Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 98

Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino

Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino

Atumwi anamvera lamulo la Yesu loti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse. Mu 47 C.E., abale a ku Antiokeya anatumiza Paulo ndi Baranaba kuti akalalikire. Anthu awiriwa anayendayenda ku Asia Minor ndipo anafika ku Debe, ku Lusitara ndi ku Ikoniyo.

Paulo ndi Baranaba ankalalikira kwa aliyense mosaganizira kuti ndi wolemera kapena wosauka, wamkulu kapena wamng’ono. Ambiri ankamvetsera ndithu. Paulo ndi Baranaba akulalikira kwa bwanamkubwa wina dzina lake Serigio Paulo, munthu wina wamatsenga ankafuna kusokoneza. Ndiyeno Paulo anamuuza kuti: ‘Iwe Yehova akulanga.’ Nthawi yomweyo munthuyo anasiya kuona. Bwanamkubwa uja ataona zimenezo anakhala wokhulupirira.

Paulo ndi Baranaba ankalalikira m’nyumba za anthu, m’misika, m’misewu ndiponso m’masunagoge. Atafika ku Lusitara anachiritsa munthu wina wolumala. Ndiyeno anthu ataona zimenezi anafuna kuwalambira poganiza kuti iwowo ndi milungu. Koma Paulo ndi Baranaba anawauza kuti: ‘Anthu inu, ifetu ndi anthu ngati inu nomwe. Muzilambira Mulungu yekha.’ Koma kenako kunabwera Ayuda amene anasokoneza maganizo a anthu. Nthawi yomweyo anthuwo anayamba kugenda Paulo ndi miyala kenako anamukokera kunja kwa mzinda poganiza kuti wafa. Koma Paulo anali adakali ndi moyo. Zitatero, abale anapita kukamutenga n’kupita naye mumzinda. Patapita nthawi, Paulo anabwerera ku Antiokeya.

Mu 49 C.E., Paulo anauyambanso ulendo wina. Atachoka ku Asia Minor, anapita kukalalikira ku Ulaya. Iye anafika ku Atene, ku Filipi, ku Tesalonika komanso m’madera ena. Pa ulendowu anali ndi Sila, Luka komanso mnyamata wina dzina lake Timoteyo. Iwo anagwira limodzi ntchito yokhazikitsa mipingo komanso kuilimbikitsa. Paulo anakhala ku Korinto kwa chaka chimodzi ndi hafu n’cholinga choti alimbikitse abale akumeneko. Iye ankalalikira, kuphunzitsa komanso kulemba makalata opita kumipingo yosiyanasiyana. Koma ankagwiranso ntchito yopanga matenti kuti azipezako ndalama. Kenako Paulo anabwerera ku Antiokeya.

Mu 52 C.E., Paulo anauyamba ulendo wachitatu. Atachoka ku Asia Minor anafika ku Filipi, komwe ndi kumpoto kwenikweni, ndipo kenako anapita ku Korinto. Iye anakhala zaka zingapo ku Efeso komwe ankaphunzitsa, kuchiritsa anthu komanso kuthandiza mpingo wakumeneko. Tsiku lililonse, ankakamba nkhani muholo yapasukulu ina. Anthu ambiri ankamvetsera uthenga wake ndipo anasintha makhalidwe awo. Paulo atalalikira m’madera ambiri anapita ku Yerusalemu.

“Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.”​—Mateyu 28:19