Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malonda a Kuba Anthu Ali Padziko Lonse

Malonda a Kuba Anthu Ali Padziko Lonse

Malonda a Kuba Anthu Ali Padziko Lonse

KUYAMBIRA zaka khumi zapitazo, kuba anthu kwafala kwambiri padziko lonse. Lipoti lina linati, pakati pa 1968 ndi 1982, anthu pafupifupi chikwi anagwidwa m’mayiko 73. Koma kumapeto kwa m’ma 1990, anthu pafupifupi 20,000 kapena mpaka 30,000 ankabedwa chaka chilichonse.

Kuba anthu kukuoneka kuti ndi mchitidwe wophwanya lamulo umene watchuka kwambiri pakati pa mbava kuchokera ku Russia mpaka kukafika ku Phillipines, ndipo mbava zimenezi zimakhala zokonzeka kuba chamoyo chilichonse. Nthaŵi ina mwana wa tsiku limodzi lokha anabedwa. Ku Guatemala mayi wazaka 84 anabedwa ali khale pampando wake wamatayala wochita kukankha kwa miyezi iŵiri. Ku Rio de Janeiro, mbava za m’misewu zikuba anthu oyenda m’misewuyo, ndipo nthaŵi zina zimafuna ndalama zokwana madola 100 okha basi monga chikole choombolera munthuyo.

Nazonso nyama n’zosatetezeka. Zaka zapitazo mbava zoopsa ku Thailand zinaba njovu yogwira ntchito yolemera matani asanu ndi limodzi ndipo zinafuna ndalama zokwana madola 1,500 zoiombolera. Magulu achifwamba ku Mexico akuti amalimbikitsa ana a m’maguluwo kuti aziyeserera pomaba nyama monga agalu ndiponso nyama zina zoŵeta kuti azoloŵere ndipo kuti kenaka azikaba bwino anthu.

M’mbuyomo, oba anthu anali kwenikweni kuba anthu olemera, koma zinthu zasintha. Lipoti lochokera ku bungwe la atolankhani lotchedwa Reuters linanena kuti: “Ku Guatemala, kuba anthu kwangosanduka chinthu chochitika tsiku ndi tsiku. Kumeneko, anthu amakumbukira masiku okoma a m’mbuyo pamene zigaŵenga zoukira boma zinkasankha kuba anthu amalonda ochepa amene anali olemera. Koma lero, olemera ndi osauka omwe, ana ndi achikulire omwe, onse akubedwa ndi magulu oba anthu.”

Nkhani zodziŵika kwambiri nthaŵi zambiri zimafalitsidwa zedi, komabe nkhani za kuba anthu zambiri zimatha popanda kufalitsidwa kulikonse. Ndiponsotu, pazifukwa zosiyanasiyana, mayiko “saona chifukwa chofalitsira nkhani zamavuto a kuba anthu.” Nkhani yotsatira ilongosola zina mwa zifukwa zimenezi.

[Mapu patsamba 19]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MEXICO

Kumeneku anthu okwana 2,000 amabedwa chaka chilichonse, ndipo kuba anthu kwatchulidwa dzina lakuti “malonda achinsinsi.”

GREAT BRITAIN

Kampani ya Lloyd’s of London yakhala ikukweza Inshuwalansi ya kuberedwa munthu ndi 50 peresenti chaka chilichonse kuchokera m’1990.

RUSSIA

Ku dera la Caucasus lokha limene lili kummwera kwa dziko la Russia, chiŵerengero cha obedwa chinakwera kuchoka pa 272 m’chaka cha 1996 kufika pa 1,500 mu 1998.

PHILIPPINES

Malingana ndi magazini ya “Asiaweek,” “Mwina dziko la Philippines ndilo likulu la kuba anthu ku Asia konse.” Magulu a mbava opitirira 40 akuba anthu kumeneko.

BRAZIL

Kumeneko, m’chaka chimodzi chokha oba anthu anapeza ndalama zokwanira 1.2 biliyoni zoperekedwa poombolera anthu.

COLOMBIA

M’zaka zaposachedwapa anthu zikwizikwi akhala akubedwa chaka chilichonse. Mu May 1999, zigaŵenga zinaba anthu 100 ku parishi amene anali kuchita Misa.

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.