Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 26

“Machimo Ako Akhululukidwa”

“Machimo Ako Akhululukidwa”

MATEYU 9:1-8 MALIKO 2:1-12 LUKA 5:17-26

  • YESU ANAKHULULUKIRA MACHIMO MUNTHU WAKUFA ZIWALO N’KUMUCHIRITSA

Anthu okhala m’madera akutali anali atamva zambiri zokhudza Yesu. Anthu ambiri ankabwera kuti adzamve zimene Yesu ankaphunzitsa komanso kudzaona zinthu zodabwitsa zimene ankachita. Anthuwa ankachokera m’madera akutali komanso ovuta kufikako. Koma Yesu atangokhala masiku ochepa anabwereranso ku Kaperenao komwe ankakhala nthawi zambiri. Anthu ambiri anadziwa mwamsanga kuti Yesu ali ku Kaperenao, mzinda womwe unali m’mbali mwa nyanja ya Galileya. Choncho ambiri anapita kunyumba imene ankakhalayo. Ena mwa anthuwa anali Afarisi komanso ophunzitsa Chilamulo omwe anachokera m’madera onse a ku Galileya, Yudeya komanso Yerusalemu.

“Anthu ochuluka anasonkhana kumeneko, moti panalibenso malo okhala, chifukwa anthu anadzaza mpaka pakhomo, ndipo anayamba kuwauza uthenga wabwino.” (Maliko 2:2) Kenako Yesu anachita zinthu zodabwitsa kwambiri. Zimene anachitazo zimatithandiza kudziwa kuti Yesu ali ndi mphamvu zotha kuthetsa mavuto amene anthu akukumana nawo komanso kuti akhoza kuchiritsa aliyense amene iye wasankha.

Yesu ali mkati mophunzitsa gulu la anthu lomwe linali m’chipindamo, panabwera anthu 4 atanyamula munthu wakufa ziwalo pamachira. Anthuwa ankafuna kuti Yesu achiritse wodwalayo. Koma chifukwa chakuti anthu anali atadzaza m’chipindamo “sanathe kum’fikitsa kwa Yesu.” (Maliko 2:4) Anthuwa ayenera kuti anakhumudwa kwambiri choncho anakwera padenga la nyumbayo n’kuboola dengalo. Kenako anatsitsira munthu wodwalayo m’nyumbamo.

Kodi Yesu anakhumudwa ndi zimene anthuwa anachita poganiza kuti akumusokoneza? Ayi. M’malomwake anakhudzika mtima ndi chikhulupiriro chimene anthuwa anali nacho moti anauza munthu wodwalayo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.” (Mateyu 9:2) Koma kodi Yesu akanathadi kukhululukira anthu machimo? Alembi ndi Afarisi anakhumudwa ndi zimene Yesu ananena ndipo anayamba kuganiza kuti: “N’chifukwa chiyani munthu ameneyu akulankhula chonchi? Akunyoza Mulungu ameneyu. Ndaninso wina amene angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?”—Maliko 2:7.

Yesu atadziwa maganizo awo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi m’mitima mwanu? Chapafupi n’chiti, kuuza wakufa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo nyamula machira ako uyende’?” (Maliko 2:8, 9) Yesu anatha kukhululukira machimo a wodwalayo chifukwa cha nsembe imene anali kudzapereka m’tsogolo.

Kenako Yesu ananena mawu omwe anathandiza gulu lonse la anthuwo, kuphatikizapo amene ankamutsutsa, kudziwa kuti ndi iye yekha padziko lapansi amene akhoza kukhululukira anthu machimo awo. Ndiyeno Yesu anatembenukira kwa wodwala uja n’kumuuza kuti: “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa, uzipita kwanu.” Nthawi yomweyo munthuyo anaimirira n’kuyamba kuyenda atanyamula machirawo anthu onse akuona. Anthuwo anadabwa kwambiri ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Zoterezi sitinazionepo.”—Maliko 2:11, 12.

N’zochititsa chidwi kuti Yesu anasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa uchimo ndi matenda komanso kuti kukhululukidwa kwa machimo n’kogwirizana ndi thanzi la munthu. Baibulo limatiuza kuti Adamu yemwe ndi kholo lathu loyamba anachimwa ndipo tonsefe tinatengera mavuto amene amayamba chifukwa cha uchimo. Ena mwa mavuto amenewa ndi matenda komanso imfa. Koma Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, Yesu adzakhululukira machimo anthu onse amene amatumikira komanso kukonda Mulungu. Zimenezi zidzachititsa kuti anthu onse asadzadwalenso.—Aroma 5:12, 18, 19.