Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 37

Yesu Anaukitsa Mwana Wamwamuna wa Mzimayi Wamasiye

Yesu Anaukitsa Mwana Wamwamuna wa Mzimayi Wamasiye

LUKA 7:11-17

  • ANAUKITSA MNYAMATA KU NAINI

Yesu atachiritsa wantchito wa kapitawo uja, anachoka ku Kaperenao n’kuyamba ulendo wopita ku tauni ya Naini. Tauniyi inali pamtunda wa makilomita 32 kum’mwera chakumadzulo kwa mzinda wa Kaperenao. Pa ulendowu Yesu anali ndi ophunzira ake komanso gulu la anthu ena. N’kutheka kuti ankayandikira ku Naini nthawi ya kumadzulo. Atatsala pang’ono kulowa m’tauniyo anakumana ndi kagulu ka Ayuda atanyamula maliro. Malirowo anali a mnyamata wina ndipo ankachoka m’tawuniyo kupita nawo kumanda.

Mayi ake a mnyamatayo omwenso anali pagululo anali ndi chisoni kwambiri. Mayiyu anali wamasiye ndipo malirowo anali a mwana wake yekhayo. Mwamuna wake atamwalira, mayiyu ankalimbako mtima chifukwa choti anatsala ndi mwana wake wa mwamunayu yemwe ankamukonda kwambiri. N’kuthekanso kuti mayiyo ankamudalira mnyamatayo kuti ndi amene adzamuthandize m’tsogolo. Koma mnyamatayu atamwalira, mayiyu analibenso munthu wina amene akanatha kukhala naye ndi kumulimbikitsa.

Yesu ataona mayiyo zinamukhudza kwambiri chifukwa ankalira momvetsa chisoni komanso chifukwa cha mmene zinthu zinalili pamoyo wake. Kenako Yesu analankhula ndi mayiyo mokoma mtima ndiponso m’njira yolimbikitsa komanso yochititsa munthu kukhala ndi chikhulupiriro. Iye anati: “Tontholani mayi.” Ndiyeno Yesu anafika pafupi n’kugwira chithatha chomwe ananyamulirapo malirowo. (Luka 7:13, 14) Zimene anachitazo zinachititsa kuti anthuwo aime ndipo mwina ankafunsana kuti: ‘Kodi akutanthauza chiyani ndipo akufuna kuchita chiyani?’

Kodi mukuganiza kuti anthu amene ankayenda ndi Yesu, omwe anali atamuonapo akuchita zinthu zamphamvu ngati kuchiritsa odwala, anamva bwanji? Anthuwa anali asanaonepo Yesu ataukitsa munthu wakufa. Ngakhale kuti anthu ena anali ataukitsidwapo kale kwambiri m’mbuyomo, n’kutheka kuti anthuwa ankadzifunsa ngati Yesu akanatha kuukitsa mnyamatayo. (1 Mafumu 17:17-23; 2 Mafumu 4:32-37) Kenako Yesu anaitana mnyamatayo kuti: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!” (Luka 7:14) Nthawi yomweyo mnyamatayo anadzuka n’kuyamba kulankhula ndipo Yesu anamupereka kwa mayi ake amene anali odabwa komanso osangalala kwambiri.

Anthuwo ataona kuti mnyamatayo ali ndi moyo analemekeza Yehova yemwe ndi Wopereka Moyo ponena kuti: “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu.” Anamvetsanso tanthauzo la zinthu zodabwitsa zimene Yesu anachitazo chifukwa ananena kuti: “Mulungu wacheukira anthu ake.” (Luka 7:16) Nkhaniyi inafala mofulumira kwambiri m’madera ozungulira komanso mumzinda wa Nazareti, womwe unali pa mtunda wa makilomita 10 kuchokera ku Naini. Nkhaniyi inafalikiranso mpaka chakum’mwera ku Yudeya.

Pa nthawiyi n’kuti Yohane M’batizi adakali m’ndende ndipo ankayesetsa kuti adziwe zinthu zodabwitsa zimene Yesu ankachita. Ophunzira ake ndi amene ankamuuza zimenezi. Kodi Yohane anatani atamva zimenezi?