Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuona Miyambo Yotchuka M’njira Yoyenera

Kuona Miyambo Yotchuka M’njira Yoyenera

Lingaliro la Baibulo

Kuona Miyambo Yotchuka M’njira Yoyenera

“PALIBE MWAMBO UMENE SUNATCHULIDWEPO MONGA WOIPA PANTHAŴI INAYAKE NDIPONSO KWINAKWAKE, KOMANSO UMENE UNAIKIDWA MONGA LAMULO PA NTHAŴI INAYAKE NDIPONSO KWINAKWAKE.”

MAWU ameneŵa, onenedwa ndi William Lecky katswiri wa mbiri yakale wa ku Ireland akulongosola za kusakhazikika kwa anthu. Zonena zake zingagwirenso ntchito pa miyambo ndi chikhalidwe kuyambira m’mibadwo yakalekale. Inde, miyambo yambiri yomwe kale ankaiona monga yofunika m’moyo wa tsiku ndi tsiku m’kupita kwa nthaŵi anena kuti n’njoipa. Zimenezi n’zosadabwitsa, chifukwa chakuti Mkristu mtumwi Paulo anati: “Maonekedwe a dziko ili apita [“akusintha,” NW].”—1 Akorinto 7:31.

Inde, mtundu wa anthu ukusintha mosalekeza. Zimenezi kaŵirikaŵiri zikuonekera m’kusintha kwakukulu kwa maganizo ndi zizoloŵezi za kakhalidwe. Akristu “sakhala a dziko lapansi” kutanthauza kuti iwo amakhala odzipatula ku mtundu wa anthu umene uli wotalikirana ndi Mulungu. Komabe, Baibulo limavomereza kuti Akristu ali “m’dziko lapansi” ndipo siliwalamula kuti akhale anthu ongochita zinthu zaokha basi. Chotero, kaonedwe koyenera ka miyambo n’kofunika kwambiri.—Yohane 17:11, 14-16; 2 Akorinto 6:14-17; Aefeso 4:17-19; 2 Petro 2:20.

Kodi Miyambo N’chiyani?

Miyambo ndi zochita zimene zimakhudzana ndi mmene anthu amakhalira m’moyo ndipo n’zofala ku malo enaake kapena ku mtundu winawake wa anthu. Miyambo ina, monga miyambo ya pachakudya ndiponso ulemu, mwina inayamba chifukwa chofuna kulinganiza chikhalidwe cha anthu akamachita zinthu pagulu, kuti athe kuchitirana zinthu molemekezana. Pankhani zoterezi, miyambo ya chikhalidwe ingayerekezedwe ndi mafuta m’lingaliro lakuti amafeŵetsa unansi wa mtundu wa anthu.

Miyambo yakhala ikusonkhezeredwa kwambiri ndi chipembedzo. Ndiponso, miyambo yambiri inachokera ku zikhulupiriro zakalekale ndi malingaliro achipembedzo osakhala a m’Baibulo. Mwachitsanzo, kupereka maluŵa kwa anamfedwa kuyenera kuti kunayamba chifukwa cha zikhulupiriro zachipembedzo. * Komanso, anthu ankaganiza kuti mtundu wa bluu umene kaŵirikaŵiri unali kuimira makanda aamuna unkapilikitsa ziŵanda. Utoto wopaka m’sidze akuti unkagwira ntchito yoteteza munthu ku diso loyang’ana mozonda, pamene utoto wopaka m’milomo akuti unkathandiza kuchititsa ulesi ziŵanda kuti zisaloŵe m’kamwa mwa mkazi ndi kumpanga kukhala waziŵanda. Ngakhale miyambo ina yosavulaza n’komwe monga kutseka pakamwa ukamayasamula ziyenera kuti zinayamba chifukwa cha malingaliro akuti mzimu wa munthu utha kutuluka ngati kukamwa kuli pululu. Komabe, m’kupita kwa zaka, kugwirizanitsa miyambo ndi chipembedzo kwalekeka, ndipo tsopano zochita ndiponso miyamboyi ilibe tanthauzo la chipembedzo.

Nkhaŵa ya Akristu

Pamene kuli kwakuti Mkristu ayenera kusankha kaya kutsatira kapena kusatsatira miyambo ina, nkhaŵa yake iyenera kukhala yakuti, Kodi lingaliro la Mulungu lolembedwa m’Baibulo pankhaniyi n’lotani? Kale Mulungu analetsa mikhalidwe ina imene mwina inkaloledwa m’mitundu ina. Izi zinaphatikizapo kupereka ana nsembe, kugwiritsa ntchito magazi molakwa, ndi zochita zosiyanasiyana zachiwerewere. (Levitiko 17:13, 14; 18:1-30; Deuteronomo 18:10) Mofananamo, miyambo ina imene yawanda masiku ano siyogwirizana ndi malamulo a Baibulo. Ina mwa miyambo imeneyi ndiyo miyambo yosapezeka m’Baibulo yokhudza maholide achipembedzo monga Khirisimasi ndi Isitala kapena yotsatira zikhulupiriro zogwirizana ndi kuopa mizimu.

