Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

Mulungu Analenga Anthu Awiri Oyamba

Mulungu Analenga Anthu Awiri Oyamba

Yehova anakonza munda wa Edeni. M’mundamu munali maluwa ndi mitengo yambiri. Munalinso nyama zosiyanasiyana. Kenako anatenga dothi n’kuumba munthu dzina lake Adamu. Iye anauzira mpweya m’mphuno mwa Adamuyo. Ukudziwa zimene zinachitika? Munthuyo anakhala wamoyo. Anamuuza kuti aziyang’anira mundawo komanso kuti nyama iliyonse aipatse dzina.

Koma Yehova anamupatsanso lamulo lofunika kwambiri lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya, kupatula za mtengo umodzi wokha. Ukadzadya zipatso za mtengo umenewu udzafa.’

Kenako Yehova ananena kuti: ‘Ndikufuna ndipange mnzake wa Adamu.’ Ndiyeno anamugonetsa kwambiri Adamuyo. Kenako anamuchotsa nthiti ndipo anagwiritsa ntchito nthitiyo n’kumupangira mkazi. Mkaziyo dzina lake anali Hava. Choncho Adamu ndi Hava anali banja loyamba. Kodi Adamu anamva bwanji Mulungu atamupangira mkazi? Anakondwera kwambiri moti ananena kuti: ‘Ndikusangalala kwambiri kuti Yehova wagwiritsa ntchito nthiti yanga n’kundipangira mkazi. Tsopano ndapeza mnzanga.’

Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti akhale ndi ana ndipo adzaze dziko lapansi. Ankafuna kuti anthuwo azigwira ntchito limodzi mosangalala n’kukonza dziko lonse kuti likhale paradaiso wokongola ngati munda wa Edeni. Koma zinthu sizinayende mmene Yehova ankafunira. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Tidzakambirana m’mutu wotsatira.

“Amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi.”​—Mateyu 19:4