Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 61

Anakana Kulambira Fano

Anakana Kulambira Fano

Patadutsa nthawi kuchokera pamene Mfumu Nebukadinezara analota, anapanga fano lalikulu la golide. Fanoli analiimika m’chigwa cha Dura ndipo anaitana anthu onse a maudindo akuluakulu m’boma kuphatikizapo Sadirake, Mesake ndi Abedinego. Anthuwo atasonkhana, mfumu inalamula kuti: ‘Mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira, mugwade ndi kulambira fanoli. Aliyense amene sagwadira fanoli aponyedwa mung’anjo ya moto.’ Kodi anyamata atatu achiheberiwo anatani? Kodi analola kugwadira fanolo kapena anatsimikiza kulambira Yehova yekha?

Kenako mfumu inalamula kuti nyimbo iyambe. Aliyense anagwada ndi kulambira fano lija. Koma Sadirake, Mesake ndi Abedinego sanagwade. Anthu ena ataona, anauza mfumu kuti: ‘Anyamata atatu achiheberiwa akukanatu kulambira fanoli.’ Nebukadinezara anaitanitsa anyamatawo n’kuwauza kuti: ‘Ndikupatsani mwayi wina woti mulambire fanoli. Ngati simulambira ndikuponyani mung’anjo ya moto ndipo palibe mulungu amene angakupulumutseni m’manja mwanga.’ Iwo anayankha kuti: ‘Musavutike n’kutipatsa mwayi wina. Mulungu wathu akhoza kutipulumutsa. Koma ngati satipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sitingalambire fano lanuli.’

Nebukadinezara atamva zimenezi, anapsa mtima kwambiri. Iye anauza anthu kuti: ‘Sonkhezerani ng’anjo kuwirikiza ka 7 kuti ikhale yotentha kuposa mmene imakhalira!’ Ndiyeno analamula asilikali ake kuti: ‘Amangeni ndipo muwaponye mung’anjomo!’ Ng’anjoyo inali itatentha kwambiri moti asilikaliwo atangoyandikira, anafa nthawi yomweyo. Aheberi atatu aja anaponyedwadi mung’anjomo. Nebukadinezara atasunzumira, anaona kuti mung’anjo muja munali anthu 4 osati atatu. Ataona izi, anachita mantha kwambiri ndipo anafunsa nduna zake kuti: ‘Kodi si paja tinaponya anthu atatu m’motomu? Inetu ndikuonamo anthu 4, ndipo winayo akuoneka ngati mngelo!’

Kenako Nebukadinezara anafika pafupi ndi ng’anjo ija n’kufuula kuti: ‘Tulukani inu atumiki a Mulungu wam’mwambamwamba!’ Anthu onse anadabwa kuona Sadirake, Mesake ndi Abedinego akutuluka osapsa paliponse. Khungu, tsitsi komanso zovala zawo sizinapse ndiponso sankamveka fungo lamoto.

Ndiyeno Nebukadinezara anati: ‘Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego. Anatumiza mngelo wake kudzawapulumutsa. Palibe mulungu wina wofanana naye.’

Kodi iweyo ungakhale wokhulupirika kwa Yehova ngakhale utakumana ndi mavuto, ngati mmene anachitira anyamata achiheberi atatuwa?

“Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”​—Mateyu 4:10