Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 116

Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza

Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza

MATEYU 26:20 MALIKO 14:17 LUKA 22:14-18 YOHANE 13:1-17

  • YESU ANADYA PASIKA WAKE WOMALIZA NDI ATUMWI

  • ANASAMBITSA MAPAZI A OPHUNZIRA AKE POFUNA KUWAPHUNZITSA MFUNDO YOFUNIKA

Petulo ndi Yohane anafika mwamsanga ku Yerusalemu kuti akakonzekere mwambo wa Pasika. Kenako Yesu ndi ophunzira ake ena 10 anawatsatira. Madzulo dzuwa likulowa, Yesu ndi ophunzira ake anatsika m’phiri la Maolivi kupita ku Yerusalemu. Limeneli linali tsiku lomaliza kuti Yesu aone dzuwa likulowa ndipo anadzalionanso ataukitsidwa.

Kenako Yesu ndi ophunzira ake aja analowa mumzinda ndipo anapita kunyumba imene anakadyerako Pasika. Atafika ku nyumbayi anakwera masitepe n’kupita m’chipinda chapamwamba. Atalowa m’chipindamo anapeza kuti zonse zofunika pa mwambowu zakonzedwa kale. Yesu ankayembekezera kupezeka pa mwambo umenewu chifukwa ananena kuti: “Ndinali wofunitsitsa kudya pasika uyu limodzi ndi inu ndisanalowe m’masautso.”—Luka 22:15.

Zaka zambiri m’mbuyomo, anthu anali atayambitsa mwambo woyendetsa makapu angapo kwa anthu amene apezeka pa mwambo wa Pasika. Ndiyeno Yesu atalandira imodzi mwa makapuwo, anayamika kenako ananena kuti: “Landirani kapu iyi, nonse imwani mopatsirana. Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utafika.” (Luka 22:17, 18) Pamene ananena mawu amenewa zinaonekeratu kuti imfa yake yayandikira.

Mwambo wa Pasika uli mkati Yesu anachita chinthu china chodabwitsa kwambiri. Anaimirira n’kuvula malaya ake akunja ndi kutenga thaulo. Kenako anathira madzi m’beseni limene linali chapafupi. Nthawi imeneyo munthu akalandira alendo ankaonetsetsa kuti wantchito wake wasambitsa mapazi a alendowo. (Luka 7:44) Koma chifukwa chakuti mwiniwake wa nyumbayo panalibe, Yesu ndi amene anagwira ntchito imeneyi. Aliyense wa atumwiwo akanatha kugwira ntchitoyi koma palibe amene anadzipereka mwina chifukwa chakuti ankakanganabe kuti wamkulu ndani. Ophunzirawo ayenera kuti anachita manyazi Yesu atayamba kuwasambitsa mapazi.

Atafika pamene panali Petulo, Petulo anakana kuti Yesu amusambitse mapazi. Iye ananena kuti: “Ndithu, sizitheka kuti inu musambitse mapazi anga.” Yesu anamuuza kuti: “Ndikapanda kukusambitsa, palibe chako kwa ine.” Ndiyeno Petulo anayankha ndi mtima wonse kuti: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, komanso manja ndi mutu womwe.” Petulo ayenera kuti anadabwa ndi zimene Yesu ananena chifukwa anati: “Amene wasamba m’thupi amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.”—Yohane 13:8-10.

Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake onse 12 kuphatikizapo Yudasi Isikariyoti. Atamaliza kuwasambitsa mapazi, anavala malaya ake akunja aja ndipo anakhalanso pansi. Kenako anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene ndachita kwa inu? Inu mumanditcha kuti ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Ambuye,’ mumalondola, pakuti ndinedi. Choncho ngati ine, wokhala Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi. Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi. Ndithudi ndikukuuzani, Kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma. Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.”—Yohane 13:12-17.

Pamenepatu Yesu anaphunzitsa otsatira ake khalidwe la kudzichepetsa. Choncho wotsatira aliyense wa Yesu ayenera kupewa mtima wofuna kukhala pa malo apamwamba poganiza kuti iyeyo ndi wofunika kwambiri kuposa anzake ndiponso kuti ena azimutumikira. M’malomwake ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu, osati posambitsa anthu ena mapazi, koma pokhala wofunitsitsa kutumikira ena modzichepetsa ndiponso mosakondera.