Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 104

Kodi Ayuda Anakhulupirira Yesu Atamva Mulungu Akulankhula?

Kodi Ayuda Anakhulupirira Yesu Atamva Mulungu Akulankhula?

YOHANE 12:28-50

  • ANTHU AMBIRI ANAMVA MAWU A MULUNGU

  • ZIMENE ZIDZACHITITSE KUTI ANTHU AWERUZIDWE

Pamene Yesu anali kukachisi, Lolemba pa Nisani 10, ananena za imfa yake. Chifukwa chodera nkhawa mmene imfa yake idzakhudzire dzina la Mulungu, Yesu ananena kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Kenako panamveka mawu amphamvu ochokera kumwamba omwe anayankha zimene Yesu ananena kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”—Yohane 12:27, 28.

Anthu amene anali pafupi anadabwa kwambiri. Ena ankaganiza kuti amva kugunda kwa bingu pomwe ena ananena kuti: “Mngelo walankhula naye.” (Yohane 12:29) Koma anthuwo anali atamva Yehova akulankhula. Kameneka sikanali koyamba kuti anthu amve Mulungu akulankhula zinthu zokhudza Yesu.

Zaka zitatu ndi hafu m’mbuyomo, pa nthawi ya ubatizo wa Yesu, Yohane M’batizi anamva Mulungu akulankhula za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” Kenako mwambo wa Pasika wa mu 32 C. E. utachitika, Yesu anasandulika ndipo zimenezi zinachitika Yakobo, Yohane ndi Petulo akuona. Pa nthawiyi anthu atatuwa anamva Mulungu akulankhula kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” (Mateyu 3:17; 17:5) Koma pa nthawi yachitatuyi m’pamene anthu ambiri anamva Yehova akulankhula.

Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Sikuti mawu amenewa amveka chifukwa cha ine ayi, koma chifukwa cha inu.” (Yohane 12:30) Choncho mawu a Mulunguwa anatsimikizira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu yemwenso ndi Mesiya amene anthu ankamuyembekezera.

Yesu anakhala wokhulupirika pa nthawi yonse imene anali ndi moyo padziko lapansi. Chifukwa cha zimenezi anapereka chitsanzo kwa anthu komanso anatsimikizira kuti Satana Mdyerekezi, yemwe ndi wolamulira wa dzikoli, ayenera kuwonongedwa. Yesu ananena kuti: “Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja tsopano.” Imfa ya Yesu siinasonyeze kuti wagonjetsedwa ndi Satana koma inasonyeza kuti wapambana. Tikutero chifukwa Yesuyo anafotokoza kuti: “Koma ine ndikadzakwezedwa m’mwamba padziko lapansi, ndidzakokera anthu osiyanasiyana kwa ine.” (Yohane 12:31, 32) Imfa ya Yesu inachititsa kuti Yesuyo akoke anthu ambiri ndipo zimenezi zinatsegulira anthuwo mwayi woti adzapeze moyo wosatha.

Yesu atanena zoti ‘adzakwezedwa m’mwamba,’ anthuwo anati: “Ife tinamva m’Chilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha. Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu adzakwezedwa m’mwamba? Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?” (Yohane 12:34) Anthu ambiri sanavomereze kuti Yesu ndi Mwana weniweni wa munthu kapena kuti Mesiya amene Mulungu analonjeza. Iwo sanavomereze zimenezi ngakhale kuti panali umboni wokwanira komanso kuti anamva Mulungu akulankhula.

Yesu ananenanso kuti iye ndi “kuwala” ngati mmene ananenera nthawi ina m’mbuyomo. (Yohane 8:12; 9:5) Iye anauza anthuwo kuti: “Kuwala kukhalabe pakati panu kanthawi pang’ono. Yendani pamene kuwalako mudakali nako, kuti mdima usakugwereni, . . . Pamene kuwala mudakali nako, sonyezani chikhulupiriro mwa kuwalako, kuti mukhale ana ake a kuwala.” (Yohane 12:35, 36) Yesu atangolankhula zimenezi anachoka chifukwa nthawi yoti aphedwe inali isanakwane. Tsikuli linali Nisani 10 ndipo Yesu ankayenera ‘kukwezedwa m’mwamba’ kapena kuti kupachikidwa pamtengo pa nthawi ya Pasika pa Nisani 14.—Agalatiya 3:13.

Pa nthawi yonse imene Yesu ankachita utumiki wake Ayuda ambiri sanafune kumukhulupirira ndipo zimenezi zinkakwaniritsa ulosi umene Yesaya analemba. Yesaya ananeneratu kuti maso a anthu adzachita khungu ndipo mitima yawo idzauma moti anthuwo sadzatembenuka n’kuchira. (Yesaya 6:10; Yohane 12:40) Ayuda ambiri anakana kwa mtuwagalu umboni wotsimikizira kuti Yesu ndiye Mpulumutsi amene analonjezedwa komanso kuti iye ndiye njira yopezera moyo.

Panali anthu ena ngati Nikodemo, Yosefe wa ku Arimateya komanso olamulira ena ambiri amene ‘anakhulupirira’ Yesu. Koma kodi anthu amenewa anachitadi zinthu zosonyeza kuti ankakhulupiriradi Yesu kapena anabwerera m’mbuyo mwina chifukwa choopa kuchotsedwa m’sunagoge kapena chifukwa ‘chokonda kwambiri ulemerero wa anthu’?—Yohane 12:42, 43.

Yesu anafotokoza zimene zimachitika ngati munthu wayamba kumukhulupirira. Iye anati: “Wokhulupirira ine sakhulupirira ine ndekha, komanso amakhulupirira iye amene anandituma ine. Amene wandiona ine waonanso amene anandituma.” Mfundo zimene Mulungu anauza Yesu kuti aphunzitse komanso zimene anapitiriza kulalikira zinali zofunika kwambiri moti Yesuyo ananena kuti: “Aliyense wondinyalanyaza ndi kusalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza.”—Yohane 12:44, 45, 48.

Kenako Yesu anamaliza ndi kunena kuti: “Sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula. Komanso ndikudziwa kuti lamulo lake limatanthauza moyo wosatha.” (Yohane 12:49, 50) Yesu ankadziwa kuti sipapita nthawi yaitali asanapereke moyo wake ngati nsembe yoombola anthu amene amamukhulupirira.—Aroma 5:8, 9.