MUTU 43
Mafanizo Ofotokoza za Ufumu
MATEYU 13:1-53 MALIKO 4:1-34 LUKA 8:4-18
-
YESU ANAFOTOKOZA MAFANIZO ONENA ZA UFUMU
Pamene Yesu ankadzudzula Afarisi n’kuti ali ku Kaperenao kunyumba imene ankakonda kukhalako nthawi zambiri. Chakumasana Yesu anachoka kunyumbako n’kupita ku nyanja ya Galileya ndipo anthu ambiri anasonkhana kumeneko. Yesu atafika kunyanjako, anakwera boti n’kusunthirako chapatali pang’ono kenako anayamba kuwaphunzitsa za Ufumu wakumwamba. Anawaphunzitsa zinthu zimenezi pogwiritsa ntchito mafanizo. Pofotokoza mafanizowa Yesu ankagwiritsa ntchito zinthu zimene anthuwo ankazidziwa, zomwe zinachititsa kuti anthuwo amvetse bwino mfundo zosiyanasiyana zokhudza Ufumuwu.
Poyamba, Yesu anafotokoza fanizo la munthu wofesa mbewu. Mbewu zina zinagwera m’mbali mwa msewu ndipo zinadyedwa ndi mbalame. Mbewu zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira. Mizu ya mbewu zimenezi siinapite pansi kwambiri ndipo mbewuzo zitamera zinawauka ndi dzuwa n’kufota. Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinalepheretsa mbewuzo kukula. Koma mbewu zina zinagwera panthaka yabwino. Mbewu zimenezi zinabala ‘zipatso 100, zina 60, ndipo zina 30.’—Mateyu 13:8.
Kenako Yesu anafotokozanso fanizo lina. M’fanizoli Yesu anayerekezera Ufumu ndi zimene zimachitika munthu akafesa mbewu. Mbewuzo zimapitirizabe kukula kaya wofesayo ali maso kapena akugona ndipo “sadziwa” mmene zimenezi zimachitikira. (Maliko 4:27) Mbewuzo zimakula pazokha n’kufika pokhwima ndipo mwiniwakeyo amadzakolola.
Kenako Yesu anafotokoza fanizo lachitatu lonena zimene zimachitika pofesa mbewu. Munthu anafesa mbewu zabwino m’munda mwake koma “anthu ali m’tulo” mdani anabwera n’kufesa namsongole m’munda wa tiriguwo. Antchito anafunsa mwiniwake wa mundawo ngati angakazule namsongoleyo. Koma mwiniwakeyo anayankha kuti: “Ayi, kuopera Mateyu 13:24-30.
kuti mwina pozula namsongole mungazule pamodzi ndi tirigu. Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. M’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Choyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga m’mitolo kuti akatenthedwe. Mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.”—Anthu ambiri amene ankamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa ankadziwa bwino ntchito yolima. Yesu ananenanso za kanjere ka mpiru kamene anthuwo ankakadziwa bwino. Kanjereka kamakula n’kukhala mtengo waukulu moti mbalame zimapeza malo okhala m’nthambi zake. Ponena za kanjereka Yesu anati: “Ufumu wakumwamba uli ngati kanjere ka mpiru kamene munthu anakatenga ndi kukabzala m’munda wake.” (Mateyu 13:31) Koma sikuti cholinga cha Yesu chinali chowaphunzitsa zaulimi. Iye anafotokoza mafanizowa pofuna kuthandiza anthuwo kumvetsa mmene kanthu kakang’ono kangakulire n’kukhala chinthu chachikulu kwambiri.
Kenako Yesu ananenanso zinthu zina zimene anthuwo ankazidziwa bwino kwambiri. Anayerekezera Ufumu wakumwamba ndi “zofufumitsa, zimene mkazi wina anazitenga ndi kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezera.” (Mateyu 13:33) Ngakhale kuti zofufumitsazo sizioneka, zimalowerera mumtandawo ndipo zimachititsa kuti mtandawo usinthe n’kufufuma ndipo munthu aliyense amatha kuona zimenezi.
