Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 15

Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita

Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita

YOHANE 2:1-12

  • UKWATI UMENE UNACHITIKA KU KANA

  • YESU ANASANDUTSA MADZI KUKHALA VINYO

Yesu pamodzi ndi ena mwa ophunzira ake analowera chakumpoto ku Galileya patangodutsa masiku atatu kuchokera pamene Natanayeli anakhala mmodzi wa ophunzira ake oyambirira. Iwo ankapita ku tauni ya Kana komwe kunali kwawo kwa Natanayeli. Tauni ya Kana inali m’dera la mapiri kumpoto kwa mzinda wa Nazareti, kumene Yesu anakulira. Iwo ankapita kumeneko chifukwa anali ataitanidwa ku phwando la ukwati.

Mariya, yemwe anali amayi ake a Yesu, anapitanso ku ukwatiwo. Zikuoneka kuti Mariya ankadziwana ndi amene ankakwatiranawo ndipo ayenera kuti ankathandiza nawo ntchito yolandira komanso kusamalira alendo. N’chifukwa chake anazindikira mwamsanga kuti zinthu zina zinali zitatha ndipo anauza Yesu kuti: “Vinyo waathera.”—Yohane 2:3.

Ponena mawu amenewa, Mariya ankafuna kuti Yesu athandizepo. Poyankha, Yesu anagwiritsa ntchito mawu okuluwika osonyeza kuti akukana. Iye anati: “Kodi ndili nanu chiyani mayi?” (Yohane 2:4) Monga Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, cholinga cha Yesu chinali kuchita zimene Atate wake wakumwamba wamuuza, osati zimene abale ake kapena anzake amuuza. Mariya anangosiya nkhaniyi m’manja mwa mwana wake ndipo anauza anthu amene ankatumikira pa ukwatiwo kuti: “Chilichonse chimene angakuuzeni, chitani chimenecho.”—Yohane 2:5.

Pamalopo panali mbiya zamiyala zokwana 6 ndipo mbiya iliyonse inkatha kusunga madzi okwana malita 40. Yesu anauza anthu amene ankagwira ntchito pa ukwatipo kuti: “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Kenako anawauza kuti: “Tunganimo tsopano mupereke kwa woyang’anira phwandoli.”—Yohane 2:7, 8.

Woyang’anira phwandoyo anasangalala kwambiri atalawa vinyoyo chifukwa anali wokoma kwambiri koma sanadziwe kuti vinyoyo anali atapangidwa mozizwitsa. Choncho anaitana mkwati n’kumuuza kuti: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino choyamba, ndipo anthu akaledzera, m’pamene amatulutsa wosakoma kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.”—Yohane 2:10.

Chimenechi chinali chozizwitsa choyamba chimene Yesu anachita. Ophunzira akewo ataona zimene Yesu anachitazi, anayamba kumukhulupirira kwambiri. Kenako Yesu, mayi ake ndi abale ake ananyamuka n’kupita ku Kaperenao, mzinda womwe unali m’mbali mwa nyanja ya Galileya, kumpoto chakumadzulo.