Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amayi Odwala AIDS Akusoŵa Pogwira

Amayi Odwala AIDS Akusoŵa Pogwira

Amayi Odwala AIDS Akusoŵa Pogwira

CYNTHIA, * mayi wa ku West Indies, anayenera kusankha pakati pa kuyamwitsa khanda lake kapena kumam’mwetsa mkaka wa m’botolo. Chingaoneke ngati chinthu chosavuta kusankha. Ndiponso tikudziŵa kale kuti kwa zaka zambiri akatswiri a zathanzi akhala akunena kuti mkaka wa mayi ndiwo “chakudya chabwino kwambiri” kwa ana. Kuphatikizanso apo, kumadera osauka, ana amene amamwetsedwa mkaka wa m’botolo ali pangozi yakuti angathe kufa chifukwa cha matenda otsegula m’mimba moŵirikiza nthaŵi 15 kusiyana ndi amene amayamwitsidwa. Ndiponsotu, bungwe la United Nations Children’s Fund (UNICEF) linanena kuti ana okwana 4,000 amafa tsiku lililonse chifukwa cha mavuto obwera chifukwa cha kugwiritsa ntchito njira zina m’malo mwa mkaka wa m’maŵere.

Komabe kumbali ya Cynthia, kusankha njira yoti aziyamwitsira mwanayo kunali ndi vuto lina losiyana. Ali ndi pakati pa miyezi isanu ndi umodzi, iye anauzidwa kuti mwamuna wake anam’patsira kachilombo kotchedwa human immunodeficiency virus (HIV), kamene kamayambitsa AIDS. Kenaka, atabereka, Cynthia anauzidwa kuti mwana wobadwa kwa mayi wa kachilombo ka HIV amakhala pa tsoka lakuti angatengere matendawo nthaŵi 7 zilizonse akamayamwa mkaka wam’maŵere. * Motero anayenera kusankhapo pa zinthu ziŵiri zoŵaŵa kwambiri: kumuika mwana wake pa tsoka limene lingabwere chifukwa cha mkaka wa m’maŵere, apo ayi kumuika pa mavuto obwera chifukwa cha kumwa mkaka wa m’botolo.

M’mbali zina za dziko kumene mliri wa AIDS wavutitsa kwambiri, aŵiri kapena atatu mwa amayi apakati khumi alionse amakhala ndi kachilombo ka HIV. M’dziko lina, kupitirira theka la amayi apakati amene anayesedwa anapezeka ndi kachilomboka. “Ziŵerengero zoopsa zimenezi zachititsa asayansi kugwira ntchito mwachamuna kuti apeze mankhwala,” inalongosola choncho Wailesi ya bungwe la United Nations. Pofuna kuchitapo kanthu pa nkhani yoopsa imeneyi, mabungwe asanu ndi limodzi a United Nations aphatikiza pamodzi nzeru zawo, zoyesayesa zawo, ndiponso zida zawo kupanga bungwe logwirizana lotchedwa Joint United Nations Programme on HIV/AIDS, lodziŵika monga UNAIDS. * Koma zimene bungwe la UNAIDS lapeza n’zakuti njira yothetsera vuto la AIDS si yapafupi.

Zopinga Zazikulu Zikulepheretsa Njira Yosavuta

Malingana ndi zimene Edith White, amene ali katswiri pa nkhani za kuyamwitsa ndiponso za kufalitsa HIV kwa ana kudzera mwa mayi ananena, ogwira ntchito zachipatala akulangiza amayi okhala ndi kachilombo ka HIV m’mayiko otukuka kuti asayamwitse ana awo, chifukwa chakuti zimenezi zimaŵirikiza tsoka lakuti mwanayo atenga matendawa. Zikuoneka kuti mkaka wopangidwa mwapadera kaamba ka ana uli njira yanzeru yoloŵa m’malo mwa kuyamwitsa. Koma m’mayiko osauka, kumene anthu ali ndi mfundo zawo zopweteketsa, njira yosavuta imeneyi si yapafupi kuitsatira.

Vuto lina n’lokhudza chikhalidwe. M’mayiko amene kuyamwitsa ndiko kuli njira ya nthaŵi zonse, amayi amene amayamwitsa ana awo mkaka wa m’botolo angakhale akulengeza kuti anatenga kachilombo ka HIV. Mayi angaope kuti anthu akadziŵa nkhaniyo, iye adzadzudzulidwa, kusayanjidwa ndi anthu ena kapena ngakhale kumenyedwa. Amayi ena amene ali mumkhalidwe woterewu amaona kuti sangachitire mwina, koma kumayamwitsa ana awo kuti asadziŵike kuti ali ndi kachilombo ka HIV.

