Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuba Anthu—Kodi Pali Njira Yokuthetsera?

Kuba Anthu—Kodi Pali Njira Yokuthetsera?

Kuba Anthu—Kodi Pali Njira Yokuthetsera?

“KUBA anthu kwafika pamlingo wakuti dziko lonse silingakulekerere, ndipo anthu onse ayenera kulimbana ndi mchitidwe woipa umenewu,” inafotokoza motero nduna yaikulu ya dziko la Chechnya pamene inali kulonjeza kuti idzathetsa vutolo, lomwe lafala kwambiri m’dziko lake limene lili ku Russia.

Kodi n’zotheka kuthetsa mchitidwe woba anthu? Cholinga chimenechi n’chabwino, koma funso n’lakuti, Athetsa bwanji?

Zomwe Akuyesa Kuchita

Boma la Colombia lasankha anthu okwana 2,000 mwachinsinsi, lasankhanso oimira boma pamilandu okwana 24 ndipo mpaka lasankhanso mkulu wapadera woyang’anira ntchito yolimbana ndi kuba anthu basi. Mumzinda wa Rio de Janeiro, ku Brazil, anthu okwana 100,000 anachita chionetsero chosonyeza kukhumudwa ndi kufala kwa mchitidwe wa kuba anthu. Ku Brazil ndi ku Colombia, magulu okhala ndi zida zankhondo abwezera pomaba achibale a mbava zoba anthu. Ndipo anthu ena a ku Phillipines aganiza zongothana nazo okha. Iwo akupha mbava zoba anthu!

Boma la Guatemala linakhazikitsa chilango cha kupha aliyense woba anthu, ndipo pulezidenti wa dzikolo anakonzekeretsa asilikali kuti athane ndi vuto la kuba anthu. Ku Italy boma linaika mfundo zokhwima kuti liletse mchitidwe woba anthu. Linaletsa kupereka ndalama zoombolera ndipo limalanda achibale ndalama ndi katundu kotero kuti asalipire. Akuluakulu a boma ku Italy akunena kuti mfundo zimenezi zachititsa kuti kuba anthu kuchepe. Komabe, anthu amene sagwirizana ndi mfundozo akuti, zimenezi zachititsa kuti mabanja azithetsa nkhanizo mwachinsinsi ndipo akuti potero chiŵerengero chodziŵika cha anthu obedwa chachepa. Mabungwe a zachitetezo akuti chiŵerengero cha obedwa ku Italy chakwera moŵirikiza kuyerekezera ndi mmene chinalili m’ma 1980.

Pali Malingaliro Ambiri Koma Njira Zochepa

Kwa mabanja ambiri a anthu obedwa, pali njira imodzi yokha yomveka, ndiyo kuombola okondedwa awo mwamsanga. Koma akatswiri amachenjeza kuti ngati ndalama zoombolera zili zambiri ndipo ngati zaperekedwa mwamsanga, oba anthu angaone kuti banja limenelo n’losavuta kulibera ndipo angadzabwerenso. Apo ayi, angafunse kuti apatsidwe ndalama zina asanamasule wobedwayo.

Mabanja ena alipira ndalama zambiri koma n’kupeza kuti wobedwayo anafa kale. Motero akatswiri amanena kuti munthu asalipire ndalama zoombolera kapena kukambirana za ndalamazi ngati asanatsimikize kuti wobedwayo ali moyo. Chitsimikizo choterechi chikhale m’njira ya funso limene wobedwa yekhayo ndiye angathe kuliyankha. Mabanja ena amafuna chithunzi cha munthuyo atanyamula nyuzipepala yaposachedwa.

Kodi bwanji kuyesa kumupulumutsa? Nthaŵi zambiri kumakhala koopsa kwambiri. “Anthu okwana 79 peresenti ya omwe amagwidwa amaphedwa mkati moyesa kuwapulumutsa ku Latin America,” anatero Brian Jenkins, katswiri wa nkhani za kuba anthu. Komabe, nthaŵi zina zimatheka kuwapulumutsa.

N’zosadabwitsa kuti nthaŵi zambiri njira yofala ndiyo kungopeŵa kubedwa. Si mabungwe a boma okha amene akuyesa kuletsa kuba anthu. Manyuzipepala amaphunzitsa anthu mmene angapeŵere kubedwa, mmene angadumphire m’galimoto ikuyenda, ndi mmene angapusitsire oba anthu. Sukulu zophunzitsa maluso omenyera zimaphunzitsa anthu mmene angadzitetezere kuti asabedwe. Makampani amagulitsa tizipangizo tating’onoting’ono kwambiri, pamtengo wa madola 15,000 timene tingathe kuikidwa m’mano mwa ana kuti tithandize apolisi kudziŵa kumene kuli anawo ngati atabedwa. Kwa amene angathe kukwanitsa, anthu ogulitsa magalimoto akupanga magalimoto “oletsa kubedwa” okhala ndi motulutsira mpweya okhetsa misozi, motulukira zipolopolo, mawindo osaloŵa zipolopolo, matayala osatheka kuphulitsidwa, ndiponso motulutsira mafuta omatira mobooka.

Anthu ena olemera amaona kuti alonda oyenda nawo ndiwo angathandize. Komabe, ponenapo za mmene zinthu zilili ku Mexico, katswiri wina wa zachitetezo wotchedwa Francisco Gomez Lerma anati: ‘Alonda oyenda nawo si othandiza chifukwa ndiwo amachititsa chidwi akuba ndiponso amatha kugwirizana ndi akuba anthuwo.’

