Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

Yesu Anakulira Ku Nazareti

Yesu Anakulira Ku Nazareti

MATEYU 13:55, 56 MALIKO 6:3

  • BANJA LA YOSEFE NDI MARIYA LINAKULA

  • YESU ANAPHUNZITSIDWA NTCHITO YAMANJA

Yesu anakulira ku Nazareti, womwe unali mzinda waung’ono kwambiri komanso wosadziwika kwa anthu ambiri. Mzindawu unali kumpoto kwa Yudeya, m’dera la mapiri lotchedwa Galileya, chakumadzulo kwa nyanja ya Galileya.

Mwina Yesu anali ndi zaka ziwiri pamene ankachoka ku Iguputo. Zikuonekanso kuti pa nthawi imeneyo iye anali mwana yekhayo m’banjali. Koma patapita nthawi, Yosefe ndi Mariya anakhalanso ndi ana ena aamuna ndi aakazi ndipo aamunawo mayina awo anali Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yuda. Choncho, Yesu anali ndi abale ake mwina okwana 6.

Yesu analinso ndi achibale ena. Tikudziwapo kale za Elizabeti komanso mwana wake wamwamuna, dzina lake Yohane, omwe ankakhala ku Yudeya. Komanso ku Galileya komweko kunali mchemwali wake wa Mariya, dzina lake Salome. Ndiye kuti Salome anali anti ake a Yesu. Mwamuna wake wa Salome anali Zebedayo. Iwo anali ndi ana aamuna awiri omwe mayina awo anali Yakobo ndi Yohane. Sitikudziwa ngati Yesu ankacheza kwambiri ndi Yakobo ndi Yohane pa nthawi imene ankakula, koma atakula anadzakhala anzake apamtima chifukwa anadzakhala m’gulu la atumwi ake.

Yosefe ankafunika kugwira ntchito mwakhama kuti azisamalira banja lake. Iye anali kalipentala ndipo chifukwa chakuti Yosefe ankalera Yesu ngati mwana wake weniweni, Yesuyo ankadziwika kuti “mwana wa mmisiri wamatabwa.” (Mateyu 13:55) Yosefe anaphunzitsanso Yesu ntchito ya ukalipentala ndipo anaidziwa bwino ntchitoyi moti pofotokoza za Yesu anthu ankati ndi “mmisiri wamatabwa.”—Maliko 6:3.

Banja la Yosefe linkakonda kulambira Yehova. Yosefe ndi Mariya ankaphunzitsa ana awo zinthu zauzimu potsatira zimene Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti aziwaphunzitsa ‘akakhala pansi m’nyumba mwawo, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 6:6-9) Ku Nazareti kunalinso sunagoge. Choncho, Yosefe ayenera kuti ankapita ndi banja lake lonse kumeneko kuti akalambire. Ndipo Yesu anapitiriza kuchita zimene atakula chifukwa Malemba amanena kuti “malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata,” anapita ku sunagoge. (Luka 4:16) Banjali linkasangalalanso ndi maulendo opita kukachisi wa Yehova ku Yerusalemu.