Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ovutika ndi Nkhondo Asintha

Anthu Ovutika ndi Nkhondo Asintha

Anthu Ovutika ndi Nkhondo Asintha

“NKHONDO zamasiku ano n’zosiyana zedi ndi zamakedzana . . . Anthu wamba, osati asilikali,” ndiwo akuvutika mowonjezerekawonjezereka, inatero pologalamu ina yotchedwa “Perspective” youlutsidwa pawailesi ya United Nations. Mwachitsanzo, m’kati mwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse anthu 5 mwa anthu 100 alionse ovulala ndiwo anali anthu wamba. Komabe, m’kati mwa nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse chiŵerengero cha anthu wamba ovulala chinakwera kufika pa 48 mwa anthu 100 alionse. Ndipo tsopano, inatero wailesi ya United Nations, “pafupifupi ovulala pankhondo onse amakhala anthu wamba, chifukwa ndi anthu 90 mwa anthu 100 alionse, ndipo ambiri a iwo amakhala akazi, ana, ndiponso okalamba.”

Malinga ndi zomwe ananena a Olara Otunnu, yemwe ndi mlembi wamkulu wa nthambi yapadera ya bungwe la United Nations yoimira ana ovutika pa nkhondo lotchedwa Special Representative for Children and Armed Conflict, “ana pafupifupi mamiliyoni aŵiri anaphedwa pa nkhondo chiyambire 1987.” Chiŵerengerochi chikusonyeza kuti tsiku lililonse ana oposa 450 akhala akuvutika chifukwa cha nkhondo m’zaka 12 zapitazi! Kuwonjezera apo, m’nthaŵi yofananayo, ana oposa mamiliyoni asanu ndi limodzi avulazidwa koopsa kapenanso kuchititsidwa kukhala olumala.

A Otunnu anati njira imodzi imene bungwe la United Nations lingathetsere vuto la kukula kwa chiŵerengero cha ana ovulala pa nkhondo ndiyo kulimbikitsa mtendere m’malo ena. “Malo amene kumakhala ana ambiri monga kusukulu, kuchipatala, ndi kumalo oseŵerera kuyenera kuonedwa monga koletsedwa kuchitirako nkhondo.” Komabe, wailesi ya United Nations inawonjezera kuti, “kuthetsa kaye nkhondoyo monga chinthu choyamba” ndiyo njira yothandiza kwambiri kuti United Nations itsimikize kuti anthu wamba sakuvulala pa nkhondo. N’zoonadi, kuthetsa kuvulala kwa anthu pa nkhondo n’kofunikiradi kuti nkhondo yeniyeniyo ithetsedwe. Kodi zimenezi zidzachitika n’komwe?

Chifukwa cha mbiri ya anthu ya kuchita nkhondo kwa nthaŵi yaitali, anthu ambiri amalondola akamaganiza kuti anthu sadzadzetsa mtendere padziko lonse lapansi. Komabe, Mawu a Mulungu, Baibulo, amalonjeza kuti Yehova Mulungu adzachita zimenezi: “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:9) Kodi zimenezi zidzachitika liti? Ndipo n’chifukwa chiyani mungakhale wotsimikiza kuti malonjezo a Mulungu onena kuti adzadzetsa mtendere padziko lonse lapansi adzakwaniritsidwa? Ngati mukufuna kumva yankho la mafunso ameneŵa, chonde lemberani kwa wofalitsa magazini ano, pogwiritsa ntchito adiresi yakufupi ndi kwanu pa maadiresi osonyezedwa pa tsamba 5, kapena pitani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yomwe muli nayo pafupi. Kumeneko samakupemphani kuchita chilichonse kapena kukulipitsani, kumangokhala mayankho omveka bwino basi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

CHITHUNZI CHA UN 156450/J. Isaac