Yesu atafotokoza mafanizo amenewa, anauza anthuwo kuti abwerere kwawo ndipo iye anapita kunyumba imene ankakhala. Chifukwa chakuti ophunzira ake ankafuna kumvetsa zimene anaphunzitsazo, anamupempha kuti awafotokozere zimene mafanizowo ankatanthauza.
ZIMENE TIKUPHUNZIRA PA MAFANIZO A YESU
Ophunzirawo anali atamvapo Yesu akugwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa, koma aka kanali koyamba kumumva akufotokoza mafanizo ambiri chonchi nthawi imodzi. Choncho anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulankhula nawo mwa mafanizo?”—Mateyu 13:10.
Chifukwa chimodzi chimene Yesu ankachitira zimenezi chinali kukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Mu nkhani imene Mateyu analemba ananena kuti: “Sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo, kuti zikwaniritsidwe zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri amene anati: “Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mafanizo, ndidzafalitsa zinthu zobisika kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi.’”—Mateyu 13:34, 35; Salimo 78:2.
Komabe panali zifukwa zinanso zimene Yesu ankagwiritsira ntchito mafanizo. Zimene anthuwa ankachita akamva mafanizo zinkasonyeza zimene zinali m’mitima yawo. Ngakhale kuti anthu ambiri ankachita chidwi ndi Yesu chifukwa chakuti ankafotokoza bwino nkhani ndiponso kuchita zinthu zodabwitsa, sankamuona ngati Ambuye woyenera kumumvera komanso kumutsatira ndi mtima wonse. (Luka 6:46, 47) Anthuwa sankafunanso kusintha maganizo awo, zochita zawo ndipo sankalola kuti mawuwo akhazikike m’mitima yawo.
Poyankha funso la ophunzira ake lija, Yesu ananena kuti: “N’chifukwa chake ndikulankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti ngakhale akuona, kuona kwawo n’kopanda phindu. Ngakhale akumva, kumva kwawo n’kopanda phindu, ndipo sazindikira tanthauzo lake. Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa, umene umati: ‘. . . Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira.’”—Mateyu 13:13-15; Yesaya 6:9, 10.
Koma sikuti anthu onse ankachita zimenezi. Yesu anafotokoza kuti: “Koma inu ndinu odala chifukwa maso anu amaona, komanso makutu anu amamva. Pakuti ndikukuuzani ndithu, Aneneri ambiri komanso anthu olungama analakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione, kutinso amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve.”—Mateyu 13:16, 17.
Atumwi 12 a Yesu komanso ophunzira ena okhulupirika anali ndi mitima yabwino chifukwa ankafunitsitsa Mateyu 13:11) Chifukwa chakuti ophunzirawo anali ndi mtima wofunitsitsa kumvetsa zimene Yesu ankaphunzitsa, Yesu anawauza tanthauzo la fanizo la munthu wofesa mbewu.
kusintha akaphunzira zinthu zatsopano. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika za ufumu wakumwamba, koma anthu amenewa sanapatsidwe mwayi umenewo.” (Yesu ananena kuti “mbewuzo ndi mawu a Mulungu.” (Luka 8:11) Ndipo nthaka ikuimira mtima wa munthu. Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri kuti munthu amvetse tanthauzo la fanizoli.
Ponena za mbewu zomwe zinapondedwapondedwa m’mbali mwa msewu, Yesu ananena kuti: “Mdyerekezi amabwera ndi kudzachotsa mawuwo m’mitima yawo kuti asakhulupirire ndi kupulumuka.” (Luka 8:12) Ponena za mbewu zimene zinagwera panthaka yamiyala, Yesu ananena kuti mbewuzi zikuimira mitima ya anthu amene amalandira mawu mosangalala komabe mawuwo sakhazikika m’mitima yawo. Anafotokozanso kuti: “Pamene chisautso kapena mazunzo zayamba chifukwa cha mawuwo, iye amapunthwa mwamsanga,” kutanthauza kuti “nthawi yoyesedwa” ikafika munthuyo amagwa, mwina chifukwa chotsutsidwa ndi achibale ake kapena anthu ena.—Mateyu 13:21; Luka 8:13.
