Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 105

Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro

Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro

MATEYU 21:19-27 MALIKO 11:19-33 LUKA 20:1-8

  • ANAPHUNZIRA KUFUNIKA KOKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO CHIFUKWA CHA MTENGO WA MKUYU UMENE UNAFOTA

  • ANTHU ANAFUNSA YESU KUMENE ANKATENGA ULAMULIRO WOCHITIRA ZINTHU

Lolemba masana Yesu anachoka ku Yerusalemu n’kubwerera ku Betaniya, mzinda womwe unali m’mphepete mwa phiri la Maolivi chakum’mawa. Mosakayikira anakagona kunyumba kwa Lazaro, Mariya ndi Marita omwe anali anzake.

Tsiku lotsatira pa Nisani 11 m’mawa, Yesu ndi ophunzira ake anayambanso ulendo wopita ku Yerusalemu kukachisi. Kameneka kanali komaliza kuti Yesu akapezeke pakachisi komanso linali tsiku lake lomaliza kuti alalikire poyera. Kenako patapita masiku ochepa anachita mwambo wa Pasika, anakhazikitsa mwambo wokumbukira imfa yake, anaimbidwa mlandu ndipo pamapeto pake anaphedwa.

Ali m’njira popita ku Yerusalemu, Petulo anaona mtengo womwe Yesu anautemberera chadzulo lake ndipo ananena kuti: “Rabi, onani! mkuyu umene munautemberera uja wafota.”—Maliko 11:21.

Koma n’chifukwa chiyani Yesu anachititsa kuti mtengowu ufote? Zimene Yesu ananena zimatithandiza kudziwa yankho la funso limeneli. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro, osakayika, mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzachitikadi. Chinthu chilichonse chimene mudzapempha m’mapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.” (Mateyu 21:21, 22) Pamenepa Yesu ankabwereza mfundo imene anali atanenapo kale m’mbuyomu kuti ngati munthu atakhala ndi chikhulupiriro akhoza kusuntha phiri.—Mateyu 17:20.

Choncho pamene Yesu anachititsa kuti mtengowo ufote, anaphunzitsa anthu za kufunika kokhulupirira Mulungu. Iye ananenanso kuti: “Pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.” (Maliko 11:24) Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri kwa anthu onse amene amatsatira Yesu. Inalinso yothandiza kwambiri kwa atumwi amene anali atatsala pang’ono kukumana ndi mavuto aakulu. Zimene Yesu anachita pochititsa kuti mtengowo ufote zinasonyezanso kufunika kokhala ndi chikhulupiriro champhamvu.

Mofanana ndi mmene mtengo wamkuyu uja unkaonekera, ndi mmenenso mtundu wa Isiraeli unalili. Aisiraeli anachita pangano ndi Mulungu ndipo zinkaoneka ngati ankatsatira Chilamulo. Koma mtundu umenewu unalibe chikhulupiriro ndiponso sunkabala zipatso zabwino. Iwo anafika mpaka pokana Mwana wa Mulungu. Choncho pamene Yesu anachititsa kuti mtengo wa mkuyu umene sunkabala zipatso uja ufote, anasonyeza zimene zidzachitikire mtunduwu womwe unalibe chikhulupiriro komanso umene sunkabala zipatso.

Pasanapite nthawi yaitali, Yesu ndi ophunzira ake anafika ku Yerusalemu. Monga mwa chizolowezi chake Yesu anakalowa m’kachisi n’kuyamba kuphunzitsa. Ansembe aakulu komanso akulu atakumbukira zimene Yesu anachitira anthu osintha ndalama chadzulo lake, anamufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani anakupatsani ulamuliro umenewu?”—Maliko 11:28.

Yesu anayankha kuti: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zinthu zimenezi. Kodi ubatizo wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu? Ndiyankheni.” Yesu atawafunsa zimenezi nkhani inawatembenukira. Ansembe komanso akulu anayamba kukambirana zoti amuyankhe. Iwo ankafunsana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ Koma nanga tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthu’ ngati?” . . . Anali kuopa khamu la anthu, chifukwa anthu onsewo anali kukhulupirira kuti Yohane analidi mneneri.”—Maliko 11:29-32.

Anthu amene ankatsutsa Yesu analephera kupeza yankho lolondola moti anangomuyankha kuti: “Sitikudziwa.” Nayenso Yesu powayankha ananena kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”—Maliko 11:33.