndamusankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukukondwera naye. Ndidzaika mzimu wanga pa iye, ndipo adzasonyeza bwinobwino chilungamo chenicheni kwa anthu a mitundu ina. Sadzakangana ndi munthu, kapena kufuula, ndipo palibe amene adzamva mawu ake m’misewu. Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa, kufikira atakwanitsa kubweretsa chilungamo. Ndithudi, m’dzina lake mitundu ya anthu idzayembekezera zabwino.”—Mateyu 12:18-21; Yesaya 42:1-4.

Yesu ndi mtumiki amene Mulungu anamusankha ndipo Mulungu anachita kunena yekha kuti amakondwera naye. Zimene Yesu ankachita zinathandiza anthu kudziwa chilungamo chenicheni, chomwe chinkabisika chifukwa cha miyambo yachipembedzo chonyenga. Chifukwa chosowa chilungamo, Afarisi ankapotoza Chilamulo cha Mulungu moti sankathandiza ngakhale munthu wodwala pa tsiku la Sabata. Pofuna kusonyeza chilungamo cha Mulungu komanso kuti mzimu wa Mulungu uli pa iye, Yesu anathandiza anthu amene ankaponderezedwa kuti amasuke ku miyambo yopanda chilungamo imene Afarisi ankalimbikitsa. Chifukwa cha zimenezi, atsogoleri achipembedzo anayamba kukonza zoti amuphe. Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni kwambiri.

Kodi ulosi wakuti “sadzakangana ndi munthu, kapena kufuula, ndipo palibe amene adzamva mawu ake m’misewu,” unkatanthauza chiyani? Pochiritsa anthu, Yesu sankalola kuti ziwanda kapena anthuwo ‘amuulule.’ (Maliko 3:12) Sankafuna kuti anthu adziwe za iye chifukwa chakuti winawake akulengeza mofuula m’misewu kapena kudzera m’zokambakamba za anthu zomwe nthawi zambiri zimakhala zosinjirira.

Komanso Yesu ankapereka uthenga wotonthoza kwa anthu amene anali ngati bango lophwanyika, lopindika komanso lothyoka. Anthuwa analinso ngati chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima. Yesu sanasansanthe bango lophwanyika kapena kuzimitsa chingwe cha nyale yofuka. M’malomwake, analimbikitsa anthu odzichepetsa ndipo anachita zimenezi mwachifundo komanso mwachikondi. Pamenepa n’zoonekeratu kuti Yesu ndi yekhayo amene anthu angamudalire kuti adzasintha zinthu.