Kodi Mukudziŵa?
Kodi Mukudziŵa?
(Mayankho a mafunso otsatiraŵa mungawapeze m’Baibulo m’malemba amene asonyezedwa, ndiponso mayankho onse alembedwa pa tsamba 29. Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka, onani m’buku lotchedwa “Insight on the Scriptures,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.)
1. Kodi ndi mawu otani amene Yesu anali kugwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri kuti agogomezere kwa omumvetsera kulondola kwa mawu ake? (Mateyu 5:18)
2. Kodi mawu akuti: “Wamng’ono wa iwo anayang’anira zana limodzi, ndi wamkulu wa iwo anayang’anira chikwi chimodzi,” anali kunena za ayani? (1 Mbiri 12:8-14)
3. Kodi ndi dzina la yani limene nthaŵi zambiri limayendera limodzi ndi ankhondo a Davide amphamvu awa, Yoabu, Abisai ndi Asaheli? (2 Samueli 2:18)
4. Ngakhale kuti munthu angadedwe chifukwa cha dzina la Yesu, kodi iye ananena kuti munthu ayenera kuchita chiyani kuti apulumuke? (Marko 13:13)
5. Kodi Hamani anali ndi ana aamuna angati omwe onse anaphedwa chifukwa cha udani wake ndi Ayuda? (Estere 9:10)
6. N’cholengedwa chauzimu chamtundu wanji chomwe chinakhudza milomo ya Yesaya ndi khala lamoto kuti akwaniritse ntchito yake yauneneri? (Yesaya 6:6)
7. Kodi ndani anali kapitawo wa Herode amene mkazi wake Yohana, anatumikira Yesu? (Luka 8:3)
8. Kodi ndi malo audindo wotani amene Paulo analimbikitsa amuna mumpingo kukalamira? (1 Timoteo 3:1)
9. Tchulani mayina a mitsinje inayi yomwe inapatuka kuchokera mumtsinje umene “unatuluka m’Edene”? (Genesis 2:10-14)
10. Kodi Paulo ananena kuti chotupitsa pang’ono chingathe kuchita chiyani? (Agalatiya 5:9)
11. Tchulani mayina a ana aamuna atatu a Nowa, komwe kunachokera ‘anthu onse a padziko lapansi?’ (Genesis 9:18, 19)
12. Kodi atate ake a mneneri Samueli anali ayani? (1 Samueli 1:19, 20)
13. Kodi ndi mumzinda uti wa m’phepete mwa Chigwa cha Yezreeli kumene nkhondo zambiri zazikulu zinamenyedwera? (Oweruza 5:19)
14. Atapulumutsidwa chifukwa cha kuchenjera kwawo, kodi ndi ntchito yotani imene Agibeoni anapatsidwa kuti achite? (Yoswa 9:21)
15. Kodi ophunzira 12 amene Yesu anadzisankhira anapatsidwa dzina lotani? (Mateyu 10:2)
16. Kodi ndi mayina ake okha aulemu ati amene Yesu anauza ophunzira ake kuti sayenera kutchedwa? (Mateyu 23:8, 10)
17. Tchulani dziko limene Paulo analiko pamene ankalemba buku la Ahebri? (Ahebri 13:24)
18. Kodi ndi mawu otani amene Yobu anagwiritsa ntchito kutanthauza kuti anatsala pang’ono kufa? (Yobu 19:20)
19. M’nthaŵi zakale, kodi n’kuti kumene anali kuchotsa njere ku makoko ndi gaga? (Rute 3:3)
20. Kodi abale a Yosefe anamuda pa zifukwa zotani? (Genesis 37:3-11)
Mayankho patsamba 29
Mayankho
1. “Indetu ndinena kwa inu”
2. Amuna aliŵiro ndiponso olimba mtima ndi amphamvu a mtundu wa Gadi amene anagwirizana ndi Davide m’chipululu pa nthaŵi imene iye anali pampanipani chifukwa cha Mfumu Sauli
3. Amayi awo, Zeruya
4. Kupirira kufikira chimaliziro
5. Khumi
6. Mserafi
7. Kuza
8. “Udindo wa woyang’anira”
9. Pisoni, Gihoni, Hidikeli, ndi Firate
10. Kutupitsa mtanda wonse
11. Semu, Hamu ndi Yafeti
12. Elikana
13. Megido
14. Anasanduka “akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse ndi paguwa la Yehova”
15. Atumwi
16. Rabi ndi M’tsogoleri
17. Italiya
18. “Ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga”
19. Popunthirapo
20. Chifukwa chakuti atate ake anali kum’konda kwambiri ndiponso chifukwa cha maloto amene analota