Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zimachititsa—Kuba Anthu

Zimene Zimachititsa—Kuba Anthu

Zimene Zimachititsa—Kuba Anthu

KUBA anthu kwasanduka mliri wamakono. Ndipo zateronso ndi mchitidwe wa kupha anthu, kugwiririra, kuba, kuvutitsa ana, ndipo ngakhale kupha fuko lonse. N’chifukwa chiyani moyo uli woopsa chonchi, kwakuti nthaŵi zambiri anthu amaopa kutuluka m’nyumba zawo usiku?

Chimene chimachititsa kufala kwa kuphwanya lamulo kotereku, kuphatikizaponso kuba anthu, ndicho kulephera kwakukulu kwa anthu. Kodi mukudziŵa kuti pafupifupi zaka 2000 zapitazo, Baibulo linalosera nthaŵi zoopsa zino? Chonde taonani zimene linalosera pa 2 Timoteo 3:2-5.

“Anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”

Mwina mukuvomereza kuti mawu ameneŵa amene analembedwa kale kwambiri akulongosola ndendende mmene zinthu zilili lero. M’nthaŵi yathu ino kulephera kwakukulu kwa anthu kwabweretsa mavuto aakulu kwambiri. Motero, m’Baibulo, mawu ali pamwambapo amene akulongosola khalidwe lomvetsa chisoni la anthu, akuyamba ndi mawu akuti: “M’masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Tiyeni tione zolephera zitatu zokha za anthu zimene zachititsa vuto la kuba anthu.

Mavuto a Kukhazikitsa Lamulo

“Popeza sam’bwezera choipa chake posachedwa atam’tsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.”Mlaliki 8:11.

Magulu ambiri a apolisi alibe zida zokwanira kuthetsera kufala kwa umbava. Motero m’mayiko ambiri, kuba anthu ndi umbava wopindulitsa. M’chaka cha 1996 oba anthu a ku Colombia okwana 2 peresenti okha ndiwo anaimbidwa mlandu. Ku Mexico, ndalama zosachepera madola 200 miliyoni anazipereka poombolera anthu mu 1997. Oba anthu ena ku Phillipines alola kulandira cheke cha malipiro oombolera anthu.

Kuphatikizanso apo, nthaŵi zina apolisi ndiponso maunduna a boma oona za malamulo amalandira ziphuphu ndipo izi zimalepheretsa kugonjetsa umbava. Nawonso akuluakulu a magulu olimbana ndi mchitidwe wa kuba anthu ku Mexico, Colombia, ndi mayiko a Soviet wakale atchulidwa kuti amaba anthu. M’magazini yotchedwa Asiaweek, pulezidenti wa nyumba ya malamulo ya ku Phillipines, Blas Ople, ananena kuti chiŵerengero chotsimikizika bwino chikusonyeza kuti 52 peresenti ya nkhani za kuba anthu ku Phillipines zikukhudza apolisi kapena asilikali amene akugwirabe ntchito kapena amene anapuma. Munthu woba anthu wotchuka wa ku Mexico akuti anali wotetezedwa ndi “akuluakulu mothandizidwa ndi ziphuphu zoperekedwa kwa apolisi ndiponso oweruza milandu.”

Umphaŵi Ndiponso Kusoŵa Chilungamo

“Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.”—Mlaliki 4:1.

Anthu ambiri lero ali m’mavuto aakulu a zachuma komanso mavuto ena, ndipo nthaŵi zambiri iwo ndiwo amaba ena. Motero m’dziko lino, limene pali kusiyana kwakukulu kwambiri pakati pa olemera ndi osauka ndiponso poti kupeza ndalama mwachilungamo kukuvuta, kuba anthu kuzikopabe anthu. Malinga ngati kutsenderezana kukhalapobe, kuba anthu nako kukhalapo monga njira yobwezera ndiponso yosonyeza kuti m’povuta kukhalabe motsenderezedwa.

Umbombo Ndiponso Kusoŵa Chikondi

“Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama.” (1 Timoteo 6:10) “Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.”—Mateyu 24:12.

Nthaŵi yonse m’mbuyomu kukonda ndalama kwapangitsa anthu kuchita zinthu zoipa kwambiri. Ndipo mwina palibenso mchitidwe wina woipa, umene ena amapindula nawo, umene umabweretsa chisoni, kudandaula, ndi kutaya chikhulupiriro mofanana ndi kuba anthu. Umbombo kapena kukonda ndalama ndi zimene zimachititsa anthu ambiri kuti azizunza munthu wosam’dziŵa ndi kuika banja lake m’chiyeso chachikulu kwa masabata, miyezi, ndipo nthaŵi zina ngakhale zaka.

Mwachionekere, china n’cholakwika ngati anthu akuona ndalama monga chinthu chofunika koposa zonse, ndipo n’kumapondereza ulemu wa umunthu. Mosakayikira, zimenezi zikuchititsa kuti pakhale kuphwanya lamulo kwamitundumitundu, kuphatikizapo kuba anthu.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tikukhala m’masiku amene Baibulo limawatcha kuti “masiku otsiriza”? Ngati n’choncho kodi ndiye kuti nkhaniyi ikukhudza bwanji dziko lapansi ndiponso ife? Kodi pali njira yothetsera mavuto osautsa omwe anthu akupeza, kuphatikizaponso kuba anthu?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

Sizachilendo

Chilamulo cha Mose chinaika chilango cha imfa kwa anthu oba anzawo m’mbuyomo m’zaka za m’ma 1500 B.C.E. (Deuteronomo 24:⁠7) M’ma 100 B.C.E., Julius Ceasar anamuba ndipo akubawo anafuna kuti achite kumuombola. Richard 1, wotchedwa kuti Wamtima wa Mkango, amene anali mfumu ya England, m’ma 1200 C.E. nayenso anabedwa. Mtengo wokwera kwambiri woombolera munthu unali matani 24 a golidi ndi siliva amene fuko la a Inca linapereka kwa kazembe olanda wachispanya wotchedwa Francisco Pizarro pofuna kuombola mfumu yawo Atahuallpa pamene inagwidwa mu 1533. Komabe anthu olandawo anamupha.

[Chithunzi patsamba 25]

Ngakhale kuti pali apolisi, kuba anthu kukuchulukabe