Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 135

Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri

Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri

LUKA 24:13-49 YOHANE 20:19-29

  • YESU ANAONEKERA PA MSEWU WOPITA KU EMAU

  • ANAPITIRIZA KUFOTOKOZERA OPHUNZIRA AKE MALEMBA

  • TOMASI ANASIYA KUKAYIKIRA

Pofika Lamlungu pa Nisani 16, ophunzira a Yesu anali ndi chisoni chachikulu. Iwo sankamvetsabe kuti n’chifukwa chiyani sanapeze thupi la Yesu m’manda muja. (Mateyu 28:9, 10; Luka 24:11) Tsiku lomwelo, ophunzira awiri ankachoka mumzinda wa Yerusalemu kupita kumudzi wa Emau, womwe unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 11 kuchokera ku Yerusalemu. Mmodzi wa ophunzirawa dzina lake anali Keleopa.

Ali m’njira ankakambirana zimene zinachitikazo. Kenako anakumana ndi munthu wina ndipo anayamba kuyenda naye limodzi. Munthuyo anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zanji zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?” Keleopa anamufunsa kuti: “Kodi iwe ukukhala wekhawekha m’Yerusalemu monga mlendo, moti sukudziwa zimene zachitika mmenemo m’masiku amenewa?” Munthuyo anafunsanso kuti: “Zinthu zotani?”—Luka 24:17-19.

Ophunzirawo anamuyankha kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti, . . . ife tinali kuyembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.”—Luka 24:19-21.

Kenako Keleopa ndi wophunzira winayo anayamba kufotokozera munthu uja zimene zinachitika tsiku limenelo. Iwo anamuuza kuti azimayi ena anapita kumanda a Yesu koma thupi lake sanakalipezeko ndiponso kuti azimayiwo anaona angelo omwe anawauza kuti Yesu waukitsidwa. Anauzanso munthuyo kuti anthu ena anapita kumandako ndipo “anapezadi kuti zili momwemo, mmene amayiwo ananenera.”—Luka 24:24.

Ophunzira awiriwo ankaoneka kuti sakumvetsa komanso asokonezeka ndi zimene zachitikazo. Koma munthuyo anawalankhula mwamphamvu ndipo anawathandiza kusintha maganizo awo olakwika, omwe anawachititsanso kuti akhale okhumudwa kwambiri. Munthuyo anawauza kuti: “Opanda nzeru inu ndi okayikakayika pa zonse zimene aneneri ananena! Kodi sikunali kofunikira kuti Khristu amve zowawa zonsezi ndi kulowa mu ulemerero wake?” (Luka 24:25, 26) Anawafotokozeranso Malemba ambiri omwe ankanena za Khristu.

Atatsala pang’ono kufika m’mudzi wa Emau, ophunzira awiri aja ankafuna kumva zambiri, choncho anauza munthu uja kuti: “Tiyeni tikhalebe limodzi, chifukwa kunja kwayamba kuda ndipo tsiku latha kale.” Munthu uja analola ndipo atalowa m’mudzimo anadyera limodzi chakudya. Pamene ankadya chakudyacho, munthu uja anapemphera, kutenga mkate n’kuunyemanyema kenako anawapatsa kuti adye. Atangochita zimenezi, ophunzirawo anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu, koma kenako anazimiririka. (Luka 24:29-31) Tsopano anali ndi umboni woti Yesu waukitsidwadi.

Ophunzirawa anasangalala kwambiri moti anayamba kukambirana zimene zinachitikazo kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” (Luka 24:32) Kenako anabwereranso ku Yerusalemu ndipo atafika kumeneko anapeza atumwi alinso ndi anthu ena. Keleopa asanayambe n’komwe kufotokoza zimene zinawachitikira anamva anthu enanso akunena kuti: “N’zoonadi, Ambuye wauka kwa akufa ndipo waonekera kwa Simoni!” (Luka 24:34) Keleopa ndi wophunzira wina uja anafotokozanso zimene zinawachitikira. Nawonso anali ngati mboni chifukwa anaona ndi maso awo kuti Yesu waukadi.

Koma kenako panachitika chinthu chodabwitsa kwambiri. Yesu anaonekera m’chipinda chomwecho. Zimenezi zinali zodabwitsa chifukwa zitseko zonse zinali zokhoma. Anthuwo anadzikhomera m’nyumba chifukwa choopa Ayuda. Anthu onse omwe anali m’chipindamo anaona Yesu. Iye anawauza modekha kuti: “Mtendere ukhale nanu.” Anthuwo anachita mantha chifukwa ‘ankaganiza kuti aona mzimu,’ ngati mmene anachitira pa nthawi imene Yesu anayenda panyanja ija.—Luka 24:36, 37; Mateyu 14:25-27.

Pofuna kuwathandiza ophunzirawo kudziwa kuti sanali mzimu koma munthu, Yesu anawaonetsa manja ndi mapazi ake n’kuwauza kuti: “N’chifukwa chiyani mukuvutika maganizo? Bwanji mukukayikakayika m’mitima yanu? Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone, chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa ngati anga amene mukuwaonawa.” (Luka 24:36-39) Anthuwo anasangalala kwambiri komanso kudabwa, komabe ankakayikira pang’ono.

Pofuna kuwathandiza kuti asiye kukayikira, Yesu anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” Anamupatsa kachidutswa ka nsomba yowotcha ndipo anadya. Kenako anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi [ndisanafe] ndinakuuzani mawu akuti, zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo ziyenera kukwaniritsidwa.”—Luka 24:41-44.

Yesu ataonekera kwa Keleopa ndi wophunzira wina uja anawathandiza kumvetsa Malemba. Ndipo zimenezi ndi zimene ankachitanso pa nthawiyi. Iye anauza anthu onse omwe anali m’chipindamo kuti: “Mmene zachitikiramu ndi mmene zinalembedwera kuti Khristu adzazunzika ndi kuuka kwa akufa tsiku lachitatu, ndipo pa maziko a dzina lake, m’mitundu yonse mudzalalikidwa za kulapa kuti machimo akhululukidwe. Kuyambira ku Yerusalemu inu mudzakhala mboni za zimenezi.”—Luka 24:46-48.

Pa gulu la anthu amene anasonkhana m’chipindacho panalibe Tomasi. Koma anthu omwe analipowo atakumana naye anamuuza mosangalala kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Tomasi anayankha kuti: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo, ine sindikhulupirira ayi.”—Yohane 20:25.

Patatha masiku 8, ophunzira anakumana m’chipinda china ndipo anakhomanso zitseko zonse. Koma pa nthawiyi Tomasi analipo. Yesu anaonekeranso ali ndi thupi ngati munthu ndipo anawapatsa moni kuti: “Mtendere ukhale nanu.” Kenako Yesu anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa, ndiponso ona m’manja mwangamu. Gwiranso ndi dzanja lako m’mbali mwa mimba yangamu, kuti usakhalenso wosakhulupirira.” Koma Tomasi ananena kuti: “Mbuyanga ndi Mulungu wanga!” (Yohane 20:26-28) Tsopano Tomasi anakhulupirira kuti Yesu waukitsidwadi ndi thupi lauzimu ndipo akuimira Yehova Mulungu.

Yesu anamuuza kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Odala ndi amene amakhulupirira ngakhale sanaone.”—Yohane 20:29.