Nanga bwanji za mbewu zimene zinagwera paminga? Yesu ananena kuti mbewu zimenezi zikuimira anthu amene amamva mawu koma “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” zimawasokoneza. (Mateyu 13:22) Mawuwo amawafikadi pamtima koma amalephera kukula ndipo sabereka zipatso.
Yesu anafotokozanso za mtundu wina wa nthaka yomwe inali nthaka yabwino. Nthakayi ikuimira anthu amene akamva mawuwo amazindikira tanthauzo lake ndipo ‘amabala zipatso.’ Chifukwa chakuti anthuwa amasiyana pa zinthu ngati zaka komanso thanzi lawo, sachita zinthu mofanana moti ena amabala zipatso 100, ena 60 ndipo ena 30. Mulungu amadalitsa “anthu amene Luka 8:15.
pambuyo pomva mawuwo ndi mtima woona komanso wabwino, amawagwiritsitsa ndi kubereka zipatso mwa kupirira.”—Zimenezi ziyenera kuti zinasangalatsa kwambiri ophunzira amene anapita kwa Yesu kuti akawatanthauzire zimene ankawaphunzitsa. Iwo anamvetsa zimene Yesu ankatanthauza. Yesu ankafuna kuti ophunzirawo amvetse bwino mafanizo ake n’cholinga choti nawonso akaphunzitse anthu ena mfundo za choonadi. Kenako iye anawafunsa kuti: “Nyale saivundikira ndi dengu loyezera zinthu kapena kuiika pansi pa bedi, amatero kodi? Koma amaiika pachoikapo nyale, si choncho kodi?” Ndiyeno anawauza kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”—Maliko 4:21-23.
YESU ANAWAPATSA MALANGIZO ENA
Yesu atatanthauzira fanizo la wofesa mbewu, ophunzira a Yesu anafuna kudziwa zinthu zambiri. Iwo anamupempha kuti: “Timasulireni fanizo lija la namsongole m’munda.”—Mateyu 13:36.
Zimene anachitazi zinasonyeza kuti ophunzirawa anali osiyana kwambiri ndi gulu la anthu amene ankamvetsera zimene Yesu anaphunzitsa. Apa zinaonekeratu kuti ngakhale anthuwo anamva koma sankafuna kudziwa tanthauzo la mafanizowo komanso mmene akanagwiritsira ntchito zimene aphunzirazo. Iwo ankangokhutira kumva Yesu akufotokoza mafanizowo basi. Yesu anasonyeza kusiyana komwe kunalipo pakati pa anthu ena onsewo ndi ophunzira ake omwe anali ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri. Iye ananena kuti:
“Samalani zimene mukumvazi. Muyezo umene mukuyezera, nanunso adzakuyezerani womwewo. Inde, adzakuwonjezerani zochuluka.” (Maliko 4:24) Ophunzirawo anamvetsera mwachidwi zimene Yesu ankafotokoza. Ndipo anathanso kuona bwino kuti Yesu ankachita nawo chidwi chifukwa anawapatsa malangizo ena komanso anawathandiza kumvetsa bwino zinthu. Choncho poyankha zimene ophunzira ake anamufunsa zokhudza fanizo la tirigu ndi namsongole, Yesu anawauza kuti:
“Wofesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu. Munda ndiwo dziko ndipo mbewu zabwino ndi ana a ufumu. Koma namsongole ndi ana a woipayo, ndipo mdani amene anafesa namsongole ndi Mdyerekezi. Nthawi yokolola ikuimira mapeto a nthawi ino, ndipo okololawo ndi angelo.”—Mateyu 13:37-39.
