Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 35

Hana Anapempha Kuti Mulungu Amupatse Mwana Wamwamuna

Hana Anapempha Kuti Mulungu Amupatse Mwana Wamwamuna

Bambo wina wa ku Isiraeli dzina lake Elikana anali ndi akazi awiri. Mayina a akaziwo anali Hana ndi Penina. Koma Elikana ankakonda kwambiri Hana. Penina anali ndi ana ambiri koma Hana analibe ngakhale mmodzi. Chifukwa cha zimenezi, Penina ankanyoza Hana nthawi zonse. Chaka chilichonse, Elikana ankapita kukalambira ku Silo limodzi ndi banja lake. Tsiku lina ali kumeneko, anazindikira kuti Hana wakhumudwa kwambiri. Iye anamuuza kuti: ‘Hana usalire. Ndimakukonda kwambiri. Kodi si ine woposa ana amene ukufunawo?’

Kenako Hana ananyamuka kupita kukapemphera. Iye anapempha Yehova kuti amuthandize ndipo ankapemphera uku akulira mosatulutsa mawu. Hana analonjeza kuti: ‘Yehova, mukandipatsa mwana wamwamuna ndidzakupatsani kuti azikutumikirani kwa moyo wake wonse.’

Ndiyeno mkulu wa ansembe dzina lake Eli ataona milomo ya Hana ikugwedera, anaganiza kuti waledzera. Koma Hana anayankha kuti: ‘Ayi, mbuyanga, inetu sindinaledzere. Ndili ndi vuto lalikulu kwambiri limene ndikufotokozera Yehova.’ Eli anazindikira kuti walakwitsa ndipo anauza Hanayo kuti: ‘Mulungu akupatse zimene ukufunazo.’ Zitatero Hana anayamba kumva bwino mumtima ndipo anabwerera. Chaka chisanathe, anabereka mwana n’kumupatsa dzina loti Samueli. Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri.

Hana sanaiwale zimene analonjeza kwa Yehova. Samueli atangosiya kuyamwa, anamupereka kuti azikatumikira kuchihema. Iye anauza Eli kuti: ‘Mwana uyu ndi amene ndinkapempha nthawi ijayi. Ndamupereka kuti atumikire Yehova kwa moyo wake wonse.’ Chaka chilichonse, Elikana ndi Hana ankapita kukaona Samueli ndipo ankamutengera malaya odula manja. Yehova anapatsa Hana ana ena, aamuna atatu ndi aakazi awiri.

“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza.”​—Mateyu 7:7