MUTU 40
Davide Anapha Goliyati
Yehova anauza Samueli kuti: ‘Pita kunyumba ya Jese. Mwana wake wina adzakhala mfumu ya Isiraeli.’ Samueli anapitadi ndipo ataona mwana woyamba wa Jese, anaganiza kuti: ‘Amene adzakhale mfumu uja ndi ameneyu.’ Koma Yehova anauza Samueli kuti si ameneyo. Kenako anamuuzanso kuti: ‘Ine ndimaona mtima wa munthu osati zimene anthu amaona.’
Jese anabweretsa ana ake ena 6 koma Samueli anati: ‘Apa palibe aliyense amene Yehova wamusankha. Kodi anyamata anu onse ndi omwewa basi?’ Jese anati: ‘Watsala mmodzi wamng’ono kwambiri, dzina lake Davide. Wapita koweta nkhosa.’ Davide atafika, Yehova anauza Samueli kuti: ‘Ndi ameneyu!’ Zitatero Samueli anathira mafuta pamutu pa Davide. Kusonyeza kuti anamudzoza kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli.
Pa nthawi ina, Aisiraeli ankamenyana ndi Afilisiti. Ndiyeno kumbali ya Afilisitiwo kunali chimunthu chachikulu komanso champhamvu dzina lake Goliyati. Tsiku lililonse, Goliyati ankanyoza Aisiraeli. Ankanena kuti: ‘Ndipatseni munthu woti ndimenyane naye! Ngati angandigonjetse nʼkundipha, ndiye kuti tidzakhala antchito anu. Koma ngati ndingamugonjetse, inuyo mudzakhala antchito athu.’
Davide anafika pamalo pamene panali asilikali a Isiraeli n’cholinga choti apereke chakudya kwa azichimwene ake omwe anali asilikali. Davide anamva zimene Goliyati ankanena ndipo anati: ‘Ine ndikamenyana naye ameneyu.’ Mfumu Sauli atamva anati: ‘Iwe ndiwe mwana.’ Davide anayankha kuti: ‘Yehova andithandiza.’
Sauli anaveka Davide zovala zake zomenyera nkhondo koma iye anati: ‘Sindingathe kumenya nkhondo ndi zovala zimenezi.’ Choncho anangotenga chinthu choponyera miyala chotchedwa gulaye n’kutsetserekera kukamtsinje. Ndiyeno anatola miyala yosalala bwino 5 n’kuika m’kachikwama kake. Kenako Davide anayamba kuthamangira kumene kunali Goliyati. Goliyatiyo atamuona anati: ‘Mwana iwe! Bwera ndikuphe ndipo ukhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakutchire.’ Davide sanachite mantha. M’malomwake anamuyankha kuti: ‘Iwe ukubwera kudzamenyana ndi ine ndi lupanga komanso mkondo, koma ine ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova. Sukumenyana ndi ine ayi koma ndi Mulungu. Ndipo onse amene ali panowa adziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo. Nonsenu akuperekani mʼmanja mwathu.’
Kenako Davide anaika mwala pagulaye uja n’kuuponya mwamphamvu kwambiri. Yehova anamuthandiza moti mwalawo unathamanga n’kukaboola Goliyati pachipumi. Nthawi yomweyo Goliyati anagwa n’kufa. Afilisiti ataona zimenezi anayamba kuthawa. Kodi iweyo umadalira Yehova ngati mmene Davide ankachitira?
“Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma sizili choncho kwa Mulungu chifukwa zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”—Maliko 10:27