Palinso mavuto ena. Mwachitsanzo taganizirani za Margaret amene ali ndi zaka 20. Iyeyo sanayezedweko kuti aone ngati ali ndi kachilombo ka HIV monganso amayi ena osachepera 95 peresenti a ku Uganda. Koma Margaret ali ndi chifukwa chokwanira chokhalira ndi nkhaŵa. Mwana wake woyamba anamwalira, ndipo mwana wake wachiŵiri ndi woonda ndiponso wodwaladwala. Margaret amayamwitsa mwana wake wachitatu nthaŵi khumi tsiku lililonse, ngakhale kuti mwina ali ndi HIV. “Sindingathe kuyamwitsa mwana wanga mkaka wa m’botolo,” iye akutero. N’chifukwa chiyani sangathe? Margaret akuti mtengo wa mkaka wa m’botolo wokwana kumwetsa mwana m’modzi ndi woŵirikiza kamodzi ndi theka kuchuluka kwa ndalama zimene banja limodzi m’mudzi mwake limapeza pachaka chathunthu. Ngakhale mkaka ukanapezeka kwaulere, pakadakhalabe vuto lopeza madzi abwino kuti akonze mkakawo monga chakudya chabwino kwa mwana. *

Ena mwa mavuto ameneŵa angathe kuchepetsedwa ngati makolo okhala ndi HIV akukhazikidwa mwaukhondo, akupatsidwa zakudya zokwanira zoloŵa mmalo mwa mkaka wa m’maŵere, ndiponso ngati angapeze madzi abwino. Kodi zimenezi n’zofunika ndalama zambiri? Mwinadi. Komatu, chodabwitsa n’chakuti kuti zimenezi zitheke vuto si ndalama ayi koma kusankha chimene chili chofunika kwambiri. Inde, bungwe la United Nations likunena kuti mayiko ena osaukitsitsa akuwononga ndalama pa nkhani ya zachitetezo moŵirikiza kuyerekezera ndi zimene amawonongera pa za umoyo ndiponso maphunziro.

Nanga Nkhani ya Mankhwala Ochepetsa AIDS Ili Pati?

Asayansi a bungwe la United Nations anena kuti mankhwala osavuta, ndiponso otsikirako mtengo amene dzina lake ndi AZT angathe kuchepetsa kwambiri kupatsira HIV kwa ana kudzera mwa mayi. Ndi chithandizo cha bungwe la UNAIDS, mtengo wa chithandizo chimenechi watsika kufika pa madola 50. Kuphatizanso apo, ofufuza za AIDS analengeza mu July 1999 kuti zikuoneka kuti kupereka mankhwala a nevirapine okwana madola atatu okha kumathandiza kupeŵa kupatsirana HIV kumeneku kuposa mankhwala a AZT. Akatswiri a zaumoyo ananena kuti nevirapine angathandize makanda okwanira 400,000 chaka chilichonse kuti moyo wawo asauyambe ndi kachilombo ka HIV.

Komabe, anthu ena amatsutsa mchitidwe wopereka mankhwala otereŵa, ponena kuti chifukwa chakuti amangothandiza kuti mayi asapatsire mwanayo kachilomboko, m’kupita kwa nthaŵi mayi uja adzafa ndi AIDS ndipo mwanayo adzakhala wamasiye. A bungwe la United Nations akuyankha kuti, njira ina imenenso ili yovuta, ndiyo kulola kuti mwanayo atenge HIV, kotero kuti nayenso ngakhale ali wosalakwa afe mozunzika ndi momvetsa chisoni. Iwo ananenso kuti amayi okhala ndi HIV angathe kukhalabe ndi moyo kwa zaka zambiri. Taganizirani nkhani ya Cynthia uja tam’tchula poyambirira. Iye anauzidwa kuti ali ndi HIV mu 1985, pamene mwana wake anabadwa, koma sanadwalepo mpaka panatha zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo ngakhale kuti pobadwa mwana wake anali ndi HIV, pofika zaka ziŵiri mwanayo anali alibe kachilomboko.

Mawu otonthoza otsimikizirika a m’Baibulo ndi akuti malo abwinodi ndiponso njira yothetseratu mavuto monga AIDS ili pafupi. (Chivumbulutso 21:1-4) Yehova Mulungu akulonjeza dziko latsopano mmene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Mboni za Yehova zingakonde kukuuzani za yankho lokhalitsa limeneli. Kuti mudziŵe zambiri, lemberani kalata kwa ofalitsa a magazini ano kapena pezani a Mboni za Yehova amene ali kumene mukukhala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Si dzina lake lenileni.

^ ndime 3 Malingana ndi zimene linanena bungwe la UNICEF, makanda pafupifupi 500 kapena mpaka 700 amatenga matendawa kudzera mumkaka wa amayi awo amene ali ndi kachilombo ka HIV.

^ ndime 4 Mabungwe asanu ndi limodzi ameneŵa ndiwo bungwe la UNICEF, la United Nations Development Programme, la United Nations Population Fund, la World Health Organization, la World Bank, ndi la United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization. Bungwe la UNAIDS analikhazikitsa mu 1995.

^ ndime 8 Kufufuza kwaposachedwa kwasonyeza kuti kuphatikiza mkaka wa m’botolo ndi mkaka wa m’maŵere kungakulitse tsoka lakutenga kachilombo ka HIV ndipo kuti mkaka wa m’maŵere ungathe kukhala ndi mankhwala amene angathe kufoketsa kachilomboko. Ngati zimenezi zili zoona ndiye kuti chosankha chabwino chingakhale kuyamwitsa mkaka wa m’maŵere koma mosamala, ngakhale kuti njirayi ili n’zovuta zina. Komabe, pakali pano palibe umboni wonse wotsimikizira kufufuza kumeneku.

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

WHO/E. Hooper