Vuto la kuba anthu n’lalikulu kwambiri ndipo maziko ake ndi olimba kwambiri kotero zikuoneka kuti palibe chimene munthu angachite chokwanira kulithetsa. Choncho, kodi palibe njira yeniyeni yolithetsera?

Njira Ilipo

Magazini ino yanena mobwerezabwereza za njira imodzi yokha yothetsera mavuto onse amene anthu ali nawo. Njira yake ndiyo imene Mwana wa Mulungu Yesu Kristu anali kutchula pamene ankaphunzitsa atsatiri ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10.

Mwachionekere, tifunikira boma lolungama lapadziko lonse kuti liyendetse zochita za anthu osiyanasiyana amene ali padziko lapansi. Inde, Ufumu wa Mulungu umene Yesu anautchula. Chifukwa chakuti anthu alephera kukhazikitsa boma lotereli, n’kwanzeru ngati tikudalira Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Mawu ake Baibulo, amati cholinga chake n’chakuti adzachite zimenezi.—Salmo 83:18.

Mneneri Danieli analemba zifuno za Yehova, ponena kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse. . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Baibulo limalongosola mmene boma la Mulungu limeneli lidzachitire zotheka kuti lithetse mchitidwe uliwonse woipa, kuphatikizapo mchitidwe woba anthu.

Maphunziro Oyenera Ndiwo Akufunika

N’zosakayikitsa kuti mungavomereze kuti kuphunzitsa anthu makhalidwe abwino n’kofunika kuti vuto la kuba anthu lithe. Mwachitsanzo, tangoyerekezerani mmene zinthu zingakhalire ngati anthu onse akadamatsatira malangizo a m’Baibulo otsatiraŵa akuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni.” (Ahebri 13:5) “Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko.”Aroma 13:8.

Mungathe kuona mmene moyo ukadakhalira mwakuyang’ana ntchito ya kuphunzitsa imene Mboni za Yehova zikuchita m’mayiko oposa 230 padziko lonse lapansi. Ntchito imeneyi yasintha anthu ambiri amene poyamba anali aumbombo kapena mbava zoopsa. Munthu wina amene kale ankaba anthu ananena kuti: “Mkupita kwa nthaŵi, ndinaona kuti ngati ndikufuna kusangalatsa Mulungu ndiyenera kuchotsa umunthu wanga wakale ndi kuvala watsopano, wofatsa ndiponso wofanana ndi wa Kristu Yesu.”

Komabe, ngakhale patakhala ntchito ya kuphunzitsa yabwino kwambiri si kuti ophwanya lamulo onse angasinthe, ambiri angapitirizebe. Kodi amene akukana kusinthawo chidzawachitikire n’chiyani?

Kuchotsa Oipa

Anthu ochita zoipa mwadala sadzaloledwa kukhala mu Ufumu wa Mulungu. Baibulo limati: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, . . . kapena osirira, . . . kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko . . . Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.”Miyambo 2:21, 22.

Malingana ndi Lamulo la Mulungu m’nthaŵi zakale, mbava yoba anthu yosalapa inayenera kuphedwa. (Deuteronomo 24:7) Anthu aumbombo monga oba anthu, sadzakhala ndi malo alionse mu Ufumu wa Mulungu. Lero anthu ophwanya lamulo angathe kuzemba chiŵeruzo cha anthu, koma sadzatha kuzemba chiŵeruzo cha Mulungu. Ochita zoipa onse ayenera kusintha mayendedwe awo ngati akufuna kudzakhala muulamuliro wolungama wa Ufumu wa Yehova.

Mwachionekere, ngati mikhalidwe yochulukitsa kuipa ikhalapobe, kuphwanya lamulo nakonso kudzachuluka. Koma, Ufumu wa Mulungu sudzalola zimenezi kuchitika, chifukwa Baibulo limalonjeza kuti: ‘Ufumuwo udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse,’ kuphatikizaponso onse ochita zoipa. Ulosi wa Baibulo umenewu umapitiriza kunena kuti Ufumu wa Mulungu udzakhala kosatha. (Danieli 2:44) Tangoganizirani kusintha kumene kudzakhalepo!

Dziko Latsopano Lachilungamo

Taganizirani ulosi wina wa m’Baibulo. Ulosi umenewu umalongosola kuti m’tsogolo mudzakhala mokoma ponena mawu awa: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku amtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”Yesaya 65:21, 22.

Ufumu wa Mulungu udzasinthiratu dziko lonseli. Onse amene adzakhale ndi moyo adzasangalala ndi moyo kotheratu, ndipo adzakulitsa maluso awo achibadwa pochita ntchito zokhutiritsa ndiponso maseŵera osangalatsa. Mikhalidwe ya padziko lonse idzakhala yabwino kwambiri kwakuti palibe amene angadzaganize n’komwe zoba mnzake. Kudzakhaladi bata. (Mika 4:4) Motero, Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuba anthu koopsaku kukhala mbiri chabe imene palibe munthu amene adzaiganizirenso n’komwe.—Yesaya 65:17.

[Chithunzi patsamba 26]

“Sipadzakhala wakuwawopsa”—Mika 4:4