Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 73

Yohane Anakonza Njira

Yohane Anakonza Njira

Paja Yohane anali mwana wa Zekariya ndi Elizabeti. Iye atakula anakhala mneneri. Yehova anagwiritsa ntchito Yohane pophunzitsa anthu kuti Mesiya akubwera. Yohane sankaphunzitsa m’masunagoge kapena m’tauni koma ankalalikira m’chipululu. Anthu ochokera ku Yerusalemu komanso ku Yudeya konse ankapita kwa Yohane kuti akawaphunzitse. Iye ankawaphunzitsa kuti ayenera kusiya zoipa kuti asangalatse Mulungu. Anthu ambiri akamva uthenga wakewu, ankalapa ndipo iye ankawabatiza mumtsinje wa Yorodano.

Yohane sankakonda chuma. Ankangovala chovala chaubweya wa ngamila ndipo ankadya dzombe ndi uchi. Anthu ambiri ankachita naye chidwi. Nawonso Afarisi ndi Asaduki ankapita kukamuona ngakhale kuti iwo anali onyada. Koma Yohane ankawauza kuti: ‘Muyenera kusiya zoipa n’kulapa. Musaganize kuti ndinu apadera chifukwa chakuti mumati ndinu ana a Abulahamu. Umenewo si umboni woti ndinu ana a Mulungu.’

Anthu ambiri ankapita kwa Yohane kukamufunsa kuti: ‘Titani kuti tisangalatse Mulungu?’ Yohane ankauza Ayuda kuti: ‘Ngati muli ndi malaya awiri, enawo mupatseko munthu amene alibe.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake ankanena zimenezi? Ankafuna kuti ophunzira ake adziwe zoti, kuti asangalatse Mulungu ayenera kukhala achikondi.

Okhometsa misonkho ankawauza kuti: ‘Muzichita zinthu mwachilungamo ndipo musamabere aliyense.’ Asilikali ankawauza kuti: ‘Musamalandire ziphuphu komanso musamaname.’

Ansembe ndi Alevi nawonso ankabwera kwa Yohane ndipo ankamufunsa kuti: ‘Kodi ndinu ndani? Anthutu akufuna kukudziwani.’ Koma Yohane ankawayankha kuti: ‘Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu. Ndimathandiza anthu kudziwa Yehova mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera.’

Anthu ankakonda zimene Yohane ankawaphunzitsa. Ambiri ankaganiza kuti mwina iye ndi Mesiya. Koma Yohane ankawauza kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwera. Ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake. Paja ine ndimabatiza m’madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.’

“Munthu ameneyu anabwera monga mboni, kudzachitira umboni za kuwala, kuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.”​—Yohane 1:7