Koma kodi tiyenera kuona bwanji zochita zimene kale zinali kugwirizana ndi mikhalidwe yokayikitsa koma yomwe tsopano ikuonedwa kukhala mwambo wachikhalidwe? Mwachitsanzo, miyambo yotchuka ya paukwati, kuphatikizapo kupatsana mphete, ndiponso kudyetsana keke, iyenera kuti inayamba ndi akunja. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akristu sayenera kuchita miyambo yotereyi? Kodi Akristu ayenera kupenda mosamalitsa mwambo uliwonse wa anthu m’deralo kuti aone ngati penapake kapena nthaŵi ina unali ndi tanthauzo losakhala la m’Malemba?

Paulo ananena kuti “pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17; Yakobo 1:25) Mulungu sakufuna kuti ife tigwiritse ntchito ufulu umenewu monga chinthu chotilimbikitsa kuchita zoipa, koma akufuna kuti tiphunzitse mphamvu ya kuzindikira kusiyanitsira chabwino ndi choipa. (Agalatiya 5:13; Ahebri 5:14; 1 Petro 2:16) Choncho, pankhani imene siikuswa malamulo a Baibulo moonekeratu, Mboni za Yehova siziikapo malamulo okhwima. M’malo mwake, Mkristu aliyense ayenera kupenda mkhalidwe umene alimo ndi kusankha chochita.

Funafunani Zopindulitsa Ena

Kodi izi zikutanthauza kuti nthaŵi zonse n’koyenera kuchita nawo mwambo winawake malinga ngati sukutsutsana mwachindunji ndi ziphunzitso za Baibulo? Ayi. (Agalatiya 5:13) Paulo anasonyeza kuti Mkristu sayenera kungofunafuna phindu la iye yekha ‘komanso la unyinjiwo.’ Ayenera ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu’ ndipo asakhale wokhumudwitsa. (1 Akorinto 10:31-33) Chotero munthu wofunafuna chivomerezo cha Mulungu angafune kudzifunsa kuti: ‘Kodi ena amauona motani mwambo umenewu? Kodi anthu amatanthauzira mwambo umenewu m’njira ina yokayikitsa? Kodi ndikachita nawo mwambo umenewu ndisonyeza kuti ndikugwirizana ndi zochita kapena malingaliro amene sakondweretsa Mulungu?’—1 Akorinto 9:19, 23; 10:23, 24.

Ngakhale kuti nthaŵi zambiri palibe vuto lililonse, miyambo ina m’deralo ingamachitike m’njira zimene zili zosemphana ndi malamulo a Baibulo. Mwachitsanzo, pa zochitika zinazake kupereka maluŵa kungakhale kopanda tanthauzo lenileni lomwe likutsutsana ndi ziphunzitso za Baibulo. Choncho, kodi chinthu choyamba chimene Mkristu ayenera kudera nacho nkhaŵa n’chiyani? Ngakhale kuti mwina pangakhale chifukwa chofufuzira magwero a mwambo winawake, nthaŵi zina kumakhala kothandiza kwambiri kuganizira zimene mwambowo umatanthauza kwa anthu panthaŵi ndiponso kudera kumene munthuwe ukukhala. Ngati mwambowo umakhala ndi matanthauzo osemphana ndi malemba kapena osayenera pa nthaŵi inayake ya chaka kapenanso pa zochitika zina, Akristu angasankhe mwanzeru kupeŵa mwambowo nthaŵi zonse.

Paulo anapemphera kuti Akristu apitirizebe kulola chikondi chawo kusefuka m’chidziŵitso ndi kuzindikira konse. Mwa kupitiriza kuona miyambo yotchuka m’njira yoyenera, Akristu amakhala ‘otsimikizira zinthu zofunika kwambiri, kuti [iwo] akakhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena.’ (Afilipi 1:9, 10, NW) Panthaŵi imodzimodziyo, iwo amalola kuti ‘kufatsa kwawo kuzindikirike ndi anthu onse.’—Afilipi 4:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Malinga ndi zomwe wopenda za chikhalidwe wina ananena, mipukutu ya maluŵa nthaŵi ina inkagwiritsidwa ntchito monga nsembe kwa akufa kuwaletsa kuti asavulaze amoyo.

[Zithunzi patsamba 15]

Miyambo ina yakale, monga ngati kutseka pakamwa ukamayasamula ndiponso kupereka maluŵa kwa anamfedwa ilibe matanthauzo omwe inali nawo pachiyambi