Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 14

Yesu Anayamba Kupeza Ophunzira

Yesu Anayamba Kupeza Ophunzira

YOHANE 1:29-51

  • ANTHU OYAMBIRIRA KUKHALA OPHUNZIRA A YESU

Yesu atakhala masiku 40 m’chipululu anapitanso kwa Yohane amene anam’batiza uja. Pamene Yesu ankamuyandikira, Yohane anamuloza n’kuuza anthu amene anali nawo kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko! Uyu ndi amene ndinali kunena uja kuti, ‘M’mbuyo mwanga mukubwera munthu wina amene wandipitirira ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’” (Yohane 1:29, 30) Ngakhale kuti Yohane anali wamkulu kwa Yesu, ankadziwa kuti Yesu anakhalako kumwamba ndi thupi lauzimu iye asanabadwe.

Kutatsala milungu ingapo Yesu asanapite kwa Yohane kuti akamubatize, Yohane anali asanatsimikize kuti Yesu ndi amene adzakhale Mesiya. Yohane ananena kuti: “Inenso sindinali kumudziwa, koma chimene ndikubatizira anthu m’madzi n’chakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”—Yohane 1:31.

Kenako Yohane anapitiriza kufotokozera anthu zimene zinachitika pamene ankabatiza Yesu. Iye anati: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba, ndipo unakhalabe pa iye. Inenso sindinali kumudziwa, koma Amene anandituma kudzabatiza m’madzi anandiuza kuti, ‘Ukadzaona mzimu ukutsika ndi kukhazikika pa munthu wina, ameneyo ndiye wobatiza ndi mzimu woyera.’ Ndipo ine ndaonadi zimenezo, ndachitira umboni ndithu kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”—Yohane 1:32-34.

Tsiku lotsatira, Yesu anapitanso kwa Yohane ndipo pa nthawiyi Yohane anali ndi ophunzira ake awiri. Ndiyeno Yohane ananena kuti: “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu.” (Yohane 1:36) Atangonena zimenezi, ophunzira awiri a Yohane aja anayamba kuyenda ndi Yesu. Mmodzi wa ophunzirawo dzina lake anali Andireya. Ndipo n’kutheka kuti wophunzira winayo ndi amenenso analemba nkhani zimenezi ndipo dzina lake anali Yohane. Zikuonekanso kuti Yohane ameneyu anali m’bale wake wa Yesu chifukwa anali mwana wa Salome. Salome anali mchemwali wake wa Mariya ndipo mwamuna wake anali Zebedayo.

Yesu atatembenuka n’kuona Andireya ndi Yohane akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?”

Iwo anamufunsa kuti: “Rabi, kodi mukukhala kuti?”

Yesu anawayankha kuti: “Tiyeni mukaoneko.”—Yohane 1:37-39.

Andireya ndi Yohane anakhala ndi Yesu tsiku lonse. Cha m’ma 4 koloko madzulo, Andireya anakumana ndi m’bale wake Simoni, yemwe ankadziwikanso kuti Petulo, ndipo mosangalala anamuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.” (Yohane 1:41) Andireya anatengana ndi Petulo n’kupita kwa Yesu. Zinthu zinanso zimene zinachitika pambuyo pake zimasonyeza kuti nayenso Yohane anakumana ndi m’bale wake Yakobo ndipo anapita naye kwa Yesu. Koma Yohane sanafotokoze zimenezi m’nkhani imene analemba.

Tsiku lotsatira, Yesu anakumana ndi Filipo wa ku Betsaida. Mzinda wa Betsaida unali kumpoto kwa nyanja ya Galileya ndipo n’kumene kunali kwawo kwa Andireya ndi Petulo. Yesu anauza Filipo kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”—Yohane 1:43.

Kenako Filipo anakumana ndi Natanayeli, yemwe ankadziwikanso kuti Batolomeyo, ndipo anamuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri, ife tam’peza. Iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe, wa ku Nazareti.” Natanayeli anakayikira zimenezi ndipo anafunsa Filipo kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?”

Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.” Yesu ataona Natanayeli akubwera, ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”

Pamenepo Natanayeli anafunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?”

Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona, muja unali pansi pa mkuyu paja.”

Natanayeli anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Rabi, ndinudi Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Isiraeli.”

Kenako Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mkuyu? Udzaona zazikulu kuposa izi.” Yesu anawatsimikiziranso ophunzirawo kuti: “Ndithudi ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsikira kwa Mwana wa munthu.”—Yohane 1:45-51.

Pasanapite nthawi yaitali zimenezi zitangochitika, Yesu pamodzi ndi ophunzira ake, omwe anali atangowapeza kumenewo, anachoka ku Yorodano n’kupita ku Galileya.