Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 30

Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza Dziko

Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza Dziko

Aisiraeli awiri amene anatumidwa kukafufuza mzinda wa Yeriko anakafikira m’nyumba ya mayi wina dzina lake Rahabi. Mfumu ya kumeneko itazindikira, inatumiza asilikali kunyumbako. Koma Rahabi anabisa Aisiraeliwo padenga n’kuuza asilikaliwo kuti alowere njira ina. Kenako anauza Aisiraeliwo kuti: ‘Ndikukuthandizani chifukwa ndikudziwa kuti Yehova akukumenyerani nkhondo ndipo mugonjetsa mzindawu. Chonde, lonjezani kuti simudzapha ineyo ndi abale anga.’

Aisiraeliwo anauza Rahabi kuti: ‘Tikulonjeza kuti aliyense amene adzakhale m’nyumba yakoyi sadzaphedwa.’ Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Umangirire chingwe chofiira pawindo kuti iwe ndi abale ako mudzatetezeke.’

Rahabi anagwiritsa ntchito chingwe potulutsira Aisiraeliwo pawindo kuti azipita. Iwo anakabisala m’mapiri kwa masiku atatu asanabwerere kumene kunali Yoswa. Kenako Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano ndipo anayamba kukonzekera kuti alande dzikolo. Mzinda woyamba kuugonjetsa unali wa Yeriko. Yehova anawauza kuti azizungulira mzindawo kamodzi pa tsiku kwa masiku 6. Koma pa tsiku la 7 anawauza kuti auzungulire maulendo 7 ansembe akuimba malipenga, kenako asilikali anayamba kuchita phokoso kwambiri. Zitatero, mpanda wa mzindawo unagwa. Koma nyumba ya Rahabi yomwe inalumikizana ndi mpandawo, sinagwe. Rahabi ndi anthu a m’banja lake anapulumuka chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova.

“Mofanana ndi zimenezi, kodi Rahabi . . . sanaonedwenso kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atalandira bwino anthu amene ankafufuza dziko lawo nʼkuwathandiza kuti athawe kudzera njira ina?”​—Yakobo 2:25