Yesu atafotokoza tanthauzo la mbali iliyonse ya fanizolo anafotokozanso zotsatirapo zake. Ananena kuti pa mapeto a dziko loipali angelo, amene ndi okolola, adzasiyanitsa Akhristu onyenga amene ali ngati namsongole ndi “ana a ufumu.” Pa nthawi imeneyo “olungama” adzasonkhanitsidwa ndipo adzawala kwambiri “mu ufumu wa Atate wawo.” Nanga n’chiyani chidzachitikire “ana a woipayo?” Adzawonongedwa, zomwe zidzachititse kuti ‘adzalire ndi kukukuta mano.’—Mateyu 13:41-43.
Kenako Yesu anauza ophunzira ake mafanizo ena atatu. Fanizo loyamba linali lakuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa Mateyu 13:44.
cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.”—Anafotokozanso fanizo lina kuti: “Komanso ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino. Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali, anapita mwamsanga n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo.”—Mateyu 13:45, 46.
Pogwiritsa ntchito mafanizo awiriwa, Yesu anasonyeza kuti munthu amalolera kukhala wopanda zinthu zina kuti apeze chinthu chofunika kwambiri. Mwachitsanzo, wamalonda uja analolera kugulitsa “zinthu zonse zimene anali nazo” n’cholinga choti akagule ngale imodzi imene inali ya mtengo wapatali kwambiri. Ophunzira a Yesu ayenera kuti anamvetsa bwino fanizo la ngale. Komanso wamalonda amene anapeza chuma chobisika m’munda, ‘anagulitsa zinthu zonse’ kuti agule mundawo. M’mafanizo awiri onsewa, anthuwo anapeza chinthu chamtengo wapatali chomwe atachipeza anafunika kuchiteteza. Nayenso munthu amene akufuna kupeza zosowa zake zauzimu, amalolera kusiya zinthu zina kuti apeze zinthu zauzimu zomwe ndi zamtengo wapatali. (Mateyu 5:3) Anthu ena amene ankamvetsera Yesu akufotokoza mafanizowa anali atasonyeza kale kuti anali okonzeka kuchita zambiri n’cholinga choti aphunzire zinthu zauzimu komanso kuti akhale otsatira okhulupirika a Yesu.—Mateyu 4:19, 20; 19:27.
Kenako Yesu anafotokoza fanizo lachitatu lomwe anayerekezera Ufumu wakumwamba ndi khoka limene limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu. (Mateyu 13:47) Akasankha nsombazo, zabwino amazisunga koma zoipa amazitaya. Yesu ananena kuti zimenezi ndi zimene zidzachitikenso pa mapeto a dziko loipali. Pa nthawiyi angelo adzachotsa anthu oipa pakati pa olungama.
Yesu ankagwira ntchito yosodza mwauzimu pamene anaitana ophunzira ake oyambirira kuti akhale “asodzi a anthu.” (Maliko 1:17) Komabe iye anafotokoza kuti fanizo la khokali lidzakwaniritsidwa m’tsogolo pa mapeto a dziko loipali. (Mateyu 13:49) Choncho atumwi a Yesu komanso ophunzira ake ena amene ankamva zimene Yesu ankaphunzitsazi anadziwa kuti zinthu zambiri zochititsa chidwi zidzachitika m’tsogolo.
Anthu amene anamva Yesu akufotokoza mafanizo ali m’boti anaphunzira zinthu zambiri. Koma Yesu anasonyeza kuti ankafunitsitsa “kufotokoza zonse kwa ophunzira ake” ali kwa okha. (Maliko 4:34) Yesu anali ngati “mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.” (Mateyu 13:5) Pamene Yesu ankapereka mafanizo amenewa sankadzionetsera kuti anali ndi luso pophunzitsa koma ankauza ophunzira ake choonadi chimene chili ngati chuma chamtengo wapatali. Iye analidi ‘mphunzitsi wa anthu’ kuposa aliyense.