Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 24

Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza

Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza

Yehova anauza Mose kuti: ‘Bwera kuphiri kuno. Ndidzalemba malamulo anga pamiyala n’kukupatsa.’ Mose anapita kuphiriko ndipo anakhalako masiku 40. Ali komweko, Yehova analemba Malamulo 10 pamiyala iwiri n’kumupatsa.

Patapita nthawi, Aisiraeli anaganiza zoti Mose wawathawa. Choncho anauza Aroni kuti: ‘Tikufuna mtsogoleri wina. Tipangire mulungu.’ Aroni anawauza kuti: ‘Ndipatseni golide wanu.’ Ndiyeno anasungunula golideyo n’kupanga fano la mwana wa ng’ombe. Zitatero, Aisiraeliwo anati: ‘Uyu ndiye Mulungu amene anatipulumutsa ku Iguputo.’ Anayamba kulambira fano la mwana wa ng’ombelo ndipo anachita mwambo wosonyeza kukondwera. Apatu analakwa kwambiri. Iwo analonjeza kuti azilambira Yehova yekha koma si zimene ankachita.

Yehova anaona zimene zinkachitikazi ndipo anauza Mose kuti: ‘Pita ukaone zimene anthu aja akuchita. Asiya kundimvera ndipo akulambira mulungu wonyenga.’ Mose ananyamuka, uku atanyamula miyala iwiri ija.

Atayandikira anamva anthu akuimba. Kenako anawaona akuvina komanso kugwadira mwana wa ng’ombe. Mose anakwiya kwambiri. Anaponya pansi miyala iwiri ija moti inasweka. Nthawi yomweyo anawotcha fanolo n’kuliperapera. Kenako anamufunsa Aroni kuti: ‘Koma iwe zoona unamvera anthuwa n’kupanga zinthu zoipa chonchi?’ Aroni anayankha kuti: ‘Pepani musandikwiyire. Mukudziwa bwino mmene anthuwa alili. Iwo amafuna mulungu ndiye ndinangotenga golide kuika pamoto, n’kupanga kang’ombeka.’ Komatu Aroni sankayenera kuchita zimenezi. Mose anapitanso kuphiri kuja n’kukapempha Yehova kuti akhululukire anthuwo.

Yehova anakhululukira anthu onse amene analapa n’kuyambiranso kumumvera. Ndipotu Aisiraeli ankafunika kumvera zinthu zonse zimene Mose ankawauza.

“Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako, chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa. Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.”​—Mlaliki 5:4