Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 44

Nyumba ya Yehova

Nyumba ya Yehova

Solomo atakhala mfumu ya Isiraeli, Yehova anamufunsa kuti: ‘Kodi ukufuna ndikupatse chiyani?’ Solomo anayankha kuti: ‘Ndine mwana ndipo sindikudziwa zambiri. Ndipatseni nzeru kuti ndizitha kulamulira bwino anthu anu.’ Yehova anamuyankha kuti: ‘Popeza wandipempha nzeru, ndipangitsa kuti ukhale munthu wanzeru kuposa wina aliyense. Koma ndikupatsanso chuma. Ndipo ukamandimvera, udzakhala ndi moyo wautali.’

Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Anagwiritsa ntchito golide, siliva, mitengo komanso miyala ndipo zonsezi zinali zamtengo wapatali. Panali amuna ndi akazi aluso amene ankagwira ntchito yomanga nyumbayo. Patadutsa zaka 7 ntchito yomangayi inatha ndipo inali nthawi yoti nyumbayo aipereke kwa Yehova. Nyumbayi inali ndi guwa pomwe anaikapo nsembe. Solomo anagwada patsogolo pa guwalo n’kupemphera kuti: ‘Yehova, nyumbayi si yokongola kwambiri komanso si yaikulu kwambiri moti inu n’kukwanamo. Koma tiloleni kuti tizikulambirani m’nyumbayi ndipo muzimva mapemphero athu.’ Kodi Yehova anamva bwanji ndi zimene Solomo ananena m’pempheroli? Solomo atangomaliza kupemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba n’kupsereza nsembe zonse zimene zinali paguwa zija. Izi zinasonyeza kuti Yehova anasangalala ndi nyumbayi ndipo Aisiraeli ataona zimenezi, anasangalala kwambiri.

Mfumu Solomo ankadziwika mu Isiraeli monse komanso m’madera akutali kuti anali wanzeru. Anthu ankabwera kwa iye kuti adzawathandize pa mavuto awo. Nayonso mfumukazi ya ku Seba inabwera kudzamuyesa pomufunsa mafunso ovuta. Koma itamva mayankho a Solomo inati: ‘Sindinkakhulupirira zimene anthu anandiuza zokhudza inu. Koma panopa ndaona kuti mulidi ndi nzeru kwambiri kuposanso mmene anthuwo ankafotokozera. Yehova Mulungu wanu wakudalitsani kwambiri.’ Zonse zinkayenda bwino ku Isiraeli ndipo anthu ankasangalala. Koma patapita nthawi zinthu zinasintha.

“Tsopano wina woposa Solomo ali pano.”—Mateyu 12:42